×

سورة الطور باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة الطور

ترجمة معاني سورة الطور باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة الطور مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Tur in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة الطور باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 49 - رقم السورة 52 - الصفحة 523.

بسم الله الرحمن الرحيم

وَالطُّورِ (1)
Ndi pali phiri
وَكِتَابٍ مَّسْطُورٍ (2)
Ndi pali Buku lolemekezeka
فِي رَقٍّ مَّنشُورٍ (3)
Lili chikopa chosapinda
وَالْبَيْتِ الْمَعْمُورِ (4)
Ndi pali Bait – Ul-Ma’mur (Nyumba imene ili kumwamba yolingana ndi Kaaba imene ili ku Makka ndipo imaonedwa ndi angelo pafupipafupi)
وَالسَّقْفِ الْمَرْفُوعِ (5)
Ndi pali denga lonyamuka
وَالْبَحْرِ الْمَسْجُورِ (6)
Ndi pali nyanja yodzadzidwa ndi madzi ambiri
إِنَّ عَذَابَ رَبِّكَ لَوَاقِعٌ (7)
Ndithudi chilango cha Ambuye wako chidzakwaniritsidwa
مَّا لَهُ مِن دَافِعٍ (8)
Palibe wina amene angachiletse
يَوْمَ تَمُورُ السَّمَاءُ مَوْرًا (9)
Pa tsiku limeneli, kumwamba kudzagwedezeka koopsa
وَتَسِيرُ الْجِبَالُ سَيْرًا (10)
Ndipo mapiri adzagudubuzika osakhalanso china chake
فَوَيْلٌ يَوْمَئِذٍ لِّلْمُكَذِّبِينَ (11)
Kotero tsoka, patsiku limeneli kwa anthu abodza
الَّذِينَ هُمْ فِي خَوْضٍ يَلْعَبُونَ (12)
Amene amatangwanika ndi mabodza
يَوْمَ يُدَعُّونَ إِلَىٰ نَارِ جَهَنَّمَ دَعًّا (13)
Patsikuli iwo adzatengedwa ndi kuponyedwa mwamphamvu ku moto wa ku Gahena
هَٰذِهِ النَّارُ الَّتِي كُنتُم بِهَا تُكَذِّبُونَ (14)
Uwu ndi moto umene mumati ndi bodza
أَفَسِحْرٌ هَٰذَا أَمْ أَنتُمْ لَا تُبْصِرُونَ (15)
Kodi amenewa ndi matsenga kapena simutha kuona
اصْلَوْهَا فَاصْبِرُوا أَوْ لَا تَصْبِرُوا سَوَاءٌ عَلَيْكُمْ ۖ إِنَّمَا تُجْزَوْنَ مَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (16)
Lawani kutentha kwake ndipo kaya inu mupirira kapena ayi, kwa inu ndi chimodzimodzi; inu muli kulandira malipiro a ntchito zomwe mumachita
إِنَّ الْمُتَّقِينَ فِي جَنَّاتٍ وَنَعِيمٍ (17)
Ndithudi iwo amene ali olungama, adzakhala m’minda mwamtendere
فَاكِهِينَ بِمَا آتَاهُمْ رَبُّهُمْ وَوَقَاهُمْ رَبُّهُمْ عَذَابَ الْجَحِيمِ (18)
Kusangalala chifukwa cha zimene Ambuye wawo wawapatsa ndipo Ambuye wawo wawapulumutsa ku chilango cha ku Gahena
كُلُوا وَاشْرَبُوا هَنِيئًا بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (19)
“Idyani ndi kumwa mwachisangalalo chifukwa cha ntchito zanu zabwino zomwe mudachita.”
مُتَّكِئِينَ عَلَىٰ سُرُرٍ مَّصْفُوفَةٍ ۖ وَزَوَّجْنَاهُم بِحُورٍ عِينٍ (20)
Iwo adzakhala pa mipando yawofowofo, yoikidwa m’mizere. Ndipo Ife tidzawakwatitsa kwa amene ali ndi maso akuluakulu ndi okongola
وَالَّذِينَ آمَنُوا وَاتَّبَعَتْهُمْ ذُرِّيَّتُهُم بِإِيمَانٍ أَلْحَقْنَا بِهِمْ ذُرِّيَّتَهُمْ وَمَا أَلَتْنَاهُم مِّنْ عَمَلِهِم مِّن شَيْءٍ ۚ كُلُّ امْرِئٍ بِمَا كَسَبَ رَهِينٌ (21)
Ndipo iwo amene amakhulupirira ndipo ana awo amawatsatira m’chipembedzo, oterewa tidzawakumaniza ndi mabanja awo ndipo Ife sitidzawachotsera chilichonse cha malipiro a ntchito zawo zabwino. Munthu aliyense adzafunsidwa malinga ndi ntchito zake
وَأَمْدَدْنَاهُم بِفَاكِهَةٍ وَلَحْمٍ مِّمَّا يَشْتَهُونَ (22)
Ndipo tidzawapatsa zipatso ndi nyama zimene iwo afuna
يَتَنَازَعُونَ فِيهَا كَأْسًا لَّا لَغْوٌ فِيهَا وَلَا تَأْثِيمٌ (23)
Kumeneko iwo adzapatsana wina ndi mnzake chikho chimene mulibe zinthu zopanda pake kapena uchimo
۞ وَيَطُوفُ عَلَيْهِمْ غِلْمَانٌ لَّهُمْ كَأَنَّهُمْ لُؤْلُؤٌ مَّكْنُونٌ (24)
Iwo adzazunguliridwa ndi kutchingidwa bwino ndi anyamata awoawo amene adzawatumizira ngati kuti iwo anali ndolo zobisika
وَأَقْبَلَ بَعْضُهُمْ عَلَىٰ بَعْضٍ يَتَسَاءَلُونَ (25)
Ndipo iwo adzafunsana wina ndi mnzake ndi kuyankhulitsana
قَالُوا إِنَّا كُنَّا قَبْلُ فِي أَهْلِنَا مُشْفِقِينَ (26)
Iwo adzati, “Kale ife tidali a mantha ndi mabanja athu.”
فَمَنَّ اللَّهُ عَلَيْنَا وَوَقَانَا عَذَابَ السَّمُومِ (27)
“Koma Mulungu wationetsera chisomo chake ndipo watipulumutsa ife ku chilango cha kumoto.”
إِنَّا كُنَّا مِن قَبْلُ نَدْعُوهُ ۖ إِنَّهُ هُوَ الْبَرُّ الرَّحِيمُ (28)
“Ndithudi ife tinali kumupempha Iye yekha. Ndithudi Iye ndiye Mwini chifundo ndi Mwini chisoni chosatha.”
فَذَكِّرْ فَمَا أَنتَ بِنِعْمَتِ رَبِّكَ بِكَاهِنٍ وَلَا مَجْنُونٍ (29)
Motero pitiriza kukumbutsa ndi kulalikira. Chifukwa cha chisomo cha Ambuye wako, iwe si ndiwe munthu wonyenga kapena wamisala
أَمْ يَقُولُونَ شَاعِرٌ نَّتَرَبَّصُ بِهِ رَيْبَ الْمَنُونِ (30)
Kapena iwo amati, “Ndi Mlakatuli, ife tili kuyembekezera kuti choipa chidze pa iye.”
قُلْ تَرَبَّصُوا فَإِنِّي مَعَكُم مِّنَ الْمُتَرَبِّصِينَ (31)
Nena, “Yembekezerani! Nanenso ndili mmodzi wa oyembekezera.”
أَمْ تَأْمُرُهُمْ أَحْلَامُهُم بِهَٰذَا ۚ أَمْ هُمْ قَوْمٌ طَاغُونَ (32)
Kodi ndi maganizo awo amene ali kumawauza izi kapena iwo ndi anthu amene amaswa malamulo mosadodoma
أَمْ يَقُولُونَ تَقَوَّلَهُ ۚ بَل لَّا يُؤْمِنُونَ (33)
Kodi kapena iwo amati, “Iye wapeka yekha uthengawu? Iyayi! iwo alibe chikhulupiriro.”
فَلْيَأْتُوا بِحَدِيثٍ مِّثْلِهِ إِن كَانُوا صَادِقِينَ (34)
Alekeni nawo abweretse mawu olingana ndi awa ngati iwo ali kunena zoona
أَمْ خُلِقُوا مِنْ غَيْرِ شَيْءٍ أَمْ هُمُ الْخَالِقُونَ (35)
Kodi iwo adalengedwa popanda china chake kapena iwo ndiwo a Namalenga
أَمْ خَلَقُوا السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ ۚ بَل لَّا يُوقِنُونَ (36)
Kapena ndiwo amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi? Iyayi! iwo alibe chikhulupiriro chokhazikika
أَمْ عِندَهُمْ خَزَائِنُ رَبِّكَ أَمْ هُمُ الْمُصَيْطِرُونَ (37)
Kodi ndiwo amene amasunga chuma cha Ambuye wako? Kapena iwo ndiwo a nkhanza amene ali ndi ulamuliro wonena chilichonse chimene afuna
أَمْ لَهُمْ سُلَّمٌ يَسْتَمِعُونَ فِيهِ ۖ فَلْيَأْتِ مُسْتَمِعُهُم بِسُلْطَانٍ مُّبِينٍ (38)
Kodi kapena iwo ali ndi njira yomvetsera zomwe zinali kunenedwa? Motero mulekeni kazitape wawo kuti apereke umboni wokwanira
أَمْ لَهُ الْبَنَاتُ وَلَكُمُ الْبَنُونَ (39)
Kodi kapena Iye ali ndi ana aakazi okha pamene inuyo muli ndi ana aamuna
أَمْ تَسْأَلُهُمْ أَجْرًا فَهُم مِّن مَّغْرَمٍ مُّثْقَلُونَ (40)
Kodi kapena iwe uli kuwafunsa malipiro kotero kuti iwo apanikizidwa kwambiri ndi ngongole
أَمْ عِندَهُمُ الْغَيْبُ فَهُمْ يَكْتُبُونَ (41)
Kodi kapena ali ndi zobisika ndipo amazilemba
أَمْ يُرِيدُونَ كَيْدًا ۖ فَالَّذِينَ كَفَرُوا هُمُ الْمَكِيدُونَ (42)
Kodi kapena ali kukonza chiwembu? Koma iwo amene sakhulupirira ndiwo amene ali ndi chiwembu
أَمْ لَهُمْ إِلَٰهٌ غَيْرُ اللَّهِ ۚ سُبْحَانَ اللَّهِ عَمَّا يُشْرِكُونَ (43)
Kodi kapena ali ndi mulungu wina kupatula Mulungu weniweni? Mulungu alemekezeke kuposa zimene iwo amamufanizira nazo
وَإِن يَرَوْا كِسْفًا مِّنَ السَّمَاءِ سَاقِطًا يَقُولُوا سَحَابٌ مَّرْكُومٌ (44)
Ndipo iwo akadaona gawo lina la kumwamba lili kugwa pansi ndipo iwo akadati, “Ndi mitambo youndana.”
فَذَرْهُمْ حَتَّىٰ يُلَاقُوا يَوْمَهُمُ الَّذِي فِيهِ يُصْعَقُونَ (45)
Motero alekeni mpaka pamene iwo akumana ndi tsiku lawo limene iwo adzakomoka ndi mantha
يَوْمَ لَا يُغْنِي عَنْهُمْ كَيْدُهُمْ شَيْئًا وَلَا هُمْ يُنصَرُونَ (46)
Tsiku limene chiwembu sichidzawathandiza china chilichonse ndipo chithandizo sichidzaperekedwa kwa iwo
وَإِنَّ لِلَّذِينَ ظَلَمُوا عَذَابًا دُونَ ذَٰلِكَ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (47)
Ndipo, ndithudi, onse amene amachita zoipa, kuli chilango china pa chilango ichi koma ambiri a iwo sadziwa
وَاصْبِرْ لِحُكْمِ رَبِّكَ فَإِنَّكَ بِأَعْيُنِنَا ۖ وَسَبِّحْ بِحَمْدِ رَبِّكَ حِينَ تَقُومُ (48)
Motero pirira podikira chiweruzo cha Ambuye wako, chifukwa ndithudi iwe uli kusamalidwa ndi Ife ndipo lemekeza Ambuye wako pamene uuka ku tulo
وَمِنَ اللَّيْلِ فَسَبِّحْهُ وَإِدْبَارَ النُّجُومِ (49)
Nthawi ya usiku, lemekeza ulemerero wake ndi pa nthawi yolowa nyenyezi
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس