×

Surah Al-Muddaththir in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Muddathir

Translation of the Meanings of Surah Muddathir in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Muddathir translated into Chichewa, Surah Al-Muddaththir in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Muddathir in Chichewa - نيانجا, Verses 56 - Surah Number 74 - Page 575.

بسم الله الرحمن الرحيم

يَا أَيُّهَا الْمُدَّثِّرُ (1)
ohiweamenewakutidwa
قُمْ فَأَنذِرْ (2)
Dzukandikuperekachenjezo
وَرَبَّكَ فَكَبِّرْ (3)
Ndipo lemekeza Ambuye wako
وَثِيَابَكَ فَطَهِّرْ (4)
Ndipo yeretsa zovala zako
وَالرُّجْزَ فَاهْجُرْ (5)
Ndipo pewa zonse za mafano
وَلَا تَمْنُن تَسْتَكْثِرُ (6)
Ndipo usapereke thandizo ndi cholinga chopezamo cholowa
وَلِرَبِّكَ فَاصْبِرْ (7)
Ndipo khala wopirira chifukwa cha Ambuye wako
فَإِذَا نُقِرَ فِي النَّاقُورِ (8)
Ndipo pamene lipenga lidzalira
فَذَٰلِكَ يَوْمَئِذٍ يَوْمٌ عَسِيرٌ (9)
Ndithudi limeneli lidzakhala tsiku loopsa
عَلَى الْكَافِرِينَ غَيْرُ يَسِيرٍ (10)
Tsiku lamavuto kwa anthu onse osakhulupirira
ذَرْنِي وَمَنْ خَلَقْتُ وَحِيدًا (11)
Ndisiye ndekha kuthana ndi munthu amene ndidamulenga ndekha
وَجَعَلْتُ لَهُ مَالًا مَّمْدُودًا (12)
Ndipo ndidamupatsa chuma chosawerengeka
وَبَنِينَ شُهُودًا (13)
Ndi ana okhala pambali pake
وَمَهَّدتُّ لَهُ تَمْهِيدًا (14)
Ndipo Ine ndidamuchitira zonse kuti zikhale zolongosoka ndi zapafupi
ثُمَّ يَطْمَعُ أَنْ أَزِيدَ (15)
Koma nthawi zonse amafuna kuti ndizimupatsabe zinthu zambiri
كَلَّا ۖ إِنَّهُ كَانَ لِآيَاتِنَا عَنِيدًا (16)
Kosatheka! Ndithudi iye wakhala ali kuchitira mwano chivumbulutso chathu
سَأُرْهِقُهُ صَعُودًا (17)
Ine ndidzamukhaulitsa pomupatsa chilango chowawa
إِنَّهُ فَكَّرَ وَقَدَّرَ (18)
Ndithudi iye adaganiza ndipo adakonza chiwembu
فَقُتِلَ كَيْفَ قَدَّرَ (19)
Ndipo ayenera kutembererewa chifukwa cha chiwembu chake
ثُمَّ قُتِلَ كَيْفَ قَدَّرَ (20)
Motero iye ayenera kutembereredwa chifukwa cha chiwembu chake
ثُمَّ نَظَرَ (21)
Ndipo iye anayang’ana
ثُمَّ عَبَسَ وَبَسَرَ (22)
Ndipo iye adachita matsinya ndipo anaonetsa kuipidwa
ثُمَّ أَدْبَرَ وَاسْتَكْبَرَ (23)
Kenaka adatembenukira kumbali modzikweza
فَقَالَ إِنْ هَٰذَا إِلَّا سِحْرٌ يُؤْثَرُ (24)
Ndipo iye adati: “Ichi sichina koma matsenga a anthu a amakedzana!”
إِنْ هَٰذَا إِلَّا قَوْلُ الْبَشَرِ (25)
“Ichi sichina koma mawu a munthu chabe.”
سَأُصْلِيهِ سَقَرَ (26)
Ine ndidzamuponya iye ku Gahena
وَمَا أَدْرَاكَ مَا سَقَرُ (27)
Kodi chidzakudziwitsa kuti moto wa ku Gahena ndi chiani
لَا تُبْقِي وَلَا تَذَرُ (28)
Iwo susunga kapena kusiya
لَوَّاحَةٌ لِّلْبَشَرِ (29)
Umatentha matupi
عَلَيْهَا تِسْعَةَ عَشَرَ (30)
Umasamalidwandiangelokhumindiasanundianayi
وَمَا جَعَلْنَا أَصْحَابَ النَّارِ إِلَّا مَلَائِكَةً ۙ وَمَا جَعَلْنَا عِدَّتَهُمْ إِلَّا فِتْنَةً لِّلَّذِينَ كَفَرُوا لِيَسْتَيْقِنَ الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ وَيَزْدَادَ الَّذِينَ آمَنُوا إِيمَانًا ۙ وَلَا يَرْتَابَ الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ وَالْمُؤْمِنُونَ ۙ وَلِيَقُولَ الَّذِينَ فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٌ وَالْكَافِرُونَ مَاذَا أَرَادَ اللَّهُ بِهَٰذَا مَثَلًا ۚ كَذَٰلِكَ يُضِلُّ اللَّهُ مَن يَشَاءُ وَيَهْدِي مَن يَشَاءُ ۚ وَمَا يَعْلَمُ جُنُودَ رَبِّكَ إِلَّا هُوَ ۚ وَمَا هِيَ إِلَّا ذِكْرَىٰ لِلْبَشَرِ (31)
Ife sitidasankhe wina aliyense koma angelo kuti aziyang’anira moto ndipo tinakhazikitsa chiwerengero chawo ngati mayesero kwa anthu osakhulupirira, kuti iwo onse amene alandira mawu a Mulungu akhulupirire ndi kuti anthu okhulupirira m’choonadi apitirize chikhulupiriro chawo; kuti iwo amene adalandira kale mawu a Mulungu ndiponso anthu onse okhulupirira moona asakhale ndi chikaiko china chilichonse; ndipo kuti onse amene m’mitima mwawo muli matenda pamodzi ndi anthu osakhulupirira anganene kuti: “Kodi Mulungu afuna kutanthauza chiyani pa chitsanzo chotere?” Mmenemo ndi mmene Mulungu amasokeretsera munthu aliyense amene Iye wamufuna ndi kutsogolera aliyense amene Iye wamufuna. Palibe munthu amene amadziwa asirikali a Ambuye wako kupatula Iye mwini. Ichi si china chilichonse koma chikumbutso kwa anthu onse
كَلَّا وَالْقَمَرِ (32)
Iyayi, ndilumbira pali mwezi
وَاللَّيْلِ إِذْ أَدْبَرَ (33)
Ndi pali usiku pamene uli n’kutha
وَالصُّبْحِ إِذَا أَسْفَرَ (34)
Ndi pali m’mbandakucha pamene uli n’kudza
إِنَّهَا لَإِحْدَى الْكُبَرِ (35)
Ndithudi ili ndi limodzi la masoka akuluakulu
نَذِيرًا لِّلْبَشَرِ (36)
Ndi chenjezo kwa anthu onse
لِمَن شَاءَ مِنكُمْ أَن يَتَقَدَّمَ أَوْ يَتَأَخَّرَ (37)
Kwa yense wa inu amene afuna kupitirirabe mtsogolo kapena afuna kutsalira m’mbuyo
كُلُّ نَفْسٍ بِمَا كَسَبَتْ رَهِينَةٌ (38)
Munthu aliyense adzafunsidwa molingana ndi ntchito zake
إِلَّا أَصْحَابَ الْيَمِينِ (39)
Kupatula iwo amene adzakhala kudzanja lamanja
فِي جَنَّاتٍ يَتَسَاءَلُونَ (40)
M’minda, iwo azidzafunsana wina ndi mnzake. Qiyamah
عَنِ الْمُجْرِمِينَ (41)
Za anthu ochimwa kuti
مَا سَلَكَكُمْ فِي سَقَرَ (42)
Kodi ndi chiyani chimene chakulowetsani inu ku moto
قَالُوا لَمْ نَكُ مِنَ الْمُصَلِّينَ (43)
Iwo adzayankha nati: “Ife sitimapemphera.”
وَلَمْ نَكُ نُطْعِمُ الْمِسْكِينَ (44)
Ndiponso sitimadyetsa anthu a njala
وَكُنَّا نَخُوضُ مَعَ الْخَائِضِينَ (45)
Ife timangotsutsa zinthu mwaumbuli
وَكُنَّا نُكَذِّبُ بِيَوْمِ الدِّينِ (46)
Ndipo tidali kunena kuti kulibe tsiku lachiweruzo
حَتَّىٰ أَتَانَا الْيَقِينُ (47)
Mpaka pamene imfa idatipeza
فَمَا تَنفَعُهُمْ شَفَاعَةُ الشَّافِعِينَ (48)
Motero palibe chidandaulo chochokera kwa wina aliyense chimene chidzamveka
فَمَا لَهُمْ عَنِ التَّذْكِرَةِ مُعْرِضِينَ (49)
Kodindichifukwachiyaniiwoalikuthawachikumbutso ichi
كَأَنَّهُمْ حُمُرٌ مُّسْتَنفِرَةٌ (50)
Monga abulu odzidzimutsidwa
فَرَّتْ مِن قَسْوَرَةٍ (51)
omwe anali kuthawa Mlenje, Mkango kapena nyama ina yoopsya
بَلْ يُرِيدُ كُلُّ امْرِئٍ مِّنْهُمْ أَن يُؤْتَىٰ صُحُفًا مُّنَشَّرَةً (52)
Iai! Aliyense wa iwo afuna kuti apatsidwe masamba a Buku otambasula
كَلَّا ۖ بَل لَّا يَخَافُونَ الْآخِرَةَ (53)
Ndikosatheka! Koma iwo alibe mantha ndi zimene zili nkudza
كَلَّا إِنَّهُ تَذْكِرَةٌ (54)
Iyayi. Ndithudi ili ndi chenjezo
فَمَن شَاءَ ذَكَرَهُ (55)
Motero musiyeni amene afuna kuti awerenge ndi kulandira chenjezo
وَمَا يَذْكُرُونَ إِلَّا أَن يَشَاءَ اللَّهُ ۚ هُوَ أَهْلُ التَّقْوَىٰ وَأَهْلُ الْمَغْفِرَةِ (56)
Ndipo iwo sadzalandira chenjezo pokha pokha ngati Mulungu afuna. Iye ndiye Ambuye wofunika kuti anthu onse azichita mantha ndi Iye, ndipo Iye ndi Ambuye wokhululukira
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas