يُسَبِّحُ لِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ الْمَلِكِ الْقُدُّوسِ الْعَزِيزِ الْحَكِيمِ (1) Chilichonse chimene chili mlengalenga ndi padziko lapansi chimatamanda ndi kulemekeza Mulungu, Mfumu ya Mafumu, Woyera, Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru |
هُوَ الَّذِي بَعَثَ فِي الْأُمِّيِّينَ رَسُولًا مِّنْهُمْ يَتْلُو عَلَيْهِمْ آيَاتِهِ وَيُزَكِّيهِمْ وَيُعَلِّمُهُمُ الْكِتَابَ وَالْحِكْمَةَ وَإِن كَانُوا مِن قَبْلُ لَفِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (2) Ndiye amene adatumiza kugulu la anthu osaphunzira Mtumwi, wochokera m’gulu lawo, kuwauza iwo zizindikiro zake, kuwayeretsa ndi kuwaphunzitsa Buku. Ndithudi iwo anali kuchita zoipa kuyambira kale |
وَآخَرِينَ مِنْهُمْ لَمَّا يَلْحَقُوا بِهِمْ ۚ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (3) Ndipo Iye wamutumiza iye pamodzi ndi ena amene anali pakati pawo amene sadalowe m’gulu lawo. Ndipo Iye ndi Wamphamvu ndi Wanzeru |
ذَٰلِكَ فَضْلُ اللَّهِ يُؤْتِيهِ مَن يَشَاءُ ۚ وَاللَّهُ ذُو الْفَضْلِ الْعَظِيمِ (4) Chimenchi ndicho chisomo cha Mulungu chimene amachipereka kwa aliyense amene Iye wamufuna. Ndipo Mulungu ndiye Ambuye wachisomo chapamwamba chosatha |
مَثَلُ الَّذِينَ حُمِّلُوا التَّوْرَاةَ ثُمَّ لَمْ يَحْمِلُوهَا كَمَثَلِ الْحِمَارِ يَحْمِلُ أَسْفَارًا ۚ بِئْسَ مَثَلُ الْقَوْمِ الَّذِينَ كَذَّبُوا بِآيَاتِ اللَّهِ ۚ وَاللَّهُ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الظَّالِمِينَ (5) Fanizo la iwo amene adapatsidwa Buku la Chipangano Chakale ndipo adalephera kukwaniritsa malamulo ake, lili ngati Bulu amene amasenza katundu wambiri wolemera wa mabuku. Loipa ndi fanizo la anthu amene amakana zizindikiro za Mulungu. Ndipo Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa |
قُلْ يَا أَيُّهَا الَّذِينَ هَادُوا إِن زَعَمْتُمْ أَنَّكُمْ أَوْلِيَاءُ لِلَّهِ مِن دُونِ النَّاسِ فَتَمَنَّوُا الْمَوْتَ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (6) Nena: “oh inu Ayuda! Ngati inu mumaganiza kuti inu nokha ndinu abwenzi a Mulungu Al Jumua 599 kusiyana ndi anthu ena, pemphani imfa kuti idze pa inu ngati ndinu a chilungamo |
وَلَا يَتَمَنَّوْنَهُ أَبَدًا بِمَا قَدَّمَتْ أَيْدِيهِمْ ۚ وَاللَّهُ عَلِيمٌ بِالظَّالِمِينَ (7) Koma iwo sadzaipempha iyo chifukwa cha ntchito zimene manja awo adachita. Ndipo Mulungu amadziwa onse amene amachita zoipa |
قُلْ إِنَّ الْمَوْتَ الَّذِي تَفِرُّونَ مِنْهُ فَإِنَّهُ مُلَاقِيكُمْ ۖ ثُمَّ تُرَدُّونَ إِلَىٰ عَالِمِ الْغَيْبِ وَالشَّهَادَةِ فَيُنَبِّئُكُم بِمَا كُنتُمْ تَعْمَلُونَ (8) Nena: “Ndithudi imfa imene muli kuopa, ndithudi, idzadza pa inu ndipo inu mudzabwerera kwa Iye amene amadziwa zinthu zonse zobisika ndi zooneka ndipo Iye adzakuuzani zonse zimene munali kuchita |
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِذَا نُودِيَ لِلصَّلَاةِ مِن يَوْمِ الْجُمُعَةِ فَاسْعَوْا إِلَىٰ ذِكْرِ اللَّهِ وَذَرُوا الْبَيْعَ ۚ ذَٰلِكُمْ خَيْرٌ لَّكُمْ إِن كُنتُمْ تَعْلَمُونَ (9) Oh inu anthu okhulupirira! Ngati mumva kuitana kwa mapemphero a masana a tsiku lachisanu, fulumirani kukakumbukira Mulungu ndipo siyani ntchito zanu. Chimenechondichochabwinokwainungatimukadadziwa |
فَإِذَا قُضِيَتِ الصَّلَاةُ فَانتَشِرُوا فِي الْأَرْضِ وَابْتَغُوا مِن فَضْلِ اللَّهِ وَاذْكُرُوا اللَّهَ كَثِيرًا لَّعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ (10) Ndipo ngati mapemphero akutha, mukhoza kumwazikana, padziko kukafunafuna zokoma za Mulungu ndipo muzikumbukira Mulungu kwambiri kuti mukhale opambana |
وَإِذَا رَأَوْا تِجَارَةً أَوْ لَهْوًا انفَضُّوا إِلَيْهَا وَتَرَكُوكَ قَائِمًا ۚ قُلْ مَا عِندَ اللَّهِ خَيْرٌ مِّنَ اللَّهْوِ وَمِنَ التِّجَارَةِ ۚ وَاللَّهُ خَيْرُ الرَّازِقِينَ (11) Ndipo iwo akaona katundu wa malonda kapena zinthu zina zosangalatsa, iwo amazithamangira izo ndi kukusiya wekha uli chiimire pa mapamphero. Nena: “Zimene Mulungu ali nazo ndi zabwino kwambiri kuposa katundu wina aliyense wamalonda kapena chisangalalo.” Mulungu ndiye amene amapereka moolowa manja |