×

Surah Abasa in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Abasa

Translation of the Meanings of Surah Abasa in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Abasa translated into Chichewa, Surah Abasa in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Abasa in Chichewa - نيانجا, Verses 42 - Surah Number 80 - Page 585.

بسم الله الرحمن الرحيم

عَبَسَ وَتَوَلَّىٰ (1)
Iye anachita matsinya ndi kuyang’ana kumbali
أَن جَاءَهُ الْأَعْمَىٰ (2)
Chifukwa munthu wakhungu anadza kwa iye
وَمَا يُدْرِيكَ لَعَلَّهُ يَزَّكَّىٰ (3)
Ndipo iwe ungadziwe bwanji kuti mwina angadziyeretse
أَوْ يَذَّكَّرُ فَتَنفَعَهُ الذِّكْرَىٰ (4)
Kapena iye adzalandira chenjezo ndipo chenjezo likanamupindulira kanthu kena
أَمَّا مَنِ اسْتَغْنَىٰ (5)
Koma iye amene amadziyesa kuti sasowa kanthu
فَأَنتَ لَهُ تَصَدَّىٰ (6)
Ameneyo ndiye amene uli naye ndi chidwi
وَمَا عَلَيْكَ أَلَّا يَزَّكَّىٰ (7)
Kodi uli nazo chiani ngati iye sadziyeretsa
وَأَمَّا مَن جَاءَكَ يَسْعَىٰ (8)
Koma kwa iye amene amakuthamangira
وَهُوَ يَخْشَىٰ (9)
Ndipo iye amaopa
فَأَنتَ عَنْهُ تَلَهَّىٰ (10)
Iwe siudamulabadire ayi
كَلَّا إِنَّهَا تَذْكِرَةٌ (11)
Iyayi! Ndithudi chimenechi ndi chikumbutso
فَمَن شَاءَ ذَكَرَهُ (12)
Muloleni aliyense amene afuna kuti achilabadire
فِي صُحُفٍ مُّكَرَّمَةٍ (13)
Ichi chidalembedwa m’Buku la Mulungu lolemekezeka
مَّرْفُوعَةٍ مُّطَهَّرَةٍ (14)
Loyeretsedwa ndi losungidwa bwino ndi loyera
بِأَيْدِي سَفَرَةٍ (15)
M’manja mwa Alembi
كِرَامٍ بَرَرَةٍ (16)
Wolemekezeka ndipo womvera
قُتِلَ الْإِنسَانُ مَا أَكْفَرَهُ (17)
Atembereredwe munthu! Kodi ndi chiani chili kumuletsa kuthokoza
مِنْ أَيِّ شَيْءٍ خَلَقَهُ (18)
Kodi Iye adamulenga kuchokera ku chiyani
مِن نُّطْفَةٍ خَلَقَهُ فَقَدَّرَهُ (19)
Kuchokera ku dontho la umuna, Iye adamulenga ndipo adamukonza bwino
ثُمَّ السَّبِيلَ يَسَّرَهُ (20)
Ndipo Iye adamukonzera iye njira yapafupi
ثُمَّ أَمَاتَهُ فَأَقْبَرَهُ (21)
Ndipo amamupha ndi kumusunga m’manda
ثُمَّ إِذَا شَاءَ أَنشَرَهُ (22)
Ndithudi Iye adzamudzutsa monga momwe afunira
كَلَّا لَمَّا يَقْضِ مَا أَمَرَهُ (23)
Iyayi, koma munthu sanachite zimene Iye adamulamulira
فَلْيَنظُرِ الْإِنسَانُ إِلَىٰ طَعَامِهِ (24)
Mulekeni munthu kuti aganize za chakudya chake
أَنَّا صَبَبْنَا الْمَاءَ صَبًّا (25)
Kuti Ife timagwetsa mvula yambiri
ثُمَّ شَقَقْنَا الْأَرْضَ شَقًّا (26)
Ndipo timaphwanya nthaka
فَأَنبَتْنَا فِيهَا حَبًّا (27)
Ndipo Ife Al-Takwir 641 timameretsa njere
وَعِنَبًا وَقَضْبًا (28)
Mphesa ndi Msipu
وَزَيْتُونًا وَنَخْلًا (29)
Mitengo ya mafuta, ndi mitengo ya tende
وَحَدَائِقَ غُلْبًا (30)
Ndi minda imene ili ndi mitengo yambiri
وَفَاكِهَةً وَأَبًّا (31)
Ndi mitengo ya zipatso ndi msipu
مَّتَاعًا لَّكُمْ وَلِأَنْعَامِكُمْ (32)
Chakudya cha inu ndi ziweto zanu
فَإِذَا جَاءَتِ الصَّاخَّةُ (33)
Koma pamene kulira kogonthetsa mkhutu kudzamveka
يَوْمَ يَفِرُّ الْمَرْءُ مِنْ أَخِيهِ (34)
Patsiku limene munthu adzakana m’bale wake
وَأُمِّهِ وَأَبِيهِ (35)
Amai ake ndi bambo ake
وَصَاحِبَتِهِ وَبَنِيهِ (36)
Mkazi wake ndi ana ake
لِكُلِّ امْرِئٍ مِّنْهُمْ يَوْمَئِذٍ شَأْنٌ يُغْنِيهِ (37)
Chifukwa aliyense patsiku limeneli, adzakhala otangwanika ndi mavuto ake
وُجُوهٌ يَوْمَئِذٍ مُّسْفِرَةٌ (38)
Patsiku limeneli padzakhala nkhope zambiri zowala
ضَاحِكَةٌ مُّسْتَبْشِرَةٌ (39)
Zosekerera ndi zachimwemwe chifukwa cha nkhani yabwino
وَوُجُوهٌ يَوْمَئِذٍ عَلَيْهَا غَبَرَةٌ (40)
Ndipo pa tsikuli padzakhala nkhope zina zokutidwa ndi fumbi
تَرْهَقُهَا قَتَرَةٌ (41)
M’dima udzakuta iwo
أُولَٰئِكَ هُمُ الْكَفَرَةُ الْفَجَرَةُ (42)
Awa adzakhala anthu osakhulupirira ndi ochita zoipa
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas