لَا أُقْسِمُ بِيَوْمِ الْقِيَامَةِ (1) Ine ndilumbira pali tsiku lachiweruzo |
وَلَا أُقْسِمُ بِالنَّفْسِ اللَّوَّامَةِ (2) Ndipo ndilumbira pali munthu amene amadzidzudzula yekha |
أَيَحْسَبُ الْإِنسَانُ أَلَّن نَّجْمَعَ عِظَامَهُ (3) Kodi munthu amaganiza kuti Ife sitidzalumikiza mafupa ake |
بَلَىٰ قَادِرِينَ عَلَىٰ أَن نُّسَوِّيَ بَنَانَهُ (4) Inde Ife tikhoza kulumikiza mwaubwino nsonga za zala zake |
بَلْ يُرِيدُ الْإِنسَانُ لِيَفْجُرَ أَمَامَهُ (5) Ngakhale tero, munthu amafuna kupitiliza kuchita zoipa |
يَسْأَلُ أَيَّانَ يَوْمُ الْقِيَامَةِ (6) Iye amafunsa: “Kodi zimenezi zidzachitika liti?” |
فَإِذَا بَرِقَ الْبَصَرُ (7) Motero pamene maso adzathodwa |
وَخَسَفَ الْقَمَرُ (8) Ndipo pamene mwezi udetsedwa |
وَجُمِعَ الشَّمْسُ وَالْقَمَرُ (9) Pamene dzuwa ndi mwezi zidzakumana |
يَقُولُ الْإِنسَانُ يَوْمَئِذٍ أَيْنَ الْمَفَرُّ (10) Patsikuli munthu adzafunsa kuti: “Kodi ndithawira kuti tsopano?” |
كَلَّا لَا وَزَرَ (11) Iai! Kulibe malo othawirako |
إِلَىٰ رَبِّكَ يَوْمَئِذٍ الْمُسْتَقَرُّ (12) Ndi kwa Ambuye wako kokha kumene kudzakhala kothawira |
يُنَبَّأُ الْإِنسَانُ يَوْمَئِذٍ بِمَا قَدَّمَ وَأَخَّرَ (13) Patsiku limeneli, munthu adzauzidwa zonse zimene adachita kuyambira poyamba mpaka pomaliza |
بَلِ الْإِنسَانُ عَلَىٰ نَفْسِهِ بَصِيرَةٌ (14) Iai! Munthu adzadzichitira umboni wodzineneza yekha |
وَلَوْ أَلْقَىٰ مَعَاذِيرَهُ (15) Ngakhale kuti iye azidzayesa kudzipulumutsa yekha |
لَا تُحَرِّكْ بِهِ لِسَانَكَ لِتَعْجَلَ بِهِ (16) Usagwedeze lilime lako zokhudza Korani ponena mofulumira |
إِنَّ عَلَيْنَا جَمْعَهُ وَقُرْآنَهُ (17) Ndi udindo wathu kuisonkhanitsa ndi kukupatsa nzeru kuilakatula iyo |
فَإِذَا قَرَأْنَاهُ فَاتَّبِعْ قُرْآنَهُ (18) Ndipo pamene talakatula, tsatira mwandondomeko kalakatulidwe kake |
ثُمَّ إِنَّ عَلَيْنَا بَيَانَهُ (19) Ndi udindo wathu kukufotokozera tanthauzo lake |
كَلَّا بَلْ تُحِبُّونَ الْعَاجِلَةَ (20) Iyayi!Komainumukondamoyowothamsanga |
وَتَذَرُونَ الْآخِرَةَ (21) Ndipo simufuna kulabadira za moyo umene uli nkudza |
وُجُوهٌ يَوْمَئِذٍ نَّاضِرَةٌ (22) Nkhope zina, pa tsiku limeneli, zidzakhala zowala ndi chisangalalo |
إِلَىٰ رَبِّهَا نَاظِرَةٌ (23) Zili kuyang’ana kwa Ambuye wawo |
وَوُجُوهٌ يَوْمَئِذٍ بَاسِرَةٌ (24) Ndipo nkhope zina, patsiku limeneli, zidzakhala zachisoni |
تَظُنُّ أَن يُفْعَلَ بِهَا فَاقِرَةٌ (25) Pozindikira kuti chilango chowawa chidzagwa pa iwo |
كَلَّا إِذَا بَلَغَتِ التَّرَاقِيَ (26) Iyayi, pamene ufika mpaka pa khosi |
وَقِيلَ مَنْ ۜ رَاقٍ (27) Ndipo kudzanenedwa kuti: “Kodi palibe woti angamuchize ndi kumupulumutsa ku imfa?” |
وَظَنَّ أَنَّهُ الْفِرَاقُ (28) Ndipo iye adzadziwa kuti awa ndi mathero a moyo wake |
وَالْتَفَّتِ السَّاقُ بِالسَّاقِ (29) Ndipo mwendo udzatembenuzika pa unzake |
إِلَىٰ رَبِّكَ يَوْمَئِذٍ الْمَسَاقُ (30) Tsiku limeneli zonse zidzabwerera kwa Ambuye wako |
فَلَا صَدَّقَ وَلَا صَلَّىٰ (31) Iye sanali kuvomereza chilungamo kapena kupemphera |
وَلَٰكِن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ (32) Koma m’malo mwake adakana choonadi ndi kubwerera m’mbuyo |
ثُمَّ ذَهَبَ إِلَىٰ أَهْلِهِ يَتَمَطَّىٰ (33) Ndipo iye anapita kubanja lake monyada ali kudziyamikila yekha |
أَوْلَىٰ لَكَ فَأَوْلَىٰ (34) Tsoka kwa iwe. Ndiponso tsoka kwa iwe |
ثُمَّ أَوْلَىٰ لَكَ فَأَوْلَىٰ (35) Kachiwiri tsoka lili pafupi ndi iwe, tsopano tsoka lili pafupi |
أَيَحْسَبُ الْإِنسَانُ أَن يُتْرَكَ سُدًى (36) Kodi munthu amaganiza kuti tidzangomulekerera kuti azichita chilichonse chimene afuna |
أَلَمْ يَكُ نُطْفَةً مِّن مَّنِيٍّ يُمْنَىٰ (37) Kodi iye sanali dontho la umuna limene lidatuluka |
ثُمَّ كَانَ عَلَقَةً فَخَلَقَ فَسَوَّىٰ (38) Ndipo iye adakhala kam’bulu ka magazi. Ndipo Mulungu adamuumba ndipo adamukonza m’maonekedwe okongola |
فَجَعَلَ مِنْهُ الزَّوْجَيْنِ الذَّكَرَ وَالْأُنثَىٰ (39) Ndipo adamulenga m’mitundu iwiri, mwamuna ndi mkazi |
أَلَيْسَ ذَٰلِكَ بِقَادِرٍ عَلَىٰ أَن يُحْيِيَ الْمَوْتَىٰ (40) Kodi Iye alibe mphamvu yopereka moyo kwa anthu akufa |