×

Surah Adh-Dhariyat in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah zariyat

Translation of the Meanings of Surah zariyat in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah zariyat translated into Chichewa, Surah Adh-Dhariyat in Chichewa. We provide accurate translation of Surah zariyat in Chichewa - نيانجا, Verses 60 - Surah Number 51 - Page 520.

بسم الله الرحمن الرحيم

وَالذَّارِيَاتِ ذَرْوًا (1)
Pali mphepo imene imamwaza fumbi
فَالْحَامِلَاتِ وِقْرًا (2)
Ndi mitambo imene ili yolemedwa ndi madzi
فَالْجَارِيَاتِ يُسْرًا (3)
Ndi zombo zimene zimayenda mosavutika ndi mwabata
فَالْمُقَسِّمَاتِ أَمْرًا (4)
Ndipo pali iwo amene amagawa madalitso ndi chilolezo chathu
إِنَّمَا تُوعَدُونَ لَصَادِقٌ (5)
Ndithudi chimene mwalonjezedwa, ndithudi, ndi choona
وَإِنَّ الدِّينَ لَوَاقِعٌ (6)
Ndithudi chiweruzo chidzakwaniritsidwa
وَالسَّمَاءِ ذَاتِ الْحُبُكِ (7)
Pali kumwamba kumene kuli njira zambiri
إِنَّكُمْ لَفِي قَوْلٍ مُّخْتَلِفٍ (8)
Ndithudi inu muli ndi maganizo osiyana
يُؤْفَكُ عَنْهُ مَنْ أُفِكَ (9)
Amene abwezedwa ku icho ndiye amene wabwezedwa
قُتِلَ الْخَرَّاصُونَ (10)
wotembereredwa akhale amene amanama
الَّذِينَ هُمْ فِي غَمْرَةٍ سَاهُونَ (11)
Amene akutidwa ndi kusamvera
يَسْأَلُونَ أَيَّانَ يَوْمُ الدِّينِ (12)
Iwo amafunsa kuti, “Kodi tsiku lachiweruzo lidzadza liti?”
يَوْمَ هُمْ عَلَى النَّارِ يُفْتَنُونَ (13)
Tsiku limene iwo adzaweruzidwa ndi kuponyedwa ku Zariat 559 moto
ذُوقُوا فِتْنَتَكُمْ هَٰذَا الَّذِي كُنتُم بِهِ تَسْتَعْجِلُونَ (14)
Lawani chilango chanu! Ichi ndicho chimene munali kufuna kuti chidze msanga
إِنَّ الْمُتَّقِينَ فِي جَنَّاتٍ وَعُيُونٍ (15)
Ndithudi iwo amene amalewa machimo adzakhala m’minda imene ili ndi a kasupe
آخِذِينَ مَا آتَاهُمْ رَبُّهُمْ ۚ إِنَّهُمْ كَانُوا قَبْلَ ذَٰلِكَ مُحْسِنِينَ (16)
Kulandira zimene Ambuye wawo awapatsa. Ndithudi kale iwo anali kuchita zinthu zabwino
كَانُوا قَلِيلًا مِّنَ اللَّيْلِ مَا يَهْجَعُونَ (17)
Iwo anali kugona nthawi yochepa usiku
وَبِالْأَسْحَارِ هُمْ يَسْتَغْفِرُونَ (18)
Ndipo m’bandakucha anali kupempha chikhululukiro
وَفِي أَمْوَالِهِمْ حَقٌّ لِّلسَّائِلِ وَالْمَحْرُومِ (19)
Ndipo mu chuma chawo mudali gawo limene linali kuperekedwa kwa anthu opempha ndi osowa
وَفِي الْأَرْضِ آيَاتٌ لِّلْمُوقِنِينَ (20)
Ndipo m’dziko muli zizindikiro kwa iwo okhulupirira
وَفِي أَنفُسِكُمْ ۚ أَفَلَا تُبْصِرُونَ (21)
Ndi mizimu yanu kodi simungaone
وَفِي السَّمَاءِ رِزْقُكُمْ وَمَا تُوعَدُونَ (22)
Ndipo kumwamba ndiko kuli chakudya chanu ndi zimene muli kulonjezedwa
فَوَرَبِّ السَّمَاءِ وَالْأَرْضِ إِنَّهُ لَحَقٌّ مِّثْلَ مَا أَنَّكُمْ تَنطِقُونَ (23)
Ndiye, pali Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chimenechi ndi cholinga ndi choonadi chomwe inu mumayankhula
هَلْ أَتَاكَ حَدِيثُ ضَيْفِ إِبْرَاهِيمَ الْمُكْرَمِينَ (24)
Kodi udamva nkhani ya alendo olemekezeka a Abrahamu
إِذْ دَخَلُوا عَلَيْهِ فَقَالُوا سَلَامًا ۖ قَالَ سَلَامٌ قَوْمٌ مُّنكَرُونَ (25)
Pamene iwo adadza kwa iye, iwo adati, “Mtendere.” Ndipo iye adati, “Mtendere.” Ndipo iye adati, “Inu ndinu alendo kwa ine.”
