إِذَا وَقَعَتِ الْوَاقِعَةُ (1) Pamene ola la chiweruzo lidza |
لَيْسَ لِوَقْعَتِهَا كَاذِبَةٌ (2) Ndipo palibe mzimu umene udzakana kudza kwake |
خَافِضَةٌ رَّافِعَةٌ (3) Kutsitsa gulu lina ndikukweza gulu linzake |
إِذَا رُجَّتِ الْأَرْضُ رَجًّا (4) Pamene dziko lidzagwedezeka ndi chigwedezo choopsya |
وَبُسَّتِ الْجِبَالُ بَسًّا (5) Ndi pamene mapiri adzafumbutuka kukhala fumbi lokhalokha |
فَكَانَتْ هَبَاءً مُّنبَثًّا (6) Motero iwo adzakhala fumbi louluzika paliponse |
وَكُنتُمْ أَزْوَاجًا ثَلَاثَةً (7) Ndipo inu mudzagawidwa m’magulu atatu |
فَأَصْحَابُ الْمَيْمَنَةِ مَا أَصْحَابُ الْمَيْمَنَةِ (8) Iwo a ku dzanja la manja. Kodi a ku dzanja la manja adzakhala ndani |
وَأَصْحَابُ الْمَشْأَمَةِ مَا أَصْحَابُ الْمَشْأَمَةِ (9) Iwo akudzanja la mazere. Kodi akudzanja la mazere adzakhala ndani |
وَالسَّابِقُونَ السَّابِقُونَ (10) Ndipo gulu la iwo amene adzakhala kutsogolo m’chikhulupiriro adzakhala kutsogolo m’moyo umene uli nkudza |
أُولَٰئِكَ الْمُقَرَّبُونَ (11) Awa ndiwo amene adzakhala kufupi ndi Mulungu |
فِي جَنَّاتِ النَّعِيمِ (12) M’minda ya Paradiso |
ثُلَّةٌ مِّنَ الْأَوَّلِينَ (13) Gulu lalikulu lidzachokera ku mibadwo ya kale |
وَقَلِيلٌ مِّنَ الْآخِرِينَ (14) Ndi gulu lochepa lidzachokera ku mibadwo ya m’mbuyo mwake |
عَلَىٰ سُرُرٍ مَّوْضُونَةٍ (15) Iwo adzakhala pa mipando yawofowofo yomatidwa golide ndi miyala ya mtengo wapatali |
مُّتَّكِئِينَ عَلَيْهَا مُتَقَابِلِينَ (16) Atakhala pa iyo ndi kumayang’anizana |
يَطُوفُ عَلَيْهِمْ وِلْدَانٌ مُّخَلَّدُونَ (17) Iwo adzatumikiridwa ndi anyamata a muyaya |
بِأَكْوَابٍ وَأَبَارِيقَ وَكَأْسٍ مِّن مَّعِينٍ (18) Ndi mabakuli, miphika ndi zikho za vinyo wabwino |
لَّا يُصَدَّعُونَ عَنْهَا وَلَا يُنزِفُونَ (19) Amene sadzawawitsa mitu yawo kapena kuwatopetsa |
وَفَاكِهَةٍ مِّمَّا يَتَخَيَّرُونَ (20) Ndi zipatso zimene adzasankhepo |
وَلَحْمِ طَيْرٍ مِّمَّا يَشْتَهُونَ (21) Ndi nyama ya nkhuku imene angafune |
وَحُورٌ عِينٌ (22) Ndipo padzakhala anzawo okongola, a maso akulu ndi ochititsa kaso |
كَأَمْثَالِ اللُّؤْلُؤِ الْمَكْنُونِ (23) Monga ndolo zosamalidwa bwino |
جَزَاءً بِمَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (24) Malipiro a ntchito zimene adachita kale |
لَا يَسْمَعُونَ فِيهَا لَغْوًا وَلَا تَأْثِيمًا (25) Palibe nkhani zopanda pake kapena zolaula zimene adzamva |
إِلَّا قِيلًا سَلَامًا سَلَامًا (26) Kupatula mawu akuti Mtendere, Mtendere |
