عَبَسَ وَتَوَلَّىٰ (1) Iye anachita matsinya ndi kuyang’ana kumbali |
أَن جَاءَهُ الْأَعْمَىٰ (2) Chifukwa munthu wakhungu anadza kwa iye |
وَمَا يُدْرِيكَ لَعَلَّهُ يَزَّكَّىٰ (3) Ndipo iwe ungadziwe bwanji kuti mwina angadziyeretse |
أَوْ يَذَّكَّرُ فَتَنفَعَهُ الذِّكْرَىٰ (4) Kapena iye adzalandira chenjezo ndipo chenjezo likanamupindulira kanthu kena |
أَمَّا مَنِ اسْتَغْنَىٰ (5) Koma iye amene amadziyesa kuti sasowa kanthu |
فَأَنتَ لَهُ تَصَدَّىٰ (6) Ameneyo ndiye amene uli naye ndi chidwi |
وَمَا عَلَيْكَ أَلَّا يَزَّكَّىٰ (7) Kodi uli nazo chiani ngati iye sadziyeretsa |
وَأَمَّا مَن جَاءَكَ يَسْعَىٰ (8) Koma kwa iye amene amakuthamangira |
وَهُوَ يَخْشَىٰ (9) Ndipo iye amaopa |
فَأَنتَ عَنْهُ تَلَهَّىٰ (10) Iwe siudamulabadire ayi |
كَلَّا إِنَّهَا تَذْكِرَةٌ (11) Iyayi! Ndithudi chimenechi ndi chikumbutso |
فَمَن شَاءَ ذَكَرَهُ (12) Muloleni aliyense amene afuna kuti achilabadire |
فِي صُحُفٍ مُّكَرَّمَةٍ (13) Ichi chidalembedwa m’Buku la Mulungu lolemekezeka |
مَّرْفُوعَةٍ مُّطَهَّرَةٍ (14) Loyeretsedwa ndi losungidwa bwino ndi loyera |
بِأَيْدِي سَفَرَةٍ (15) M’manja mwa Alembi |
كِرَامٍ بَرَرَةٍ (16) Wolemekezeka ndipo womvera |
قُتِلَ الْإِنسَانُ مَا أَكْفَرَهُ (17) Atembereredwe munthu! Kodi ndi chiani chili kumuletsa kuthokoza |
مِنْ أَيِّ شَيْءٍ خَلَقَهُ (18) Kodi Iye adamulenga kuchokera ku chiyani |
مِن نُّطْفَةٍ خَلَقَهُ فَقَدَّرَهُ (19) Kuchokera ku dontho la umuna, Iye adamulenga ndipo adamukonza bwino |
ثُمَّ السَّبِيلَ يَسَّرَهُ (20) Ndipo Iye adamukonzera iye njira yapafupi |
ثُمَّ أَمَاتَهُ فَأَقْبَرَهُ (21) Ndipo amamupha ndi kumusunga m’manda |
ثُمَّ إِذَا شَاءَ أَنشَرَهُ (22) Ndithudi Iye adzamudzutsa monga momwe afunira |
كَلَّا لَمَّا يَقْضِ مَا أَمَرَهُ (23) Iyayi, koma munthu sanachite zimene Iye adamulamulira |
فَلْيَنظُرِ الْإِنسَانُ إِلَىٰ طَعَامِهِ (24) Mulekeni munthu kuti aganize za chakudya chake |
أَنَّا صَبَبْنَا الْمَاءَ صَبًّا (25) Kuti Ife timagwetsa mvula yambiri |
ثُمَّ شَقَقْنَا الْأَرْضَ شَقًّا (26) Ndipo timaphwanya nthaka |
فَأَنبَتْنَا فِيهَا حَبًّا (27) Ndipo Ife Al-Takwir 641 timameretsa njere |
وَعِنَبًا وَقَضْبًا (28) Mphesa ndi Msipu |
وَزَيْتُونًا وَنَخْلًا (29) Mitengo ya mafuta, ndi mitengo ya tende |
وَحَدَائِقَ غُلْبًا (30) Ndi minda imene ili ndi mitengo yambiri |
وَفَاكِهَةً وَأَبًّا (31) Ndi mitengo ya zipatso ndi msipu |
مَّتَاعًا لَّكُمْ وَلِأَنْعَامِكُمْ (32) Chakudya cha inu ndi ziweto zanu |
فَإِذَا جَاءَتِ الصَّاخَّةُ (33) Koma pamene kulira kogonthetsa mkhutu kudzamveka |
يَوْمَ يَفِرُّ الْمَرْءُ مِنْ أَخِيهِ (34) Patsiku limene munthu adzakana m’bale wake |
وَأُمِّهِ وَأَبِيهِ (35) Amai ake ndi bambo ake |
وَصَاحِبَتِهِ وَبَنِيهِ (36) Mkazi wake ndi ana ake |
لِكُلِّ امْرِئٍ مِّنْهُمْ يَوْمَئِذٍ شَأْنٌ يُغْنِيهِ (37) Chifukwa aliyense patsiku limeneli, adzakhala otangwanika ndi mavuto ake |
وُجُوهٌ يَوْمَئِذٍ مُّسْفِرَةٌ (38) Patsiku limeneli padzakhala nkhope zambiri zowala |
ضَاحِكَةٌ مُّسْتَبْشِرَةٌ (39) Zosekerera ndi zachimwemwe chifukwa cha nkhani yabwino |
وَوُجُوهٌ يَوْمَئِذٍ عَلَيْهَا غَبَرَةٌ (40) Ndipo pa tsikuli padzakhala nkhope zina zokutidwa ndi fumbi |
تَرْهَقُهَا قَتَرَةٌ (41) M’dima udzakuta iwo |
أُولَٰئِكَ هُمُ الْكَفَرَةُ الْفَجَرَةُ (42) Awa adzakhala anthu osakhulupirira ndi ochita zoipa |