فَرَاغَ إِلَىٰ أَهْلِهِ فَجَاءَ بِعِجْلٍ سَمِينٍ (26)
Ndipo iye atapita ku banja lake adabweretsa nyama ya ng’ombe yowotcha
فَقَرَّبَهُ إِلَيْهِمْ قَالَ أَلَا تَأْكُلُونَ (27)
Motero iye adadza nayo kwa iwo nati, “Kodi simufuna kudya?”
فَأَوْجَسَ مِنْهُمْ خِيفَةً ۖ قَالُوا لَا تَخَفْ ۖ وَبَشَّرُوهُ بِغُلَامٍ عَلِيمٍ (28)
Motero iye adayamba kuchita mantha mu mtima mwake. Ndipo iwo adati, “Usaope.” Ndipo iwo adamuuza nkhani yabwino yakubadwa kwa mwana wamwamuna yemwe adzakhala wanzeru kwambiri
فَأَقْبَلَتِ امْرَأَتُهُ فِي صَرَّةٍ فَصَكَّتْ وَجْهَهَا وَقَالَتْ عَجُوزٌ عَقِيمٌ (29)
Ndipo mkazi wake adadza modzichepetsa ndipo adamenya pa mphumi pake nati, “Nkhalamba yaikazi yosaberekapo!”
قَالُوا كَذَٰلِكِ قَالَ رَبُّكِ ۖ إِنَّهُ هُوَ الْحَكِيمُ الْعَلِيمُ (30)
Iwo adati, “Ngakhale ndi choncho, Ambuye wako wayankhula. Iye ndi wodzala ndi luntha ndiponso nzeru.”
۞ قَالَ فَمَا خَطْبُكُمْ أَيُّهَا الْمُرْسَلُونَ (31)
Iye adati, “Kodi inu Atumwi uthenga wanu ndi wotani?”
قَالُوا إِنَّا أُرْسِلْنَا إِلَىٰ قَوْمٍ مُّجْرِمِينَ (32)
Iwo adati, “Ife tatumidwa kwa anthu ochimwa.”
لِنُرْسِلَ عَلَيْهِمْ حِجَارَةً مِّن طِينٍ (33)
“Kuti tigwetse pa iwo miyala yamakande.”
مُّسَوَّمَةً عِندَ رَبِّكَ لِلْمُسْرِفِينَ (34)
“Idakonzedwa ndi Ambuye wako kudza kwa anthu oswa malamulo.”
فَأَخْرَجْنَا مَن كَانَ فِيهَا مِنَ الْمُؤْمِنِينَ (35)
Ndipo Ife tidatulutsa anthu okhulupirira amene adali momwemo
فَمَا وَجَدْنَا فِيهَا غَيْرَ بَيْتٍ مِّنَ الْمُسْلِمِينَ (36)
Koma sitidapezemo mabanja a Chisilamu kupatula banja limodzi lokha basi
وَتَرَكْنَا فِيهَا آيَةً لِّلَّذِينَ يَخَافُونَ الْعَذَابَ الْأَلِيمَ (37)
Ndipo Ife tidasiyamo chizindikiro kwa iwo amene amaopa chilango chowawa
وَفِي مُوسَىٰ إِذْ أَرْسَلْنَاهُ إِلَىٰ فِرْعَوْنَ بِسُلْطَانٍ مُّبِينٍ (38)
Ndi mwa Mose. Pamene tidamutumiza kwa Farawo ndi zizindikiro zooneka
فَتَوَلَّىٰ بِرُكْنِهِ وَقَالَ سَاحِرٌ أَوْ مَجْنُونٌ (39)
Koma Farawo adakana pamodzi ndi mafumu ake nati, “Ndiwe munthu wamatsenga kapena munthu wa misala.”
فَأَخَذْنَاهُ وَجُنُودَهُ فَنَبَذْنَاهُمْ فِي الْيَمِّ وَهُوَ مُلِيمٌ (40)
Motero tidamugwira pamodzi ndi gulu la asirikali ake ndi kuwamiza onse m’nyanja pamene iye ndiye adali wolakwa
وَفِي عَادٍ إِذْ أَرْسَلْنَا عَلَيْهِمُ الرِّيحَ الْعَقِيمَ (41)
Ndipo mwa a Aad pamene tidawatumizira mphepo yoononga
مَا تَذَرُ مِن شَيْءٍ أَتَتْ عَلَيْهِ إِلَّا جَعَلَتْهُ كَالرَّمِيمِ (42)
Imene sidasiye chilichonse chimene idalimbana nacho kupatula kuchiononga ndi kuchisandutsa phulusa
وَفِي ثَمُودَ إِذْ قِيلَ لَهُمْ تَمَتَّعُوا حَتَّىٰ حِينٍ (43)
Ndipo mwa anthu a Thamoud. Pamene adauzidwa kuti, “Basangalalani kanthawi kochepa.”
فَعَتَوْا عَنْ أَمْرِ رَبِّهِمْ فَأَخَذَتْهُمُ الصَّاعِقَةُ وَهُمْ يَنظُرُونَ (44)
Koma iwo adaphwanya lamulo la Ambuye wawo mwamwano, kotero mabingu adawaononga iwo ali kuona
فَمَا اسْتَطَاعُوا مِن قِيَامٍ وَمَا كَانُوا مُنتَصِرِينَ (45)
Kotero iwo adalibe mphamvu zodzuka kapena zodzitetezera
وَقَوْمَ نُوحٍ مِّن قَبْلُ ۖ إِنَّهُمْ كَانُوا قَوْمًا فَاسِقِينَ (46)
Ndi anthu a Nowa iwo asanadze. Ndithudi iwo adali anthu oswa malamulo
وَالسَّمَاءَ بَنَيْنَاهَا بِأَيْدٍ وَإِنَّا لَمُوسِعُونَ (47)
Ife tidakonza kumwamba mwamphamvu ndiponso mwaluso. Ndipo, ndithudi, ndife amene timapanga kukula kwa mlengalenga
وَالْأَرْضَ فَرَشْنَاهَا فَنِعْمَ الْمَاهِدُونَ (48)
Ndipo dziko, tidamwaza. Kodi ndife omwaza bwino bwanji
وَمِن كُلِّ شَيْءٍ خَلَقْنَا زَوْجَيْنِ لَعَلَّكُمْ تَذَكَّرُونَ (49)
Ndipo zonse zimene tidalenga tidazilenga ziwiriziwiri kuti mukhoza kukumbukira
فَفِرُّوا إِلَى اللَّهِ ۖ إِنِّي لَكُم مِّنْهُ نَذِيرٌ مُّبِينٌ (50)
Kotero thawirani kwa Mulungu. Ndithudi Ine ndine mchenjezi wooneka kwa inu wochokera kwa Iye
وَلَا تَجْعَلُوا مَعَ اللَّهِ إِلَٰهًا آخَرَ ۖ إِنِّي لَكُم مِّنْهُ نَذِيرٌ مُّبِينٌ (51)
Ndipo musapange fano kukhala lopembedzedwa pamodzi ndi Mulungu. Ndithudi ine ndine mchenjezi wooneka kwa inu wochokera kwa Iye
كَذَٰلِكَ مَا أَتَى الَّذِينَ مِن قَبْلِهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا قَالُوا سَاحِرٌ أَوْ مَجْنُونٌ (52)
Chimodzimodzi palibe Mtumwi amene adadza kwa anthu amene sadamunenere mawu ofanana monga akuti: “Wamatsenga kapena munthu wopenga!”
أَتَوَاصَوْا بِهِ ۚ بَلْ هُمْ قَوْمٌ طَاغُونَ (53)
Kodi uwu ndi mwambo umene akhala ali kusiyirana wina ndi mnzake? Iyayi, iwo ndi anthu amene ali kuswa malamulo mopyola muyeso
فَتَوَلَّ عَنْهُمْ فَمَا أَنتَ بِمَلُومٍ (54)
Kotero uwaleke chifukwa iwe ulibe mlandu
وَذَكِّرْ فَإِنَّ الذِّكْرَىٰ تَنفَعُ الْمُؤْمِنِينَ (55)
Ndipo kumbutsa chifukwa chikumbutso chimathandiza anthu okhulupirira
وَمَا خَلَقْتُ الْجِنَّ وَالْإِنسَ إِلَّا لِيَعْبُدُونِ (56)
Ndipo Ine ndidalenga majini ndi anthu kuti azindipembedza Ine
مَا أُرِيدُ مِنْهُم مِّن رِّزْقٍ وَمَا أُرِيدُ أَن يُطْعِمُونِ (57)
Ine sindiwapempha chakudya ndipo sindiwafunsa kuti azindidyetsa Ine
إِنَّ اللَّهَ هُوَ الرَّزَّاقُ ذُو الْقُوَّةِ الْمَتِينُ (58)
Ndithudi ndi Mulungu yekha amene amapereka chakudya chonse, Mwini mphamvu zonse ndi wolimba kwambiri
فَإِنَّ لِلَّذِينَ ظَلَمُوا ذَنُوبًا مِّثْلَ ذَنُوبِ أَصْحَابِهِمْ فَلَا يَسْتَعْجِلُونِ (59)
Ndithudi anthu onse olakwa adzalandira gawo longa limene anzawo olakwa akale adalandira, kotero asandifunse Ine kuchita mofulumira
فَوَيْلٌ لِّلَّذِينَ كَفَرُوا مِن يَوْمِهِمُ الَّذِي يُوعَدُونَ (60)
Kotero tsoka kwa onse osakhulupirira kuchokera ku tsiku lomwe iwo alonjezedwa
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas