The Quran in Chichewa - Surah Zalzalah translated into Chichewa, Surah Az-Zalzalah in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Zalzalah in Chichewa - نيانجا, Verses 8 - Surah Number 99 - Page 599.

| إِذَا زُلْزِلَتِ الْأَرْضُ زِلْزَالَهَا (1) Pamene dziko lidzagwedezeka ndi chivomerezi chomaliza |
| وَأَخْرَجَتِ الْأَرْضُ أَثْقَالَهَا (2) Ndipo pamene nthaka idzatulutsa katundu amene ali m’kati mwake |
| وَقَالَ الْإِنسَانُ مَا لَهَا (3) Ndipo munthu adzafunsa: “Kodi yatani?” |
| يَوْمَئِذٍ تُحَدِّثُ أَخْبَارَهَا (4) Pa tsikuli nthaka idzaulula zonse |
| بِأَنَّ رَبَّكَ أَوْحَىٰ لَهَا (5) Chifukwa Ambuye wako wayiuza kuti itero |
| يَوْمَئِذٍ يَصْدُرُ النَّاسُ أَشْتَاتًا لِّيُرَوْا أَعْمَالَهُمْ (6) Pa tsikuli mtundu wa anthu udzadza m’magulu osiyana siyana kudzalangizidwa ntchito zawo |
| فَمَن يَعْمَلْ مِثْقَالَ ذَرَّةٍ خَيْرًا يَرَهُ (7) Motero aliyense amene amachita chabwino cholemera ngati njere ya mpiru, adzachiona |
| وَمَن يَعْمَلْ مِثْقَالَ ذَرَّةٍ شَرًّا يَرَهُ (8) Ndipo aliyense amene amachita choipa cholemera ngati njere ya mpiru, adzachiona |