The Quran in Chichewa - Surah Duha translated into Chichewa, Surah Ad-Dhuha in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Duha in Chichewa - نيانجا, Verses 11 - Surah Number 93 - Page 596.

| وَالضُّحَىٰ (1) Pali usana |
| وَاللَّيْلِ إِذَا سَجَىٰ (2) Ndi pali usiku pamene ulipo |
| مَا وَدَّعَكَ رَبُّكَ وَمَا قَلَىٰ (3) Ambuye wako sadakutaye iwe ndiponso sakudana nawe ayi |
| وَلَلْآخِرَةُ خَيْرٌ لَّكَ مِنَ الْأُولَىٰ (4) Ndipo, ndithudi, moyo umene uli nkudza ndi wabwino kwa iwe kuposa moyo uno |
| وَلَسَوْفَ يُعْطِيكَ رَبُّكَ فَتَرْضَىٰ (5) Ndithudi Ambuye wako adzakupatsa, ndipo iwe chidzakukondweretsa |
| أَلَمْ يَجِدْكَ يَتِيمًا فَآوَىٰ (6) Kodi sadakupeze iwe uli wa masiye ndipo adakupatsa malo okhala |
| وَوَجَدَكَ ضَالًّا فَهَدَىٰ (7) Kodi sadakupeze uli wosochera ndipo Iye adakutsogolera |
| وَوَجَدَكَ عَائِلًا فَأَغْنَىٰ (8) Kodi sadakupeze iwe waumphawi ndipo adakulemeretsa |
| فَأَمَّا الْيَتِيمَ فَلَا تَقْهَرْ (9) Motero iwe usapondereze pansi mwana wa masiye |
| وَأَمَّا السَّائِلَ فَلَا تَنْهَرْ (10) Ndipo usapirikitse munthu wopempha |
| وَأَمَّا بِنِعْمَةِ رَبِّكَ فَحَدِّثْ (11) Koma lengeza chisomo cha a Ambuye wako |