×

Surah Luqman in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Luqman

Translation of the Meanings of Surah Luqman in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Luqman translated into Chichewa, Surah Luqman in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Luqman in Chichewa - نيانجا, Verses 34 - Surah Number 31 - Page 411.

بسم الله الرحمن الرحيم

الم (1)
Alif Lam Mim
تِلْكَ آيَاتُ الْكِتَابِ الْحَكِيمِ (2)
Awa ndi mawu a m’Buku la nzeru
هُدًى وَرَحْمَةً لِّلْمُحْسِنِينَ (3)
Chilangizo ndi chifundo kwa anthu angwiro
الَّذِينَ يُقِيمُونَ الصَّلَاةَ وَيُؤْتُونَ الزَّكَاةَ وَهُم بِالْآخِرَةِ هُمْ يُوقِنُونَ (4)
Amene amapemphera nthawi zonse, amene amapereka msonkho wothandiza anthu osauka ndipo amakhulupirira m’moyo umene uli nkudza
أُولَٰئِكَ عَلَىٰ هُدًى مِّن رَّبِّهِمْ ۖ وَأُولَٰئِكَ هُمُ الْمُفْلِحُونَ (5)
Amenewa ndiwo amene atsogozedwa bwino ndi Ambuye wawo ndipo ndithudi adzakhala opambana
وَمِنَ النَّاسِ مَن يَشْتَرِي لَهْوَ الْحَدِيثِ لِيُضِلَّ عَن سَبِيلِ اللَّهِ بِغَيْرِ عِلْمٍ وَيَتَّخِذَهَا هُزُوًا ۚ أُولَٰئِكَ لَهُمْ عَذَابٌ مُّهِينٌ (6)
Koma pakati pa anthu, alipo ena amene amagula nkhani zopanda pake ndi zopanda tanthauzo ndi cholinga chosocheretsa anthu ku njira ya Mulungu ndi kuipanga iyo kukhala chinthu choseketsa. Awa adzalandira chilango chochititsa manyazi
وَإِذَا تُتْلَىٰ عَلَيْهِ آيَاتُنَا وَلَّىٰ مُسْتَكْبِرًا كَأَن لَّمْ يَسْمَعْهَا كَأَنَّ فِي أُذُنَيْهِ وَقْرًا ۖ فَبَشِّرْهُ بِعَذَابٍ أَلِيمٍ (7)
Ndipo pamene chivumbulutso chathuchilakatulidwakwaiye, iyeamatembenukamonyada kuoneka ngati kuti sadamve china chilichonse, kapena ngati kuti m’makutu mwake muli phula kotero muuzeni za chilango chowawa
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ لَهُمْ جَنَّاتُ النَّعِيمِ (8)
Akakhala iwo amene akhulupirira ndipo amachita ntchito za bwino, ndithudi, adzakhala ku Paradiso
خَالِدِينَ فِيهَا ۖ وَعْدَ اللَّهِ حَقًّا ۚ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (9)
Kukhalamo mpaka kalekale ndi lonjezo loona la Mulungu. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu ndipo ndi wanzeru zonse
خَلَقَ السَّمَاوَاتِ بِغَيْرِ عَمَدٍ تَرَوْنَهَا ۖ وَأَلْقَىٰ فِي الْأَرْضِ رَوَاسِيَ أَن تَمِيدَ بِكُمْ وَبَثَّ فِيهَا مِن كُلِّ دَابَّةٍ ۚ وَأَنزَلْنَا مِنَ السَّمَاءِ مَاءً فَأَنبَتْنَا فِيهَا مِن كُلِّ زَوْجٍ كَرِيمٍ (10)
Iye adalenga kumwamba popanda nsanamira monga muonera ndipo adalenga mapiri pa dziko lapansi kuti mwina dziko likhoza kuyenda pamodzi ndi inu. Ndipo m’dzikomo adaikamo nyama za mtundu uliwonse. Ndipo ife timatumiza mvula kuchokera ku mtambo ndipo timameretsa mbewu za mitundu yosiyanasiyana
هَٰذَا خَلْقُ اللَّهِ فَأَرُونِي مَاذَا خَلَقَ الَّذِينَ مِن دُونِهِ ۚ بَلِ الظَّالِمُونَ فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (11)
Ichi ndi chilengedwe cha Mulungu ndipo ndionetseni zimene iwo amene amakhala pafupi naye adalenga. Iyayi, anthu opanda chilungamo ndi olakwa
وَلَقَدْ آتَيْنَا لُقْمَانَ الْحِكْمَةَ أَنِ اشْكُرْ لِلَّهِ ۚ وَمَن يَشْكُرْ فَإِنَّمَا يَشْكُرُ لِنَفْسِهِ ۖ وَمَن كَفَرَ فَإِنَّ اللَّهَ غَنِيٌّ حَمِيدٌ (12)
Ndithudi Ife tidamupatsa nzeru Luqman ponena kuti, “Thokozani Mulungu. Aliyense amene amathokoza Mulungu, amathokoza chifukwa cha mzimu wake ndipo aliyense amene sathokoza, ndithudi, Mulungu sasowa kanthu ndipo ndi wolemekezeka.”
