وَالْمُرْسَلَاتِ عُرْفًا (1) Pali mphepo imene imatsatana pafupipafupi |
فَالْعَاصِفَاتِ عَصْفًا (2) Pali mphepo ya mkuntho |
وَالنَّاشِرَاتِ نَشْرًا (3) Pali mphepo imene imamwaza mitambo ndi mvula |
فَالْفَارِقَاتِ فَرْقًا (4) Pali mavesi amene amasiyanitsa chabwino |
فَالْمُلْقِيَاتِ ذِكْرًا (5) Pali angelo amene amabweretsa chivumbulutso kwa Atumwi |
عُذْرًا أَوْ نُذْرًا (6) Kuthetsa kukangana kapena kuwachenjeza |
إِنَّمَا تُوعَدُونَ لَوَاقِعٌ (7) Ndithudi zonse zimene mwalonjezedwa zidzachitika |
فَإِذَا النُّجُومُ طُمِسَتْ (8) Pamene nyenyezi zidetsedwa |
وَإِذَا السَّمَاءُ فُرِجَتْ (9) Ndi pamene thambo la kumwamba ling’ambika pakati |
وَإِذَا الْجِبَالُ نُسِفَتْ (10) Ndi pamene mapiri aphwanyika kukhala fumbi |
وَإِذَا الرُّسُلُ أُقِّتَتْ (11) Ndi pamene Atumwi onse asonkhanitsidwa kukhala pamalo amodzi |
لِأَيِّ يَوْمٍ أُجِّلَتْ (12) Kodi ndi tsiku liti limene izi zidzachitike |
لِيَوْمِ الْفَصْلِ (13) Lidzakhala tsiku la chiweruzo |
وَمَا أَدْرَاكَ مَا يَوْمُ الْفَصْلِ (14) Kodi ndi chiyani chidzakudziwitse zatsiku la chiweruzo |
وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (15) Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira |
أَلَمْ نُهْلِكِ الْأَوَّلِينَ (16) Kodi Ife sitinaononge anthu a makedzana |
ثُمَّ نُتْبِعُهُمُ الْآخِرِينَ (17) Kotero tidzaipanga mibadwo yotsatira kuti ione zomwezo |
كَذَٰلِكَ نَفْعَلُ بِالْمُجْرِمِينَ (18) Mmenemu ndi mmene timakhaulitsira anthu ochita zoipa |
وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (19) Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira |
أَلَمْ نَخْلُقكُّم مِّن مَّاءٍ مَّهِينٍ (20) Kodi sitidakulengeni inu kuchokera ku madzi onyozeka |
فَجَعَلْنَاهُ فِي قَرَارٍ مَّكِينٍ (21) Amene tidasunga pamalo okhazikika |
إِلَىٰ قَدَرٍ مَّعْلُومٍ (22) Mpaka nthawi yake itakwana |
فَقَدَرْنَا فَنِعْمَ الْقَادِرُونَ (23) Motero Ife tinayesa ndipo Ife wodziwa kuyesa |
وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (24) Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira |
أَلَمْ نَجْعَلِ الْأَرْضَ كِفَاتًا (25) Kodi Ife sitinapange nthaka ngati malo okumaniranamo |
أَحْيَاءً وَأَمْوَاتًا (26) Amoyo ndi akufa |
وَجَعَلْنَا فِيهَا رَوَاسِيَ شَامِخَاتٍ وَأَسْقَيْنَاكُم مَّاءً فُرَاتًا (27) Ndipo tidalenga Al Mursalat 635 mapiri atali pa dziko ndi kukupatsani madzi okoma kuti muzimwa |
وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (28) Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira |
انطَلِقُوا إِلَىٰ مَا كُنتُم بِهِ تُكَذِّبُونَ (29) (Zidzanenedwa kuti): “Pitani ku chilango chimene munkati sichidzabwera!” |
انطَلِقُوا إِلَىٰ ظِلٍّ ذِي ثَلَاثِ شُعَبٍ (30) Pitani inu mu chithunzi, mu magulu atatu |
لَّا ظَلِيلٍ وَلَا يُغْنِي مِنَ اللَّهَبِ (31) Opanda mthunzi kapena pokhala pokutetezani ku malawi a moto |
إِنَّهَا تَرْمِي بِشَرَرٍ كَالْقَصْرِ (32) Ndithudi! Umatulutsa malawi ake akulu akulu ngati nyumba zachifumu |
كَأَنَّهُ جِمَالَتٌ صُفْرٌ (33) Ndipo ooneka ngati ngamira ya chikasu |
وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (34) Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira |
هَٰذَا يَوْمُ لَا يَنطِقُونَ (35) Patsiku limeneli iwo sadzatha kulankhula |
وَلَا يُؤْذَنُ لَهُمْ فَيَعْتَذِرُونَ (36) Ndipo sadzaloledwa kuti apereke chidandaulo |
وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (37) Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira |
هَٰذَا يَوْمُ الْفَصْلِ ۖ جَمَعْنَاكُمْ وَالْأَوَّلِينَ (38) Limeneli ndilo tsiku la chiweruzo. Ife takusonkhanitsani nonse pamodzi ndi anthu a makedzana |
فَإِن كَانَ لَكُمْ كَيْدٌ فَكِيدُونِ (39) Tsopano ngati inu muli ndi chiwembu, chitani chiwembu chanu kwa Ine |
وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (40) Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira |
إِنَّ الْمُتَّقِينَ فِي ظِلَالٍ وَعُيُونٍ (41) Ndithudi anthu angwiro adzakhala mu mthunzi wozizira ndi pa akasupe |
وَفَوَاكِهَ مِمَّا يَشْتَهُونَ (42) Ndi zipatso zimene afuna kukhosi kwawo |
كُلُوا وَاشْرَبُوا هَنِيئًا بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (43) Idyani ndipo imwani mosangalala chifukwa cha zimene mudachita |
إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ (44) Ndithudi, mmenemo ndi mmene timalipirira anthu angwiro |
وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (45) Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira |
كُلُوا وَتَمَتَّعُوا قَلِيلًا إِنَّكُم مُّجْرِمُونَ (46) Idyani ndipo musangalale kwa kanthawi kochepa. Ndithudi inu ndinu oipa kwambiri |
وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (47) Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira |
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ارْكَعُوا لَا يَرْكَعُونَ (48) Ndipo zikanenedwa kwa iwo kuti: “Weramani.” Iwo amakana kutero |
وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (49) Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira |
فَبِأَيِّ حَدِيثٍ بَعْدَهُ يُؤْمِنُونَ (50) Kodi ndi Uthenga uti woposa uwu umene adzaukhulupirire |