سَبِّحِ اسْمَ رَبِّكَ الْأَعْلَى (1) Lemekeza dzina la Ambuye wako wapamwambamwamba |
الَّذِي خَلَقَ فَسَوَّىٰ (2) Amene adalenga zonse ndi kuzikonza bwinobwino |
وَالَّذِي قَدَّرَ فَهَدَىٰ (3) Amene adalamula tsogolo lawo ndi kuwatsogolera |
وَالَّذِي أَخْرَجَ الْمَرْعَىٰ (4) Amene amameretsa msipu |
فَجَعَلَهُ غُثَاءً أَحْوَىٰ (5) Ndipo amausanduliza kukhala udzu ouma |
سَنُقْرِئُكَ فَلَا تَنسَىٰ (6) Tidzakuphunzitsa kulakatula chivumbulutso chathu ndipo sudzaiwala |
إِلَّا مَا شَاءَ اللَّهُ ۚ إِنَّهُ يَعْلَمُ الْجَهْرَ وَمَا يَخْفَىٰ (7) Kupatula chokhacho chimene Mulungu amafuna. Ndithudi Iye amadziwa chilichonse chooneka ndi chobisika |
وَنُيَسِّرُكَ لِلْيُسْرَىٰ (8) Ndipo Ife tidzakufupikitsira, m’njira yaifupi |
فَذَكِّرْ إِن نَّفَعَتِ الذِّكْرَىٰ (9) Motero kumbutsa mwina chikumbutso chingawathandize |
سَيَذَّكَّرُ مَن يَخْشَىٰ (10) Chikumbutso chidzalandiridwa ndi iye amene amaopa Mulungu |
وَيَتَجَنَّبُهَا الْأَشْقَى (11) Koma munthu wochimwa adzachisiya |
الَّذِي يَصْلَى النَّارَ الْكُبْرَىٰ (12) Amene adzaponyedwa mu ng’anjo yamoto ndi kulawa ululu wake |
ثُمَّ لَا يَمُوتُ فِيهَا وَلَا يَحْيَىٰ (13) Mmene iye sadzafa kapena kukhala ndi moyo |
قَدْ أَفْلَحَ مَن تَزَكَّىٰ (14) Zoonadi iye amene adziyeretsa adzakhala wopambana |
وَذَكَرَ اسْمَ رَبِّهِ فَصَلَّىٰ (15) Amene amakumbukira dzina la Ambuye wake ndipo amapemphera panthawi yake |
بَلْ تُؤْثِرُونَ الْحَيَاةَ الدُّنْيَا (16) Iyayi, koma inu mumasangalala ndi zinthu za m’moyo uno |
وَالْآخِرَةُ خَيْرٌ وَأَبْقَىٰ (17) Ndipo moyo umene uli nkudza ndi wabwino ndi wosatha |
إِنَّ هَٰذَا لَفِي الصُّحُفِ الْأُولَىٰ (18) Ndithudi! Zonsezi zidalembedwa mu Mabuku akale a Mulungu |
صُحُفِ إِبْرَاهِيمَ وَمُوسَىٰ (19) Mabuku a Abrahamu ndi Mose |