وَالْفَجْرِ (1) Pali m’mbandakucha |
وَلَيَالٍ عَشْرٍ (2) Ndi pali usiku khumi |
وَالشَّفْعِ وَالْوَتْرِ (3) Pali chofanana ndi chosiyana |
وَاللَّيْلِ إِذَا يَسْرِ (4) Pali usiku pamene uli nkutha |
هَلْ فِي ذَٰلِكَ قَسَمٌ لِّذِي حِجْرٍ (5) Ndithudi m’menemu muli umboni wokwanira kwa anthu a nzeru |
أَلَمْ تَرَ كَيْفَ فَعَلَ رَبُّكَ بِعَادٍ (6) Kodi iwe siudaone mmene Ambuye wako adakhaulitsira anthu a Aad |
إِرَمَ ذَاتِ الْعِمَادِ (7) Amene anali atali atali ngati nsanamila zitali zitali |
الَّتِي لَمْ يُخْلَقْ مِثْلُهَا فِي الْبِلَادِ (8) wolingana nawo amene sanalengedwepo padziko |
وَثَمُودَ الَّذِينَ جَابُوا الصَّخْرَ بِالْوَادِ (9) Ndi anthu a Thamoud, amene ankakumba nyumba zawo m’miyala ya m’dambo |
وَفِرْعَوْنَ ذِي الْأَوْتَادِ (10) Ndi Farao, amene anali ndi zichiri |
الَّذِينَ طَغَوْا فِي الْبِلَادِ (11) Amene anali kuphwanya malamulo paliponse m’dziko |
فَأَكْثَرُوا فِيهَا الْفَسَادَ (12) Ndipo adachulukitsa chisokonezo |
فَصَبَّ عَلَيْهِمْ رَبُّكَ سَوْطَ عَذَابٍ (13) Motero Ambuye wako adabweretsa chilango chosiyana siyana chowawa pa iwo |
إِنَّ رَبَّكَ لَبِالْمِرْصَادِ (14) Ndithudi Ambuye wako amaona |
فَأَمَّا الْإِنسَانُ إِذَا مَا ابْتَلَاهُ رَبُّهُ فَأَكْرَمَهُ وَنَعَّمَهُ فَيَقُولُ رَبِّي أَكْرَمَنِ (15) Ndipo nthawi zonse munthu, pamene Ambuye wake amuyesa pomukweza ndi kumuonetsera chifundo chake, iye amati: “Ambuye wanga wandilemekeza ine.” |
وَأَمَّا إِذَا مَا ابْتَلَاهُ فَقَدَرَ عَلَيْهِ رِزْقَهُ فَيَقُولُ رَبِّي أَهَانَنِ (16) Koma akamuyesa pomumana zinthu, iye amati: “Ambuye wanga ali kundizunza ine.” |
كَلَّا ۖ بَل لَّا تُكْرِمُونَ الْيَتِيمَ (17) Iyayi! Koma inu simuonetsa chifundo kwa ana a masiye |
وَلَا تَحَاضُّونَ عَلَىٰ طَعَامِ الْمِسْكِينِ (18) Ndi kuuzana kuti mudzidyetsa anthu osauka |
وَتَأْكُلُونَ التُّرَاثَ أَكْلًا لَّمًّا (19) Inu mumalanda chuma cha anthu opanda mphamvu chifukwa cha umbombo |
وَتُحِبُّونَ الْمَالَ حُبًّا جَمًّا (20) Ndipo mumakonda chuma ndi mitima yanu yonse |
كَلَّا إِذَا دُكَّتِ الْأَرْضُ دَكًّا دَكًّا (21) Iyayi! Koma pamene dziko lidzasinjidwa kukhala ufa |
وَجَاءَ رَبُّكَ وَالْمَلَكُ صَفًّا صَفًّا (22) Ndipo Ambuye wanu adzadza pamodzi ndi angelo ali pa mizere |
وَجِيءَ يَوْمَئِذٍ بِجَهَنَّمَ ۚ يَوْمَئِذٍ يَتَذَكَّرُ الْإِنسَانُ وَأَنَّىٰ لَهُ الذِّكْرَىٰ (23) Ndipo Gahena idzabweretsedwa pafupi patsikuli. Ndipo patsikuli munthu adzakumbukira. Koma, kodi chikumbumtima chake chidzamuthandiza motani |
يَقُولُ يَا لَيْتَنِي قَدَّمْتُ لِحَيَاتِي (24) Iye adzanena kuti: “Kalanga ine! Ndikanakhala ndinali kuchita zabwino pamene ndinali ndi moyo.” |
فَيَوْمَئِذٍ لَّا يُعَذِّبُ عَذَابَهُ أَحَدٌ (25) Motero patsikuli, palibe wina amene adzalanga monga momwe Iye adzalangire |
وَلَا يُوثِقُ وَثَاقَهُ أَحَدٌ (26) Ndipo palibe wina amene adzamanga monga ngati momwe Iye adzamangire |
يَا أَيَّتُهَا النَّفْسُ الْمُطْمَئِنَّةُ (27) oh! Iwe wokhutitsidwa |
ارْجِعِي إِلَىٰ رَبِّكِ رَاضِيَةً مَّرْضِيَّةً (28) Bwerera kwa Ambuye wako mosangalala ndi Iye, ndi Iye mosangalala ndi iwe |
فَادْخُلِي فِي عِبَادِي (29) Lowa m’gulu la akapolo anga wolemekezeka |
وَادْخُلِي جَنَّتِي (30) Ndipo lowa mu Paradiso yanga |