إِذَا السَّمَاءُ انشَقَّتْ (1) Pamene thambo lidzang’ambika |
وَأَذِنَتْ لِرَبِّهَا وَحُقَّتْ (2) Ndipo limva ndi kumvera Ambuye wake ndipo ling’ambikadi |
وَإِذَا الْأَرْضُ مُدَّتْ (3) Pamene nthaka idzatambasulidwa |
وَأَلْقَتْ مَا فِيهَا وَتَخَلَّتْ (4) Ndi kutulutsa zonse zimene zinakwiriridwa m’kati mwake ndi kukhala yopanda kanthu |
وَأَذِنَتْ لِرَبِّهَا وَحُقَّتْ (5) Ndipo limva ndi kumvera Ambuye wake ndipo ling’ambikadi |
يَا أَيُّهَا الْإِنسَانُ إِنَّكَ كَادِحٌ إِلَىٰ رَبِّكَ كَدْحًا فَمُلَاقِيهِ (6) oh iwe munthu! Ndithudi iwe uli kubwerera kupita kwa Ambuye wako ndi ntchito zako. Kubwerera kotsimikizidwa. Motero udzakumana nazo |
فَأَمَّا مَنْ أُوتِيَ كِتَابَهُ بِيَمِينِهِ (7) Koma Iye amene adzapatsidwa Buku lake m’dzanja lamanja |
فَسَوْفَ يُحَاسَبُ حِسَابًا يَسِيرًا (8) Adzawerengedwa mosavuta |
وَيَنقَلِبُ إِلَىٰ أَهْلِهِ مَسْرُورًا (9) Ndipo adzabwerera kwa anthu ake ndi chisangalalo |
وَأَمَّا مَنْ أُوتِيَ كِتَابَهُ وَرَاءَ ظَهْرِهِ (10) Koma iye amene adzapatsidwa buku lake kumbuyo kwake |
فَسَوْفَ يَدْعُو ثُبُورًا (11) Iye adzalira |
وَيَصْلَىٰ سَعِيرًا (12) Ndipo akalowa ku moto walawi – lawi ku Gahena |
إِنَّهُ كَانَ فِي أَهْلِهِ مَسْرُورًا (13) Ndithudi iye adali wansangala pakati pa anthu ake |
إِنَّهُ ظَنَّ أَن لَّن يَحُورَ (14) Ndithudi iye anali kuganiza kuti sadzabwerera kwa Mulungu |
بَلَىٰ إِنَّ رَبَّهُ كَانَ بِهِ بَصِيرًا (15) Inde! Ndithudi Ambuye wake anali kuona zonse zimene iye ankachita |
فَلَا أُقْسِمُ بِالشَّفَقِ (16) Ine ndilumbira pali kufiira kwa kulowa kwa dzuwa |
وَاللَّيْلِ وَمَا وَسَقَ (17) Ndi pali usiku ndi zonse zimene umabweretsa mu mdima |
وَالْقَمَرِ إِذَا اتَّسَقَ (18) Ndi pali mwezi pamene ufika pa chimake penipeni |
لَتَرْكَبُنَّ طَبَقًا عَن طَبَقٍ (19) Ndipo inu, ndithudi, mudzayenda kupita kutsogolo, kuchoka apa ndi kufika apo |
فَمَا لَهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ (20) Kodi ndi chifukwa chiyani choti iwo alibe chikhulupiriro |
وَإِذَا قُرِئَ عَلَيْهِمُ الْقُرْآنُ لَا يَسْجُدُونَ ۩ (21) Ndipo pamene Korani ili kuwerengedwa kwa iwo sagwa pansi. Al-Buruj |
بَلِ الَّذِينَ كَفَرُوا يُكَذِّبُونَ (22) Iyayi! Koma anthu osakhulupirira amalikana |
وَاللَّهُ أَعْلَمُ بِمَا يُوعُونَ (23) Ndipo Mulungu amadziwa zinthu zonse zimene amasonkhanitsa |
فَبَشِّرْهُم بِعَذَابٍ أَلِيمٍ (24) Choncho auze iwo za chilango chowawa |
إِلَّا الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ لَهُمْ أَجْرٌ غَيْرُ مَمْنُونٍ (25) Kupatula okhawo amene akhulupirira ndi kumachita ntchito zabwino, chifukwa iwo ali ndi malipiro opanda malire |