Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 275 - البَقَرَة - Page - Juz 3
﴿ٱلَّذِينَ يَأۡكُلُونَ ٱلرِّبَوٰاْ لَا يَقُومُونَ إِلَّا كَمَا يَقُومُ ٱلَّذِي يَتَخَبَّطُهُ ٱلشَّيۡطَٰنُ مِنَ ٱلۡمَسِّۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمۡ قَالُوٓاْ إِنَّمَا ٱلۡبَيۡعُ مِثۡلُ ٱلرِّبَوٰاْۗ وَأَحَلَّ ٱللَّهُ ٱلۡبَيۡعَ وَحَرَّمَ ٱلرِّبَوٰاْۚ فَمَن جَآءَهُۥ مَوۡعِظَةٞ مِّن رَّبِّهِۦ فَٱنتَهَىٰ فَلَهُۥ مَا سَلَفَ وَأَمۡرُهُۥٓ إِلَى ٱللَّهِۖ وَمَنۡ عَادَ فَأُوْلَٰٓئِكَ أَصۡحَٰبُ ٱلنَّارِۖ هُمۡ فِيهَا خَٰلِدُونَ ﴾
[البَقَرَة: 275]
﴿الذين يأكلون الربا لا يقومون إلا كما يقوم الذي يتخبطه الشيطان من﴾ [البَقَرَة: 275]
Khaled Ibrahim Betala “Amene akudya riba (chuma cha katapira) sadzauka (m’manda) koma monga momwe amaimira munthu okhudzidwa ndi ziwanda, mwamisala. (Ndipo) izi nchifukwa chakuti amanena: “Malonda ngolingana ndi katapira,” pomwe Allah waloleza malonda ndipo waletsa katapira. Ndipo amene wamufika ulaliki wochokera kwa Mbuye wake (woletsa katapira) nasiya, choncho chomwe chidapita nchake. Ndipo chiweruzo chake chili kwa Allah (akaona chochita naye). Koma amene abwerera (kuchita malonda a katapira), amenewo ndiwo anthu a ku Moto, mmenemo adzakhalamo nthawi yaitali |