| لَا أُقْسِمُ بِيَوْمِ الْقِيَامَةِ (1) Ine ndilumbira pali tsiku lachiweruzo
 | 
| وَلَا أُقْسِمُ بِالنَّفْسِ اللَّوَّامَةِ (2) Ndipo ndilumbira pali munthu amene amadzidzudzula yekha
 | 
| أَيَحْسَبُ الْإِنسَانُ أَلَّن نَّجْمَعَ عِظَامَهُ (3) Kodi munthu amaganiza kuti Ife sitidzalumikiza mafupa ake
 | 
| بَلَىٰ قَادِرِينَ عَلَىٰ أَن نُّسَوِّيَ بَنَانَهُ (4) Inde Ife tikhoza kulumikiza mwaubwino nsonga za zala zake
 | 
| بَلْ يُرِيدُ الْإِنسَانُ لِيَفْجُرَ أَمَامَهُ (5) Ngakhale tero, munthu amafuna kupitiliza kuchita zoipa
 | 
| يَسْأَلُ أَيَّانَ يَوْمُ الْقِيَامَةِ (6) Iye amafunsa: “Kodi zimenezi zidzachitika liti?”
 | 
| فَإِذَا بَرِقَ الْبَصَرُ (7) Motero pamene maso adzathodwa
 | 
| وَخَسَفَ الْقَمَرُ (8) Ndipo pamene mwezi udetsedwa
 | 
| وَجُمِعَ الشَّمْسُ وَالْقَمَرُ (9) Pamene dzuwa ndi mwezi zidzakumana
 | 
| يَقُولُ الْإِنسَانُ يَوْمَئِذٍ أَيْنَ الْمَفَرُّ (10) Patsikuli munthu adzafunsa kuti: “Kodi ndithawira kuti tsopano?”
 | 
| كَلَّا لَا وَزَرَ (11) Iai! Kulibe malo othawirako
 | 
| إِلَىٰ رَبِّكَ يَوْمَئِذٍ الْمُسْتَقَرُّ (12) Ndi kwa Ambuye wako kokha kumene kudzakhala kothawira
 | 
| يُنَبَّأُ الْإِنسَانُ يَوْمَئِذٍ بِمَا قَدَّمَ وَأَخَّرَ (13) Patsiku limeneli, munthu adzauzidwa zonse zimene adachita kuyambira poyamba mpaka pomaliza
 | 
| بَلِ الْإِنسَانُ عَلَىٰ نَفْسِهِ بَصِيرَةٌ (14) Iai! Munthu adzadzichitira umboni wodzineneza yekha
 | 
| وَلَوْ أَلْقَىٰ مَعَاذِيرَهُ (15) Ngakhale kuti iye azidzayesa kudzipulumutsa yekha
 | 
| لَا تُحَرِّكْ بِهِ لِسَانَكَ لِتَعْجَلَ بِهِ (16) Usagwedeze lilime lako zokhudza Korani ponena mofulumira
 | 
| إِنَّ عَلَيْنَا جَمْعَهُ وَقُرْآنَهُ (17) Ndi udindo wathu kuisonkhanitsa ndi kukupatsa nzeru kuilakatula iyo
 | 
| فَإِذَا قَرَأْنَاهُ فَاتَّبِعْ قُرْآنَهُ (18) Ndipo pamene talakatula, tsatira mwandondomeko kalakatulidwe kake
 | 
| ثُمَّ إِنَّ عَلَيْنَا بَيَانَهُ (19) Ndi udindo wathu kukufotokozera tanthauzo lake
 | 
| كَلَّا بَلْ تُحِبُّونَ الْعَاجِلَةَ (20) Iyayi!Komainumukondamoyowothamsanga
 | 
| وَتَذَرُونَ الْآخِرَةَ (21) Ndipo simufuna kulabadira za moyo umene uli nkudza
 | 
| وُجُوهٌ يَوْمَئِذٍ نَّاضِرَةٌ (22) Nkhope zina, pa tsiku limeneli, zidzakhala zowala ndi chisangalalo
 | 
| إِلَىٰ رَبِّهَا نَاظِرَةٌ (23) Zili kuyang’ana kwa Ambuye wawo
 | 
| وَوُجُوهٌ يَوْمَئِذٍ بَاسِرَةٌ (24) Ndipo nkhope zina, patsiku limeneli, zidzakhala zachisoni
 | 
| تَظُنُّ أَن يُفْعَلَ بِهَا فَاقِرَةٌ (25) Pozindikira kuti chilango chowawa chidzagwa pa iwo
 | 
| كَلَّا إِذَا بَلَغَتِ التَّرَاقِيَ (26) Iyayi, pamene ufika mpaka pa khosi
 | 
| وَقِيلَ مَنْ ۜ رَاقٍ (27) Ndipo kudzanenedwa kuti: “Kodi palibe woti angamuchize ndi kumupulumutsa ku imfa?”
 | 
| وَظَنَّ أَنَّهُ الْفِرَاقُ (28) Ndipo iye adzadziwa kuti awa ndi mathero a moyo wake
 | 
| وَالْتَفَّتِ السَّاقُ بِالسَّاقِ (29) Ndipo mwendo udzatembenuzika pa unzake
 | 
| إِلَىٰ رَبِّكَ يَوْمَئِذٍ الْمَسَاقُ (30) Tsiku limeneli zonse zidzabwerera kwa Ambuye wako
 | 
| فَلَا صَدَّقَ وَلَا صَلَّىٰ (31) Iye sanali kuvomereza chilungamo kapena kupemphera
 | 
| وَلَٰكِن كَذَّبَ وَتَوَلَّىٰ (32) Koma m’malo mwake adakana choonadi ndi kubwerera m’mbuyo
 | 
| ثُمَّ ذَهَبَ إِلَىٰ أَهْلِهِ يَتَمَطَّىٰ (33) Ndipo iye anapita kubanja lake monyada ali kudziyamikila yekha
 | 
| أَوْلَىٰ لَكَ فَأَوْلَىٰ (34) Tsoka kwa iwe. Ndiponso tsoka kwa iwe
 | 
| ثُمَّ أَوْلَىٰ لَكَ فَأَوْلَىٰ (35) Kachiwiri tsoka lili pafupi ndi iwe, tsopano tsoka lili pafupi
 | 
| أَيَحْسَبُ الْإِنسَانُ أَن يُتْرَكَ سُدًى (36) Kodi munthu amaganiza kuti tidzangomulekerera kuti azichita chilichonse chimene afuna
 | 
| أَلَمْ يَكُ نُطْفَةً مِّن مَّنِيٍّ يُمْنَىٰ (37) Kodi iye sanali dontho la umuna limene lidatuluka
 | 
| ثُمَّ كَانَ عَلَقَةً فَخَلَقَ فَسَوَّىٰ (38) Ndipo iye adakhala kam’bulu ka magazi. Ndipo Mulungu adamuumba ndipo adamukonza m’maonekedwe okongola
 | 
| فَجَعَلَ مِنْهُ الزَّوْجَيْنِ الذَّكَرَ وَالْأُنثَىٰ (39) Ndipo adamulenga m’mitundu iwiri, mwamuna ndi mkazi
 | 
| أَلَيْسَ ذَٰلِكَ بِقَادِرٍ عَلَىٰ أَن يُحْيِيَ الْمَوْتَىٰ (40) Kodi Iye alibe mphamvu yopereka moyo kwa anthu akufa
 |