The Quran in Chichewa - Surah Takathur translated into Chichewa, Surah At-Takathur in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Takathur in Chichewa - نيانجا, Verses 8 - Surah Number 102 - Page 600.
أَلْهَاكُمُ التَّكَاثُرُ (1) Mpikisano wosonkhanitsa chuma cha padziko wakutangwanikitsani inu |
حَتَّىٰ زُرْتُمُ الْمَقَابِرَ (2) Mpaka pamene inu mulowa m’manda |
كَلَّا سَوْفَ تَعْلَمُونَ (3) Iyayi! Inu mudzadziwa |
ثُمَّ كَلَّا سَوْفَ تَعْلَمُونَ (4) Kachiwiri, Iyayi! Inu mudzadziwa |
كَلَّا لَوْ تَعْلَمُونَ عِلْمَ الْيَقِينِ (5) Iyayi! Inu mukanadziwa kwenikweni |
لَتَرَوُنَّ الْجَحِيمَ (6) Ndithudi inu mudzaona moto woyaka |
ثُمَّ لَتَرَوُنَّهَا عَيْنَ الْيَقِينِ (7) Kachiwiri inu mudzauona ndi maso anu |
ثُمَّ لَتُسْأَلُنَّ يَوْمَئِذٍ عَنِ النَّعِيمِ (8) Ndipo patsiku limeneli inu mudzafunsidwa za chisangalalo chimene munali kuchita |