إِذَا الشَّمْسُ كُوِّرَتْ (1) Pamene dzuwa lidzavundikiridwa |
وَإِذَا النُّجُومُ انكَدَرَتْ (2) Ndi pamene nyenyezi zidzagwa pansi |
وَإِذَا الْجِبَالُ سُيِّرَتْ (3) Ndi pamene mapiri adzachotsedwa |
وَإِذَا الْعِشَارُ عُطِّلَتْ (4) Ndi pamene ngamila zabele zizakhala zosasamalidwa |
وَإِذَا الْوُحُوشُ حُشِرَتْ (5) Ndi nyama za m’tchire zidzasonkhanitsidwa pamodzi |
وَإِذَا الْبِحَارُ سُجِّرَتْ (6) Ndi pamene nyanja zidzayatsidwa moto kapena zidzasefukira |
وَإِذَا النُّفُوسُ زُوِّجَتْ (7) Ndi pamene mizimu idzakumanitsidwa ndi matupi awo |
وَإِذَا الْمَوْءُودَةُ سُئِلَتْ (8) Ndi pamene mwana wa mkazi wa mng’ono, amene adaundilidwa wa moyo adzafunsidwa |
بِأَيِّ ذَنبٍ قُتِلَتْ (9) Chifukwa chimene anamuphera |
وَإِذَا الصُّحُفُ نُشِرَتْ (10) Ndi pamene mabuku olembamo ntchito za munthu aliyense adzatulutsidwa |
وَإِذَا السَّمَاءُ كُشِطَتْ (11) Ndi pamene kumwamba kudzafafanizidwa ndi kuchotsedwa ku malo ake |
وَإِذَا الْجَحِيمُ سُعِّرَتْ (12) Ndi pamene Gahena idzatenthetsedwa kwambiri |
وَإِذَا الْجَنَّةُ أُزْلِفَتْ (13) Ndi pamene Paradiso idzafikitsidwa pafupi |
عَلِمَتْ نَفْسٌ مَّا أَحْضَرَتْ (14) Ndithudi munthu aliyense adzadziwa chimene adachita |
فَلَا أُقْسِمُ بِالْخُنَّسِ (15) Motero, ndithudi, Ine ndili kulumbira pali nyenyezi zimene zimalowa |
الْجَوَارِ الْكُنَّسِ (16) Ndi pali maiko zimene zimayenda mofulumira ndi kudzibisa okha |
وَاللَّيْلِ إِذَا عَسْعَسَ (17) Ndi pali usiku pamene uchoka |
وَالصُّبْحِ إِذَا تَنَفَّسَ (18) Ndipalim’mawapamenekulikucha |
إِنَّهُ لَقَوْلُ رَسُولٍ كَرِيمٍ (19) Ndithudi awa ndi Mau a Mtumwi wolemekezeka |
ذِي قُوَّةٍ عِندَ ذِي الْعَرْشِ مَكِينٍ (20) Mwini mphamvu amene amalemekezedwa ndi Ambuye, Mwini Mpando wa Chifumu |
مُّطَاعٍ ثَمَّ أَمِينٍ (21) Amamveredwa ndi wokhulupirika |
وَمَا صَاحِبُكُم بِمَجْنُونٍ (22) Ndipo m’bale wanu uyu si wa misala ayi |
وَلَقَدْ رَآهُ بِالْأُفُقِ الْمُبِينِ (23) Ndipo, ndithudi, iye adamuona iye mu mlengalenga |
وَمَا هُوَ عَلَى الْغَيْبِ بِضَنِينٍ (24) Iye sabisa zinthu zosaoneka |
وَمَا هُوَ بِقَوْلِ شَيْطَانٍ رَّجِيمٍ (25) Ndipo zimene alankhula sizochokera kwa Satana wotembereredwa |
فَأَيْنَ تَذْهَبُونَ (26) Kodi inu muli kupita kuti |
إِنْ هُوَ إِلَّا ذِكْرٌ لِّلْعَالَمِينَ (27) Ndithudi ichi si china chilichonse ayi koma chikumbutso kwa anthu a mitundu yonse |
لِمَن شَاءَ مِنكُمْ أَن يَسْتَقِيمَ (28) Kwa aliyense wa inu amene afuna kuyenda moongoka |
وَمَا تَشَاءُونَ إِلَّا أَن يَشَاءَ اللَّهُ رَبُّ الْعَالَمِينَ (29) Koma inu simungathe kutero pokhapokha ndi chifuniro cha Mulungu, Ambuye wa zolengedwe zonse |