الْحَاقَّةُ (1) Choonadi chenicheni |
مَا الْحَاقَّةُ (2) Kodi choonadi chenicheni ndi chiyani |
وَمَا أَدْرَاكَ مَا الْحَاقَّةُ (3) Kodi ndi chiyani chimene chingakupangitse kuti udziwe kuti choonadi chenicheni ndi chiti |
كَذَّبَتْ ثَمُودُ وَعَادٌ بِالْقَارِعَةِ (4) Mtundu wa Thamoud ndi Ad adakana ola la chionongeko |
فَأَمَّا ثَمُودُ فَأُهْلِكُوا بِالطَّاغِيَةِ (5) Ndipo anthu a Thamoud adaonongeka ndi mfuwu woopsya |
وَأَمَّا عَادٌ فَأُهْلِكُوا بِرِيحٍ صَرْصَرٍ عَاتِيَةٍ (6) Ndipo anthu a Aad adaonongeka ndi chimphepo cha mkuntho |
سَخَّرَهَا عَلَيْهِمْ سَبْعَ لَيَالٍ وَثَمَانِيَةَ أَيَّامٍ حُسُومًا فَتَرَى الْقَوْمَ فِيهَا صَرْعَىٰ كَأَنَّهُمْ أَعْجَازُ نَخْلٍ خَاوِيَةٍ (7) Chimene Mulungu adachilamulira kuti chikunthe pa iwo usiku usanu ndi uwiri ndi usana usanu ndi utatu mosalekeza. Moti iwe ukadawaona anthu atagonagona ukadayesa kuti ndi mitengo ya migwalangwa yakugwa |
فَهَلْ تَرَىٰ لَهُم مِّن بَاقِيَةٍ (8) Kodi uli kuona wina wa iwo opulumuka |
وَجَاءَ فِرْعَوْنُ وَمَن قَبْلَهُ وَالْمُؤْتَفِكَاتُ بِالْخَاطِئَةِ (9) Ndipo Farao ndi anthu amene adalipo iye asadabadwe, ndi a mizinda imene idaonongeka anali kuchita zoipa |
فَعَصَوْا رَسُولَ رَبِّهِمْ فَأَخَذَهُمْ أَخْذَةً رَّابِيَةً (10) Ndipo iwo sanamvere Mtumwi wochokera kwa Ambuye wawo ndipo Iye adawalanga ndi chilango chowawa zedi |
إِنَّا لَمَّا طَغَى الْمَاءُ حَمَلْنَاكُمْ فِي الْجَارِيَةِ (11) Ndithudi!Pamenemadzianasefukira,Ifetidakunyamulani inu m’chombo |
لِنَجْعَلَهَا لَكُمْ تَذْكِرَةً وَتَعِيَهَا أُذُنٌ وَاعِيَةٌ (12) Kuti tikhoza kuchipanga icho kukhala chikumbutso ndi kuti khutu la kumva limve |
فَإِذَا نُفِخَ فِي الصُّورِ نَفْخَةٌ وَاحِدَةٌ (13) Ndipo pamene lipenga lidzaimbidwa kamodzi |
وَحُمِلَتِ الْأَرْضُ وَالْجِبَالُ فَدُكَّتَا دَكَّةً وَاحِدَةً (14) Ndipo nthaka ndi mapiri anyamulidwa pamodzi ndi kuponyedwa pansi mwamphamvu kamodzi |
فَيَوْمَئِذٍ وَقَعَتِ الْوَاقِعَةُ (15) Patsiku limeneli chinthu choopsa chidzachitika |
وَانشَقَّتِ السَّمَاءُ فَهِيَ يَوْمَئِذٍ وَاهِيَةٌ (16) Ndipo thambo lidzaphwanyika ndipo lidzakhala lopanda mphamvu |
وَالْمَلَكُ عَلَىٰ أَرْجَائِهَا ۚ وَيَحْمِلُ عَرْشَ رَبِّكَ فَوْقَهُمْ يَوْمَئِذٍ ثَمَانِيَةٌ (17) Ndipo Angelo adzaima mbali zonse ndipo angelo asanu ndi atatu pa tsikuli adzanyamula Mpando wa Chifumu wa Ambuye wako |
يَوْمَئِذٍ تُعْرَضُونَ لَا تَخْفَىٰ مِنكُمْ خَافِيَةٌ (18) Patsiku limeneli mudzaweruzidwa ndipo palibe chinthu chachinsinsi chimene chidzabisika |
فَأَمَّا مَنْ أُوتِيَ كِتَابَهُ بِيَمِينِهِ فَيَقُولُ هَاؤُمُ اقْرَءُوا كِتَابِيَهْ (19) Ndipo yense amene adzapatsidwa Buku lake kudzanja lamanja adzati: “Ah taonani! Werengani Buku langa!” |
إِنِّي ظَنَنتُ أَنِّي مُلَاقٍ حِسَابِيَهْ (20) Ndithudi, ine ndidakhululupira kuti tsiku lina zochita zanga zidzaweruzidwa |
فَهُوَ فِي عِيشَةٍ رَّاضِيَةٍ (21) Kotero iye adzakhala ndi moyo wa chisangalalo |
فِي جَنَّةٍ عَالِيَةٍ (22) M’munda wapamwamba |
قُطُوفُهَا دَانِيَةٌ (23) Wa zipatso zokoma zimene zili pafupi |
كُلُوا وَاشْرَبُوا هَنِيئًا بِمَا أَسْلَفْتُمْ فِي الْأَيَّامِ الْخَالِيَةِ (24) Idyani ndipo imwani mmene mufunire chifukwa cha ntchito zanu zabwino zimene mudatumiza patsogolo panu m’masiku apitawo |
وَأَمَّا مَنْ أُوتِيَ كِتَابَهُ بِشِمَالِهِ فَيَقُولُ يَا لَيْتَنِي لَمْ أُوتَ كِتَابِيَهْ (25) Koma iye amene adzapatsidwe buku lake m’dzanja lamanzere, adzati: “Kukadakhala bwino ngati Buku langa likadakhala losaperekedwa kwa ine.” |
وَلَمْ أَدْرِ مَا حِسَابِيَهْ (26) “Ndipo sindikadziwa kuti zochita zanga zachuluka bwanji.” |
يَا لَيْتَهَا كَانَتِ الْقَاضِيَةَ (27) “Ikadakhala bwino imfa ikadangodza pa ine.” |
مَا أَغْنَىٰ عَنِّي مَالِيَهْ ۜ (28) “Chuma changa sichidandithandize chilichonse.” |
هَلَكَ عَنِّي سُلْطَانِيَهْ (29) “Ulamuliro wanga wonse wachoka kwa ine.” |
خُذُوهُ فَغُلُّوهُ (30) “Mugwireni ndipo mumumange.” |
ثُمَّ الْجَحِيمَ صَلُّوهُ (31) “Ndipo m’ponyeni M’ng’anjo ya moto.” |
ثُمَّ فِي سِلْسِلَةٍ ذَرْعُهَا سَبْعُونَ ذِرَاعًا فَاسْلُكُوهُ (32) “Ndipo mumangeni ndi unyolo wotalika malipande makumi asanu ndi awiri.” |
إِنَّهُ كَانَ لَا يُؤْمِنُ بِاللَّهِ الْعَظِيمِ (33) Ndithudi, iye samakhulupirira mwa Mulungu wamkulu |
وَلَا يَحُضُّ عَلَىٰ طَعَامِ الْمِسْكِينِ (34) Ndipo sadali kuthandiza kudyetsa anthu osowa |
فَلَيْسَ لَهُ الْيَوْمَ هَاهُنَا حَمِيمٌ (35) Motero lero iye sadzakhala ndi bwenzi aliyense |
وَلَا طَعَامٌ إِلَّا مِنْ غِسْلِينٍ (36) Kapena chakudya china chilichonse kupatula zonyasa zochoka pa zilonda |
لَّا يَأْكُلُهُ إِلَّا الْخَاطِئُونَ (37) Palibe amene adzachidya kupatula ochimwa ndi osakhulupilira |
فَلَا أُقْسِمُ بِمَا تُبْصِرُونَ (38) Motero Ine ndilumbira pali chilichonse chimene uli nkuona |
وَمَا لَا تُبْصِرُونَ (39) Ndi chimene chili chobisika |
إِنَّهُ لَقَوْلُ رَسُولٍ كَرِيمٍ (40) Kuti ndithudi awa ndi mawu a Mtumwi wolemekezeka |
وَمَا هُوَ بِقَوْلِ شَاعِرٍ ۚ قَلِيلًا مَّا تُؤْمِنُونَ (41) Ndipo si mawu a Mlakatuli ayi ndipo chikhulupiriro chanu ndi chochepa |
وَلَا بِقَوْلِ كَاهِنٍ ۚ قَلِيلًا مَّا تَذَكَّرُونَ (42) Ndipo si mawu a munthu wa maula ayi, ndipo ndi zochepa zimene inu mukumbukira |
تَنزِيلٌ مِّن رَّبِّ الْعَالَمِينَ (43) Ichi ndi chivumbulutso chochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse |
وَلَوْ تَقَوَّلَ عَلَيْنَا بَعْضَ الْأَقَاوِيلِ (44) Ndipo iye akanapeka nkhani yokhudza Ife |
لَأَخَذْنَا مِنْهُ بِالْيَمِينِ (45) Ndithudi Ife tikadagwira dzanja lake lamanja |
ثُمَّ لَقَطَعْنَا مِنْهُ الْوَتِينَ (46) Ndipo, ndithudi, Ifetikadadulamtsemphawakewamoyo |
فَمَا مِنكُم مِّنْ أَحَدٍ عَنْهُ حَاجِزِينَ (47) Ndipo palibe, wina wa inu, amene akadatiletsa Ife kumugwira |
وَإِنَّهُ لَتَذْكِرَةٌ لِّلْمُتَّقِينَ (48) Ndipo, ndithudi, Korani iyi ndi chikumbutso kwa iwo amene amapewa zoipa |
وَإِنَّا لَنَعْلَمُ أَنَّ مِنكُم مُّكَذِّبِينَ (49) Ndipo, ndithudi, Ife timadziwa kuti alipo ena a inu amene amaikana |
وَإِنَّهُ لَحَسْرَةٌ عَلَى الْكَافِرِينَ (50) Ndipo, ndithudi, ilo lidzakhala lomvetsa chisoni kwa anthu osakhulupirira |
وَإِنَّهُ لَحَقُّ الْيَقِينِ (51) Ndipo, ndithudi, ichi ndi choonadi chokhachokha |
فَسَبِّحْ بِاسْمِ رَبِّكَ الْعَظِيمِ (52) Motero lemekeza dzina la Ambuye wako, Wamkulu kulu |