| إِذَا السَّمَاءُ انفَطَرَتْ (1) Pamene thambo lidzang’ambika
 | 
| وَإِذَا الْكَوَاكِبُ انتَثَرَتْ (2) Pamene nyenyezi zidzagwa ndi kubalalitsidwa
 | 
| وَإِذَا الْبِحَارُ فُجِّرَتْ (3) Ndi pamene nyanja zikuluzikulu zidzaphulika
 | 
| وَإِذَا الْقُبُورُ بُعْثِرَتْ (4) Pamene manda adzatseguka
 | 
| عَلِمَتْ نَفْسٌ مَّا قَدَّمَتْ وَأَخَّرَتْ (5) Pamenepo Mzimu uliwonse udzadziwa chimene udatumiza ndi chimene udasiya m’mbuyo
 | 
| يَا أَيُّهَا الْإِنسَانُ مَا غَرَّكَ بِرَبِّكَ الْكَرِيمِ (6) oh Iwe munthu! Kodi ndi chiyani chikukunamiza kuti usiye kutsatira malamulo a Ambuye wako Wolemekezeka
 | 
| الَّذِي خَلَقَكَ فَسَوَّاكَ فَعَدَلَكَ (7) Amene adakulenga iwe ndi kukukonza kuti uzioneka bwino monga mmene uonekeramu
 | 
| فِي أَيِّ صُورَةٍ مَّا شَاءَ رَكَّبَكَ (8) Ndi nkhope ina iliyonse imene idamukondweretsa anakulenga iwe
 | 
| كَلَّا بَلْ تُكَذِّبُونَ بِالدِّينِ (9) Iyayi! Koma inu mukukana kuti kudzakhala tsiku lachiweruzo
 | 
| وَإِنَّ عَلَيْكُمْ لَحَافِظِينَ (10) Koma pakati panu pali ena amene ali kukuyang’anirani
 | 
| كِرَامًا كَاتِبِينَ (11) Olemekezeka ndi odziwa kulemba
 | 
| يَعْلَمُونَ مَا تَفْعَلُونَ (12) Iwo amadziwa chilichonse chimene mumachita
 | 
| إِنَّ الْأَبْرَارَ لَفِي نَعِيمٍ (13) Ndithudi anthu onse angwiro adzakhala mu mtendere
 | 
| وَإِنَّ الْفُجَّارَ لَفِي جَحِيمٍ (14) Ndipo, ndithudi, anthu onse oipa adzakhala ku Gahena
 | 
| يَصْلَوْنَهَا يَوْمَ الدِّينِ (15) Imene iwo adzalowako ndi kulawa malawi ake patsiku lachiweruzo
 | 
| وَمَا هُمْ عَنْهَا بِغَائِبِينَ (16) Iwo sadzatha kuthawa ayi
 | 
| وَمَا أَدْرَاكَ مَا يَوْمُ الدِّينِ (17) Kodi chidzakuuza ndi chiani za tsiku lachiweruzo
 | 
| ثُمَّ مَا أَدْرَاكَ مَا يَوْمُ الدِّينِ (18) Tinenanso kodi chidzakuuza ndi chiani za tsiku lachiweruzo
 | 
| يَوْمَ لَا تَمْلِكُ نَفْسٌ لِّنَفْسٍ شَيْئًا ۖ وَالْأَمْرُ يَوْمَئِذٍ لِّلَّهِ (19) Ndi tsiku limene mzimu uliwonse sudzatha kuthandiza wina aliyense ndipo Mulungu yekha ndiye amene adzaweruza
 |