The Quran in Chichewa - Surah Qariah translated into Chichewa, Surah Al-Qariah in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Qariah in Chichewa - نيانجا, Verses 11 - Surah Number 101 - Page 600.
الْقَارِعَةُ (1) Tsiku louka kwa akufa |
مَا الْقَارِعَةُ (2) Kodi tsiku louka kwa akufa ndi chiyani |
وَمَا أَدْرَاكَ مَا الْقَارِعَةُ (3) Kodi ndi chiyani chimene chidzakuuze iwe kuti tsiku louka kwa akufa ndi chiani |
يَوْمَ يَكُونُ النَّاسُ كَالْفَرَاشِ الْمَبْثُوثِ (4) Ndi tsiku limene anthu adzakhala ngati dzombe louluka paliponse |
وَتَكُونُ الْجِبَالُ كَالْعِهْنِ الْمَنفُوشِ (5) Ndi mapiri adzakhala ngati fumbefumbe za ubweya |
فَأَمَّا مَن ثَقُلَتْ مَوَازِينُهُ (6) Ndipo iye amene muyeso wake wa ntchito zabwino udzakhala wolemera |
فَهُوَ فِي عِيشَةٍ رَّاضِيَةٍ (7) Adzakhala ndi moyo wa chimwemwe ndi chisangalalo |
وَأَمَّا مَنْ خَفَّتْ مَوَازِينُهُ (8) Koma iye amene muyeso wake wa ntchito zabwino udzapezeka wopepuka |
فَأُمُّهُ هَاوِيَةٌ (9) Mudzi wake udzakhala dzenje lamoto |
وَمَا أَدْرَاكَ مَا هِيَهْ (10) Kodi ndi chiyani chimene chidzakuuze zinthu zonsezi |
نَارٌ حَامِيَةٌ (11) Ndi moto wa malawi osatha |