| وَالْمُرْسَلَاتِ عُرْفًا (1) Pali mphepo imene imatsatana pafupipafupi
 | 
| فَالْعَاصِفَاتِ عَصْفًا (2) Pali mphepo ya mkuntho
 | 
| وَالنَّاشِرَاتِ نَشْرًا (3) Pali mphepo imene imamwaza mitambo ndi mvula
 | 
| فَالْفَارِقَاتِ فَرْقًا (4) Pali mavesi amene amasiyanitsa chabwino
 | 
| فَالْمُلْقِيَاتِ ذِكْرًا (5) Pali angelo amene amabweretsa chivumbulutso kwa Atumwi
 | 
| عُذْرًا أَوْ نُذْرًا (6) Kuthetsa kukangana kapena kuwachenjeza
 | 
| إِنَّمَا تُوعَدُونَ لَوَاقِعٌ (7) Ndithudi zonse zimene mwalonjezedwa zidzachitika
 | 
| فَإِذَا النُّجُومُ طُمِسَتْ (8) Pamene nyenyezi zidetsedwa
 | 
| وَإِذَا السَّمَاءُ فُرِجَتْ (9) Ndi pamene thambo la kumwamba ling’ambika pakati
 | 
| وَإِذَا الْجِبَالُ نُسِفَتْ (10) Ndi pamene mapiri aphwanyika kukhala fumbi
 | 
| وَإِذَا الرُّسُلُ أُقِّتَتْ (11) Ndi pamene Atumwi onse asonkhanitsidwa kukhala pamalo amodzi
 | 
| لِأَيِّ يَوْمٍ أُجِّلَتْ (12) Kodi ndi tsiku liti limene izi zidzachitike
 | 
| لِيَوْمِ الْفَصْلِ (13) Lidzakhala tsiku la chiweruzo
 | 
| وَمَا أَدْرَاكَ مَا يَوْمُ الْفَصْلِ (14) Kodi ndi chiyani chidzakudziwitse zatsiku la chiweruzo
 | 
| وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (15) Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira
 | 
| أَلَمْ نُهْلِكِ الْأَوَّلِينَ (16) Kodi Ife sitinaononge anthu a makedzana
 | 
| ثُمَّ نُتْبِعُهُمُ الْآخِرِينَ (17) Kotero tidzaipanga mibadwo yotsatira kuti ione zomwezo
 | 
| كَذَٰلِكَ نَفْعَلُ بِالْمُجْرِمِينَ (18) Mmenemu ndi mmene timakhaulitsira anthu ochita zoipa
 | 
| وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (19) Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira
 | 
| أَلَمْ نَخْلُقكُّم مِّن مَّاءٍ مَّهِينٍ (20) Kodi sitidakulengeni inu kuchokera ku madzi onyozeka
 | 
| فَجَعَلْنَاهُ فِي قَرَارٍ مَّكِينٍ (21) Amene tidasunga pamalo okhazikika
 | 
| إِلَىٰ قَدَرٍ مَّعْلُومٍ (22) Mpaka nthawi yake itakwana
 | 
| فَقَدَرْنَا فَنِعْمَ الْقَادِرُونَ (23) Motero Ife tinayesa ndipo Ife wodziwa kuyesa
 | 
| وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (24) Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira
 | 
| أَلَمْ نَجْعَلِ الْأَرْضَ كِفَاتًا (25) Kodi Ife sitinapange nthaka ngati malo okumaniranamo
 | 
| أَحْيَاءً وَأَمْوَاتًا (26) Amoyo ndi akufa
 | 
| وَجَعَلْنَا فِيهَا رَوَاسِيَ شَامِخَاتٍ وَأَسْقَيْنَاكُم مَّاءً فُرَاتًا (27) Ndipo tidalenga Al Mursalat	635 mapiri atali pa dziko ndi kukupatsani madzi okoma kuti muzimwa
 | 
| وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (28) Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira
 | 
| انطَلِقُوا إِلَىٰ مَا كُنتُم بِهِ تُكَذِّبُونَ (29) (Zidzanenedwa kuti): “Pitani ku chilango chimene munkati sichidzabwera!”
 | 
| انطَلِقُوا إِلَىٰ ظِلٍّ ذِي ثَلَاثِ شُعَبٍ (30) Pitani inu mu chithunzi, mu magulu atatu
 | 
| لَّا ظَلِيلٍ وَلَا يُغْنِي مِنَ اللَّهَبِ (31) Opanda mthunzi kapena pokhala pokutetezani ku malawi a moto
 | 
| إِنَّهَا تَرْمِي بِشَرَرٍ كَالْقَصْرِ (32) Ndithudi! Umatulutsa malawi ake akulu akulu ngati nyumba zachifumu
 | 
| كَأَنَّهُ جِمَالَتٌ صُفْرٌ (33) Ndipo ooneka ngati ngamira ya chikasu
 | 
| وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (34) Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira
 | 
| هَٰذَا يَوْمُ لَا يَنطِقُونَ (35) Patsiku limeneli iwo sadzatha kulankhula
 | 
| وَلَا يُؤْذَنُ لَهُمْ فَيَعْتَذِرُونَ (36) Ndipo sadzaloledwa kuti apereke chidandaulo
 | 
| وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (37) Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira
 | 
| هَٰذَا يَوْمُ الْفَصْلِ ۖ جَمَعْنَاكُمْ وَالْأَوَّلِينَ (38) Limeneli ndilo tsiku la chiweruzo. Ife takusonkhanitsani nonse pamodzi ndi anthu a makedzana
 | 
| فَإِن كَانَ لَكُمْ كَيْدٌ فَكِيدُونِ (39) Tsopano ngati inu muli ndi chiwembu, chitani chiwembu chanu kwa Ine
 | 
| وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (40) Tsoka pa tsiku limeneli kwa anthu osakhulupirira
 | 
| إِنَّ الْمُتَّقِينَ فِي ظِلَالٍ وَعُيُونٍ (41) Ndithudi anthu angwiro adzakhala mu mthunzi wozizira ndi pa akasupe
 | 
| وَفَوَاكِهَ مِمَّا يَشْتَهُونَ (42) Ndi zipatso zimene afuna kukhosi kwawo
 | 
| كُلُوا وَاشْرَبُوا هَنِيئًا بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (43) Idyani ndipo imwani mosangalala chifukwa cha zimene mudachita
 | 
| إِنَّا كَذَٰلِكَ نَجْزِي الْمُحْسِنِينَ (44) Ndithudi, mmenemo ndi mmene timalipirira anthu angwiro
 | 
| وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (45) Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira
 | 
| كُلُوا وَتَمَتَّعُوا قَلِيلًا إِنَّكُم مُّجْرِمُونَ (46) Idyani ndipo musangalale kwa kanthawi kochepa. Ndithudi inu ndinu oipa kwambiri
 | 
| وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (47) Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira
 | 
| وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ ارْكَعُوا لَا يَرْكَعُونَ (48) Ndipo zikanenedwa kwa iwo kuti: “Weramani.” Iwo amakana kutero
 | 
| وَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (49) Tsoka pa tsikuli kwa anthu osakhulupirira
 | 
| فَبِأَيِّ حَدِيثٍ بَعْدَهُ يُؤْمِنُونَ (50) Kodi ndi Uthenga uti woposa uwu umene adzaukhulupirire
 |