إِذَا السَّمَاءُ انفَطَرَتْ (1) Pamene thambo lidzang’ambika |
وَإِذَا الْكَوَاكِبُ انتَثَرَتْ (2) Pamene nyenyezi zidzagwa ndi kubalalitsidwa |
وَإِذَا الْبِحَارُ فُجِّرَتْ (3) Ndi pamene nyanja zikuluzikulu zidzaphulika |
وَإِذَا الْقُبُورُ بُعْثِرَتْ (4) Pamene manda adzatseguka |
عَلِمَتْ نَفْسٌ مَّا قَدَّمَتْ وَأَخَّرَتْ (5) Pamenepo Mzimu uliwonse udzadziwa chimene udatumiza ndi chimene udasiya m’mbuyo |
يَا أَيُّهَا الْإِنسَانُ مَا غَرَّكَ بِرَبِّكَ الْكَرِيمِ (6) oh Iwe munthu! Kodi ndi chiyani chikukunamiza kuti usiye kutsatira malamulo a Ambuye wako Wolemekezeka |
الَّذِي خَلَقَكَ فَسَوَّاكَ فَعَدَلَكَ (7) Amene adakulenga iwe ndi kukukonza kuti uzioneka bwino monga mmene uonekeramu |
فِي أَيِّ صُورَةٍ مَّا شَاءَ رَكَّبَكَ (8) Ndi nkhope ina iliyonse imene idamukondweretsa anakulenga iwe |
كَلَّا بَلْ تُكَذِّبُونَ بِالدِّينِ (9) Iyayi! Koma inu mukukana kuti kudzakhala tsiku lachiweruzo |
وَإِنَّ عَلَيْكُمْ لَحَافِظِينَ (10) Koma pakati panu pali ena amene ali kukuyang’anirani |
كِرَامًا كَاتِبِينَ (11) Olemekezeka ndi odziwa kulemba |
يَعْلَمُونَ مَا تَفْعَلُونَ (12) Iwo amadziwa chilichonse chimene mumachita |
إِنَّ الْأَبْرَارَ لَفِي نَعِيمٍ (13) Ndithudi anthu onse angwiro adzakhala mu mtendere |
وَإِنَّ الْفُجَّارَ لَفِي جَحِيمٍ (14) Ndipo, ndithudi, anthu onse oipa adzakhala ku Gahena |
يَصْلَوْنَهَا يَوْمَ الدِّينِ (15) Imene iwo adzalowako ndi kulawa malawi ake patsiku lachiweruzo |
وَمَا هُمْ عَنْهَا بِغَائِبِينَ (16) Iwo sadzatha kuthawa ayi |
وَمَا أَدْرَاكَ مَا يَوْمُ الدِّينِ (17) Kodi chidzakuuza ndi chiani za tsiku lachiweruzo |
ثُمَّ مَا أَدْرَاكَ مَا يَوْمُ الدِّينِ (18) Tinenanso kodi chidzakuuza ndi chiani za tsiku lachiweruzo |
يَوْمَ لَا تَمْلِكُ نَفْسٌ لِّنَفْسٍ شَيْئًا ۖ وَالْأَمْرُ يَوْمَئِذٍ لِّلَّهِ (19) Ndi tsiku limene mzimu uliwonse sudzatha kuthandiza wina aliyense ndipo Mulungu yekha ndiye amene adzaweruza |