الم (1) Alif Lam Mim |
تِلْكَ آيَاتُ الْكِتَابِ الْحَكِيمِ (2) Awa ndi mawu a m’Buku la nzeru |
هُدًى وَرَحْمَةً لِّلْمُحْسِنِينَ (3) Chilangizo ndi chifundo kwa anthu angwiro |
الَّذِينَ يُقِيمُونَ الصَّلَاةَ وَيُؤْتُونَ الزَّكَاةَ وَهُم بِالْآخِرَةِ هُمْ يُوقِنُونَ (4) Amene amapemphera nthawi zonse, amene amapereka msonkho wothandiza anthu osauka ndipo amakhulupirira m’moyo umene uli nkudza |
أُولَٰئِكَ عَلَىٰ هُدًى مِّن رَّبِّهِمْ ۖ وَأُولَٰئِكَ هُمُ الْمُفْلِحُونَ (5) Amenewa ndiwo amene atsogozedwa bwino ndi Ambuye wawo ndipo ndithudi adzakhala opambana |
وَمِنَ النَّاسِ مَن يَشْتَرِي لَهْوَ الْحَدِيثِ لِيُضِلَّ عَن سَبِيلِ اللَّهِ بِغَيْرِ عِلْمٍ وَيَتَّخِذَهَا هُزُوًا ۚ أُولَٰئِكَ لَهُمْ عَذَابٌ مُّهِينٌ (6) Koma pakati pa anthu, alipo ena amene amagula nkhani zopanda pake ndi zopanda tanthauzo ndi cholinga chosocheretsa anthu ku njira ya Mulungu ndi kuipanga iyo kukhala chinthu choseketsa. Awa adzalandira chilango chochititsa manyazi |
وَإِذَا تُتْلَىٰ عَلَيْهِ آيَاتُنَا وَلَّىٰ مُسْتَكْبِرًا كَأَن لَّمْ يَسْمَعْهَا كَأَنَّ فِي أُذُنَيْهِ وَقْرًا ۖ فَبَشِّرْهُ بِعَذَابٍ أَلِيمٍ (7) Ndipo pamene chivumbulutso chathuchilakatulidwakwaiye, iyeamatembenukamonyada kuoneka ngati kuti sadamve china chilichonse, kapena ngati kuti m’makutu mwake muli phula kotero muuzeni za chilango chowawa |
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ لَهُمْ جَنَّاتُ النَّعِيمِ (8) Akakhala iwo amene akhulupirira ndipo amachita ntchito za bwino, ndithudi, adzakhala ku Paradiso |
خَالِدِينَ فِيهَا ۖ وَعْدَ اللَّهِ حَقًّا ۚ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (9) Kukhalamo mpaka kalekale ndi lonjezo loona la Mulungu. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu ndipo ndi wanzeru zonse |
خَلَقَ السَّمَاوَاتِ بِغَيْرِ عَمَدٍ تَرَوْنَهَا ۖ وَأَلْقَىٰ فِي الْأَرْضِ رَوَاسِيَ أَن تَمِيدَ بِكُمْ وَبَثَّ فِيهَا مِن كُلِّ دَابَّةٍ ۚ وَأَنزَلْنَا مِنَ السَّمَاءِ مَاءً فَأَنبَتْنَا فِيهَا مِن كُلِّ زَوْجٍ كَرِيمٍ (10) Iye adalenga kumwamba popanda nsanamira monga muonera ndipo adalenga mapiri pa dziko lapansi kuti mwina dziko likhoza kuyenda pamodzi ndi inu. Ndipo m’dzikomo adaikamo nyama za mtundu uliwonse. Ndipo ife timatumiza mvula kuchokera ku mtambo ndipo timameretsa mbewu za mitundu yosiyanasiyana |
هَٰذَا خَلْقُ اللَّهِ فَأَرُونِي مَاذَا خَلَقَ الَّذِينَ مِن دُونِهِ ۚ بَلِ الظَّالِمُونَ فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (11) Ichi ndi chilengedwe cha Mulungu ndipo ndionetseni zimene iwo amene amakhala pafupi naye adalenga. Iyayi, anthu opanda chilungamo ndi olakwa |
وَلَقَدْ آتَيْنَا لُقْمَانَ الْحِكْمَةَ أَنِ اشْكُرْ لِلَّهِ ۚ وَمَن يَشْكُرْ فَإِنَّمَا يَشْكُرُ لِنَفْسِهِ ۖ وَمَن كَفَرَ فَإِنَّ اللَّهَ غَنِيٌّ حَمِيدٌ (12) Ndithudi Ife tidamupatsa nzeru Luqman ponena kuti, “Thokozani Mulungu. Aliyense amene amathokoza Mulungu, amathokoza chifukwa cha mzimu wake ndipo aliyense amene sathokoza, ndithudi, Mulungu sasowa kanthu ndipo ndi wolemekezeka.” |
وَإِذْ قَالَ لُقْمَانُ لِابْنِهِ وَهُوَ يَعِظُهُ يَا بُنَيَّ لَا تُشْرِكْ بِاللَّهِ ۖ إِنَّ الشِّرْكَ لَظُلْمٌ عَظِيمٌ (13) Ndi pamene Luqman adamuuza mwana wake adamulangiza kuti, “Mwana wanga usamafanizire Mulungu ndi china chilichonse chifukwa ndi tchimo loopsa.” |
وَوَصَّيْنَا الْإِنسَانَ بِوَالِدَيْهِ حَمَلَتْهُ أُمُّهُ وَهْنًا عَلَىٰ وَهْنٍ وَفِصَالُهُ فِي عَامَيْنِ أَنِ اشْكُرْ لِي وَلِوَالِدَيْكَ إِلَيَّ الْمَصِيرُ (14) Ndipo Ife timamulamula munthu kuonetsa chifundo kwa makolo ake. Movutika amayi ake adamubereka iye ndipo m’zaka ziwiri adamuyamwitsa. Kotero, thokozani Ine ndiponso thokozani makolo anu chifukwa ndi kwa Ine kumene mudzabwerera |
وَإِن جَاهَدَاكَ عَلَىٰ أَن تُشْرِكَ بِي مَا لَيْسَ لَكَ بِهِ عِلْمٌ فَلَا تُطِعْهُمَا ۖ وَصَاحِبْهُمَا فِي الدُّنْيَا مَعْرُوفًا ۖ وَاتَّبِعْ سَبِيلَ مَنْ أَنَابَ إِلَيَّ ۚ ثُمَّ إِلَيَّ مَرْجِعُكُمْ فَأُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (15) Koma ngati akuuza kuti uzindifanizira Ine ndi china chake chimene siuchidziwa, usawamvere. Aonetsere chifundo ndipo utsatire zochita za iye amene amalapa kwa Ine ndi kundimvera. Ndipo kwa Ine ndi kumene nonse mudzabwerera ndiponso ndidzakuuzani zonse zimene mudachita |
يَا بُنَيَّ إِنَّهَا إِن تَكُ مِثْقَالَ حَبَّةٍ مِّنْ خَرْدَلٍ فَتَكُن فِي صَخْرَةٍ أَوْ فِي السَّمَاوَاتِ أَوْ فِي الْأَرْضِ يَأْتِ بِهَا اللَّهُ ۚ إِنَّ اللَّهَ لَطِيفٌ خَبِيرٌ (16) “oh mwana wanga! Choipa ngakhale chitakhala ngati njere ya mpiru imene idakwiriridwa m’kati mwa mwala kapena kwina kulikonse kumwamba kapena pa dziko lapansi, Mulungu adzachitulutsa. Mulungu ali ndi nzeru ndiponso amadziwa chinthu china chilichonse.” |
يَا بُنَيَّ أَقِمِ الصَّلَاةَ وَأْمُرْ بِالْمَعْرُوفِ وَانْهَ عَنِ الْمُنكَرِ وَاصْبِرْ عَلَىٰ مَا أَصَابَكَ ۖ إِنَّ ذَٰلِكَ مِنْ عَزْمِ الْأُمُورِ (17) “Oh mwana wanga! Limbikira kupemphera, khazikitsa chilungamo ndipo udziletse kuchita zoipa. Khala opirira pa chilichonse chimene chidza pa iwe.” Ndithudi! Awa ndi malamulo ofunika amene adalamula Mulungu ndipo ayenera kutsatidwa |
وَلَا تُصَعِّرْ خَدَّكَ لِلنَّاسِ وَلَا تَمْشِ فِي الْأَرْضِ مَرَحًا ۖ إِنَّ اللَّهَ لَا يُحِبُّ كُلَّ مُخْتَالٍ فَخُورٍ (18) “Usanyodole anthu kapena kuyenda modzitukumula pa dziko. Mulungu sakonda anthu odzitukumula.” |
وَاقْصِدْ فِي مَشْيِكَ وَاغْضُضْ مِن صَوْتِكَ ۚ إِنَّ أَنكَرَ الْأَصْوَاتِ لَصَوْتُ الْحَمِيرِ (19) “Ndipo uyenera kukhala wofatsa ndipo mawu ako azikhala otsika chifukwa mawu aukali kwambiri ndi kulira kwa bulu.” |
أَلَمْ تَرَوْا أَنَّ اللَّهَ سَخَّرَ لَكُم مَّا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ وَأَسْبَغَ عَلَيْكُمْ نِعَمَهُ ظَاهِرَةً وَبَاطِنَةً ۗ وَمِنَ النَّاسِ مَن يُجَادِلُ فِي اللَّهِ بِغَيْرِ عِلْمٍ وَلَا هُدًى وَلَا كِتَابٍ مُّنِيرٍ (20) Kodi simuona kuti Mulungu wapanga zinthu zimene zili kumwamba ndiponso zimene zili padziko lapansi kukumverani inu ndipo adakupatsani inu zabwino zooneka ndi zosaoneka ndi maso? Ndipo pakati pa anthu pali iye amene amatsutsa zinthu zokhudza Mulungu ngakhale iye sadziwa china chilichonse, kapena chilangizo kapena Buku lopereka muuni |
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ اتَّبِعُوا مَا أَنزَلَ اللَّهُ قَالُوا بَلْ نَتَّبِعُ مَا وَجَدْنَا عَلَيْهِ آبَاءَنَا ۚ أَوَلَوْ كَانَ الشَّيْطَانُ يَدْعُوهُمْ إِلَىٰ عَذَابِ السَّعِيرِ (21) Ndipo zikanenedwa kwa iwo kuti: Tsatirani zimene Mulungu wavumbulutsa iwo amati, Iyayi. Ife sititsatira china chilichonse koma zokhazo zimene tidapeza makolo athu ali kutsatira. Ngakhale kuti Satana ali kuwaitanira iwo ku chilango cha moto |
۞ وَمَن يُسْلِمْ وَجْهَهُ إِلَى اللَّهِ وَهُوَ مُحْسِنٌ فَقَدِ اسْتَمْسَكَ بِالْعُرْوَةِ الْوُثْقَىٰ ۗ وَإِلَى اللَّهِ عَاقِبَةُ الْأُمُورِ (22) Aliyense amene adzipereka kwa Mulungu ndipo amachita ntchito zabwino, amagwiritsa chotsekulira chimene chiyenera kugwiridwa ndipo kwa Mulungu zinthu zonse zidzabwerera |
وَمَن كَفَرَ فَلَا يَحْزُنكَ كُفْرُهُ ۚ إِلَيْنَا مَرْجِعُهُمْ فَنُنَبِّئُهُم بِمَا عَمِلُوا ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (23) Koma ngati wina akana kukhulupirira, usalole kuti kusakhulupirira kwakeko kuti kukumvetse chisoni. Kwa Ife, anthu onse adzabwerera ndipo tidzawauza zoona za ntchito zawo. Mulungu amadziwa bwino zonse zimene zili m’mitima mwa anthu |
نُمَتِّعُهُمْ قَلِيلًا ثُمَّ نَضْطَرُّهُمْ إِلَىٰ عَذَابٍ غَلِيظٍ (24) Ife timawalekerera pa kanthawi kochepa ndipo pomaliza Ife tidzawakankha kupita ku chilango chowawa |
وَلَئِن سَأَلْتَهُم مَّنْ خَلَقَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ لَيَقُولُنَّ اللَّهُ ۚ قُلِ الْحَمْدُ لِلَّهِ ۚ بَلْ أَكْثَرُهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (25) Ndipo ngati iwe uwafunsa kuti ndani amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi, ndithudi, iwo adzati, “Mulungu.” Nena, “Ulemerero ukhale kwa Mulungu.” Iyayi! Ambiri a iwo sadziwa |
لِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ إِنَّ اللَّهَ هُوَ الْغَنِيُّ الْحَمِيدُ (26) Chilichonse chimene chili kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi cha Mulungu. Ndithudi Mulungu sasowa chilichonse ndipo ndi woyamikidwa |
وَلَوْ أَنَّمَا فِي الْأَرْضِ مِن شَجَرَةٍ أَقْلَامٌ وَالْبَحْرُ يَمُدُّهُ مِن بَعْدِهِ سَبْعَةُ أَبْحُرٍ مَّا نَفِدَتْ كَلِمَاتُ اللَّهِ ۗ إِنَّ اللَّهَ عَزِيزٌ حَكِيمٌ (27) Ndipo kukadakhala kuti mtengo uliwonse umene uli pa dziko lapansi udasanduka kukhala cholembera ndipo nyanja kusanduka kukhala inki mothandizidwandi nyanja zina zisanu ndi ziwiri ndithudi, mawu a Mulungu sakadatha. Ndithudi Mulungu ndi wamphamvu ndi waluntha |
مَّا خَلْقُكُمْ وَلَا بَعْثُكُمْ إِلَّا كَنَفْسٍ وَاحِدَةٍ ۗ إِنَّ اللَّهَ سَمِيعٌ بَصِيرٌ (28) Kalengedwe kanu ndi kuukitsidwa kwanu kwa akufa si chinthu chovuta ayi. Ndithudi Mulungu ndi wakumva ndi wowona |
أَلَمْ تَرَ أَنَّ اللَّهَ يُولِجُ اللَّيْلَ فِي النَّهَارِ وَيُولِجُ النَّهَارَ فِي اللَّيْلِ وَسَخَّرَ الشَّمْسَ وَالْقَمَرَ كُلٌّ يَجْرِي إِلَىٰ أَجَلٍ مُّسَمًّى وَأَنَّ اللَّهَ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرٌ (29) Kodi inu simuona mmene Mulungu amasandulizira usiku kuti ukhale usana ndi usana kuti ukhale usiku ndipo wapangira dzuwa ndi mwezi kuti zizikumverani inu? Ndiponso kodi simuona kuti chilichonse chimayenda m’njira yake mpaka pa nthawi yokhazikitsidwa ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene inu mumachita |
ذَٰلِكَ بِأَنَّ اللَّهَ هُوَ الْحَقُّ وَأَنَّ مَا يَدْعُونَ مِن دُونِهِ الْبَاطِلُ وَأَنَّ اللَّهَ هُوَ الْعَلِيُّ الْكَبِيرُ (30) Ichi ndi chifukwa chakuti Mulungu ndiye choonadi ndipo kuti chimene iwo amapembedza kuonjezera pa Mulungu ndi chinthu wamba chabe. Mulungu ndi wapamwamba ndi wamkulu |
أَلَمْ تَرَ أَنَّ الْفُلْكَ تَجْرِي فِي الْبَحْرِ بِنِعْمَتِ اللَّهِ لِيُرِيَكُم مِّنْ آيَاتِهِ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَاتٍ لِّكُلِّ صَبَّارٍ شَكُورٍ (31) Kodiinusimuonammenezombozimayenderapanyanja mwachisomo cha Mulungu ndi mmene amakuonetserani inu zizindikiro zake? Ndithudi muli chiphunzitso mu zimenezi kwa anthu olimbikira ndiponso kwa oyamika |
وَإِذَا غَشِيَهُم مَّوْجٌ كَالظُّلَلِ دَعَوُا اللَّهَ مُخْلِصِينَ لَهُ الدِّينَ فَلَمَّا نَجَّاهُمْ إِلَى الْبَرِّ فَمِنْهُم مُّقْتَصِدٌ ۚ وَمَا يَجْحَدُ بِآيَاتِنَا إِلَّا كُلُّ خَتَّارٍ كَفُورٍ (32) Ndipo pamene mafunde okhala ngati mapiri awaphimba, iwo amapempha kwa Mulungu modzichepetsa. Koma Iye akangowafikitsa bwino pa mtunda, ena a iwo amatsatira njira ya pakati ndipo palibe amene amakana chiphunzitso chathu koma yekhayo amene sathokoza ndiponso amene ndi wamwano |
يَا أَيُّهَا النَّاسُ اتَّقُوا رَبَّكُمْ وَاخْشَوْا يَوْمًا لَّا يَجْزِي وَالِدٌ عَن وَلَدِهِ وَلَا مَوْلُودٌ هُوَ جَازٍ عَن وَالِدِهِ شَيْئًا ۚ إِنَّ وَعْدَ اللَّهِ حَقٌّ ۖ فَلَا تَغُرَّنَّكُمُ الْحَيَاةُ الدُّنْيَا وَلَا يَغُرَّنَّكُم بِاللَّهِ الْغَرُورُ (33) oh anthu inu! opani Ambuye wanu ndipo liopeni tsiku limene kholo silidzathandiza mwana wake kapena mwana kuthandiza kholo lake. Ndithudi lonjezo la Mulungu ndi loona. Kotero musalole moyo wa padziko lino lapansi kuti ukunyengeni inu kapena kuti Satana akunyengeni pa nkhani zokhudza Mulungu |
إِنَّ اللَّهَ عِندَهُ عِلْمُ السَّاعَةِ وَيُنَزِّلُ الْغَيْثَ وَيَعْلَمُ مَا فِي الْأَرْحَامِ ۖ وَمَا تَدْرِي نَفْسٌ مَّاذَا تَكْسِبُ غَدًا ۖ وَمَا تَدْرِي نَفْسٌ بِأَيِّ أَرْضٍ تَمُوتُ ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلِيمٌ خَبِيرٌ (34) Ndithudi Mulungu ndiye yekha amene amadziwa za kudza kwake kwa tsiku lachiweruzo. Ndiye amene amatsitsa mvula ndiponso amadziwa zimene zili m’mimba mwa akazi. Ndipo palibe amene amadziwa zimene zingamuonekere mawa ndipo palibe amene amadziwa dziko limene adzafere. Ndithudi Mulungu ndi Wodziwa ndi Wozindikira |