ن ۚ وَالْقَلَمِ وَمَا يَسْطُرُونَ (1) Nun. Pali cholembera ndi zimene amalemba |
مَا أَنتَ بِنِعْمَةِ رَبِّكَ بِمَجْنُونٍ (2) Mwachisomo cha Ambuye wako, sindiwe wamisala ayi |
وَإِنَّ لَكَ لَأَجْرًا غَيْرَ مَمْنُونٍ (3) Ndithudi iwe udzalandira mphotho yosatha |
وَإِنَّكَ لَعَلَىٰ خُلُقٍ عَظِيمٍ (4) Ndithudi iwe uli ndi makhalidwe abwino |
فَسَتُبْصِرُ وَيُبْصِرُونَ (5) Iwe udzaona ndipo nawo adzaona |
بِأَييِّكُمُ الْمَفْتُونُ (6) Kuti ndani wa inu amene ndi wamisala |
إِنَّ رَبَّكَ هُوَ أَعْلَمُ بِمَن ضَلَّ عَن سَبِيلِهِ وَهُوَ أَعْلَمُ بِالْمُهْتَدِينَ (7) Ndithudi Ambuye wako amadziwa bwino amene wasochera ku njira yake ndipo amadziwa bwino amene amayenda m’njira yoyenera |
فَلَا تُطِعِ الْمُكَذِّبِينَ (8) Motero usatsatire zochita za anthu osakhulupirira |
وَدُّوا لَوْ تُدْهِنُ فَيُدْهِنُونَ (9) Iwo afuna utagwirizana nawo kuti nawonso agwirizane nawe |
وَلَا تُطِعْ كُلَّ حَلَّافٍ مَّهِينٍ (10) Ndipo usamvere zonena za munthu wotukwana amene alibe phindu |
هَمَّازٍ مَّشَّاءٍ بِنَمِيمٍ (11) Woononga mbiri ya anzake ponena Al Qalam 613 za bodza |
مَّنَّاعٍ لِّلْخَيْرِ مُعْتَدٍ أَثِيمٍ (12) Woletsa ntchito zachilungamo, wophwanya malamulo ndi wochita zoipa |
عُتُلٍّ بَعْدَ ذَٰلِكَ زَنِيمٍ (13) woipa mtima ndipo wobadwa mosalongosoka |
أَن كَانَ ذَا مَالٍ وَبَنِينَ (14) Chifukwa iye ali ndi chuma ndi ana |
إِذَا تُتْلَىٰ عَلَيْهِ آيَاتُنَا قَالَ أَسَاطِيرُ الْأَوَّلِينَ (15) Pamene chivumbulutso chathu chilakatulidwa kwa iye, amati: “Ndi nkhani za anthu a makedzana.” |
سَنَسِمُهُ عَلَى الْخُرْطُومِ (16) Ife tidzaika chizindikiro pa mphuno pake |
إِنَّا بَلَوْنَاهُمْ كَمَا بَلَوْنَا أَصْحَابَ الْجَنَّةِ إِذْ أَقْسَمُوا لَيَصْرِمُنَّهَا مُصْبِحِينَ (17) Ndithudi Ife tidawayesa iwo monga momwe tidawayesera eni ake a munda, amene adalumbira kuti adzakolola mbewu zawo m’mawa mwake |
وَلَا يَسْتَثْنُونَ (18) Osaonjezera mawu oti: “Ngati Mulungu alola.” |
فَطَافَ عَلَيْهَا طَائِفٌ مِّن رَّبِّكَ وَهُمْ نَائِمُونَ (19) Kotero kudadutsa china chake chochokera kwa Ambuye wako nthawi ya usiku ndi kuwotcha pamene iwo anali kugona |
فَأَصْبَحَتْ كَالصَّرِيمِ (20) Ndipo m’mawa, munda udasanduka wakuda monga mdima wa usiku |
فَتَنَادَوْا مُصْبِحِينَ (21) Ndipo mmawa iwo adaitanizana wina ndi mnzake |
أَنِ اغْدُوا عَلَىٰ حَرْثِكُمْ إِن كُنتُمْ صَارِمِينَ (22) Nati: “Mulawirire ku munda ngati mufuna kukakolola.” |
فَانطَلَقُوا وَهُمْ يَتَخَافَتُونَ (23) Ndipo iwo adapita, namanong’onezana wina ndi mnzake |
أَن لَّا يَدْخُلَنَّهَا الْيَوْمَ عَلَيْكُم مِّسْكِينٌ (24) “Palibe munthu wosauka amene adzaloledwa kulowa m’mundamo kudzapempha” |
وَغَدَوْا عَلَىٰ حَرْدٍ قَادِرِينَ (25) Ndipo m’mawa, onse adapita ndi mphamvu zotchinjirizira anthu osauka |
فَلَمَّا رَأَوْهَا قَالُوا إِنَّا لَضَالُّونَ (26) Koma pamene iwo adaona zimene zidachitika, onse adati: “Ndithudi ife talakwa.” |
بَلْ نَحْنُ مَحْرُومُونَ (27) “Iai! Ndithudi ife tapwetekeka.” |
قَالَ أَوْسَطُهُمْ أَلَمْ أَقُل لَّكُمْ لَوْلَا تُسَبِّحُونَ (28) wangwiro amene anali pakati pawo adati: “Kodi ine sindidakuuzeni kuti bwanji inu simunena kuti: Ngati Mulungu alola?” |
قَالُوا سُبْحَانَ رَبِّنَا إِنَّا كُنَّا ظَالِمِينَ (29) “Iwo adati ulemerero ukhale kwa Ambuye wathu! Ndithudi ife ndife olakwa.” |
فَأَقْبَلَ بَعْضُهُمْ عَلَىٰ بَعْضٍ يَتَلَاوَمُونَ (30) Ndipo iwo adayamba kudzudzulana kuti wina adali wolakwa |
قَالُوا يَا وَيْلَنَا إِنَّا كُنَّا طَاغِينَ (31) Iwo adati: “Tsoka kwa ife! Ndithudi Ife tidali ophwanya malamulo.” |
عَسَىٰ رَبُّنَا أَن يُبْدِلَنَا خَيْرًا مِّنْهَا إِنَّا إِلَىٰ رَبِّنَا رَاغِبُونَ (32) “Mwina kuti Ambuye wathu adzatipatsa munda wina wabwino m’malo mwa uwu. Ndithudi ndi kwa Iye kumene timapempha modzichepetsa.” |
كَذَٰلِكَ الْعَذَابُ ۖ وَلَعَذَابُ الْآخِرَةِ أَكْبَرُ ۚ لَوْ كَانُوا يَعْلَمُونَ (33) Chimenechi ndicho chilango koma ndithudi chilango cha m’moyo umene uli nkudza ndi chowawa kwambiri, iwo akadadziwa |
إِنَّ لِلْمُتَّقِينَ عِندَ رَبِّهِمْ جَنَّاتِ النَّعِيمِ (34) Ndithudi anthu onse angwiro adzalandira minda ya madalitso imene ili ndi Ambuye wawo |
أَفَنَجْعَلُ الْمُسْلِمِينَ كَالْمُجْرِمِينَ (35) Kodi Ife tidzasamala anthu angwiro chimodzimodzi ndi anthu ochimwa |
مَا لَكُمْ كَيْفَ تَحْكُمُونَ (36) Kodi mwatani? Kodi inu mumaweruza bwanji |
أَمْ لَكُمْ كِتَابٌ فِيهِ تَدْرُسُونَ (37) Kapena kodi muli ndi Buku limene mumawerengamo |
إِنَّ لَكُمْ فِيهِ لَمَا تَخَيَّرُونَ (38) Kuti inu mudzapeza m’menemo chilichonse chimene mukufuna |
أَمْ لَكُمْ أَيْمَانٌ عَلَيْنَا بَالِغَةٌ إِلَىٰ يَوْمِ الْقِيَامَةِ ۙ إِنَّ لَكُمْ لَمَا تَحْكُمُونَ (39) Kapena inu mwalandira kuchokera kwa Ife, lonjezo lotsimikizika mpaka pa tsiku louka kwa akufa kuti, ndithudi, inu mudzapeza zimene mukufuna |
سَلْهُمْ أَيُّهُم بِذَٰلِكَ زَعِيمٌ (40) Tawafunsa ngati wina wa iwo angachitire umboni za lonjezolo |
أَمْ لَهُمْ شُرَكَاءُ فَلْيَأْتُوا بِشُرَكَائِهِمْ إِن كَانُوا صَادِقِينَ (41) Kapena, kodi iwo ali ndi milungu ina? Aleke abweretse milungu yawo ngati iwo anena zoona |
يَوْمَ يُكْشَفُ عَن سَاقٍ وَيُدْعَوْنَ إِلَى السُّجُودِ فَلَا يَسْتَطِيعُونَ (42) Ndipatsikulimenechinthuchoopsachidzachitika, iwo adzaitanidwa kuti apembedze, koma adzalephera kutero |
خَاشِعَةً أَبْصَارُهُمْ تَرْهَقُهُمْ ذِلَّةٌ ۖ وَقَدْ كَانُوا يُدْعَوْنَ إِلَى السُّجُودِ وَهُمْ سَالِمُونَ (43) Maso awo adzayang’ana pansi ndipo adzanyozedwa kwambiri chifukwa iwo adauzidwa kupembedza pamene adali pa mtendere |
فَذَرْنِي وَمَن يُكَذِّبُ بِهَٰذَا الْحَدِيثِ ۖ سَنَسْتَدْرِجُهُم مِّنْ حَيْثُ لَا يَعْلَمُونَ (44) Kotero ndisiyire aliyense amene akutsutsana ndi chenjezo ili. Ife tidzawalanga pang’onopang’ono m’njira imene iwo saizindikira |
وَأُمْلِي لَهُمْ ۚ إِنَّ كَيْدِي مَتِينٌ (45) Ndipo Ine ndidzalekerera pa kanthawi! Ndithudi chikonzero changa ndi champhamvu |
أَمْ تَسْأَلُهُمْ أَجْرًا فَهُم مِّن مَّغْرَمٍ مُّثْقَلُونَ (46) Kapena kodi iwe uli kuwafunsa malipiro moti iwo ali ndi ngongole yambiri |
أَمْ عِندَهُمُ الْغَيْبُ فَهُمْ يَكْتُبُونَ (47) Kapena kodi iwo amadziwa za Buku lobisika kuti iwo akhoza kulemba |
فَاصْبِرْ لِحُكْمِ رَبِّكَ وَلَا تَكُن كَصَاحِبِ الْحُوتِ إِذْ نَادَىٰ وَهُوَ مَكْظُومٌ (48) Motero pirira podikilira chiweruzo cha Ambuye wako ndipo usakhale ngati amene adamezedwa ndi nsomba pamene adalira kupempha chithandizo iye ali m’mavuto |
لَّوْلَا أَن تَدَارَكَهُ نِعْمَةٌ مِّن رَّبِّهِ لَنُبِذَ بِالْعَرَاءِ وَهُوَ مَذْمُومٌ (49) Ngati Ambuye wake akadapanda kumuonetsa chisomo chake, ndithudi iye akadakhalabe koma iye adaponyedwa pa mtunda pamene anali wolakwa |
فَاجْتَبَاهُ رَبُّهُ فَجَعَلَهُ مِنَ الصَّالِحِينَ (50) Koma Ambuye wake adamusankha ndipo adamuchititsa kukhala wabwino |
وَإِن يَكَادُ الَّذِينَ كَفَرُوا لَيُزْلِقُونَكَ بِأَبْصَارِهِمْ لَمَّا سَمِعُوا الذِّكْرَ وَيَقُولُونَ إِنَّهُ لَمَجْنُونٌ (51) Ndipo, ndithudi, iwo onse osakhulupirira akadakusokeretsa ndi maso awo pamene amakumbutsidwa ndipo amati: “Ndithudi uyu ndi Wamisala.” |
وَمَا هُوَ إِلَّا ذِكْرٌ لِّلْعَالَمِينَ (52) Koma ichi si china koma chikumbutso kwa zolengedwa zonse |