وَالطُّورِ (1) Ndi pali phiri |
وَكِتَابٍ مَّسْطُورٍ (2) Ndi pali Buku lolemekezeka |
فِي رَقٍّ مَّنشُورٍ (3) Lili chikopa chosapinda |
وَالْبَيْتِ الْمَعْمُورِ (4) Ndi pali Bait – Ul-Ma’mur (Nyumba imene ili kumwamba yolingana ndi Kaaba imene ili ku Makka ndipo imaonedwa ndi angelo pafupipafupi) |
وَالسَّقْفِ الْمَرْفُوعِ (5) Ndi pali denga lonyamuka |
وَالْبَحْرِ الْمَسْجُورِ (6) Ndi pali nyanja yodzadzidwa ndi madzi ambiri |
إِنَّ عَذَابَ رَبِّكَ لَوَاقِعٌ (7) Ndithudi chilango cha Ambuye wako chidzakwaniritsidwa |
مَّا لَهُ مِن دَافِعٍ (8) Palibe wina amene angachiletse |
يَوْمَ تَمُورُ السَّمَاءُ مَوْرًا (9) Pa tsiku limeneli, kumwamba kudzagwedezeka koopsa |
وَتَسِيرُ الْجِبَالُ سَيْرًا (10) Ndipo mapiri adzagudubuzika osakhalanso china chake |
فَوَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (11) Kotero tsoka, patsiku limeneli kwa anthu abodza |
الَّذِينَ هُمْ فِي خَوْضٍ يَلْعَبُونَ (12) Amene amatangwanika ndi mabodza |
يَوْمَ يُدَعُّونَ إِلَىٰ نَارِ جَهَنَّمَ دَعًّا (13) Patsikuli iwo adzatengedwa ndi kuponyedwa mwamphamvu ku moto wa ku Gahena |
هَٰذِهِ النَّارُ الَّتِي كُنتُم بِهَا تُكَذِّبُونَ (14) Uwu ndi moto umene mumati ndi bodza |
أَفَسِحْرٌ هَٰذَا أَمْ أَنتُمْ لَا تُبْصِرُونَ (15) Kodi amenewa ndi matsenga kapena simutha kuona |
اصْلَوْهَا فَاصْبِرُوا أَوْ لَا تَصْبِرُوا سَوَاءٌ عَلَيْكُمْ ۖ إِنَّمَا تُجْزَوْنَ مَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (16) Lawani kutentha kwake ndipo kaya inu mupirira kapena ayi, kwa inu ndi chimodzimodzi; inu muli kulandira malipiro a ntchito zomwe mumachita |
إِنَّ الْمُتَّقِينَ فِي جَنَّاتٍ وَنَعِيمٍ (17) Ndithudi iwo amene ali olungama, adzakhala m’minda mwamtendere |
فَاكِهِينَ بِمَا آتَاهُمْ رَبُّهُمْ وَوَقَاهُمْ رَبُّهُمْ عَذَابَ الْجَحِيمِ (18) Kusangalala chifukwa cha zimene Ambuye wawo wawapatsa ndipo Ambuye wawo wawapulumutsa ku chilango cha ku Gahena |
كُلُوا وَاشْرَبُوا هَنِيئًا بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (19) “Idyani ndi kumwa mwachisangalalo chifukwa cha ntchito zanu zabwino zomwe mudachita.” |
مُتَّكِئِينَ عَلَىٰ سُرُرٍ مَّصْفُوفَةٍ ۖ وَزَوَّجْنَاهُم بِحُورٍ عِينٍ (20) Iwo adzakhala pa mipando yawofowofo, yoikidwa m’mizere. Ndipo Ife tidzawakwatitsa kwa amene ali ndi maso akuluakulu ndi okongola |
وَالَّذِينَ آمَنُوا وَاتَّبَعَتْهُمْ ذُرِّيَّتُهُم بِإِيمَانٍ أَلْحَقْنَا بِهِمْ ذُرِّيَّتَهُمْ وَمَا أَلَتْنَاهُم مِّنْ عَمَلِهِم مِّن شَيْءٍ ۚ كُلُّ امْرِئٍ بِمَا كَسَبَ رَهِينٌ (21) Ndipo iwo amene amakhulupirira ndipo ana awo amawatsatira m’chipembedzo, oterewa tidzawakumaniza ndi mabanja awo ndipo Ife sitidzawachotsera chilichonse cha malipiro a ntchito zawo zabwino. Munthu aliyense adzafunsidwa malinga ndi ntchito zake |
وَأَمْدَدْنَاهُم بِفَاكِهَةٍ وَلَحْمٍ مِّمَّا يَشْتَهُونَ (22) Ndipo tidzawapatsa zipatso ndi nyama zimene iwo afuna |
يَتَنَازَعُونَ فِيهَا كَأْسًا لَّا لَغْوٌ فِيهَا وَلَا تَأْثِيمٌ (23) Kumeneko iwo adzapatsana wina ndi mnzake chikho chimene mulibe zinthu zopanda pake kapena uchimo |
۞ وَيَطُوفُ عَلَيْهِمْ غِلْمَانٌ لَّهُمْ كَأَنَّهُمْ لُؤْلُؤٌ مَّكْنُونٌ (24) Iwo adzazunguliridwa ndi kutchingidwa bwino ndi anyamata awoawo amene adzawatumizira ngati kuti iwo anali ndolo zobisika |
وَأَقْبَلَ بَعْضُهُمْ عَلَىٰ بَعْضٍ يَتَسَاءَلُونَ (25) Ndipo iwo adzafunsana wina ndi mnzake ndi kuyankhulitsana |
قَالُوا إِنَّا كُنَّا قَبْلُ فِي أَهْلِنَا مُشْفِقِينَ (26) Iwo adzati, “Kale ife tidali a mantha ndi mabanja athu.” |
فَمَنَّ اللَّهُ عَلَيْنَا وَوَقَانَا عَذَابَ السَّمُومِ (27) “Koma Mulungu wationetsera chisomo chake ndipo watipulumutsa ife ku chilango cha kumoto.” |
إِنَّا كُنَّا مِن قَبْلُ نَدْعُوهُ ۖ إِنَّهُ هُوَ الْبَرُّ الرَّحِيمُ (28) “Ndithudi ife tinali kumupempha Iye yekha. Ndithudi Iye ndiye Mwini chifundo ndi Mwini chisoni chosatha.” |
فَذَكِّرْ فَمَا أَنتَ بِنِعْمَتِ رَبِّكَ بِكَاهِنٍ وَلَا مَجْنُونٍ (29) Motero pitiriza kukumbutsa ndi kulalikira. Chifukwa cha chisomo cha Ambuye wako, iwe si ndiwe munthu wonyenga kapena wamisala |
أَمْ يَقُولُونَ شَاعِرٌ نَّتَرَبَّصُ بِهِ رَيْبَ الْمَنُونِ (30) Kapena iwo amati, “Ndi Mlakatuli, ife tili kuyembekezera kuti choipa chidze pa iye.” |
قُلْ تَرَبَّصُوا فَإِنِّي مَعَكُم مِّنَ الْمُتَرَبِّصِينَ (31) Nena, “Yembekezerani! Nanenso ndili mmodzi wa oyembekezera.” |
أَمْ تَأْمُرُهُمْ أَحْلَامُهُم بِهَٰذَا ۚ أَمْ هُمْ قَوْمٌ طَاغُونَ (32) Kodi ndi maganizo awo amene ali kumawauza izi kapena iwo ndi anthu amene amaswa malamulo mosadodoma |
أَمْ يَقُولُونَ تَقَوَّلَهُ ۚ بَل لَّا يُؤْمِنُونَ (33) Kodi kapena iwo amati, “Iye wapeka yekha uthengawu? Iyayi! iwo alibe chikhulupiriro.” |
فَلْيَأْتُوا بِحَدِيثٍ مِّثْلِهِ إِن كَانُوا صَادِقِينَ (34) Alekeni nawo abweretse mawu olingana ndi awa ngati iwo ali kunena zoona |
أَمْ خُلِقُوا مِنْ غَيْرِ شَيْءٍ أَمْ هُمُ الْخَالِقُونَ (35) Kodi iwo adalengedwa popanda china chake kapena iwo ndiwo a Namalenga |
أَمْ خَلَقُوا السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ ۚ بَل لَّا يُوقِنُونَ (36) Kapena ndiwo amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi? Iyayi! iwo alibe chikhulupiriro chokhazikika |
أَمْ عِندَهُمْ خَزَائِنُ رَبِّكَ أَمْ هُمُ الْمُصَيْطِرُونَ (37) Kodi ndiwo amene amasunga chuma cha Ambuye wako? Kapena iwo ndiwo a nkhanza amene ali ndi ulamuliro wonena chilichonse chimene afuna |
أَمْ لَهُمْ سُلَّمٌ يَسْتَمِعُونَ فِيهِ ۖ فَلْيَأْتِ مُسْتَمِعُهُم بِسُلْطَانٍ مُّبِينٍ (38) Kodi kapena iwo ali ndi njira yomvetsera zomwe zinali kunenedwa? Motero mulekeni kazitape wawo kuti apereke umboni wokwanira |
أَمْ لَهُ الْبَنَاتُ وَلَكُمُ الْبَنُونَ (39) Kodi kapena Iye ali ndi ana aakazi okha pamene inuyo muli ndi ana aamuna |
أَمْ تَسْأَلُهُمْ أَجْرًا فَهُم مِّن مَّغْرَمٍ مُّثْقَلُونَ (40) Kodi kapena iwe uli kuwafunsa malipiro kotero kuti iwo apanikizidwa kwambiri ndi ngongole |
أَمْ عِندَهُمُ الْغَيْبُ فَهُمْ يَكْتُبُونَ (41) Kodi kapena ali ndi zobisika ndipo amazilemba |
أَمْ يُرِيدُونَ كَيْدًا ۖ فَالَّذِينَ كَفَرُوا هُمُ الْمَكِيدُونَ (42) Kodi kapena ali kukonza chiwembu? Koma iwo amene sakhulupirira ndiwo amene ali ndi chiwembu |
أَمْ لَهُمْ إِلَٰهٌ غَيْرُ اللَّهِ ۚ سُبْحَانَ اللَّهِ عَمَّا يُشْرِكُونَ (43) Kodi kapena ali ndi mulungu wina kupatula Mulungu weniweni? Mulungu alemekezeke kuposa zimene iwo amamufanizira nazo |
وَإِن يَرَوْا كِسْفًا مِّنَ السَّمَاءِ سَاقِطًا يَقُولُوا سَحَابٌ مَّرْكُومٌ (44) Ndipo iwo akadaona gawo lina la kumwamba lili kugwa pansi ndipo iwo akadati, “Ndi mitambo youndana.” |
فَذَرْهُمْ حَتَّىٰ يُلَاقُوا يَوْمَهُمُ الَّذِي فِيهِ يُصْعَقُونَ (45) Motero alekeni mpaka pamene iwo akumana ndi tsiku lawo limene iwo adzakomoka ndi mantha |
يَوْمَ لَا يُغْنِي عَنْهُمْ كَيْدُهُمْ شَيْئًا وَلَا هُمْ يُنصَرُونَ (46) Tsiku limene chiwembu sichidzawathandiza china chilichonse ndipo chithandizo sichidzaperekedwa kwa iwo |
وَإِنَّ لِلَّذِينَ ظَلَمُوا عَذَابًا دُونَ ذَٰلِكَ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (47) Ndipo, ndithudi, onse amene amachita zoipa, kuli chilango china pa chilango ichi koma ambiri a iwo sadziwa |
وَاصْبِرْ لِحُكْمِ رَبِّكَ فَإِنَّكَ بِأَعْيُنِنَا ۖ وَسَبِّحْ بِحَمْدِ رَبِّكَ حِينَ تَقُومُ (48) Motero pirira podikira chiweruzo cha Ambuye wako, chifukwa ndithudi iwe uli kusamalidwa ndi Ife ndipo lemekeza Ambuye wako pamene uuka ku tulo |
وَمِنَ اللَّيْلِ فَسَبِّحْهُ وَإِدْبَارَ النُّجُومِ (49) Nthawi ya usiku, lemekeza ulemerero wake ndi pa nthawi yolowa nyenyezi |