×

سورة النازعات باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة النازعات

ترجمة معاني سورة النازعات باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة النازعات مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Naziat in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة النازعات باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 46 - رقم السورة 79 - الصفحة 583.

بسم الله الرحمن الرحيم

وَالنَّازِعَاتِ غَرْقًا (1)
Pali iwo amene amalanda mwankhanza
وَالنَّاشِطَاتِ نَشْطًا (2)
Ndi pali iwo amene amachotsa mwaufulu
وَالسَّابِحَاتِ سَبْحًا (3)
Ndi pali iwo amene amauluka
فَالسَّابِقَاتِ سَبْقًا (4)
Ndi pali iwo amene amathamanga ngati ali pa liwiro loopsya
فَالْمُدَبِّرَاتِ أَمْرًا (5)
Ndi pali angelo amene amakwaniritsa kuchita malamulo a Ambuye wawo
يَوْمَ تَرْجُفُ الرَّاجِفَةُ (6)
Patsiku limene dziko ndi mapiri zidzagwedezeka kwambiri
تَتْبَعُهَا الرَّادِفَةُ (7)
Ndi kulira kwa lipenga kawiri
قُلُوبٌ يَوْمَئِذٍ وَاجِفَةٌ (8)
Mitima, patsiku limeneli, idzafumuka ndi kuda nkhawa
أَبْصَارُهَا خَاشِعَةٌ (9)
Maso awo atagwetsa pansi
يَقُولُونَ أَإِنَّا لَمَرْدُودُونَ فِي الْحَافِرَةِ (10)
Iwo amanena kuti: “Kodi ife tidzabwerera monga momwe tinali poyamba?”
أَإِذَا كُنَّا عِظَامًا نَّخِرَةً (11)
“Angakhale mafupa athu ataola?”
قَالُوا تِلْكَ إِذًا كَرَّةٌ خَاسِرَةٌ (12)
Iwo amati: “Kubwerera kotero ndi kopanda phindu.”
فَإِنَّمَا هِيَ زَجْرَةٌ وَاحِدَةٌ (13)
Koma udzakhala mfuwu umodzi okha
فَإِذَا هُم بِالسَّاهِرَةِ (14)
Pamene, taona, iwo adzadzipeza okha ali pamwamba pa nthaka ali ndi moyo
هَلْ أَتَاكَ حَدِيثُ مُوسَىٰ (15)
Kodiinumudaimvankhaniya Mose
إِذْ نَادَاهُ رَبُّهُ بِالْوَادِ الْمُقَدَّسِ طُوًى (16)
PameneAmbuye wake adamuitana mu dambo lodalitsika la Tuwa
اذْهَبْ إِلَىٰ فِرْعَوْنَ إِنَّهُ طَغَىٰ (17)
“Pita kwa Farao; Ndithudi iye waphwanya malamulo mopyola muyezo.”
فَقُلْ هَل لَّكَ إِلَىٰ أَن تَزَكَّىٰ (18)
“Ndipo ukamuuze kuti: Kodi ungadziyeretse wekha?”
وَأَهْدِيَكَ إِلَىٰ رَبِّكَ فَتَخْشَىٰ (19)
“Ndi kuti ine ndikulondolere kwa Ambuye wako kuti uzimuopa Iye?”
فَأَرَاهُ الْآيَةَ الْكُبْرَىٰ (20)
Kotero iye adamuonetsa chizindikiro cha chikulu
فَكَذَّبَ وَعَصَىٰ (21)
Koma iye adachikana ndipo sanamvere
ثُمَّ أَدْبَرَ يَسْعَىٰ (22)
Iye adapitirizabe kuchita zoipa
فَحَشَرَ فَنَادَىٰ (23)
Ndipo iye adaitana anthu ake onse ndipo anafuula mokweza
فَقَالَ أَنَا رَبُّكُمُ الْأَعْلَىٰ (24)
Nati: “Ine ndine Ambuye wanu wapamwamba mwamba.” Al-Naziat
فَأَخَذَهُ اللَّهُ نَكَالَ الْآخِرَةِ وَالْأُولَىٰ (25)
Motero Mulungu adamugwetsera iye chilango chifukwa cha mau ake omaliza ndi oyamba
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَعِبْرَةً لِّمَن يَخْشَىٰ (26)
Ndithudi mu izi muli phunziro lomveka kwa anthu oopa Mulungu
أَأَنتُمْ أَشَدُّ خَلْقًا أَمِ السَّمَاءُ ۚ بَنَاهَا (27)
Kodi inu ndinu ovuta kulenga kapena thambo la mlengalenga limene Mulungu adalilenga
رَفَعَ سَمْكَهَا فَسَوَّاهَا (28)
Iye analikweza m’mwamba ndi kulikonza bwino
وَأَغْطَشَ لَيْلَهَا وَأَخْرَجَ ضُحَاهَا (29)
Usiku wake amaukuta ndi m’dima ndipo masana ake amatulutsa kuwala
وَالْأَرْضَ بَعْدَ ذَٰلِكَ دَحَاهَا (30)
Ndipo pambuyo pake adalikulitsa dziko
أَخْرَجَ مِنْهَا مَاءَهَا وَمَرْعَاهَا (31)
Ndipo anatulutsa madzi ndi msipu
وَالْجِبَالَ أَرْسَاهَا (32)
Ndipo adazika mapiri molimbika
مَتَاعًا لَّكُمْ وَلِأَنْعَامِكُمْ (33)
Chakudya cha phindu kwa inu ndi kwa zoweta zanu
فَإِذَا جَاءَتِ الطَّامَّةُ الْكُبْرَىٰ (34)
Koma pamene mavuto akulu akudza
يَوْمَ يَتَذَكَّرُ الْإِنسَانُ مَا سَعَىٰ (35)
Tsiku limene munthu adzayamba kuganiza ntchito zake zonse
وَبُرِّزَتِ الْجَحِيمُ لِمَن يَرَىٰ (36)
Ndipo Gahena idzabweretsedwa pafupi kuti aliyense aione
فَأَمَّا مَن طَغَىٰ (37)
Ndipo kwa iye ophwanya malamulo
وَآثَرَ الْحَيَاةَ الدُّنْيَا (38)
Ndipo anasankha moyo wapadziko lino
فَإِنَّ الْجَحِيمَ هِيَ الْمَأْوَىٰ (39)
Ndithudi malo ake okhala ndi ku Gahena
وَأَمَّا مَنْ خَافَ مَقَامَ رَبِّهِ وَنَهَى النَّفْسَ عَنِ الْهَوَىٰ (40)
Koma kwa iwo amene amaopa kukaima pamaso pa Ambuye wake ndi machimo ndipo anali kudziletsa kuchita chifuniro chopanda pake
فَإِنَّ الْجَنَّةَ هِيَ الْمَأْوَىٰ (41)
Ndithudi adzakhala ku Paradiso
يَسْأَلُونَكَ عَنِ السَّاعَةِ أَيَّانَ مُرْسَاهَا (42)
Amakufunsa za nthawi imene chigumula chidzabwere
فِيمَ أَنتَ مِن ذِكْرَاهَا (43)
Iwe siudziwa zoti unene china chili chonse
إِلَىٰ رَبِّكَ مُنتَهَاهَا (44)
Ndi Ambuye wako yekha amene amadziwa tsiku
إِنَّمَا أَنتَ مُنذِرُ مَن يَخْشَاهَا (45)
Iwe ndiwe mchenjezi chabe kwa iwo amene ali kuliopa tsikuli
كَأَنَّهُمْ يَوْمَ يَرَوْنَهَا لَمْ يَلْبَثُوا إِلَّا عَشِيَّةً أَوْ ضُحَاهَا (46)
Patsiku limene iwo adzachiona chigumula, kudzakhala ngati kuti iwo sanakhale padziko lapansi nthawi yaitali koma usiku umodzi kapena usana wokha
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس