×

Surah Al-Haqqah in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Al-Haqqah

Translation of the Meanings of Surah Al-Haqqah in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Al-Haqqah translated into Chichewa, Surah Al-Haqqah in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Al-Haqqah in Chichewa - نيانجا, Verses 52 - Surah Number 69 - Page 566.

بسم الله الرحمن الرحيم

الْحَاقَّةُ (1)
Choonadi chenicheni
مَا الْحَاقَّةُ (2)
Kodi choonadi chenicheni ndi chiyani
وَمَا أَدْرَاكَ مَا الْحَاقَّةُ (3)
Kodi ndi chiyani chimene chingakupangitse kuti udziwe kuti choonadi chenicheni ndi chiti
كَذَّبَتْ ثَمُودُ وَعَادٌ بِالْقَارِعَةِ (4)
Mtundu wa Thamoud ndi Ad adakana ola la chionongeko
فَأَمَّا ثَمُودُ فَأُهْلِكُوا بِالطَّاغِيَةِ (5)
Ndipo anthu a Thamoud adaonongeka ndi mfuwu woopsya
وَأَمَّا عَادٌ فَأُهْلِكُوا بِرِيحٍ صَرْصَرٍ عَاتِيَةٍ (6)
Ndipo anthu a Aad adaonongeka ndi chimphepo cha mkuntho
سَخَّرَهَا عَلَيْهِمْ سَبْعَ لَيَالٍ وَثَمَانِيَةَ أَيَّامٍ حُسُومًا فَتَرَى الْقَوْمَ فِيهَا صَرْعَىٰ كَأَنَّهُمْ أَعْجَازُ نَخْلٍ خَاوِيَةٍ (7)
Chimene Mulungu adachilamulira kuti chikunthe pa iwo usiku usanu ndi uwiri ndi usana usanu ndi utatu mosalekeza. Moti iwe ukadawaona anthu atagonagona ukadayesa kuti ndi mitengo ya migwalangwa yakugwa
فَهَلْ تَرَىٰ لَهُم مِّن بَاقِيَةٍ (8)
Kodi uli kuona wina wa iwo opulumuka
وَجَاءَ فِرْعَوْنُ وَمَن قَبْلَهُ وَالْمُؤْتَفِكَاتُ بِالْخَاطِئَةِ (9)
Ndipo Farao ndi anthu amene adalipo iye asadabadwe, ndi a mizinda imene idaonongeka anali kuchita zoipa
فَعَصَوْا رَسُولَ رَبِّهِمْ فَأَخَذَهُمْ أَخْذَةً رَّابِيَةً (10)
Ndipo iwo sanamvere Mtumwi wochokera kwa Ambuye wawo ndipo Iye adawalanga ndi chilango chowawa zedi
إِنَّا لَمَّا طَغَى الْمَاءُ حَمَلْنَاكُمْ فِي الْجَارِيَةِ (11)
Ndithudi!Pamenemadzianasefukira,Ifetidakunyamulani inu m’chombo
لِنَجْعَلَهَا لَكُمْ تَذْكِرَةً وَتَعِيَهَا أُذُنٌ وَاعِيَةٌ (12)
Kuti tikhoza kuchipanga icho kukhala chikumbutso ndi kuti khutu la kumva limve
فَإِذَا نُفِخَ فِي الصُّورِ نَفْخَةٌ وَاحِدَةٌ (13)
Ndipo pamene lipenga lidzaimbidwa kamodzi
وَحُمِلَتِ الْأَرْضُ وَالْجِبَالُ فَدُكَّتَا دَكَّةً وَاحِدَةً (14)
Ndipo nthaka ndi mapiri anyamulidwa pamodzi ndi kuponyedwa pansi mwamphamvu kamodzi
فَيَوْمَئِذٍ وَقَعَتِ الْوَاقِعَةُ (15)
Patsiku limeneli chinthu choopsa chidzachitika
وَانشَقَّتِ السَّمَاءُ فَهِيَ يَوْمَئِذٍ وَاهِيَةٌ (16)
Ndipo thambo lidzaphwanyika ndipo lidzakhala lopanda mphamvu
وَالْمَلَكُ عَلَىٰ أَرْجَائِهَا ۚ وَيَحْمِلُ عَرْشَ رَبِّكَ فَوْقَهُمْ يَوْمَئِذٍ ثَمَانِيَةٌ (17)
Ndipo Angelo adzaima mbali zonse ndipo angelo asanu ndi atatu pa tsikuli adzanyamula Mpando wa Chifumu wa Ambuye wako
يَوْمَئِذٍ تُعْرَضُونَ لَا تَخْفَىٰ مِنكُمْ خَافِيَةٌ (18)
Patsiku limeneli mudzaweruzidwa ndipo palibe chinthu chachinsinsi chimene chidzabisika
فَأَمَّا مَنْ أُوتِيَ كِتَابَهُ بِيَمِينِهِ فَيَقُولُ هَاؤُمُ اقْرَءُوا كِتَابِيَهْ (19)
Ndipo yense amene adzapatsidwa Buku lake kudzanja lamanja adzati: “Ah taonani! Werengani Buku langa!”
إِنِّي ظَنَنتُ أَنِّي مُلَاقٍ حِسَابِيَهْ (20)
Ndithudi, ine ndidakhululupira kuti tsiku lina zochita zanga zidzaweruzidwa
فَهُوَ فِي عِيشَةٍ رَّاضِيَةٍ (21)
Kotero iye adzakhala ndi moyo wa chisangalalo
فِي جَنَّةٍ عَالِيَةٍ (22)
M’munda wapamwamba
قُطُوفُهَا دَانِيَةٌ (23)
Wa zipatso zokoma zimene zili pafupi
كُلُوا وَاشْرَبُوا هَنِيئًا بِمَا أَسْلَفْتُمْ فِي الْأَيَّامِ الْخَالِيَةِ (24)
Idyani ndipo imwani mmene mufunire chifukwa cha ntchito zanu zabwino zimene mudatumiza patsogolo panu m’masiku apitawo
وَأَمَّا مَنْ أُوتِيَ كِتَابَهُ بِشِمَالِهِ فَيَقُولُ يَا لَيْتَنِي لَمْ أُوتَ كِتَابِيَهْ (25)
Koma iye amene adzapatsidwe buku lake m’dzanja lamanzere, adzati: “Kukadakhala bwino ngati Buku langa likadakhala losaperekedwa kwa ine.”
وَلَمْ أَدْرِ مَا حِسَابِيَهْ (26)
“Ndipo sindikadziwa kuti zochita zanga zachuluka bwanji.”
يَا لَيْتَهَا كَانَتِ الْقَاضِيَةَ (27)
“Ikadakhala bwino imfa ikadangodza pa ine.”
مَا أَغْنَىٰ عَنِّي مَالِيَهْ ۜ (28)
“Chuma changa sichidandithandize chilichonse.”
هَلَكَ عَنِّي سُلْطَانِيَهْ (29)
“Ulamuliro wanga wonse wachoka kwa ine.”
خُذُوهُ فَغُلُّوهُ (30)
“Mugwireni ndipo mumumange.”
ثُمَّ الْجَحِيمَ صَلُّوهُ (31)
“Ndipo m’ponyeni M’ng’anjo ya moto.”
ثُمَّ فِي سِلْسِلَةٍ ذَرْعُهَا سَبْعُونَ ذِرَاعًا فَاسْلُكُوهُ (32)
“Ndipo mumangeni ndi unyolo wotalika malipande makumi asanu ndi awiri.”
إِنَّهُ كَانَ لَا يُؤْمِنُ بِاللَّهِ الْعَظِيمِ (33)
Ndithudi, iye samakhulupirira mwa Mulungu wamkulu
وَلَا يَحُضُّ عَلَىٰ طَعَامِ الْمِسْكِينِ (34)
Ndipo sadali kuthandiza kudyetsa anthu osowa
فَلَيْسَ لَهُ الْيَوْمَ هَاهُنَا حَمِيمٌ (35)
Motero lero iye sadzakhala ndi bwenzi aliyense
وَلَا طَعَامٌ إِلَّا مِنْ غِسْلِينٍ (36)
Kapena chakudya china chilichonse kupatula zonyasa zochoka pa zilonda
لَّا يَأْكُلُهُ إِلَّا الْخَاطِئُونَ (37)
Palibe amene adzachidya kupatula ochimwa ndi osakhulupilira
فَلَا أُقْسِمُ بِمَا تُبْصِرُونَ (38)
Motero Ine ndilumbira pali chilichonse chimene uli nkuona
وَمَا لَا تُبْصِرُونَ (39)
Ndi chimene chili chobisika
إِنَّهُ لَقَوْلُ رَسُولٍ كَرِيمٍ (40)
Kuti ndithudi awa ndi mawu a Mtumwi wolemekezeka
وَمَا هُوَ بِقَوْلِ شَاعِرٍ ۚ قَلِيلًا مَّا تُؤْمِنُونَ (41)
Ndipo si mawu a Mlakatuli ayi ndipo chikhulupiriro chanu ndi chochepa
وَلَا بِقَوْلِ كَاهِنٍ ۚ قَلِيلًا مَّا تَذَكَّرُونَ (42)
Ndipo si mawu a munthu wa maula ayi, ndipo ndi zochepa zimene inu mukumbukira
تَنزِيلٌ مِّن رَّبِّ الْعَالَمِينَ (43)
Ichi ndi chivumbulutso chochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse
وَلَوْ تَقَوَّلَ عَلَيْنَا بَعْضَ الْأَقَاوِيلِ (44)
Ndipo iye akanapeka nkhani yokhudza Ife
لَأَخَذْنَا مِنْهُ بِالْيَمِينِ (45)
Ndithudi Ife tikadagwira dzanja lake lamanja
ثُمَّ لَقَطَعْنَا مِنْهُ الْوَتِينَ (46)
Ndipo, ndithudi, Ifetikadadulamtsemphawakewamoyo
فَمَا مِنكُم مِّنْ أَحَدٍ عَنْهُ حَاجِزِينَ (47)
Ndipo palibe, wina wa inu, amene akadatiletsa Ife kumugwira
وَإِنَّهُ لَتَذْكِرَةٌ لِّلْمُتَّقِينَ (48)
Ndipo, ndithudi, Korani iyi ndi chikumbutso kwa iwo amene amapewa zoipa
وَإِنَّا لَنَعْلَمُ أَنَّ مِنكُم مُّكَذِّبِينَ (49)
Ndipo, ndithudi, Ife timadziwa kuti alipo ena a inu amene amaikana
وَإِنَّهُ لَحَسْرَةٌ عَلَى الْكَافِرِينَ (50)
Ndipo, ndithudi, ilo lidzakhala lomvetsa chisoni kwa anthu osakhulupirira
وَإِنَّهُ لَحَقُّ الْيَقِينِ (51)
Ndipo, ndithudi, ichi ndi choonadi chokhachokha
فَسَبِّحْ بِاسْمِ رَبِّكَ الْعَظِيمِ (52)
Motero lemekeza dzina la Ambuye wako, Wamkulu kulu
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas