| وَالْفَجْرِ (1) Pali m’mbandakucha
 | 
| وَلَيَالٍ عَشْرٍ (2) Ndi pali usiku khumi
 | 
| وَالشَّفْعِ وَالْوَتْرِ (3) Pali chofanana ndi chosiyana
 | 
| وَاللَّيْلِ إِذَا يَسْرِ (4) Pali usiku pamene uli nkutha
 | 
| هَلْ فِي ذَٰلِكَ قَسَمٌ لِّذِي حِجْرٍ (5) Ndithudi m’menemu muli umboni wokwanira kwa anthu a nzeru
 | 
| أَلَمْ تَرَ كَيْفَ فَعَلَ رَبُّكَ بِعَادٍ (6) Kodi iwe siudaone mmene Ambuye wako adakhaulitsira anthu a Aad
 | 
| إِرَمَ ذَاتِ الْعِمَادِ (7) Amene anali atali atali ngati nsanamila zitali zitali
 | 
| الَّتِي لَمْ يُخْلَقْ مِثْلُهَا فِي الْبِلَادِ (8) wolingana nawo amene sanalengedwepo padziko
 | 
| وَثَمُودَ الَّذِينَ جَابُوا الصَّخْرَ بِالْوَادِ (9) Ndi anthu a Thamoud, amene ankakumba nyumba zawo m’miyala ya m’dambo
 | 
| وَفِرْعَوْنَ ذِي الْأَوْتَادِ (10) Ndi Farao, amene anali ndi zichiri
 | 
| الَّذِينَ طَغَوْا فِي الْبِلَادِ (11) Amene anali kuphwanya malamulo paliponse m’dziko
 | 
| فَأَكْثَرُوا فِيهَا الْفَسَادَ (12) Ndipo adachulukitsa chisokonezo
 | 
| فَصَبَّ عَلَيْهِمْ رَبُّكَ سَوْطَ عَذَابٍ (13) Motero Ambuye wako adabweretsa chilango chosiyana siyana chowawa pa iwo
 | 
| إِنَّ رَبَّكَ لَبِالْمِرْصَادِ (14) Ndithudi Ambuye wako amaona
 | 
| فَأَمَّا الْإِنسَانُ إِذَا مَا ابْتَلَاهُ رَبُّهُ فَأَكْرَمَهُ وَنَعَّمَهُ فَيَقُولُ رَبِّي أَكْرَمَنِ (15) Ndipo nthawi zonse munthu, pamene Ambuye wake amuyesa pomukweza ndi kumuonetsera chifundo chake, iye amati: “Ambuye wanga wandilemekeza ine.”
 | 
| وَأَمَّا إِذَا مَا ابْتَلَاهُ فَقَدَرَ عَلَيْهِ رِزْقَهُ فَيَقُولُ رَبِّي أَهَانَنِ (16) Koma akamuyesa pomumana zinthu, iye amati: “Ambuye wanga ali kundizunza ine.”
 | 
| كَلَّا ۖ بَل لَّا تُكْرِمُونَ الْيَتِيمَ (17) Iyayi! Koma inu simuonetsa chifundo kwa ana a masiye
 | 
| وَلَا تَحَاضُّونَ عَلَىٰ طَعَامِ الْمِسْكِينِ (18) Ndi kuuzana kuti mudzidyetsa anthu osauka
 | 
| وَتَأْكُلُونَ التُّرَاثَ أَكْلًا لَّمًّا (19) Inu mumalanda chuma cha anthu opanda mphamvu chifukwa cha umbombo
 | 
| وَتُحِبُّونَ الْمَالَ حُبًّا جَمًّا (20) Ndipo mumakonda chuma ndi mitima yanu yonse
 | 
| كَلَّا إِذَا دُكَّتِ الْأَرْضُ دَكًّا دَكًّا (21) Iyayi! Koma pamene dziko lidzasinjidwa kukhala ufa
 | 
| وَجَاءَ رَبُّكَ وَالْمَلَكُ صَفًّا صَفًّا (22) Ndipo Ambuye wanu adzadza pamodzi ndi angelo ali pa mizere
 | 
| وَجِيءَ يَوْمَئِذٍ بِجَهَنَّمَ ۚ يَوْمَئِذٍ يَتَذَكَّرُ الْإِنسَانُ وَأَنَّىٰ لَهُ الذِّكْرَىٰ (23) Ndipo Gahena idzabweretsedwa pafupi patsikuli. Ndipo patsikuli munthu adzakumbukira. Koma, kodi chikumbumtima chake chidzamuthandiza motani
 | 
| يَقُولُ يَا لَيْتَنِي قَدَّمْتُ لِحَيَاتِي (24) Iye adzanena kuti: “Kalanga ine! Ndikanakhala ndinali kuchita zabwino pamene ndinali ndi moyo.”
 | 
| فَيَوْمَئِذٍ لَّا يُعَذِّبُ عَذَابَهُ أَحَدٌ (25) Motero patsikuli, palibe wina amene adzalanga monga momwe Iye adzalangire
 | 
| وَلَا يُوثِقُ وَثَاقَهُ أَحَدٌ (26) Ndipo palibe wina amene adzamanga monga ngati momwe Iye adzamangire
 | 
| يَا أَيَّتُهَا النَّفْسُ الْمُطْمَئِنَّةُ (27) oh! Iwe wokhutitsidwa
 | 
| ارْجِعِي إِلَىٰ رَبِّكِ رَاضِيَةً مَّرْضِيَّةً (28) Bwerera kwa Ambuye wako mosangalala ndi Iye, ndi Iye mosangalala ndi iwe
 | 
| فَادْخُلِي فِي عِبَادِي (29) Lowa m’gulu la akapolo anga wolemekezeka
 | 
| وَادْخُلِي جَنَّتِي (30) Ndipo lowa mu Paradiso yanga
 |