وَأَصْحَابُ الْيَمِينِ مَا أَصْحَابُ الْيَمِينِ (27) Iwo a kudzanja lamanja, kodi akudzanja lamanja adzakhala ndani |
فِي سِدْرٍ مَّخْضُودٍ (28) Iwo adzakhala pakati pa m’mithunzi ya mitengo ya Sidrah |
وَطَلْحٍ مَّنضُودٍ (29) Ndi m’mapata a nthochi zokhala ndi mikoko wina pamwamba pa unzake |
وَظِلٍّ مَّمْدُودٍ (30) M’mithunzi yotambasuka |
وَمَاءٍ مَّسْكُوبٍ (31) Pambali pa madzi osefukira |
وَفَاكِهَةٍ كَثِيرَةٍ (32) Ndi zipatso zochuluka |
لَّا مَقْطُوعَةٍ وَلَا مَمْنُوعَةٍ (33) Zimene nyengo yake sikutha ndipo kuchuluka kwake kudzakhalabe |
وَفُرُشٍ مَّرْفُوعَةٍ (34) Ndi pa mipando yawofowofo yokwezedwa |
إِنَّا أَنشَأْنَاهُنَّ إِنشَاءً (35) Ndithudi Ife tawalenga iwo mu chilengedwe cha padera |
فَجَعَلْنَاهُنَّ أَبْكَارًا (36) Ndi kuwapanga kukhala a Namwali abwino |
عُرُبًا أَتْرَابًا (37) A chikondi pa anzawo olingana nawo zaka |
لِّأَصْحَابِ الْيَمِينِ (38) A iwo amene adzakhala kudzanja lamanja |
ثُلَّةٌ مِّنَ الْأَوَّلِينَ (39) Gulu lochuluka lidzakhala lochokera ku mibadwo yoyamba, yakale |
وَثُلَّةٌ مِّنَ الْآخِرِينَ (40) Gulu lochuluka lidzakhala lochokera ku mibadwo ya pambuyo pake |
وَأَصْحَابُ الشِّمَالِ مَا أَصْحَابُ الشِّمَالِ (41) Gulu la anthu a kudzanja lamanzere. Kodi anthu a kudzanja la manzere adzakhala otani |
فِي سَمُومٍ وَحَمِيمٍ (42) M’katikati mwa malawi a moto ndi m’madzi ogaduka |
وَظِلٍّ مِّن يَحْمُومٍ (43) Ndi m’mithunzi ya utsi wakuda |
لَّا بَارِدٍ وَلَا كَرِيمٍ (44) Yosazizira kapena yabwino |
إِنَّهُمْ كَانُوا قَبْلَ ذَٰلِكَ مُتْرَفِينَ (45) Ndithudi iwo kale adali kukhala m’moyo wosavutika ndi opeza zinthu zambiri |
وَكَانُوا يُصِرُّونَ عَلَى الْحِنثِ الْعَظِيمِ (46) Ndipo adapitirira kuchita zoipa zikulu zikulu |
وَكَانُوا يَقُولُونَ أَئِذَا مِتْنَا وَكُنَّا تُرَابًا وَعِظَامًا أَإِنَّا لَمَبْعُوثُونَ (47) Ndipo iwo anali kukonda kunena kuti: “Pamene ife tafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, kodi tingadzaukitsidwenso?” |
أَوَآبَاؤُنَا الْأَوَّلُونَ (48) “Ndi makolo athu a nthawi ya makedzana?” |
قُلْ إِنَّ الْأَوَّلِينَ وَالْآخِرِينَ (49) Nena: “Ndithudi onse oyambirira ndi otsiriza.” |
لَمَجْمُوعُونَ إِلَىٰ مِيقَاتِ يَوْمٍ مَّعْلُومٍ (50) “Ndithudi onse adzasonkhanitsidwa pamodzi pa tsiku lokhazikitsidwa.” |
ثُمَّ إِنَّكُمْ أَيُّهَا الضَّالُّونَ الْمُكَذِّبُونَ (51) “Kuphatikiza inu nonse amene muchimwa ndi kukana choonadi.” |
لَآكِلُونَ مِن شَجَرٍ مِّن زَقُّومٍ (52) “Ndithudi inu mudzadya zipatso za mtengo wa Zaqqoom.” |
فَمَالِئُونَ مِنْهَا الْبُطُونَ (53) “Ndipo mudzakhutitsa mimba zanu ndi izo.” |
فَشَارِبُونَ عَلَيْهِ مِنَ الْحَمِيمِ (54) “Ndi kumwa madzi ogaduka.” |
فَشَارِبُونَ شُرْبَ الْهِيمِ (55) “Ndi kumwa monga momwe ngamira yodwala ndi yaludzu imamwera.” |
هَٰذَا نُزُلُهُمْ يَوْمَ الدِّينِ (56) Kumeneko ndiko kudzakhala kusangalala kwawo patsiku lachiweruzo |
نَحْنُ خَلَقْنَاكُمْ فَلَوْلَا تُصَدِّقُونَ (57) Ndife amene tidakulengani inu nanga ndi chifukwa chiyani simukhulupilira |
أَفَرَأَيْتُم مَّا تُمْنُونَ (58) Ndiuzeni za umuna umene mumatulutsa |
أَأَنتُمْ تَخْلُقُونَهُ أَمْ نَحْنُ الْخَالِقُونَ (59) Kodi ndinu amene mumaulenga kapena Ife ndife timaulenga |
نَحْنُ قَدَّرْنَا بَيْنَكُمُ الْمَوْتَ وَمَا نَحْنُ بِمَسْبُوقِينَ (60) Ife tidalamulira imfa kukhala pakati panu ndipo Ife sitingagonjetsedwe ayi |
عَلَىٰ أَن نُّبَدِّلَ أَمْثَالَكُمْ وَنُنشِئَكُمْ فِي مَا لَا تَعْلَمُونَ (61) Kukusinthani inu ndi kukulengani kukhala china chake chimene inu simuchidziwa |
وَلَقَدْ عَلِمْتُمُ النَّشْأَةَ الْأُولَىٰ فَلَوْلَا تَذَكَّرُونَ (62) Ndithudi inu mumadziwa za chilengedwe choyamba. Nanga ndi chifukwa chiyani simulabadira |
أَفَرَأَيْتُم مَّا تَحْرُثُونَ (63) Kodi mudayamba mwaganiza za mbewu imene mumabzala |
أَأَنتُمْ تَزْرَعُونَهُ أَمْ نَحْنُ الزَّارِعُونَ (64) Kodi ndinu amene mumaimeretsa kapena ndife amene timameretsa |
لَوْ نَشَاءُ لَجَعَلْنَاهُ حُطَامًا فَظَلْتُمْ تَفَكَّهُونَ (65) Ngati titafuna, Ife tikadaiphwanya m’timagawomagawo touma ndipo inu mukadayamba kudandaula |
إِنَّا لَمُغْرَمُونَ (66) Ndithudi ife tapatsidwa chingongole cholemera |
بَلْ نَحْنُ مَحْرُومُونَ (67) Iyayi. Koma tamanidwa |
أَفَرَأَيْتُمُ الْمَاءَ الَّذِي تَشْرَبُونَ (68) Kodi inu mumawaona madzi amene mumamwa |
أَأَنتُمْ أَنزَلْتُمُوهُ مِنَ الْمُزْنِ أَمْ نَحْنُ الْمُنزِلُونَ (69) Kodi ndinu amene mumawagwetsa kuchokera ku mitambo kapena ndife |
لَوْ نَشَاءُ جَعَلْنَاهُ أُجَاجًا فَلَوْلَا تَشْكُرُونَ (70) Chikadakhala chifuniro chathu tikadawapanga iwo kukhala a mchere. Nanga ndi chifukwa chiyani simuthokoza |
أَفَرَأَيْتُمُ النَّارَ الَّتِي تُورُونَ (71) Kodi inu mumaganizira za moto umene mumasonkha |
أَأَنتُمْ أَنشَأْتُمْ شَجَرَتَهَا أَمْ نَحْنُ الْمُنشِئُونَ (72) Kodi ndinu amene mumameretsa mtengo umene umayaka moto kapena ndife amene timaumeretsa |
نَحْنُ جَعَلْنَاهَا تَذْكِرَةً وَمَتَاعًا لِّلْمُقْوِينَ (73) Ife taupanga iwo kukhala chikumbutso ndi chinthu chothandiza anthu amene ali paulendo |
فَسَبِّحْ بِاسْمِ رَبِّكَ الْعَظِيمِ (74) Kotero lemekezani dzina la Ambuye wanu Wamkulu |
۞ فَلَا أُقْسِمُ بِمَوَاقِعِ النُّجُومِ (75) Ndipo ndilumbira pali nyenyezi zimene zili kugwa |
وَإِنَّهُ لَقَسَمٌ لَّوْ تَعْلَمُونَ عَظِيمٌ (76) Ndithudi ili ndi lonjezo lalikulu inu mukadadziwa |
إِنَّهُ لَقُرْآنٌ كَرِيمٌ (77) Ndithudi ndi Buku lolemekezeka la Korani |
فِي كِتَابٍ مَّكْنُونٍ (78) Limene lili m’Buku lotetezedwa |
لَّا يَمَسُّهُ إِلَّا الْمُطَهَّرُونَ (79) Palibe amene adzalikhudza kupatula oyeretsedwa okha |
تَنزِيلٌ مِّن رَّبِّ الْعَالَمِينَ (80) Chivumbulutso chochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse |
أَفَبِهَٰذَا الْحَدِيثِ أَنتُم مُّدْهِنُونَ (81) Kodi muli kunyozabe uthenga uwu |
وَتَجْعَلُونَ رِزْقَكُمْ أَنَّكُمْ تُكَذِّبُونَ (82) Mmalo mothokoza chifukwa cha zinthu zimene amakupatsani inu mumamukana Iye |
فَلَوْلَا إِذَا بَلَغَتِ الْحُلْقُومَ (83) Nanga ndi chifukwa chiyani inu simuthandiza pamene mzimu wa munthu amene ali kufa ufika pa khosi pake |
وَأَنتُمْ حِينَئِذٍ تَنظُرُونَ (84) Pamene panthawiyo, inu mumangoyang’ana |
وَنَحْنُ أَقْرَبُ إِلَيْهِ مِنكُمْ وَلَٰكِن لَّا تُبْصِرُونَ (85) Koma Ife tili pafupi ndi iye kuposa inu koma inu simutiona |
فَلَوْلَا إِن كُنتُمْ غَيْرَ مَدِينِينَ (86) Nanga ndi chifukwa chiyani simutero ngati inu simudzaweruzidwa patsogolo pake |
تَرْجِعُونَهَا إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (87) Bwezerani mzimuwo ngati ndinu anthu a choonadi |
فَأَمَّا إِن كَانَ مِنَ الْمُقَرَّبِينَ (88) Ndipo ngati iye ndi mmodzi wa anthu amene ali kufupi ndi Mulungu |
فَرَوْحٌ وَرَيْحَانٌ وَجَنَّتُ نَعِيمٍ (89) Iye adzapeza mpumulo ndi chakudya ndi munda wa chisangalalo |
وَأَمَّا إِن كَانَ مِنْ أَصْحَابِ الْيَمِينِ (90) Ndipo ngati iye ndi wam’gulu la anthu akudzanja la manja |
فَسَلَامٌ لَّكَ مِنْ أَصْحَابِ الْيَمِينِ (91) Kotero kuli mtendere kwa iwo a kudzanja lamanja |
وَأَمَّا إِن كَانَ مِنَ الْمُكَذِّبِينَ الضَّالِّينَ (92) Ndipo ngati iye ndi mmodzi wa iwo okana choonadi ndi amene amalakwa |
فَنُزُلٌ مِّنْ حَمِيمٍ (93) Motero kulandiridwa kwake kudzakhala kwa madzi otentha kwambiri |
وَتَصْلِيَةُ جَحِيمٍ (94) Ndi kulowetsedwa ku Gahena |
إِنَّ هَٰذَا لَهُوَ حَقُّ الْيَقِينِ (95) Ndithudi ichi ndi choonadi chosakayikitsa |
فَسَبِّحْ بِاسْمِ رَبِّكَ الْعَظِيمِ (96) Motero lemekezani dzina la Ambuye wanu, Wamkulu |