| وَالنَّازِعَاتِ غَرْقًا (1) Pali iwo amene amalanda mwankhanza
 | 
| وَالنَّاشِطَاتِ نَشْطًا (2) Ndi pali iwo amene amachotsa mwaufulu
 | 
| وَالسَّابِحَاتِ سَبْحًا (3) Ndi pali iwo amene amauluka
 | 
| فَالسَّابِقَاتِ سَبْقًا (4) Ndi pali iwo amene amathamanga ngati ali pa liwiro loopsya
 | 
| فَالْمُدَبِّرَاتِ أَمْرًا (5) Ndi pali angelo amene amakwaniritsa kuchita malamulo a Ambuye wawo
 | 
| يَوْمَ تَرْجُفُ الرَّاجِفَةُ (6) Patsiku limene dziko ndi mapiri zidzagwedezeka kwambiri
 | 
| تَتْبَعُهَا الرَّادِفَةُ (7) Ndi kulira kwa lipenga kawiri
 | 
| قُلُوبٌ يَوْمَئِذٍ وَاجِفَةٌ (8) Mitima, patsiku limeneli, idzafumuka ndi kuda nkhawa
 | 
| أَبْصَارُهَا خَاشِعَةٌ (9) Maso awo atagwetsa pansi
 | 
| يَقُولُونَ أَإِنَّا لَمَرْدُودُونَ فِي الْحَافِرَةِ (10) Iwo amanena kuti: “Kodi ife tidzabwerera monga momwe tinali poyamba?”
 | 
| أَإِذَا كُنَّا عِظَامًا نَّخِرَةً (11) “Angakhale mafupa athu ataola?”
 | 
| قَالُوا تِلْكَ إِذًا كَرَّةٌ خَاسِرَةٌ (12) Iwo amati: “Kubwerera kotero ndi kopanda phindu.”
 | 
| فَإِنَّمَا هِيَ زَجْرَةٌ وَاحِدَةٌ (13) Koma udzakhala mfuwu umodzi okha
 | 
| فَإِذَا هُم بِالسَّاهِرَةِ (14) Pamene, taona, iwo adzadzipeza okha ali pamwamba pa nthaka ali ndi moyo
 | 
| هَلْ أَتَاكَ حَدِيثُ مُوسَىٰ (15) Kodiinumudaimvankhaniya Mose
 | 
| إِذْ نَادَاهُ رَبُّهُ بِالْوَادِ الْمُقَدَّسِ طُوًى (16) PameneAmbuye wake adamuitana mu dambo lodalitsika la Tuwa
 | 
| اذْهَبْ إِلَىٰ فِرْعَوْنَ إِنَّهُ طَغَىٰ (17) “Pita kwa Farao; Ndithudi iye waphwanya malamulo mopyola muyezo.”
 | 
| فَقُلْ هَل لَّكَ إِلَىٰ أَن تَزَكَّىٰ (18) “Ndipo ukamuuze kuti: Kodi ungadziyeretse wekha?”
 | 
| وَأَهْدِيَكَ إِلَىٰ رَبِّكَ فَتَخْشَىٰ (19) “Ndi kuti ine ndikulondolere kwa Ambuye wako kuti uzimuopa Iye?”
 | 
| فَأَرَاهُ الْآيَةَ الْكُبْرَىٰ (20) Kotero iye adamuonetsa chizindikiro cha chikulu
 | 
| فَكَذَّبَ وَعَصَىٰ (21) Koma iye adachikana ndipo sanamvere
 | 
| ثُمَّ أَدْبَرَ يَسْعَىٰ (22) Iye adapitirizabe kuchita zoipa
 | 
| فَحَشَرَ فَنَادَىٰ (23) Ndipo iye adaitana anthu ake onse ndipo anafuula mokweza
 | 
| فَقَالَ أَنَا رَبُّكُمُ الْأَعْلَىٰ (24) Nati: “Ine ndine Ambuye wanu wapamwamba mwamba.” Al-Naziat
 | 
| فَأَخَذَهُ اللَّهُ نَكَالَ الْآخِرَةِ وَالْأُولَىٰ (25) Motero Mulungu adamugwetsera iye chilango chifukwa cha mau ake omaliza ndi oyamba
 | 
| إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَعِبْرَةً لِّمَن يَخْشَىٰ (26) Ndithudi mu izi muli phunziro lomveka kwa anthu oopa Mulungu
 | 
| أَأَنتُمْ أَشَدُّ خَلْقًا أَمِ السَّمَاءُ ۚ بَنَاهَا (27) Kodi inu ndinu ovuta kulenga kapena thambo la mlengalenga limene Mulungu adalilenga
 | 
| رَفَعَ سَمْكَهَا فَسَوَّاهَا (28) Iye analikweza m’mwamba ndi kulikonza bwino
 | 
| وَأَغْطَشَ لَيْلَهَا وَأَخْرَجَ ضُحَاهَا (29) Usiku wake amaukuta ndi m’dima ndipo masana ake amatulutsa kuwala
 | 
| وَالْأَرْضَ بَعْدَ ذَٰلِكَ دَحَاهَا (30) Ndipo pambuyo pake adalikulitsa dziko
 | 
| أَخْرَجَ مِنْهَا مَاءَهَا وَمَرْعَاهَا (31) Ndipo anatulutsa madzi ndi msipu
 | 
| وَالْجِبَالَ أَرْسَاهَا (32) Ndipo adazika mapiri molimbika
 | 
| مَتَاعًا لَّكُمْ وَلِأَنْعَامِكُمْ (33) Chakudya cha phindu kwa inu ndi kwa zoweta zanu
 | 
| فَإِذَا جَاءَتِ الطَّامَّةُ الْكُبْرَىٰ (34) Koma pamene mavuto akulu akudza
 | 
| يَوْمَ يَتَذَكَّرُ الْإِنسَانُ مَا سَعَىٰ (35) Tsiku limene munthu adzayamba kuganiza ntchito zake zonse
 | 
| وَبُرِّزَتِ الْجَحِيمُ لِمَن يَرَىٰ (36) Ndipo Gahena idzabweretsedwa pafupi kuti aliyense aione
 | 
| فَأَمَّا مَن طَغَىٰ (37) Ndipo kwa iye ophwanya malamulo
 | 
| وَآثَرَ الْحَيَاةَ الدُّنْيَا (38) Ndipo anasankha moyo wapadziko lino
 | 
| فَإِنَّ الْجَحِيمَ هِيَ الْمَأْوَىٰ (39) Ndithudi malo ake okhala ndi ku Gahena
 | 
| وَأَمَّا مَنْ خَافَ مَقَامَ رَبِّهِ وَنَهَى النَّفْسَ عَنِ الْهَوَىٰ (40) Koma kwa iwo amene amaopa kukaima pamaso pa Ambuye wake ndi machimo ndipo anali kudziletsa kuchita chifuniro chopanda pake
 | 
| فَإِنَّ الْجَنَّةَ هِيَ الْمَأْوَىٰ (41) Ndithudi adzakhala ku Paradiso
 | 
| يَسْأَلُونَكَ عَنِ السَّاعَةِ أَيَّانَ مُرْسَاهَا (42) Amakufunsa za nthawi imene chigumula chidzabwere
 | 
| فِيمَ أَنتَ مِن ذِكْرَاهَا (43) Iwe siudziwa zoti unene china chili chonse
 | 
| إِلَىٰ رَبِّكَ مُنتَهَاهَا (44) Ndi Ambuye wako yekha amene amadziwa tsiku
 | 
| إِنَّمَا أَنتَ مُنذِرُ مَن يَخْشَاهَا (45) Iwe ndiwe mchenjezi chabe kwa iwo amene ali kuliopa tsikuli
 | 
| كَأَنَّهُمْ يَوْمَ يَرَوْنَهَا لَمْ يَلْبَثُوا إِلَّا عَشِيَّةً أَوْ ضُحَاهَا (46) Patsiku limene iwo adzachiona chigumula, kudzakhala ngati kuti iwo sanakhale padziko lapansi nthawi yaitali koma usiku umodzi kapena usana wokha
 |