وَإِذْ قَالَ لُقْمَانُ لِابْنِهِ وَهُوَ يَعِظُهُ يَا بُنَيَّ لَا تُشْرِكْ بِاللَّهِ ۖ إِنَّ الشِّرْكَ لَظُلْمٌ عَظِيمٌ (13)
Ndi pamene Luqman adamuuza mwana wake adamulangiza kuti, “Mwana wanga usamafanizire Mulungu ndi china chilichonse chifukwa ndi tchimo loopsa.”
وَوَصَّيْنَا الْإِنسَانَ بِوَالِدَيْهِ حَمَلَتْهُ أُمُّهُ وَهْنًا عَلَىٰ وَهْنٍ وَفِصَالُهُ فِي عَامَيْنِ أَنِ اشْكُرْ لِي وَلِوَالِدَيْكَ إِلَيَّ الْمَصِيرُ (14)
Ndipo Ife timamulamula munthu kuonetsa chifundo kwa makolo ake. Movutika amayi ake adamubereka iye ndipo m’zaka ziwiri adamuyamwitsa. Kotero, thokozani Ine ndiponso thokozani makolo anu chifukwa ndi kwa Ine kumene mudzabwerera
وَإِن جَاهَدَاكَ عَلَىٰ أَن تُشْرِكَ بِي مَا لَيْسَ لَكَ بِهِ عِلْمٌ فَلَا تُطِعْهُمَا ۖ وَصَاحِبْهُمَا فِي الدُّنْيَا مَعْرُوفًا ۖ وَاتَّبِعْ سَبِيلَ مَنْ أَنَابَ إِلَيَّ ۚ ثُمَّ إِلَيَّ مَرْجِعُكُمْ فَأُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (15)
Koma ngati akuuza kuti uzindifanizira Ine ndi china chake chimene siuchidziwa, usawamvere. Aonetsere chifundo ndipo utsatire zochita za iye amene amalapa kwa Ine ndi kundimvera. Ndipo kwa Ine ndi kumene nonse mudzabwerera ndiponso ndidzakuuzani zonse zimene mudachita
يَا بُنَيَّ إِنَّهَا إِن تَكُ مِثْقَالَ حَبَّةٍ مِّنْ خَرْدَلٍ فَتَكُن فِي صَخْرَةٍ أَوْ فِي السَّمَاوَاتِ أَوْ فِي الْأَرْضِ يَأْتِ بِهَا اللَّهُ ۚ إِنَّ اللَّهَ لَطِيفٌ خَبِيرٌ (16)
“oh mwana wanga! Choipa ngakhale chitakhala ngati njere ya mpiru imene idakwiriridwa m’kati mwa mwala kapena kwina kulikonse kumwamba kapena pa dziko lapansi, Mulungu adzachitulutsa. Mulungu ali ndi nzeru ndiponso amadziwa chinthu china chilichonse.”
يَا بُنَيَّ أَقِمِ الصَّلَاةَ وَأْمُرْ بِالْمَعْرُوفِ وَانْهَ عَنِ الْمُنكَرِ وَاصْبِرْ عَلَىٰ مَا أَصَابَكَ ۖ إِنَّ ذَٰلِكَ مِنْ عَزْمِ الْأُمُورِ (17)
“Oh mwana wanga! Limbikira kupemphera, khazikitsa chilungamo ndipo udziletse kuchita zoipa. Khala opirira pa chilichonse chimene chidza pa iwe.” Ndithudi! Awa ndi malamulo ofunika amene adalamula Mulungu ndipo ayenera kutsatidwa
وَلَا تُصَعِّرْ خَدَّكَ لِلنَّاسِ وَلَا تَمْشِ فِي الْأَرْضِ مَرَحًا ۖ إِنَّ اللَّهَ لَا يُحِبُّ كُلَّ مُخْتَالٍ فَخُورٍ (18)
“Usanyodole anthu kapena kuyenda modzitukumula pa dziko. Mulungu sakonda anthu odzitukumula.”
وَاقْصِدْ فِي مَشْيِكَ وَاغْضُضْ مِن صَوْتِكَ ۚ إِنَّ أَنكَرَ الْأَصْوَاتِ لَصَوْتُ الْحَمِيرِ (19)
“Ndipo uyenera kukhala wofatsa ndipo mawu ako azikhala otsika chifukwa mawu aukali kwambiri ndi kulira kwa bulu.”
أَلَمْ تَرَوْا أَنَّ اللَّهَ سَخَّرَ لَكُم مَّا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ وَأَسْبَغَ عَلَيْكُمْ نِعَمَهُ ظَاهِرَةً وَبَاطِنَةً ۗ وَمِنَ النَّاسِ مَن يُجَادِلُ فِي اللَّهِ بِغَيْرِ عِلْمٍ وَلَا هُدًى وَلَا كِتَابٍ مُّنِيرٍ (20)
Kodi simuona kuti Mulungu wapanga zinthu zimene zili kumwamba ndiponso zimene zili padziko lapansi kukumverani inu ndipo adakupatsani inu zabwino zooneka ndi zosaoneka ndi maso? Ndipo pakati pa anthu pali iye amene amatsutsa zinthu zokhudza Mulungu ngakhale iye sadziwa china chilichonse, kapena chilangizo kapena Buku lopereka muuni
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ اتَّبِعُوا مَا أَنزَلَ اللَّهُ قَالُوا بَلْ نَتَّبِعُ مَا وَجَدْنَا عَلَيْهِ آبَاءَنَا ۚ أَوَلَوْ كَانَ الشَّيْطَانُ يَدْعُوهُمْ إِلَىٰ عَذَابِ السَّعِيرِ (21)
Ndipo zikanenedwa kwa iwo kuti: Tsatirani zimene Mulungu wavumbulutsa iwo amati, Iyayi. Ife sititsatira china chilichonse koma zokhazo zimene tidapeza makolo athu ali kutsatira. Ngakhale kuti Satana ali kuwaitanira iwo ku chilango cha moto
۞ وَمَن يُسْلِمْ وَجْهَهُ إِلَى اللَّهِ وَهُوَ مُحْسِنٌ فَقَدِ اسْتَمْسَكَ بِالْعُرْوَةِ الْوُثْقَىٰ ۗ وَإِلَى اللَّهِ عَاقِبَةُ الْأُمُورِ (22)
Aliyense amene adzipereka kwa Mulungu ndipo amachita ntchito zabwino, amagwiritsa chotsekulira chimene chiyenera kugwiridwa ndipo kwa Mulungu zinthu zonse zidzabwerera
وَمَن كَفَرَ فَلَا يَحْزُنكَ كُفْرُهُ ۚ إِلَيْنَا مَرْجِعُهُمْ فَنُنَبِّئُهُم بِمَا عَمِلُوا ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (23)
Koma ngati wina akana kukhulupirira, usalole kuti kusakhulupirira kwakeko kuti kukumvetse chisoni. Kwa Ife, anthu onse adzabwerera ndipo tidzawauza zoona za ntchito zawo. Mulungu amadziwa bwino zonse zimene zili m’mitima mwa anthu
نُمَتِّعُهُمْ قَلِيلًا ثُمَّ نَضْطَرُّهُمْ إِلَىٰ عَذَابٍ غَلِيظٍ (24)
Ife timawalekerera pa kanthawi kochepa ndipo pomaliza Ife tidzawakankha kupita ku chilango chowawa
وَلَئِن سَأَلْتَهُم مَّنْ خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ لَيَقُولُنَّ اللَّهُ ۚ قُلِ الْحَمْدُ لِلَّهِ ۚ بَلْ أَكْثَرُهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (25)
Ndipo ngati iwe uwafunsa kuti ndani amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, ndithudi, iwo adzati, “Mulungu.” Nena, “Ulemerero ukhale kwa Mulungu.” Iyayi! Ambiri a iwo sadziwa
لِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ إِنَّ اللَّهَ هُوَ الْغَنِيُّ الْحَمِيدُ (26)
Chilichonse chimene chili kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi cha Mulungu. Ndithudi Mulungu sasowa chilichonse ndipo ndi woyamikidwa
وَلَوْ أَنَّمَا فِي الْأَرْضِ مِن شَجَرَةٍ أَقْلَامٌ وَالْبَحْرُ يَمُدُّهُ مِن بَعْدِهِ سَبْعَةُ أَبْحُرٍ مَّا نَفِدَتْ كَلِمَاتُ اللَّهِ ۗ إِنَّ اللَّهَ عَزِيزٌ حَكِيمٌ (27)
Ndipo kukadakhala kuti mtengo uliwonse umene uli pa dziko lapansi udasanduka kukhala cholembera ndipo nyanja kusanduka kukhala inki mothandizidwandi nyanja zina zisanu ndi ziwiri ndithudi, mawu a Mulungu sakadatha. Ndithudi Mulungu ndi wamphamvu ndi waluntha
مَّا خَلْقُكُمْ وَلَا بَعْثُكُمْ إِلَّا كَنَفْسٍ وَاحِدَةٍ ۗ إِنَّ اللَّهَ سَمِيعٌ بَصِيرٌ (28)
Kalengedwe kanu ndi kuukitsidwa kwanu kwa akufa si chinthu chovuta ayi. Ndithudi Mulungu ndi wakumva ndi wowona
أَلَمْ تَرَ أَنَّ اللَّهَ يُولِجُ اللَّيْلَ فِي النَّهَارِ وَيُولِجُ النَّهَارَ فِي اللَّيْلِ وَسَخَّرَ الشَّمْسَ وَالْقَمَرَ كُلٌّ يَجْرِي إِلَىٰ أَجَلٍ مُّسَمًّى وَأَنَّ اللَّهَ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرٌ (29)
Kodi inu simuona mmene Mulungu amasandulizira usiku kuti ukhale usana ndi usana kuti ukhale usiku ndipo wapangira dzuwa ndi mwezi kuti zizikumverani inu? Ndiponso kodi simuona kuti chilichonse chimayenda m’njira yake mpaka pa nthawi yokhazikitsidwa ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene inu mumachita
ذَٰلِكَ بِأَنَّ اللَّهَ هُوَ الْحَقُّ وَأَنَّ مَا يَدْعُونَ مِن دُونِهِ الْبَاطِلُ وَأَنَّ اللَّهَ هُوَ الْعَلِيُّ الْكَبِيرُ (30)
Ichi ndi chifukwa chakuti Mulungu ndiye choonadi ndipo kuti chimene iwo amapembedza kuonjezera pa Mulungu ndi chinthu wamba chabe. Mulungu ndi wapamwamba ndi wamkulu
أَلَمْ تَرَ أَنَّ الْفُلْكَ تَجْرِي فِي الْبَحْرِ بِنِعْمَتِ اللَّهِ لِيُرِيَكُم مِّنْ آيَاتِهِ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّكُلِّ صَبَّارٍ شَكُورٍ (31)
Kodiinusimuonammenezombozimayenderapanyanja mwachisomo cha Mulungu ndi mmene amakuonetserani inu zizindikiro zake? Ndithudi muli chiphunzitso mu zimenezi kwa anthu olimbikira ndiponso kwa oyamika
وَإِذَا غَشِيَهُم مَّوْجٌ كَالظُّلَلِ دَعَوُا اللَّهَ مُخْلِصِينَ لَهُ الدِّينَ فَلَمَّا نَجَّاهُمْ إِلَى الْبَرِّ فَمِنْهُم مُّقْتَصِدٌ ۚ وَمَا يَجْحَدُ بِآيَاتِنَا إِلَّا كُلُّ خَتَّارٍ كَفُورٍ (32)
Ndipo pamene mafunde okhala ngati mapiri awaphimba, iwo amapempha kwa Mulungu modzichepetsa. Koma Iye akangowafikitsa bwino pa mtunda, ena a iwo amatsatira njira ya pakati ndipo palibe amene amakana chiphunzitso chathu koma yekhayo amene sathokoza ndiponso amene ndi wamwano
يَا أَيُّهَا النَّاسُ اتَّقُوا رَبَّكُمْ وَاخْشَوْا يَوْمًا لَّا يَجْزِي وَالِدٌ عَن وَلَدِهِ وَلَا مَوْلُودٌ هُوَ جَازٍ عَن وَالِدِهِ شَيْئًا ۚ إِنَّ وَعْدَ اللَّهِ حَقٌّ ۖ فَلَا تَغُرَّنَّكُمُ الْحَيَاةُ الدُّنْيَا وَلَا يَغُرَّنَّكُم بِاللَّهِ الْغَرُورُ (33)
oh anthu inu! opani Ambuye wanu ndipo liopeni tsiku limene kholo silidzathandiza mwana wake kapena mwana kuthandiza kholo lake. Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona. Kotero musalole moyo wa padziko lino lapansi kuti ukunyengeni inu kapena kuti Satana akunyengeni pa nkhani zokhudza Mulungu
إِنَّ اللَّهَ عِندَهُ عِلْمُ السَّاعَةِ وَيُنَزِّلُ الْغَيْثَ وَيَعْلَمُ مَا فِي الْأَرْحَامِ ۖ وَمَا تَدْرِي نَفْسٌ مَّاذَا تَكْسِبُ غَدًا ۖ وَمَا تَدْرِي نَفْسٌ بِأَيِّ أَرْضٍ تَمُوتُ ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ خَبِيرٌ (34)
Ndithudi Mulungu ndiye yekha amene amadziwa za kudza kwake kwa tsiku lachiweruzo. Ndiye amene amatsitsa mvula ndiponso amadziwa zimene zili m’mimba mwa akazi. Ndipo palibe amene amadziwa zimene zingamuonekere mawa ndipo palibe amene amadziwa dziko limene adzafere. Ndithudi Mulungu ndi Wodziwa ndi Wozindikira
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas