| إِذَا السَّمَاءُ انشَقَّتْ (1) Pamene thambo lidzang’ambika
 | 
| وَأَذِنَتْ لِرَبِّهَا وَحُقَّتْ (2) Ndipo limva ndi kumvera Ambuye wake ndipo ling’ambikadi
 | 
| وَإِذَا الْأَرْضُ مُدَّتْ (3) Pamene nthaka idzatambasulidwa
 | 
| وَأَلْقَتْ مَا فِيهَا وَتَخَلَّتْ (4) Ndi kutulutsa zonse zimene zinakwiriridwa m’kati mwake ndi kukhala yopanda kanthu
 | 
| وَأَذِنَتْ لِرَبِّهَا وَحُقَّتْ (5) Ndipo limva ndi kumvera Ambuye wake ndipo ling’ambikadi
 | 
| يَا أَيُّهَا الْإِنسَانُ إِنَّكَ كَادِحٌ إِلَىٰ رَبِّكَ كَدْحًا فَمُلَاقِيهِ (6) oh iwe munthu! Ndithudi iwe uli kubwerera kupita kwa Ambuye wako ndi ntchito zako. Kubwerera kotsimikizidwa. Motero udzakumana nazo
 | 
| فَأَمَّا مَنْ أُوتِيَ كِتَابَهُ بِيَمِينِهِ (7) Koma Iye amene adzapatsidwa Buku lake m’dzanja lamanja
 | 
| فَسَوْفَ يُحَاسَبُ حِسَابًا يَسِيرًا (8) Adzawerengedwa mosavuta
 | 
| وَيَنقَلِبُ إِلَىٰ أَهْلِهِ مَسْرُورًا (9) Ndipo adzabwerera kwa anthu ake ndi chisangalalo
 | 
| وَأَمَّا مَنْ أُوتِيَ كِتَابَهُ وَرَاءَ ظَهْرِهِ (10) Koma iye amene adzapatsidwa buku lake kumbuyo kwake
 | 
| فَسَوْفَ يَدْعُو ثُبُورًا (11) Iye adzalira
 | 
| وَيَصْلَىٰ سَعِيرًا (12) Ndipo akalowa ku moto walawi – lawi ku Gahena
 | 
| إِنَّهُ كَانَ فِي أَهْلِهِ مَسْرُورًا (13) Ndithudi iye adali wansangala pakati pa anthu ake
 | 
| إِنَّهُ ظَنَّ أَن لَّن يَحُورَ (14) Ndithudi iye anali kuganiza kuti sadzabwerera kwa Mulungu
 | 
| بَلَىٰ إِنَّ رَبَّهُ كَانَ بِهِ بَصِيرًا (15) Inde! Ndithudi Ambuye wake anali kuona zonse zimene iye ankachita
 | 
| فَلَا أُقْسِمُ بِالشَّفَقِ (16) Ine ndilumbira pali kufiira kwa kulowa kwa dzuwa
 | 
| وَاللَّيْلِ وَمَا وَسَقَ (17) Ndi pali usiku ndi zonse zimene umabweretsa mu mdima
 | 
| وَالْقَمَرِ إِذَا اتَّسَقَ (18) Ndi pali mwezi pamene ufika pa chimake penipeni
 | 
| لَتَرْكَبُنَّ طَبَقًا عَن طَبَقٍ (19) Ndipo inu, ndithudi, mudzayenda kupita kutsogolo, kuchoka apa ndi kufika apo
 | 
| فَمَا لَهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ (20) Kodi ndi chifukwa chiyani choti iwo alibe chikhulupiriro
 | 
| وَإِذَا قُرِئَ عَلَيْهِمُ الْقُرْآنُ لَا يَسْجُدُونَ ۩ (21) Ndipo pamene Korani ili kuwerengedwa kwa iwo sagwa pansi. Al-Buruj
 | 
| بَلِ الَّذِينَ كَفَرُوا يُكَذِّبُونَ (22) Iyayi! Koma anthu osakhulupirira amalikana
 | 
| وَاللَّهُ أَعْلَمُ بِمَا يُوعُونَ (23) Ndipo Mulungu amadziwa zinthu zonse zimene amasonkhanitsa
 | 
| فَبَشِّرْهُم بِعَذَابٍ أَلِيمٍ (24) Choncho auze iwo za chilango chowawa
 | 
| إِلَّا الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ لَهُمْ أَجْرٌ غَيْرُ مَمْنُونٍ (25) Kupatula okhawo amene akhulupirira ndi kumachita ntchito zabwino, chifukwa iwo ali ndi malipiro opanda malire
 |