×

Surah Ar-Rahman in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Rahman

Translation of the Meanings of Surah Rahman in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Rahman translated into Chichewa, Surah Ar-Rahman in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Rahman in Chichewa - نيانجا, Verses 78 - Surah Number 55 - Page 531.

بسم الله الرحمن الرحيم

الرَّحْمَٰنُ (1)
Mwini Chifundo Chosatha
عَلَّمَ الْقُرْآنَ (2)
Ndiye amene adamphunzitsa munthu Korani
خَلَقَ الْإِنسَانَ (3)
Ndiye amene adalenga munthu
عَلَّمَهُ الْبَيَانَ (4)
Wamuphunzitsa iye mawu anzeru
الشَّمْسُ وَالْقَمَرُ بِحُسْبَانٍ (5)
Dzuwa ndi mwezi zimayenda m’misewu imene zinalamulidwa
وَالنَّجْمُ وَالشَّجَرُ يَسْجُدَانِ (6)
Zomera (kapena nyenyezi) ndi mitengo zonse zimagwada pomulambira Iye
وَالسَّمَاءَ رَفَعَهَا وَوَضَعَ الْمِيزَانَ (7)
Iye adakweza kumwamba ndi kukhazikitsa muyeso
أَلَّا تَطْغَوْا فِي الْمِيزَانِ (8)
Kuti inu musaphwanye muyeso
وَأَقِيمُوا الْوَزْنَ بِالْقِسْطِ وَلَا تُخْسِرُوا الْمِيزَانَ (9)
Kotero khazikitsani muyeso wachilungamo ndipo musayese monyenga
وَالْأَرْضَ وَضَعَهَا لِلْأَنَامِ (10)
Ndiye amene adalenga dziko lapansi kuti zolengedwa zake zizikhalamo
فِيهَا فَاكِهَةٌ وَالنَّخْلُ ذَاتُ الْأَكْمَامِ (11)
Mu ilo muli zipatso ndi mitengo ya tende yobereka phava la zipatso zambiri
وَالْحَبُّ ذُو الْعَصْفِ وَالرَّيْحَانُ (12)
Ndi chimanga chimene masamba ndi mapesi ake amadyedwa ndi ziweto. Ndi mitengo yonunkhira
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (13)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
خَلَقَ الْإِنسَانَ مِن صَلْصَالٍ كَالْفَخَّارِ (14)
Iye adalenga munthu kuchokera ku dothi monga dothi la mbiya
وَخَلَقَ الْجَانَّ مِن مَّارِجٍ مِّن نَّارٍ (15)
Ndipo adalenga majini kuchokera kumoto wopanda utsi
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (16)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
رَبُّ الْمَشْرِقَيْنِ وَرَبُّ الْمَغْرِبَيْنِ (17)
Ambuye wa kum’mawa kuwiri ndi Ambuye wa kumadzulo kuwiri
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (18)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
مَرَجَ الْبَحْرَيْنِ يَلْتَقِيَانِ (19)
Iye adasiya nyanja ziwiri kuti zikumane
بَيْنَهُمَا بَرْزَخٌ لَّا يَبْغِيَانِ (20)
Pakati pawo pali malire amene madzi a uku sangathe kudutsa kupita uko
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (21)
Kodi ndi zokoma ziti za Rahman 573 Ambuye wanu zimene mudzakana
يَخْرُجُ مِنْهُمَا اللُّؤْلُؤُ وَالْمَرْجَانُ (22)
Mu zonse muli nkhombe zazikulu ndi zazing’ono
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (23)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
وَلَهُ الْجَوَارِ الْمُنشَآتُ فِي الْبَحْرِ كَالْأَعْلَامِ (24)
Ndipo zake ndi zombo zimene zimayenda pa nyanja, zazikulu ngati mapiri
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (25)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
كُلُّ مَنْ عَلَيْهَا فَانٍ (26)
Zonse zimene zili pa dziko zidzatha
وَيَبْقَىٰ وَجْهُ رَبِّكَ ذُو الْجَلَالِ وَالْإِكْرَامِ (27)
Ndipo nkhope ya Ambuye wako mu Ufumu ndi mu Ulemerero idzakhalabe mpaka kalekale
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (28)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
يَسْأَلُهُ مَن فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ كُلَّ يَوْمٍ هُوَ فِي شَأْنٍ (29)
Zonse zimene zimakhala kumwamba ndi padziko lapansi zimapempha kwa Iye. Tsiku lililonse Iye amakhala ndi chochita
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (30)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
سَنَفْرُغُ لَكُمْ أَيُّهَ الثَّقَلَانِ (31)
Ife tidzadza kwa inu, Oh inu magulu awiri
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (32)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
يَا مَعْشَرَ الْجِنِّ وَالْإِنسِ إِنِ اسْتَطَعْتُمْ أَن تَنفُذُوا مِنْ أَقْطَارِ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ فَانفُذُوا ۚ لَا تَنفُذُونَ إِلَّا بِسُلْطَانٍ (33)
oh inu gulu la Majini ndi Anthu! Ngati muli ndi mphamvu zodutsa malire a kumwamba ndi dziko lapansi, dutsani. Komatu inu simungadutse popanda chilolezo
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (34)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
يُرْسَلُ عَلَيْكُمَا شُوَاظٌ مِّن نَّارٍ وَنُحَاسٌ فَلَا تَنتَصِرَانِ (35)
Malawi a moto ndi utsi zidzaponyedwa kwa inu nonse awiri ndipo simudzatha kudziteteza nokha
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (36)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
فَإِذَا انشَقَّتِ السَّمَاءُ فَكَانَتْ وَرْدَةً كَالدِّهَانِ (37)
Ndi pamene thambo lidzagawanika pakati ndikukhala lofiira ngati mafuta osungunuka
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (38)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
فَيَوْمَئِذٍ لَّا يُسْأَلُ عَن ذَنبِهِ إِنسٌ وَلَا جَانٌّ (39)
Motero patsiku limeneli, sipadzakhala mafunso kuchokera kwa Munthu kapena Majini okhudza machimo awo
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (40)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
يُعْرَفُ الْمُجْرِمُونَ بِسِيمَاهُمْ فَيُؤْخَذُ بِالنَّوَاصِي وَالْأَقْدَامِ (41)
ochimwa adzadziwika ndi zizindikiro ndipo adzawagwira tsumba ndi pamapazi pawo
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (42)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye
هَٰذِهِ جَهَنَّمُ الَّتِي يُكَذِّبُ بِهَا الْمُجْرِمُونَ (43)
Iyi ndi Gahena imene anthu ochimwa amati ndi bodza
يَطُوفُونَ بَيْنَهَا وَبَيْنَ حَمِيمٍ آنٍ (44)
Iwo adzalowa m’kati mwake ndi m’kati mwa madzi ogaduka
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (45)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
وَلِمَنْ خَافَ مَقَامَ رَبِّهِ جَنَّتَانِ (46)
Ndipo kwa iye amene aopa kuima pamaso pa Ambuye wawo, kudzakhala minda iwiri
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (47)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
ذَوَاتَا أَفْنَانٍ (48)
Zokhala ndi mphanda zotambasuka
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (49)
Kodi ndi zokoma ziti zaAmbuye wanu zimene mudzakana
فِيهِمَا عَيْنَانِ تَجْرِيَانِ (50)
Monse mudzakhala a kasupe awiri otumphuka
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (51)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
فِيهِمَا مِن كُلِّ فَاكِهَةٍ زَوْجَانِ (52)
M’menemu mudzakhala zipatso ziwiriziwiri za mitundumitundu
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (53)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
مُتَّكِئِينَ عَلَىٰ فُرُشٍ بَطَائِنُهَا مِنْ إِسْتَبْرَقٍ ۚ وَجَنَى الْجَنَّتَيْنِ دَانٍ (54)
Iwo adzagona pa makama amene nsalu yake ya m’kati idzakhala yasilika ndipo zipatso za m’minda iwiriyi zidzakhala pafupi pawo
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (55)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
فِيهِنَّ قَاصِرَاتُ الطَّرْفِ لَمْ يَطْمِثْهُنَّ إِنسٌ قَبْلَهُمْ وَلَا جَانٌّ (56)
M’menemo mudzakhala wodzisunga ndi ogwetsa nkhope zawo pansi amene Munthu kapena Majini sadawakhudze
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (57)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
كَأَنَّهُنَّ الْيَاقُوتُ وَالْمَرْجَانُ (58)
olingana ndi miyala ya rubiya ndi ndolo
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (59)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
هَلْ جَزَاءُ الْإِحْسَانِ إِلَّا الْإِحْسَانُ (60)
Kodi dipo la ntchito yabwino lingakhale lina loposa ubwino
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (61)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
وَمِن دُونِهِمَا جَنَّتَانِ (62)
Ndipo poonjezera pa minda iwiri pali minda ina iwiri
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (63)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
مُدْهَامَّتَانِ (64)
Yooneka mobiriwira
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (65)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
فِيهِمَا عَيْنَانِ نَضَّاخَتَانِ (66)
Monse mudzakhala a kasupe awiri otulutsa madzi ochuluka
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (67)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
فِيهِمَا فَاكِهَةٌ وَنَخْلٌ وَرُمَّانٌ (68)
Monse mudzakhala zipatso, tende ndi chimanga chachizungu
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (69)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
فِيهِنَّ خَيْرَاتٌ حِسَانٌ (70)
Mmenemo mudzakhala zinthu zokongola
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (71)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
حُورٌ مَّقْصُورَاتٌ فِي الْخِيَامِ (72)
Angwiro ndi okhala m’mahema
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (73)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
لَمْ يَطْمِثْهُنَّ إِنسٌ قَبْلَهُمْ وَلَا جَانٌّ (74)
Amene Munthu kapena Majini sadawakhudze
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (75)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
مُتَّكِئِينَ عَلَىٰ رَفْرَفٍ خُضْرٍ وَعَبْقَرِيٍّ حِسَانٍ (76)
Atakhala pa mipando yawofowofo, yobiriwira ndi mabedi okongola
فَبِأَيِّ آلَاءِ رَبِّكُمَا تُكَذِّبَانِ (77)
Kodi ndi zokoma ziti za Ambuye wanu zimene mudzakana
تَبَارَكَ اسْمُ رَبِّكَ ذِي الْجَلَالِ وَالْإِكْرَامِ (78)
Lidalitsike dzina la Ambuye wako, Mwini ulemerero, chuma ndi ulemu
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas