×

سورة البقرة باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة البقرة

ترجمة معاني سورة البقرة باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة البقرة مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah Baqarah in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة البقرة باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 286 - رقم السورة 2 - الصفحة 2.

بسم الله الرحمن الرحيم

الم (1)
Alif Lam Mim
ذَٰلِكَ الْكِتَابُ لَا رَيْبَ ۛ فِيهِ ۛ هُدًى لِّلْمُتَّقِينَ (2)
Ili ndi Buku limene mulibe chokaikitsa, ulangizi kwa anthu oopa Mulungu
الَّذِينَ يُؤْمِنُونَ بِالْغَيْبِ وَيُقِيمُونَ الصَّلَاةَ وَمِمَّا رَزَقْنَاهُمْ يُنفِقُونَ (3)
Amene amakhulupirira mu chinthu chosaoneka ndipo amapemphera pa nthawi yake ndipo amapereka kwa anthu osowa zina mwa zinthu zimene tawapatsa
وَالَّذِينَ يُؤْمِنُونَ بِمَا أُنزِلَ إِلَيْكَ وَمَا أُنزِلَ مِن قَبْلِكَ وَبِالْآخِرَةِ هُمْ يُوقِنُونَ (4)
Ndi amene amakhulupirira mu zimene zavumbulutsidwa kwa iwe ndiponso zimene zinavumbulutsidwa kale iwe usanadze ndipo amakhulupirira kwathunthu m’moyo umene uli nkudza
أُولَٰئِكَ عَلَىٰ هُدًى مِّن رَّبِّهِمْ ۖ وَأُولَٰئِكَ هُمُ الْمُفْلِحُونَ (5)
Amenewa ndiwo amene ali pa njira yoyenera ya Ambuye wawo ndipo ndiwo opambana
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا سَوَاءٌ عَلَيْهِمْ أَأَنذَرْتَهُمْ أَمْ لَمْ تُنذِرْهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ (6)
Ndithudi iwo amene sakhulupilira ndi chimodzimodzi kwa iwo kaya iwe uwachenjeza kapena osawachenjeza, ndipo iwo sadzakhulupilira
خَتَمَ اللَّهُ عَلَىٰ قُلُوبِهِمْ وَعَلَىٰ سَمْعِهِمْ ۖ وَعَلَىٰ أَبْصَارِهِمْ غِشَاوَةٌ ۖ وَلَهُمْ عَذَابٌ عَظِيمٌ (7)
Mulungu waika chophimba m’mitima mwawo ndi m’makutu mwawo, ndi m’maso mwawo muli chovindikira. Ndipo chawo chidzakhala chilango chachikulu
وَمِنَ النَّاسِ مَن يَقُولُ آمَنَّا بِاللَّهِ وَبِالْيَوْمِ الْآخِرِ وَمَا هُم بِمُؤْمِنِينَ (8)
Pakati pa anthu alipo amene amanena kuti: “Ife tikhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku la chiweruzo” pamene iwo sali anthu okhulupirira ngakhale pang’ono
يُخَادِعُونَ اللَّهَ وَالَّذِينَ آمَنُوا وَمَا يَخْدَعُونَ إِلَّا أَنفُسَهُمْ وَمَا يَشْعُرُونَ (9)
Iwo amangofuna kunamiza Mulungu ndi iwo amene amakhulupirira mwa Iye. Koma iwo sanamiza wina aliyense kupatula kudzinamiza okha ngakhale kuti iwo sazindikira
فِي قُلُوبِهِم مَّرَضٌ فَزَادَهُمُ اللَّهُ مَرَضًا ۖ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ بِمَا كَانُوا يَكْذِبُونَ (10)
M’mitima mwawo muli matenda ndipo Mulungu wawonjezera. Iwo adzalangidwa kwambiri chifukwa cha chinyengo chawo
وَإِذَا قِيلَ لَهُمْ لَا تُفْسِدُوا فِي الْأَرْضِ قَالُوا إِنَّمَا نَحْنُ مُصْلِحُونَ (11)
Ndipo zikanenedwa kwa iwo kuti: “Musachite zoipa m’dziko,” iwo amayankha kuti: “Ndithudi ife ndi ochita zabwino.”
أَلَا إِنَّهُمْ هُمُ الْمُفْسِدُونَ وَلَٰكِن لَّا يَشْعُرُونَ (12)
Ndithudi! Iwo ndiwo amene amachita zoipa koma kuti iwo sazindikira
وَإِذَا قِيلَ لَهُمْ آمِنُوا كَمَا آمَنَ النَّاسُ قَالُوا أَنُؤْمِنُ كَمَا آمَنَ السُّفَهَاءُ ۗ أَلَا إِنَّهُمْ هُمُ السُّفَهَاءُ وَلَٰكِن لَّا يَعْلَمُونَ (13)
Ndipo zikanenedwa kwa iwo kuti: “Khulupirirani monga momwe anthu akhulupirira.” Iwo amayankha kuti: “Kodi ife tikhulupirire monga momwe zitsiru zikhulupirira?” Ndithudi iwo ndiwo zitsiru koma iwo sazindikira
وَإِذَا لَقُوا الَّذِينَ آمَنُوا قَالُوا آمَنَّا وَإِذَا خَلَوْا إِلَىٰ شَيَاطِينِهِمْ قَالُوا إِنَّا مَعَكُمْ إِنَّمَا نَحْنُ مُسْتَهْزِئُونَ (14)
Ndipo iwo akakumana ndi anthu okhulupirira, amanena kuti: “Ife timakhulupilira!” Koma akakhala okha pakati pa a Satana awo amati: “Ndithudi ife tili ndi inu. Ndithudi ife timangowasyasyalika chabe.”
اللَّهُ يَسْتَهْزِئُ بِهِمْ وَيَمُدُّهُمْ فِي طُغْيَانِهِمْ يَعْمَهُونَ (15)
Mulungu amawasyasyalika iwo ndipo amawasiya nthawi yaitali mu uchimo ndi kumapitirirabe kuchimwa mwaumbuli
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ اشْتَرَوُا الضَّلَالَةَ بِالْهُدَىٰ فَمَا رَبِحَت تِّجَارَتُهُمْ وَمَا كَانُوا مُهْتَدِينَ (16)
Amenewa ndiwo amene agula chisokonekero m’malo mwa njira yoyenera. Iwo sanapindule pa malonda awo. Ndipo sanali wotsogozedwa
مَثَلُهُمْ كَمَثَلِ الَّذِي اسْتَوْقَدَ نَارًا فَلَمَّا أَضَاءَتْ مَا حَوْلَهُ ذَهَبَ اللَّهُ بِنُورِهِمْ وَتَرَكَهُمْ فِي ظُلُمَاتٍ لَّا يُبْصِرُونَ (17)
Iwo ali ngati munthu amene adasonkha moto ndipo pamene moto unali nkuyaka, kuunika zimene zili m’mbali mwake, Mulungu anachotsa kuwala kwawo ndipo adawasiya ali mu mdima waukulu wosathanso kuona
صُمٌّ بُكْمٌ عُمْيٌ فَهُمْ لَا يَرْجِعُونَ (18)
Iwo ndi osamva, osalankhula ndi osaona ndipo sadzabwerera ku njira yoyenera
أَوْ كَصَيِّبٍ مِّنَ السَّمَاءِ فِيهِ ظُلُمَاتٌ وَرَعْدٌ وَبَرْقٌ يَجْعَلُونَ أَصَابِعَهُمْ فِي آذَانِهِم مِّنَ الصَّوَاعِقِ حَذَرَ الْمَوْتِ ۚ وَاللَّهُ مُحِيطٌ بِالْكَافِرِينَ (19)
Kapena ali ngati mvula ya mkuntho imene mkati mwake muli mdima, kugunda ndi ziphaliwali. Ndipo amatseka zala m’makutu mwawo akamva kugunda chifukwa choopa imfa. Koma Mulungu amawadziwa bwino anthu onse osakhulupirira
يَكَادُ الْبَرْقُ يَخْطَفُ أَبْصَارَهُمْ ۖ كُلَّمَا أَضَاءَ لَهُم مَّشَوْا فِيهِ وَإِذَا أَظْلَمَ عَلَيْهِمْ قَامُوا ۚ وَلَوْ شَاءَ اللَّهُ لَذَهَبَ بِسَمْعِهِمْ وَأَبْصَارِهِمْ ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (20)
Mphenzi, pafupifupi, imawalanda kuona. Nthawi iliyonse imene iyo ing’anipa iwo amayenda ndipo kukakhala mdima iwo amaima. Ndipo ngati Mulungu akadafuna akadawalanda kumva ndi kuona kwawo. Ndithu Mulungu ali ndi mphamvu pa zinthu zonse
يَا أَيُّهَا النَّاسُ اعْبُدُوا رَبَّكُمُ الَّذِي خَلَقَكُمْ وَالَّذِينَ مِن قَبْلِكُمْ لَعَلَّكُمْ تَتَّقُونَ (21)
Oh inu anthu! Pembedzani Ambuye wanu, amene adakulengani inu ndi iwo amene adalipo kale kuti mukhale angwiro
الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ الْأَرْضَ فِرَاشًا وَالسَّمَاءَ بِنَاءً وَأَنزَلَ مِنَ السَّمَاءِ مَاءً فَأَخْرَجَ بِهِ مِنَ الثَّمَرَاتِ رِزْقًا لَّكُمْ ۖ فَلَا تَجْعَلُوا لِلَّهِ أَندَادًا وَأَنتُمْ تَعْلَمُونَ (22)
Iye adapanga dziko lapansi kukhala malo anu a mpumulo ndi mtambo ngati chokuta. Ndipo anatumiza mvula kuchokera kumwamba ndi kubweretsa kwa inu zipatso ngati zakudya zanu. Motero musakhale ndi milungu ina mowonjezera pa Mulungu m’modzi yekha pamene muli kudziwa
وَإِن كُنتُمْ فِي رَيْبٍ مِّمَّا نَزَّلْنَا عَلَىٰ عَبْدِنَا فَأْتُوا بِسُورَةٍ مِّن مِّثْلِهِ وَادْعُوا شُهَدَاءَكُم مِّن دُونِ اللَّهِ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (23)
Ngati inu muli ndi chikayiko pa zimene tavumbulutsa kwa kapolo wathu, bweretsani mutu umodzi wolingana ndi imene ili m’buku ili ndipo itanani mboni zanu kupatula Mulungu ngati muli kunena zoona
فَإِن لَّمْ تَفْعَلُوا وَلَن تَفْعَلُوا فَاتَّقُوا النَّارَ الَّتِي وَقُودُهَا النَّاسُ وَالْحِجَارَةُ ۖ أُعِدَّتْ لِلْكَافِرِينَ (24)
Koma ngati inu simubweretsa ndipo simudzabweretsa (mboni) motero opani moto umene nkhuni zake ndi anthu ndi miyala, umene wasonkhedwera anthu osakhulupirira
وَبَشِّرِ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ أَنَّ لَهُمْ جَنَّاتٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ ۖ كُلَّمَا رُزِقُوا مِنْهَا مِن ثَمَرَةٍ رِّزْقًا ۙ قَالُوا هَٰذَا الَّذِي رُزِقْنَا مِن قَبْلُ ۖ وَأُتُوا بِهِ مُتَشَابِهًا ۖ وَلَهُمْ فِيهَا أَزْوَاجٌ مُّطَهَّرَةٌ ۖ وَهُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (25)
Ndipo auze nkhani yabwino iwo amene ali ndi chikhulupiriro ndipo amachita ntchito zabwino kuti iwo adzakhala m’minda yothiriridwa ndi madzi a m’mitsinje yoyenda. Nthawi zonse akapatsidwa zipatso zochokera m’mindayo, iwo adzati: “Izi ndi zimene tinapatsidwa kale.” Chifukwa iwo adzapatsidwa zofanana nazo ndipo iwo adzakhala ndi akazi osakhuzidwa ndipo adzakhala kumeneko mpaka kalekale
۞ إِنَّ اللَّهَ لَا يَسْتَحْيِي أَن يَضْرِبَ مَثَلًا مَّا بَعُوضَةً فَمَا فَوْقَهَا ۚ فَأَمَّا الَّذِينَ آمَنُوا فَيَعْلَمُونَ أَنَّهُ الْحَقُّ مِن رَّبِّهِمْ ۖ وَأَمَّا الَّذِينَ كَفَرُوا فَيَقُولُونَ مَاذَا أَرَادَ اللَّهُ بِهَٰذَا مَثَلًا ۘ يُضِلُّ بِهِ كَثِيرًا وَيَهْدِي بِهِ كَثِيرًا ۚ وَمَا يُضِلُّ بِهِ إِلَّا الْفَاسِقِينَ (26)
Ndithudi Mulungu sachita manyazi kupereka fanizo la kanthu kakang’ono ngati udzudzu kapena chinthu chachikulu. Koma anthu okhulupirira amadziwa kuti ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wawo pamene anthu osakhulupirira amati: “Kodi Mulungu akufuna kutanthauza chiyani mufanizo ili?” Kudzera m’mafanizo otere Mulungu amasocheza anthu ambiri ndiponso amatsogolera anthu ambiri. Ndipo Iye sasokeza wina aliyense kupatula okhawo ochita zoipa
الَّذِينَ يَنقُضُونَ عَهْدَ اللَّهِ مِن بَعْدِ مِيثَاقِهِ وَيَقْطَعُونَ مَا أَمَرَ اللَّهُ بِهِ أَن يُوصَلَ وَيُفْسِدُونَ فِي الْأَرْضِ ۚ أُولَٰئِكَ هُمُ الْخَاسِرُونَ (27)
Amene amaswa lonjezo la Mulungu pambuyo pomanga ndipo amatayanitsa zinthu zimene Mulungu walamulira kuti zilumikizidwe ndiponso amachita zoipa m’dziko. Iwowo ndi anthu olephera
كَيْفَ تَكْفُرُونَ بِاللَّهِ وَكُنتُمْ أَمْوَاتًا فَأَحْيَاكُمْ ۖ ثُمَّ يُمِيتُكُمْ ثُمَّ يُحْيِيكُمْ ثُمَّ إِلَيْهِ تُرْجَعُونَ (28)
Kodi inu simungamukhulupilire Mulungu bwanji? Poona kuti inu munali akufa, Iye adakupatsani moyo ndipo Iye adzakuphani ndipo adzakupatsaninso moyo ndipo kwa Iye mudzabwerera
هُوَ الَّذِي خَلَقَ لَكُم مَّا فِي الْأَرْضِ جَمِيعًا ثُمَّ اسْتَوَىٰ إِلَى السَّمَاءِ فَسَوَّاهُنَّ سَبْعَ سَمَاوَاتٍ ۚ وَهُوَ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (29)
Iye ndiye amene adakulengerani inu zinthu zonse zimene zili padziko lapansi. Ndipo atatero analenga kumwamba ndipo adalenga miyamba isanu ndi iwiri ndipo Iye ndi wodziwa chinthu china chilichonse
وَإِذْ قَالَ رَبُّكَ لِلْمَلَائِكَةِ إِنِّي جَاعِلٌ فِي الْأَرْضِ خَلِيفَةً ۖ قَالُوا أَتَجْعَلُ فِيهَا مَن يُفْسِدُ فِيهَا وَيَسْفِكُ الدِّمَاءَ وَنَحْنُ نُسَبِّحُ بِحَمْدِكَ وَنُقَدِّسُ لَكَ ۖ قَالَ إِنِّي أَعْلَمُ مَا لَا تَعْلَمُونَ (30)
Ndipo pamene Ambuye wako adati kwa angelo: “Ine ndiika olamula padziko lapansi.” Iwo adati: “Kodi inu mudzaika padziko amene adzakhala ali kuchita zoipa ndi kukhetsa mwazi pamene ife tili kuyamika ndi kutamanda ulemerero wanu?” Iye adati: “Ine ndimadziwa zimene inu simudziwa.”
وَعَلَّمَ آدَمَ الْأَسْمَاءَ كُلَّهَا ثُمَّ عَرَضَهُمْ عَلَى الْمَلَائِكَةِ فَقَالَ أَنبِئُونِي بِأَسْمَاءِ هَٰؤُلَاءِ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (31)
Ndipo Iye adamuphunzitsa Adamu mayina a zinthu zonse ndipo adazisonkhanitsa pamaso pa angelo nati: “Ndiuzeni mayina a zinthu izi ngati ndinu achilungamo.”
قَالُوا سُبْحَانَكَ لَا عِلْمَ لَنَا إِلَّا مَا عَلَّمْتَنَا ۖ إِنَّكَ أَنتَ الْعَلِيمُ الْحَكِيمُ (32)
Iwo adati: “Ulemerero ukhale kwa Inu. Ife tilibe nzeru kupatula zokhazo zimene mutiphunzitsa. Ndithudi Inu nokha ndinu amene muli Wodziwa ndi Wanzeru.”
قَالَ يَا آدَمُ أَنبِئْهُم بِأَسْمَائِهِمْ ۖ فَلَمَّا أَنبَأَهُم بِأَسْمَائِهِمْ قَالَ أَلَمْ أَقُل لَّكُمْ إِنِّي أَعْلَمُ غَيْبَ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَأَعْلَمُ مَا تُبْدُونَ وَمَا كُنتُمْ تَكْتُمُونَ (33)
Ndipo Mulungu adati: “Iwe Adamu! Auze mayina ake.” Ndipo pamene iye adatchula mayina a zinthuzo, Mulungu adati: “Kodi Ine sindidakuuzeni inu kuti Ine ndimadziwa zobisika za kumwamba ndi za dziko lapansi ndipo ndimadziwanso zonse zimene inu mumaulula ndi zimene mumabisa?”
وَإِذْ قُلْنَا لِلْمَلَائِكَةِ اسْجُدُوا لِآدَمَ فَسَجَدُوا إِلَّا إِبْلِيسَ أَبَىٰ وَاسْتَكْبَرَ وَكَانَ مِنَ الْكَافِرِينَ (34)
Ndipo pamene Ife tidati kwa angelo: “Mugwadireni Adamu.” Ndipo onse adamugwadira kupatula Satana amene adakana ndi kudzikweza ndipo adakala m’modzi wa osakhulupilira
وَقُلْنَا يَا آدَمُ اسْكُنْ أَنتَ وَزَوْجُكَ الْجَنَّةَ وَكُلَا مِنْهَا رَغَدًا حَيْثُ شِئْتُمَا وَلَا تَقْرَبَا هَٰذِهِ الشَّجَرَةَ فَتَكُونَا مِنَ الظَّالِمِينَ (35)
Ndipo Ife tidati: “oh Adamu! Khala iwe pamodzi ndi mkazi wako m’mundamo ndipo muzidya mmene mungafunire koma musadzayandikire mtengo uwu chifukwa mudzakhala anthu ochimwa.”
فَأَزَلَّهُمَا الشَّيْطَانُ عَنْهَا فَأَخْرَجَهُمَا مِمَّا كَانَا فِيهِ ۖ وَقُلْنَا اهْبِطُوا بَعْضُكُمْ لِبَعْضٍ عَدُوٌّ ۖ وَلَكُمْ فِي الْأَرْضِ مُسْتَقَرٌّ وَمَتَاعٌ إِلَىٰ حِينٍ (36)
Koma Satana adawanyenga ndipo adawachotsetsa m’munda m’mene iwo adali. Ife tidati: “Tsikani pansi nonse ndipo inu mudzakhala mdani wa wina ndi mnzake. Ndipo dziko lapansi ndi kumene inu mudzakhala ndi chisangalalo cha kanthawi kochepa.”
فَتَلَقَّىٰ آدَمُ مِن رَّبِّهِ كَلِمَاتٍ فَتَابَ عَلَيْهِ ۚ إِنَّهُ هُوَ التَّوَّابُ الرَّحِيمُ (37)
Ndipo Adamu adalandira mawu kuchokera kwa Ambuye wake. Ndipo Ambuye wake adamukhululukira iye. Ndithudi Iye ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
قُلْنَا اهْبِطُوا مِنْهَا جَمِيعًا ۖ فَإِمَّا يَأْتِيَنَّكُم مِّنِّي هُدًى فَمَن تَبِعَ هُدَايَ فَلَا خَوْفٌ عَلَيْهِمْ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ (38)
Ife tidati: “Tsikani pansi nonsenu ndipo pamene Ulangizi wanga udzakufikani, yense amene adzatsatira Ulangiziwu, iye sadzakhala ndi mantha ndipo sadzadandaula.”
وَالَّذِينَ كَفَرُوا وَكَذَّبُوا بِآيَاتِنَا أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ النَّارِ ۖ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (39)
Koma iwo amene sakhulupilira ndipo amatsutsa zizindikiro zathu, iwo adzakhala eni ake a ku Gahena ndipo adzakhalako mpaka kalekale
يَا بَنِي إِسْرَائِيلَ اذْكُرُوا نِعْمَتِيَ الَّتِي أَنْعَمْتُ عَلَيْكُمْ وَأَوْفُوا بِعَهْدِي أُوفِ بِعَهْدِكُمْ وَإِيَّايَ فَارْهَبُونِ (40)
oh Inu ana a Israeli! Kumbukirani madalitso anga amene ndidakupatsani inu ndipo kwaniritsani lonjezo langa ndipo Ine ndikwaniritsa lonjezo lanu. Ndipo ndiopeni Ine ndekha
وَآمِنُوا بِمَا أَنزَلْتُ مُصَدِّقًا لِّمَا مَعَكُمْ وَلَا تَكُونُوا أَوَّلَ كَافِرٍ بِهِ ۖ وَلَا تَشْتَرُوا بِآيَاتِي ثَمَنًا قَلِيلًا وَإِيَّايَ فَاتَّقُونِ (41)
Ndipo khulupirirani mu zimene ndatumiza zimene zichitira umboni chivumbulutso chimene muli nacho, kotero inu musakhale anthu oyamba kuzikana, ndipo musagule ndi mau anga kanthu kakang’ono. Ndipo ndiopeni Ine ndekha
وَلَا تَلْبِسُوا الْحَقَّ بِالْبَاطِلِ وَتَكْتُمُوا الْحَقَّ وَأَنتُمْ تَعْلَمُونَ (42)
Ndipo musasakanize choonadi ndi bodza, ndi kubisa choonadi pamene muli kudziwa
وَأَقِيمُوا الصَّلَاةَ وَآتُوا الزَّكَاةَ وَارْكَعُوا مَعَ الرَّاكِعِينَ (43)
Ndipo pempherani pa nthawi yake, perekani chopereka ndipo weramani pamodzi ndi iwo amene ali kuwerama
۞ أَتَأْمُرُونَ النَّاسَ بِالْبِرِّ وَتَنسَوْنَ أَنفُسَكُمْ وَأَنتُمْ تَتْلُونَ الْكِتَابَ ۚ أَفَلَا تَعْقِلُونَ (44)
Kodi inu mumauza anthu kuchita zabwino pamene inu simulabadira kutero ngakhale mumawerenga Mau a Mulungu? Kodi mulibe nzeru
وَاسْتَعِينُوا بِالصَّبْرِ وَالصَّلَاةِ ۚ وَإِنَّهَا لَكَبِيرَةٌ إِلَّا عَلَى الْخَاشِعِينَ (45)
Funani chithandizo popirira ndi popemphera. Ndithudi izi ndi zovuta kupatula kwa anthu okhulupilira
الَّذِينَ يَظُنُّونَ أَنَّهُم مُّلَاقُو رَبِّهِمْ وَأَنَّهُمْ إِلَيْهِ رَاجِعُونَ (46)
Iwo amene amadziwa kuti adzakumana ndi Ambuye wawo ndipo kuti ndi kwa Iye kumene adzabwerera
يَا بَنِي إِسْرَائِيلَ اذْكُرُوا نِعْمَتِيَ الَّتِي أَنْعَمْتُ عَلَيْكُمْ وَأَنِّي فَضَّلْتُكُمْ عَلَى الْعَالَمِينَ (47)
oh inu ana a Israeli! Kumbukirani madalitso anga amene ndidakupatsani inu ndipo kuti ndidakukondani inu kuposa mitundu ina yonse
وَاتَّقُوا يَوْمًا لَّا تَجْزِي نَفْسٌ عَن نَّفْسٍ شَيْئًا وَلَا يُقْبَلُ مِنْهَا شَفَاعَةٌ وَلَا يُؤْخَذُ مِنْهَا عَدْلٌ وَلَا هُمْ يُنصَرُونَ (48)
Ndipo opani tsiku limene munthu sadzatha kuthandiza mnzake kapena kupepesa ndipo dipo silidzalandiridwa ndiponso sadzathandizidwa
وَإِذْ نَجَّيْنَاكُم مِّنْ آلِ فِرْعَوْنَ يَسُومُونَكُمْ سُوءَ الْعَذَابِ يُذَبِّحُونَ أَبْنَاءَكُمْ وَيَسْتَحْيُونَ نِسَاءَكُمْ ۚ وَفِي ذَٰلِكُم بَلَاءٌ مِّن رَّبِّكُمْ عَظِيمٌ (49)
Ndi mmene tidakupulumutsirani kwa anthu a Farawo, amene anali kukuzunzani kwambiri popha ana anu a amuna ndi kusiya ana anu a akazi. Ndithudi amenewa adali mayeso ochokera kwa Ambuye wanu
وَإِذْ فَرَقْنَا بِكُمُ الْبَحْرَ فَأَنجَيْنَاكُمْ وَأَغْرَقْنَا آلَ فِرْعَوْنَ وَأَنتُمْ تَنظُرُونَ (50)
Ndi pamene Ife tidagawanitsa nyanja ndi kukupulumutsani inu ndipo tidamiza anthu a Farawo inu muli kuona
وَإِذْ وَاعَدْنَا مُوسَىٰ أَرْبَعِينَ لَيْلَةً ثُمَّ اتَّخَذْتُمُ الْعِجْلَ مِن بَعْدِهِ وَأَنتُمْ ظَالِمُونَ (51)
Ndi pamene tidamusankhira Mose masiku makumi anayi ndipo inu mudakonza fanizo la ng’ombe kotero inu mudachimwa
ثُمَّ عَفَوْنَا عَنكُم مِّن بَعْدِ ذَٰلِكَ لَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ (52)
Zitatero, Ife tidakukhululukirani ndi cholinga chakuti mwinamukhozakuthokoza
وَإِذْ آتَيْنَا مُوسَى الْكِتَابَ وَالْفُرْقَانَ لَعَلَّكُمْ تَهْتَدُونَ (53)
Ndipamene Ifetidamupatsa Mose Buku ndi nzeru kuti mutsogozedwe
وَإِذْ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوْمِهِ يَا قَوْمِ إِنَّكُمْ ظَلَمْتُمْ أَنفُسَكُم بِاتِّخَاذِكُمُ الْعِجْلَ فَتُوبُوا إِلَىٰ بَارِئِكُمْ فَاقْتُلُوا أَنفُسَكُمْ ذَٰلِكُمْ خَيْرٌ لَّكُمْ عِندَ بَارِئِكُمْ فَتَابَ عَلَيْكُمْ ۚ إِنَّهُ هُوَ التَّوَّابُ الرَّحِيمُ (54)
Ndi pamene Mose adati kwa anthu ake: “oh inu anthu anga! Ndithudi inu mwadzilakwitsa nokha popembedza fano la mwana wa ng’ombe. Lapani kwa Ambuye wanu ndipo mudziphe nokha. Zimenezo zidzakhala zabwino kwa inu pamaso pa Ambuye wanu.” Ndipo Iye adzakukhululukirani inu. Iye ndi Mwini chikhululukiro ndi Mwini chisoni chosatha
وَإِذْ قُلْتُمْ يَا مُوسَىٰ لَن نُّؤْمِنَ لَكَ حَتَّىٰ نَرَى اللَّهَ جَهْرَةً فَأَخَذَتْكُمُ الصَّاعِقَةُ وَأَنتُمْ تَنظُرُونَ (55)
Ndipameneinumunati:“Oh Mose! Ifesitidzakukhulupilira iwe pokhapokha titamuona Mulungu ndi maso athu.” Nthawi yomweyo chilango chidakufikirani inu muli kuona
ثُمَّ بَعَثْنَاكُم مِّن بَعْدِ مَوْتِكُمْ لَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ (56)
Kenaka Ife tidakuukitsani kwa akufa kuti mwina mukhale othokoza
وَظَلَّلْنَا عَلَيْكُمُ الْغَمَامَ وَأَنزَلْنَا عَلَيْكُمُ الْمَنَّ وَالسَّلْوَىٰ ۖ كُلُوا مِن طَيِّبَاتِ مَا رَزَقْنَاكُمْ ۖ وَمَا ظَلَمُونَا وَلَٰكِن كَانُوا أَنفُسَهُمْ يَظْلِمُونَ (57)
Ndipo tidalamula mtambo kuti ukukuteni ndipo tidakutumizirani Manna ndi Mbalame, ndipo tidati: “Idyani zinthu zabwino zimene takupatsani.” Ndipo iwo sadatilakwire Ife ayi koma adadzilakwira okha
وَإِذْ قُلْنَا ادْخُلُوا هَٰذِهِ الْقَرْيَةَ فَكُلُوا مِنْهَا حَيْثُ شِئْتُمْ رَغَدًا وَادْخُلُوا الْبَابَ سُجَّدًا وَقُولُوا حِطَّةٌ نَّغْفِرْ لَكُمْ خَطَايَاكُمْ ۚ وَسَنَزِيدُ الْمُحْسِنِينَ (58)
Ndi pamene tidawauza kuti: Lowani mu Mzinda uwu ndipo mudye mmenemo mosangalala ndi momwe mungafunire. Lowani modzichepetsa pachipata ndipo munene kuti: “Tikhululukireni” ndipo Ife tidzakukhululukirani machimo anu ndipo tidzawaonjezera zabwino anthu onse ochita zabwino
فَبَدَّلَ الَّذِينَ ظَلَمُوا قَوْلًا غَيْرَ الَّذِي قِيلَ لَهُمْ فَأَنزَلْنَا عَلَى الَّذِينَ ظَلَمُوا رِجْزًا مِّنَ السَّمَاءِ بِمَا كَانُوا يَفْسُقُونَ (59)
Koma anthu ochita zoipa adasintha mawu amene adanenedwa kwa iwo ndipo tidawaponyera, ngati chilango, mlili ochokera kumwamba chifukwa cha zolakwa zawo
۞ وَإِذِ اسْتَسْقَىٰ مُوسَىٰ لِقَوْمِهِ فَقُلْنَا اضْرِب بِّعَصَاكَ الْحَجَرَ ۖ فَانفَجَرَتْ مِنْهُ اثْنَتَا عَشْرَةَ عَيْنًا ۖ قَدْ عَلِمَ كُلُّ أُنَاسٍ مَّشْرَبَهُمْ ۖ كُلُوا وَاشْرَبُوا مِن رِّزْقِ اللَّهِ وَلَا تَعْثَوْا فِي الْأَرْضِ مُفْسِدِينَ (60)
Ndi pamene Mose adafunsa madzi oti apatse anthu ake, Ife tidamuuza kuti: “Menya mwala ndi ndodo yako!” Ndipo nthawi yomweyo a kasupe khumi ndi awiri adatumphuka. Ndipo pfuko lililonse lidadziwamaloakeomwera. Ife tidati: “Idyanindipoimwani koma musayambitse chisokonezo m’dziko pochita zoipa.”
وَإِذْ قُلْتُمْ يَا مُوسَىٰ لَن نَّصْبِرَ عَلَىٰ طَعَامٍ وَاحِدٍ فَادْعُ لَنَا رَبَّكَ يُخْرِجْ لَنَا مِمَّا تُنبِتُ الْأَرْضُ مِن بَقْلِهَا وَقِثَّائِهَا وَفُومِهَا وَعَدَسِهَا وَبَصَلِهَا ۖ قَالَ أَتَسْتَبْدِلُونَ الَّذِي هُوَ أَدْنَىٰ بِالَّذِي هُوَ خَيْرٌ ۚ اهْبِطُوا مِصْرًا فَإِنَّ لَكُم مَّا سَأَلْتُمْ ۗ وَضُرِبَتْ عَلَيْهِمُ الذِّلَّةُ وَالْمَسْكَنَةُ وَبَاءُوا بِغَضَبٍ مِّنَ اللَّهِ ۗ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ كَانُوا يَكْفُرُونَ بِآيَاتِ اللَّهِ وَيَقْتُلُونَ النَّبِيِّينَ بِغَيْرِ الْحَقِّ ۗ ذَٰلِكَ بِمَا عَصَوا وَّكَانُوا يَعْتَدُونَ (61)
Ndi pamene mudati: “oh Mose! Ife sitingapirire kudya chakudya chamtundu umodzi. Motero tipemphere kwa Ambuye wako kuti atitulutsire zina mwa zomera m’nthaka monga masamba, minkhaka, tirigu, nyemba ndi anyezi.” Iye adati: “Kodi inu mufuna kusinthitsa chinthu chabwino ndi choipa? Pitani ku mzinda uliwonse ndipo kumeneko mudzapeza zonse zimene mufuna.” Ndipo manyazi ndi umphawi udadza pa iwo ndipo iwo adapalamula mkwiyo wa Mulungu chifukwa iwo adali kukana mau a Mulungu ndipo anali kupha Atumwi popanda chifukwa popeza iwo adali anthu aupandu ndi anthu osamvera
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَالَّذِينَ هَادُوا وَالنَّصَارَىٰ وَالصَّابِئِينَ مَنْ آمَنَ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ وَعَمِلَ صَالِحًا فَلَهُمْ أَجْرُهُمْ عِندَ رَبِّهِمْ وَلَا خَوْفٌ عَلَيْهِمْ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ (62)
Ndithudi iwo amene amakhulupirira ndi iwo amene ali Ayuda, Akhiristu ndi Asabiyani, aliyense amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza ndipo amachita ntchito zabwino, adzalandira malipiro ake kuchokera kwa Ambuye wawo. Iwo alibe china chili chonse choti aope kapena kudandaula
وَإِذْ أَخَذْنَا مِيثَاقَكُمْ وَرَفَعْنَا فَوْقَكُمُ الطُّورَ خُذُوا مَا آتَيْنَاكُم بِقُوَّةٍ وَاذْكُرُوا مَا فِيهِ لَعَلَّكُمْ تَتَّقُونَ (63)
Ndi pamene Ife tidachita pangano ndi inu ndipo tidakweza phiri kuti likhale pa inu. Ndipo tidati: “Landirani lamulo limene takupatsani inu ndipo kumbukirani zonse zili mmenemo kuti mukhale olungama.”
ثُمَّ تَوَلَّيْتُم مِّن بَعْدِ ذَٰلِكَ ۖ فَلَوْلَا فَضْلُ اللَّهِ عَلَيْكُمْ وَرَحْمَتُهُ لَكُنتُم مِّنَ الْخَاسِرِينَ (64)
Ndipo zitatero inu mudabwerera m’mbuyo. Koma pakadapanda chisomo ndi chisoni cha Mulungu pa inu, ndithudi inu mukadakhala mgulu la anthu osochera
وَلَقَدْ عَلِمْتُمُ الَّذِينَ اعْتَدَوْا مِنكُمْ فِي السَّبْتِ فَقُلْنَا لَهُمْ كُونُوا قِرَدَةً خَاسِئِينَ (65)
Ndipo, ndithudi, inu mudadziwa za anthu amene adaswa malamulo a tsiku la Sabata. Ife tidawauza kuti: “Khalani anyani, onyozedwa ndi okanidwa.”
فَجَعَلْنَاهَا نَكَالًا لِّمَا بَيْنَ يَدَيْهَا وَمَا خَلْفَهَا وَمَوْعِظَةً لِّلْمُتَّقِينَ (66)
Motero tidapereka chilango ichi ngati chitsanzo kwa anthu a mtundu wawo ndi onse amene adali kuwatsatira ndi phunziro kwa anthu angwiro
وَإِذْ قَالَ مُوسَىٰ لِقَوْمِهِ إِنَّ اللَّهَ يَأْمُرُكُمْ أَن تَذْبَحُوا بَقَرَةً ۖ قَالُوا أَتَتَّخِذُنَا هُزُوًا ۖ قَالَ أَعُوذُ بِاللَّهِ أَنْ أَكُونَ مِنَ الْجَاهِلِينَ (67)
Ndi pamene Mose adati kwa anthu ake: “Mulungu wakulamulani kuti muphe ng’ombe.” Iwo adati: “Kodi iwe ufuna kutichita chipongwe?” Mose adati: “ Ndithudi Mulungu anditeteze kuti ndisakhale mbuli.”
قَالُوا ادْعُ لَنَا رَبَّكَ يُبَيِّن لَّنَا مَا هِيَ ۚ قَالَ إِنَّهُ يَقُولُ إِنَّهَا بَقَرَةٌ لَّا فَارِضٌ وَلَا بِكْرٌ عَوَانٌ بَيْنَ ذَٰلِكَ ۖ فَافْعَلُوا مَا تُؤْمَرُونَ (68)
Iwo adati: “Pempha kwa Ambuye wako kuti atiuze ife za mtundu wa ng’ombe”. Mose adati: “Ndithudi Ambuye wanu akuti ng’ombeyi isakhale yokalamba kapena yaing’ono koma kuti ikhale pakati ndi pakati ndipo chitani chimene mwalamulidwa.”
قَالُوا ادْعُ لَنَا رَبَّكَ يُبَيِّن لَّنَا مَا لَوْنُهَا ۚ قَالَ إِنَّهُ يَقُولُ إِنَّهَا بَقَرَةٌ صَفْرَاءُ فَاقِعٌ لَّوْنُهَا تَسُرُّ النَّاظِرِينَ (69)
Iwo adati: “Pempha kwa Ambuye wako kuti atiuze ife maonekedwe a ng’ombeyo”. Mose adati: “Ambuye wanu akuti ng’ombeyo ndi yachikasu yowala ndi yokondweretsa anthu oiona.”
قَالُوا ادْعُ لَنَا رَبَّكَ يُبَيِّن لَّنَا مَا هِيَ إِنَّ الْبَقَرَ تَشَابَهَ عَلَيْنَا وَإِنَّا إِن شَاءَ اللَّهُ لَمُهْتَدُونَ (70)
Iwo adati: “Pempha kwa Ambuye wako kuti atiuze ife maonekedwe eni eni a ng’ombeyi. Ndithudi kwa ife, ng’ombe zonse ndi zofanana. Ngati Mulungu afuna, ife tidzalangizidwa bwino.”
قَالَ إِنَّهُ يَقُولُ إِنَّهَا بَقَرَةٌ لَّا ذَلُولٌ تُثِيرُ الْأَرْضَ وَلَا تَسْقِي الْحَرْثَ مُسَلَّمَةٌ لَّا شِيَةَ فِيهَا ۚ قَالُوا الْآنَ جِئْتَ بِالْحَقِّ ۚ فَذَبَحُوهَا وَمَا كَادُوا يَفْعَلُونَ (71)
Mose adati: “Ndithudi Ambuye wanu akuti ndi ng’ombe imene siinaphunzitsidwe ntchito yolima m’munda kapena yonyamula madzi othiririra m’minda, ndipo ndi ng’ombe yopanda chilema ndi yopanda banga”. Iwo adati: “Tsono iwe wadza ndi choona”. Ndipo iwo adapha ng’ombe ija ngakhale anali pafupi kuti asatero
وَإِذْ قَتَلْتُمْ نَفْسًا فَادَّارَأْتُمْ فِيهَا ۖ وَاللَّهُ مُخْرِجٌ مَّا كُنتُمْ تَكْتُمُونَ (72)
Ndi pamene mudapha munthu ndipo mudayamba kumakanirana wina ndi mnzake. Koma Mulungu anaulula zimene mumabisa
فَقُلْنَا اضْرِبُوهُ بِبَعْضِهَا ۚ كَذَٰلِكَ يُحْيِي اللَّهُ الْمَوْتَىٰ وَيُرِيكُمْ آيَاتِهِ لَعَلَّكُمْ تَعْقِلُونَ (73)
Ndipo Ife tidati: “Menya mtembo ndi mnofu wa ng’ombe”. Mmenemo ndi mmene Mulungu adzadzutsire akufa ndipo amakulangizani zizindikiro zake kuti mukhale ozindikira
ثُمَّ قَسَتْ قُلُوبُكُم مِّن بَعْدِ ذَٰلِكَ فَهِيَ كَالْحِجَارَةِ أَوْ أَشَدُّ قَسْوَةً ۚ وَإِنَّ مِنَ الْحِجَارَةِ لَمَا يَتَفَجَّرُ مِنْهُ الْأَنْهَارُ ۚ وَإِنَّ مِنْهَا لَمَا يَشَّقَّقُ فَيَخْرُجُ مِنْهُ الْمَاءُ ۚ وَإِنَّ مِنْهَا لَمَا يَهْبِطُ مِنْ خَشْيَةِ اللَّهِ ۗ وَمَا اللَّهُ بِغَافِلٍ عَمَّا تَعْمَلُونَ (74)
Ndipo zitatero mitima yanu idauma ngati mwala kapena kuposerapo. Ndithudi pali miyala ina imene imakhala magwero a mitsinje pamene ina idaphwanyika ndipo madzi adatuluka mu iyo. Ndipo, ndithudi, ina mwa iyo imagwa pansi chifukwa choopa Mulungu. Sikuti Mulungu sadziwa zimene mumachita
۞ أَفَتَطْمَعُونَ أَن يُؤْمِنُوا لَكُمْ وَقَدْ كَانَ فَرِيقٌ مِّنْهُمْ يَسْمَعُونَ كَلَامَ اللَّهِ ثُمَّ يُحَرِّفُونَهُ مِن بَعْدِ مَا عَقَلُوهُ وَهُمْ يَعْلَمُونَ (75)
Kodi inu muli kuganiza kuti iwo adzakukhulupirirani ngakh ale kuti gulu lina linali kumva mawu a Mulungu ndipo anali kumawasintha pamene iwo ali kuzindikira ndiponso iwo ali kudziwa chimenechi
وَإِذَا لَقُوا الَّذِينَ آمَنُوا قَالُوا آمَنَّا وَإِذَا خَلَا بَعْضُهُمْ إِلَىٰ بَعْضٍ قَالُوا أَتُحَدِّثُونَهُم بِمَا فَتَحَ اللَّهُ عَلَيْكُمْ لِيُحَاجُّوكُم بِهِ عِندَ رَبِّكُمْ ۚ أَفَلَا تَعْقِلُونَ (76)
Ndipo pamene iwo akumana ndi anthu okhulupirira amanena kuti: “Nafenso timakhulupirira”. Koma akakhala okha pagulu lawo amanena wina kwa mnzake kuti: “Kodi inu mudzawalalikira iwo zimene Mulungu wavumbulutsa kwa inu kuti adzakutsutseni pamaso pa Ambuye wanu? Kodi inu mulibe nzeru?”
أَوَلَا يَعْلَمُونَ أَنَّ اللَّهَ يَعْلَمُ مَا يُسِرُّونَ وَمَا يُعْلِنُونَ (77)
Kodi iwo sadziwa kuti Mulungu amadziwa zimene iwo amabisa ndi zimene amaziulula
وَمِنْهُمْ أُمِّيُّونَ لَا يَعْلَمُونَ الْكِتَابَ إِلَّا أَمَانِيَّ وَإِنْ هُمْ إِلَّا يَظُنُّونَ (78)
Ndipo pali ena mwa iwo amene ndi osaphunzira amene sadziwa za m’Buku koma amakhulupirira mabodza ndi zongoganizira chabe
فَوَيْلٌ لِّلَّذِينَ يَكْتُبُونَ الْكِتَابَ بِأَيْدِيهِمْ ثُمَّ يَقُولُونَ هَٰذَا مِنْ عِندِ اللَّهِ لِيَشْتَرُوا بِهِ ثَمَنًا قَلِيلًا ۖ فَوَيْلٌ لَّهُم مِّمَّا كَتَبَتْ أَيْدِيهِمْ وَوَيْلٌ لَّهُم مِّمَّا يَكْسِبُونَ (79)
Motero tsoka kwa iwo amene amalemba Buku ndi manja awo ndipo amanena kuti: “Mawu awa achoka kwa Mulungu ndi kugula ndi ilo mphatso yochepa”. Tsoka kwa iwo pa zimene alemba manja awo ndipo tsoka kwa iwo pa zimene akupeza chifukwa cha izo
وَقَالُوا لَن تَمَسَّنَا النَّارُ إِلَّا أَيَّامًا مَّعْدُودَةً ۚ قُلْ أَتَّخَذْتُمْ عِندَ اللَّهِ عَهْدًا فَلَن يُخْلِفَ اللَّهُ عَهْدَهُ ۖ أَمْ تَقُولُونَ عَلَى اللَّهِ مَا لَا تَعْلَمُونَ (80)
Iwo adati: “Ife sitidzakhudzidwa ndi moto kupatula masiku owerengeka okha”. Nena: “Kodi inu mwapanga lonjezo ndi Mulungu limene Iye sadzaphwanya? Kapena kodi inu mumanena zinthu zokhudzana Mulungu zimene simuzidziwa?”
بَلَىٰ مَن كَسَبَ سَيِّئَةً وَأَحَاطَتْ بِهِ خَطِيئَتُهُ فَأُولَٰئِكَ أَصْحَابُ النَّارِ ۖ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (81)
Inde! Yense amene achita zoipa ndipo azunguliridwa ndi machimo ake, adzakhala eni ake a Gahena. Kumeneko adzakhalako mpaka kalekale
وَالَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ الْجَنَّةِ ۖ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (82)
Ndipo iwo amene ali ndi chikhulupiriro ndipo amachita ntchito zabwino, iwo ndi eni ake a Paradiso ndipo adzakhala komweko mpaka kale kale
وَإِذْ أَخَذْنَا مِيثَاقَ بَنِي إِسْرَائِيلَ لَا تَعْبُدُونَ إِلَّا اللَّهَ وَبِالْوَالِدَيْنِ إِحْسَانًا وَذِي الْقُرْبَىٰ وَالْيَتَامَىٰ وَالْمَسَاكِينِ وَقُولُوا لِلنَّاسِ حُسْنًا وَأَقِيمُوا الصَّلَاةَ وَآتُوا الزَّكَاةَ ثُمَّ تَوَلَّيْتُمْ إِلَّا قَلِيلًا مِّنكُمْ وَأَنتُم مُّعْرِضُونَ (83)
Ndi pamene Ife tinamvana ndi ana a Israeli: “Musapembedze wina koma Mulungu yekha ndipo onetsani chifundo kwa makolo anu, kwa abale anu, kwa ana a masiye ndi kwa anthu ovutika, ndipo auzeni anthu kuti azichita zabwino. Pempherani pa nthawi yake ndipo perekani msonkho wothandizila anthu osauka”. Komatu inu mudabwerera m’mbuyo kupatula owerengeka okha ndipo simudalabadire china chilichonse
وَإِذْ أَخَذْنَا مِيثَاقَكُمْ لَا تَسْفِكُونَ دِمَاءَكُمْ وَلَا تُخْرِجُونَ أَنفُسَكُم مِّن دِيَارِكُمْ ثُمَّ أَقْرَرْتُمْ وَأَنتُمْ تَشْهَدُونَ (84)
Ndi pamene Ife tinamvana kuti: “Musakhetse magazi a anthu anu kapena kupirikitsa anthu anu kumalo amene muli kukhala”. Zimenezi inu mudavomera ndikuchitira umboni
ثُمَّ أَنتُمْ هَٰؤُلَاءِ تَقْتُلُونَ أَنفُسَكُمْ وَتُخْرِجُونَ فَرِيقًا مِّنكُم مِّن دِيَارِهِمْ تَظَاهَرُونَ عَلَيْهِم بِالْإِثْمِ وَالْعُدْوَانِ وَإِن يَأْتُوكُمْ أُسَارَىٰ تُفَادُوهُمْ وَهُوَ مُحَرَّمٌ عَلَيْكُمْ إِخْرَاجُهُمْ ۚ أَفَتُؤْمِنُونَ بِبَعْضِ الْكِتَابِ وَتَكْفُرُونَ بِبَعْضٍ ۚ فَمَا جَزَاءُ مَن يَفْعَلُ ذَٰلِكَ مِنكُمْ إِلَّا خِزْيٌ فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا ۖ وَيَوْمَ الْقِيَامَةِ يُرَدُّونَ إِلَىٰ أَشَدِّ الْعَذَابِ ۗ وَمَا اللَّهُ بِغَافِلٍ عَمَّا تَعْمَلُونَ (85)
Zitatha izi ndinu amene mudayamba kupha abale anu ndi kupirikitsa gulu lina la inu m’nyumba zawo ndi kuthandiza adani awo pochita machimo ndi kuswa malamulo. Ndipo iwo akamabwera kwa inu ngati akapolo, inu muwaombola ngakhale kuti kupilikitsidwa kwawo kudali koletsedwa kwa inu. Kodi inu mukhulupirira gawo lina la Mau a Mulungu ndi kukana gawo linzake? Kodi ndi malipiro otani amene angalandire wochita zimenezo mwa inu, kupatula mphotho yochititsa manyazi m’dziko lino ndi chilango chowawa kwambiri patsiku louka kwa akufa? Mulungu saiwala ntchito zanu zimene muchita
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ اشْتَرَوُا الْحَيَاةَ الدُّنْيَا بِالْآخِرَةِ ۖ فَلَا يُخَفَّفُ عَنْهُمُ الْعَذَابُ وَلَا هُمْ يُنصَرُونَ (86)
Awo ndiwo amene amagula moyo wa padziko lino lapansi pa mtengo wa moyo umene uli nkudza. Chilango chawo sichidzachepetsedwa ayi ndiponso sadzathandizidwa
وَلَقَدْ آتَيْنَا مُوسَى الْكِتَابَ وَقَفَّيْنَا مِن بَعْدِهِ بِالرُّسُلِ ۖ وَآتَيْنَا عِيسَى ابْنَ مَرْيَمَ الْبَيِّنَاتِ وَأَيَّدْنَاهُ بِرُوحِ الْقُدُسِ ۗ أَفَكُلَّمَا جَاءَكُمْ رَسُولٌ بِمَا لَا تَهْوَىٰ أَنفُسُكُمُ اسْتَكْبَرْتُمْ فَفَرِيقًا كَذَّبْتُمْ وَفَرِيقًا تَقْتُلُونَ (87)
Ndithudi Ife tidamupatsa Mose Buku, ndipo iye atachoka, Ife tidatumiza Atumwi ena. Ndipo tidamupatsa Yesu, mwana wa Maria, zizindikiro zooneka ndi maso ndipo tidamulimbikitsa iye ndi Mzimu Woyera. Kodi nthawi ili yonse imene Aneneri amabwera ndi zimene mitima yanu siifuna mumadzikweza? Gulu lina mumalikana ndipo gulu lina mumalipha
وَقَالُوا قُلُوبُنَا غُلْفٌ ۚ بَل لَّعَنَهُمُ اللَّهُ بِكُفْرِهِمْ فَقَلِيلًا مَّا يُؤْمِنُونَ (88)
Iwo adati: “Mitima yathu ndi yokutidwa.” Iyayi, Mulungu wawatemberera chifukwa cha kusakhupirira kwawo ndipo ndi zochepa zimene iwo amakhulupirira
وَلَمَّا جَاءَهُمْ كِتَابٌ مِّنْ عِندِ اللَّهِ مُصَدِّقٌ لِّمَا مَعَهُمْ وَكَانُوا مِن قَبْلُ يَسْتَفْتِحُونَ عَلَى الَّذِينَ كَفَرُوا فَلَمَّا جَاءَهُم مَّا عَرَفُوا كَفَرُوا بِهِ ۚ فَلَعْنَةُ اللَّهِ عَلَى الْكَافِرِينَ (89)
Ndipo pamene Buku lidadza kwa iwo kuchokera kwa Mulungu, kutsimikiza zimene iwo adali nazo, ngakhale kuti kuyambira kale kale akhala ali kupempha chithandizo kwa Mulungu choti agonjetse anthu osakhulupirira; ndipo pamene chidadza kwa iwo, chimene iwo amadziwa, iwo sadachikhulupirire mu icho. Motero temberero la Mulungu likhale pa anthu osakhulupirira
بِئْسَمَا اشْتَرَوْا بِهِ أَنفُسَهُمْ أَن يَكْفُرُوا بِمَا أَنزَلَ اللَّهُ بَغْيًا أَن يُنَزِّلَ اللَّهُ مِن فَضْلِهِ عَلَىٰ مَن يَشَاءُ مِنْ عِبَادِهِ ۖ فَبَاءُوا بِغَضَبٍ عَلَىٰ غَضَبٍ ۚ وَلِلْكَافِرِينَ عَذَابٌ مُّهِينٌ (90)
Ndi zoipa zomwe asinthanitsa ndi miyoyo yawo pokana zomwe Mulungu wavumbulutsa chifukwa cha kaduka kuti Mulungu wavumbulutsa zabwino kwa amene Iye wamufuna mwa akapolo ake. Iwo adziputira mkwiyo powonjezera pamkwiyo wina. Ndipo chilango choopsa chili kuwadikira anthu osakhulupirira
وَإِذَا قِيلَ لَهُمْ آمِنُوا بِمَا أَنزَلَ اللَّهُ قَالُوا نُؤْمِنُ بِمَا أُنزِلَ عَلَيْنَا وَيَكْفُرُونَ بِمَا وَرَاءَهُ وَهُوَ الْحَقُّ مُصَدِّقًا لِّمَا مَعَهُمْ ۗ قُلْ فَلِمَ تَقْتُلُونَ أَنبِيَاءَ اللَّهِ مِن قَبْلُ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (91)
Ndipo pamene adauzidwa kuti: “Khulupirirani mu zimene Mulungu wavumbulutsa”, iwo adati: “Ife timakhulupirira m’mawu amene adavumbulutsidwa kwa ife.” Ndipo iwo sakhulupilira zimene zavumbulutsidwa posachedwapa ngakhale kuti ndicho choonadi, chimene chikutsimikiza zimene ali nazo. Nena: “Nanga ndi chifukwa chiyani inu mudali kupha Atumwi a Mulungu kale ngati, mudali okhulupiriradi?”
۞ وَلَقَدْ جَاءَكُم مُّوسَىٰ بِالْبَيِّنَاتِ ثُمَّ اتَّخَذْتُمُ الْعِجْلَ مِن بَعْدِهِ وَأَنتُمْ ظَالِمُونَ (92)
Ndithudi Mose adadza kwa inu ndi zizindikiro zooneka koma inu mudatenga ng’ombe ndi kuipembedza iye atachoka ndipo inu munali ochimwa
وَإِذْ أَخَذْنَا مِيثَاقَكُمْ وَرَفَعْنَا فَوْقَكُمُ الطُّورَ خُذُوا مَا آتَيْنَاكُم بِقُوَّةٍ وَاسْمَعُوا ۖ قَالُوا سَمِعْنَا وَعَصَيْنَا وَأُشْرِبُوا فِي قُلُوبِهِمُ الْعِجْلَ بِكُفْرِهِمْ ۚ قُلْ بِئْسَمَا يَأْمُرُكُم بِهِ إِيمَانُكُمْ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (93)
Ndi pamene tidachita pangano ndi inu Ife tidakweza phiri kukhala pamwamba panu ndi kunena kuti: “Sungani zonse zimene takupatsani ndipo muzimvera”. Iwo adati: “Tamva koma sitimvera”. Chifukwa cha kusakhulupirira kwawo, kupembedza ng’ombe kudakhazikika m’mitima yawo. Nena: “Choipa ndi chimene chikhulupiriro chanu chili kukukakamizani ngati inu ndinu okhulupirira.”
قُلْ إِن كَانَتْ لَكُمُ الدَّارُ الْآخِرَةُ عِندَ اللَّهِ خَالِصَةً مِّن دُونِ النَّاسِ فَتَمَنَّوُا الْمَوْتَ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (94)
Nena: “Ngati nyumba zamtsogolo za Mulungu ndi zanu zokha ndipo kuti sizidzapatsidwa kwa anthu ena, lakalakani imfa ngati zimene munena ndi zoona.”
وَلَن يَتَمَنَّوْهُ أَبَدًا بِمَا قَدَّمَتْ أَيْدِيهِمْ ۗ وَاللَّهُ عَلِيمٌ بِالظَّالِمِينَ (95)
Koma iwo sadzalakalaka imfa m’pang’ono pomwe chifukwa cha zoipa zimene adatsogoza manja awo. Ndipo Mulungu amadziwa anthu ochita zosalungama
وَلَتَجِدَنَّهُمْ أَحْرَصَ النَّاسِ عَلَىٰ حَيَاةٍ وَمِنَ الَّذِينَ أَشْرَكُوا ۚ يَوَدُّ أَحَدُهُمْ لَوْ يُعَمَّرُ أَلْفَ سَنَةٍ وَمَا هُوَ بِمُزَحْزِحِهِ مِنَ الْعَذَابِ أَن يُعَمَّرَ ۗ وَاللَّهُ بَصِيرٌ بِمَا يَعْمَلُونَ (96)
Ndithudi iwe udzawapeza kuti iwo amakonda kwambiri moyo uno kuposa aja amene amaphatikiza Mulungu ndi zinthu zina ndipo sakhulupirira kuti kuli kuuka kwa akufa. Aliyense wa iwo akadakondwera ngati akadapatsidwa moyo wokwana zaka chikwi chimodzi. Komabe ngakhale atawonjezeredwa moyo wautali, siungamuchotsere chilango. Ndipo Mulungu ali kuona zonse zimene ali kuchita
قُلْ مَن كَانَ عَدُوًّا لِّجِبْرِيلَ فَإِنَّهُ نَزَّلَهُ عَلَىٰ قَلْبِكَ بِإِذْنِ اللَّهِ مُصَدِّقًا لِّمَا بَيْنَ يَدَيْهِ وَهُدًى وَبُشْرَىٰ لِلْمُؤْمِنِينَ (97)
Nena: “Aliyense amene ndi mdani wa Gabiriyeli, chifukwa, ndithudi, iye wabweretsa chibvumbulutso mu mtima mwako mwachifuniro cha Mulungu, kutsimikiza zimene zidadza kale icho chisanadze ndipo ndi chilangizo ndi nkhani yabwino kwa okhulupirira
مَن كَانَ عَدُوًّا لِّلَّهِ وَمَلَائِكَتِهِ وَرُسُلِهِ وَجِبْرِيلَ وَمِيكَالَ فَإِنَّ اللَّهَ عَدُوٌّ لِّلْكَافِرِينَ (98)
Aliyense amene ali mdani wa Mulungu, Angelo ake, Atumwi ake, Gabiriyeli ndi Michael, ndithudi, Mulungu ndi mdani wa anthu osakhulupirira
وَلَقَدْ أَنزَلْنَا إِلَيْكَ آيَاتٍ بَيِّنَاتٍ ۖ وَمَا يَكْفُرُ بِهَا إِلَّا الْفَاسِقُونَ (99)
Ndithudi Ife tatsitsa kwa iwe chivumbulutso chomveka bwino ndipo palibe amene amachikana kupatula anthu ochita zoipa
أَوَكُلَّمَا عَاهَدُوا عَهْدًا نَّبَذَهُ فَرِيقٌ مِّنْهُم ۚ بَلْ أَكْثَرُهُمْ لَا يُؤْمِنُونَ (100)
Kodi ndi chizolowezi chawo choti nthawi zonse iwo akachita pangano, ena mwa iwo amaliswa? Iyayi! Choonadi ndi chakuti ambiri a iwo sakhulupirira
وَلَمَّا جَاءَهُمْ رَسُولٌ مِّنْ عِندِ اللَّهِ مُصَدِّقٌ لِّمَا مَعَهُمْ نَبَذَ فَرِيقٌ مِّنَ الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ كِتَابَ اللَّهِ وَرَاءَ ظُهُورِهِمْ كَأَنَّهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (101)
Ndipo pamene kudadza kwa iwo Mtumwi wochokera kwa Mulungu, kutsimikiza zimene adali nazo, gulu lina la anthu amene adapatsidwa mau a Mulungu adataya kumbuyo kwawo Buku la Mulungu ngati kuti iwo sakulidziwa
وَاتَّبَعُوا مَا تَتْلُو الشَّيَاطِينُ عَلَىٰ مُلْكِ سُلَيْمَانَ ۖ وَمَا كَفَرَ سُلَيْمَانُ وَلَٰكِنَّ الشَّيَاطِينَ كَفَرُوا يُعَلِّمُونَ النَّاسَ السِّحْرَ وَمَا أُنزِلَ عَلَى الْمَلَكَيْنِ بِبَابِلَ هَارُوتَ وَمَارُوتَ ۚ وَمَا يُعَلِّمَانِ مِنْ أَحَدٍ حَتَّىٰ يَقُولَا إِنَّمَا نَحْنُ فِتْنَةٌ فَلَا تَكْفُرْ ۖ فَيَتَعَلَّمُونَ مِنْهُمَا مَا يُفَرِّقُونَ بِهِ بَيْنَ الْمَرْءِ وَزَوْجِهِ ۚ وَمَا هُم بِضَارِّينَ بِهِ مِنْ أَحَدٍ إِلَّا بِإِذْنِ اللَّهِ ۚ وَيَتَعَلَّمُونَ مَا يَضُرُّهُمْ وَلَا يَنفَعُهُمْ ۚ وَلَقَدْ عَلِمُوا لَمَنِ اشْتَرَاهُ مَا لَهُ فِي الْآخِرَةِ مِنْ خَلَاقٍ ۚ وَلَبِئْسَ مَا شَرَوْا بِهِ أَنفُسَهُمْ ۚ لَوْ كَانُوا يَعْلَمُونَ (102)
Iwo adatsatira zimene a Satana adanena mu Ufumu wa Solomoni. Sikuti Solomoni sadakhulupirire ai koma a Satana ndiwo sadakhulupirire. Iwo amaphunzitsa anthu matsenga ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa angelo awiri Harut ndi Marut ku Babuloni. Koma iwo samaphunzitsa wina aliyense mpaka atanena kuti: “Ndithudi ife tili kukuyesani inu, ndipo musakhale wosakhulupirira ayi.” Kuchokera kwa angelo chimene chimamasula pakati pa mwamuna ndi mkazi wake, ndipo iwo sadaononge wina aliyense ndi zimene adaphunzira kupatula ndi chilolezo cha Mulungu. Iwo amaphunzira zinthu zimene zimawaononga ndipo sizidawapindulire china chilichonse. Ndithudi iwo amadziwa kuti aliyense amene amachita matsenga sadzakhala ndi gawo m’moyo umene uli nkudza. Zopanda pake ndi zimene agulitsa nazo moyo wawo, iwo akadadziwa
وَلَوْ أَنَّهُمْ آمَنُوا وَاتَّقَوْا لَمَثُوبَةٌ مِّنْ عِندِ اللَّهِ خَيْرٌ ۖ لَّوْ كَانُوا يَعْلَمُونَ (103)
Iwo akadakhulupirira ndi kudziteteza ku zoipa, mphotho yawo yochokera kwa Ambuye wawo ikanakhala yabwino, ngati iwo akadadziwa
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَقُولُوا رَاعِنَا وَقُولُوا انظُرْنَا وَاسْمَعُوا ۗ وَلِلْكَافِرِينَ عَذَابٌ أَلِيمٌ (104)
oh inu anthu okhulupirira! Musanene kwa Mtumwi wathu kuti: “Timvere ife” koma muyenera kunena kuti mutiyang’anile ife ndipo mverani. Anthu onse osakhulupirira ali ndi chilango chowawa
مَّا يَوَدُّ الَّذِينَ كَفَرُوا مِنْ أَهْلِ الْكِتَابِ وَلَا الْمُشْرِكِينَ أَن يُنَزَّلَ عَلَيْكُم مِّنْ خَيْرٍ مِّن رَّبِّكُمْ ۗ وَاللَّهُ يَخْتَصُّ بِرَحْمَتِهِ مَن يَشَاءُ ۚ وَاللَّهُ ذُو الْفَضْلِ الْعَظِيمِ (105)
Sichifuniro cha anthu osakhulupirira amene ali pakati pa anthu otsatira za Buku kapena anthu akunja kuti china chake chabwino chidze kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako. Koma Mulungu amasankha wina aliyense amene Iye afuna kuti alandire chisomo chake ndipo Mulungu ndiye mwini zabwino zazikulu
۞ مَا نَنسَخْ مِنْ آيَةٍ أَوْ نُنسِهَا نَأْتِ بِخَيْرٍ مِّنْهَا أَوْ مِثْلِهَا ۗ أَلَمْ تَعْلَمْ أَنَّ اللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (106)
Ngati Ife tisintha vesi lina kapena tichititsa kuti liiwalike, Ife tiikamo lina labwino lolowa m’malo mwake kapena lolingana nalo. Kodi iwe siudziwa kuti Mulungu ali ndi mphamvu pa chilichonse
أَلَمْ تَعْلَمْ أَنَّ اللَّهَ لَهُ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۗ وَمَا لَكُم مِّن دُونِ اللَّهِ مِن وَلِيٍّ وَلَا نَصِيرٍ (107)
Kodi iwe siudziwa kuti ndi Mulungu amene ali Mwini ufumu wa kumwamba ndi dziko lapansi ndipo kuti kupatula Iye yekha kulibe wina amene akhoza kukuteteza kapena kukuthandiza
أَمْ تُرِيدُونَ أَن تَسْأَلُوا رَسُولَكُمْ كَمَا سُئِلَ مُوسَىٰ مِن قَبْلُ ۗ وَمَن يَتَبَدَّلِ الْكُفْرَ بِالْإِيمَانِ فَقَدْ ضَلَّ سَوَاءَ السَّبِيلِ (108)
Kapena mukufuna kumufunsa Mtumwi wanu monga mmene adamufunsira Mose kale? Ndipo aliyense amene asintha chikhulupiriro chake ndi kuyamba kusakhulupirira ndithudi wasochera ku njira yoyenera
وَدَّ كَثِيرٌ مِّنْ أَهْلِ الْكِتَابِ لَوْ يَرُدُّونَكُم مِّن بَعْدِ إِيمَانِكُمْ كُفَّارًا حَسَدًا مِّنْ عِندِ أَنفُسِهِم مِّن بَعْدِ مَا تَبَيَّنَ لَهُمُ الْحَقُّ ۖ فَاعْفُوا وَاصْفَحُوا حَتَّىٰ يَأْتِيَ اللَّهُ بِأَمْرِهِ ۗ إِنَّ اللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (109)
Anthu ambiri otsatira a m’Buku amafuna kuti akusokeretse chifukwa cha kaduka kuti ukhale osakhulupirira ngakhale pamene choonadi chaonekera poyera kwa iwo. Koma akhululukire mpaka pamene Mulungu abweretsa lamulo lake. Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu pa zinthu zonse
وَأَقِيمُوا الصَّلَاةَ وَآتُوا الزَّكَاةَ ۚ وَمَا تُقَدِّمُوا لِأَنفُسِكُم مِّنْ خَيْرٍ تَجِدُوهُ عِندَ اللَّهِ ۗ إِنَّ اللَّهَ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (110)
Ndipo pitiriza mapemphero ndipo pereka msonkho wothandiza anthu osauka. Ndipo chilichonse chabwino chimene mungatsogoze mudzachipeza kwa Mulungu. Ndithudi Mulungu amaona zonse zimene muli kuchita
وَقَالُوا لَن يَدْخُلَ الْجَنَّةَ إِلَّا مَن كَانَ هُودًا أَوْ نَصَارَىٰ ۗ تِلْكَ أَمَانِيُّهُمْ ۗ قُلْ هَاتُوا بُرْهَانَكُمْ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (111)
Iwo amanena kuti: “Palibe amene adzalowa ku Paradiso kupatula yekhayo amene ali Myuda kapena Mkhirisitu. Zimenezo ndizo zilako lako zawo. Nena: “Bweretsani umboni wanu ngati muli ndi chilungamo.”
بَلَىٰ مَنْ أَسْلَمَ وَجْهَهُ لِلَّهِ وَهُوَ مُحْسِنٌ فَلَهُ أَجْرُهُ عِندَ رَبِّهِ وَلَا خَوْفٌ عَلَيْهِمْ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ (112)
Inde aliyense amene amadzipereka kwathunthu kwa Mulungu ndipo amachita ntchito zabwino adzapeza malipiro ake kwa Ambuye wake. Iwo sadzaopa china chilichonse kapena kukhumudwa
وَقَالَتِ الْيَهُودُ لَيْسَتِ النَّصَارَىٰ عَلَىٰ شَيْءٍ وَقَالَتِ النَّصَارَىٰ لَيْسَتِ الْيَهُودُ عَلَىٰ شَيْءٍ وَهُمْ يَتْلُونَ الْكِتَابَ ۗ كَذَٰلِكَ قَالَ الَّذِينَ لَا يَعْلَمُونَ مِثْلَ قَوْلِهِمْ ۚ فَاللَّهُ يَحْكُمُ بَيْنَهُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ فِيمَا كَانُوا فِيهِ يَخْتَلِفُونَ (113)
Ayuda anati: Akhirisitu satsatira china chilichonse chabwino pamene Akhirisitu anati, Ayuda satsatira chilichonse ngakhale kuti onse amawerenga Buku la Mulungu. Izi zili chimodzimodzi ndi zimene anthu osazindikira amalankhula. Mulungu adzaweruza pakati pawo tsiku la chiweruzo mu zimene adali kusiyana maganizo awo
وَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّن مَّنَعَ مَسَاجِدَ اللَّهِ أَن يُذْكَرَ فِيهَا اسْمُهُ وَسَعَىٰ فِي خَرَابِهَا ۚ أُولَٰئِكَ مَا كَانَ لَهُمْ أَن يَدْخُلُوهَا إِلَّا خَائِفِينَ ۚ لَهُمْ فِي الدُّنْيَا خِزْيٌ وَلَهُمْ فِي الْآخِرَةِ عَذَابٌ عَظِيمٌ (114)
Kodi olakwa kwambiri ndani kuposa amene aletsa anthu kuti dzina la Mulungu lizitchulidwa mu Mizikiti ya Mulungu ndi kulimbikitsa kuiononga? Kotero iwo satha kulowa mu Mizikiti koma mwamantha. Iwo adzachititsidwa manyazi m’dziko lino ndipo adzalangidwa koposa m’dziko limene lili nkudza
وَلِلَّهِ الْمَشْرِقُ وَالْمَغْرِبُ ۚ فَأَيْنَمَا تُوَلُّوا فَثَمَّ وَجْهُ اللَّهِ ۚ إِنَّ اللَّهَ وَاسِعٌ عَلِيمٌ (115)
Mulungu ndiye Mwini wake wa ku m’mawa ndi ku madzulo, motero mbali iliyonse imene muyang’ana kuli Mulungu. Ndithudi Iye ndi okwana pa zofuna za zolengedwa zake ndipo Iye amadziwa china chilichonse
وَقَالُوا اتَّخَذَ اللَّهُ وَلَدًا ۗ سُبْحَانَهُ ۖ بَل لَّهُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ كُلٌّ لَّهُ قَانِتُونَ (116)
Iwo amati: “Mulungu wabereka mwana.” Mulungu ayeretsedwe ku zimenezi. Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi m’dziko lapansi ndipo zinthu zonse zimagonja kwa Iye
بَدِيعُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ وَإِذَا قَضَىٰ أَمْرًا فَإِنَّمَا يَقُولُ لَهُ كُن فَيَكُونُ (117)
Namalenga wa kumwamba ndi dziko lapansi! Pamene Iye alamulira chinthu amangonena kuti: “Chikhale” ndipo chimakhaladi
وَقَالَ الَّذِينَ لَا يَعْلَمُونَ لَوْلَا يُكَلِّمُنَا اللَّهُ أَوْ تَأْتِينَا آيَةٌ ۗ كَذَٰلِكَ قَالَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِم مِّثْلَ قَوْلِهِمْ ۘ تَشَابَهَتْ قُلُوبُهُمْ ۗ قَدْ بَيَّنَّا الْآيَاتِ لِقَوْمٍ يُوقِنُونَ (118)
Ndipo anthu osadziwa amati: “Kodi ndi chifukwa chiyani Mulungu sakutilankhula kapena kutibweretsera chizindikiro?” Mmenemo ndi mmene adanenera anthu amene adalipo kale iwo asadadze. Mitima yawo yonse ndi yolingana. Ndithudi Ife tafotokoza zizindikiro kwa anthu okhulupirira
إِنَّا أَرْسَلْنَاكَ بِالْحَقِّ بَشِيرًا وَنَذِيرًا ۖ وَلَا تُسْأَلُ عَنْ أَصْحَابِ الْجَحِيمِ (119)
Ndithudi Ife takutumiza ndi choonadi kuti ulalikire uthenga wosangalatsa ndi kupereka chenjezo. Siudzafunsidwa za anthu okhala ku moto
وَلَن تَرْضَىٰ عَنكَ الْيَهُودُ وَلَا النَّصَارَىٰ حَتَّىٰ تَتَّبِعَ مِلَّتَهُمْ ۗ قُلْ إِنَّ هُدَى اللَّهِ هُوَ الْهُدَىٰ ۗ وَلَئِنِ اتَّبَعْتَ أَهْوَاءَهُم بَعْدَ الَّذِي جَاءَكَ مِنَ الْعِلْمِ ۙ مَا لَكَ مِنَ اللَّهِ مِن وَلِيٍّ وَلَا نَصِيرٍ (120)
Ayuda kapena Akhirisitu sadzakondwera nawe pokhapokha ngati iwe utsatira chipembedzo chawo. Nena: “Ndithudi njira yoyenera ya Mulungu ndiyo njira yeniyeni.” Ndipo ngati iwe pamene walandira nzeru zimene wapatsidwa, utsatira zifuniro zawo, iwe siudzapeza wina aliyense wokuthandiza kapena kukuteteza ku mkwiyo wa Mulungu
الَّذِينَ آتَيْنَاهُمُ الْكِتَابَ يَتْلُونَهُ حَقَّ تِلَاوَتِهِ أُولَٰئِكَ يُؤْمِنُونَ بِهِ ۗ وَمَن يَكْفُرْ بِهِ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْخَاسِرُونَ (121)
Kwa iwo amene tidawapatsa Buku, amaliwerenga monga momwe liyenera kuwerengedwera. Iwo amakhulupirira za bukuli, koma iwo amene amalikana ilo, ndithudi ndi olephera
يَا بَنِي إِسْرَائِيلَ اذْكُرُوا نِعْمَتِيَ الَّتِي أَنْعَمْتُ عَلَيْكُمْ وَأَنِّي فَضَّلْتُكُمْ عَلَى الْعَالَمِينَ (122)
oh Inu ana a Israeli! Kumbukirani madalitso anga kwa inu ndipo ndinakudalitsani inu kuposa mitundu yonse pa dziko la pansi
وَاتَّقُوا يَوْمًا لَّا تَجْزِي نَفْسٌ عَن نَّفْسٍ شَيْئًا وَلَا يُقْبَلُ مِنْهَا عَدْلٌ وَلَا تَنفَعُهَا شَفَاعَةٌ وَلَا هُمْ يُنصَرُونَ (123)
Liopeni tsiku limene munthu sadzathandiza munthu wina pa china chilichonse ndiponso nthawi imene kupepesa kapena kupereka dipo sikudzavomerezeka ndipo iwo sadzapeza thandizo
۞ وَإِذِ ابْتَلَىٰ إِبْرَاهِيمَ رَبُّهُ بِكَلِمَاتٍ فَأَتَمَّهُنَّ ۖ قَالَ إِنِّي جَاعِلُكَ لِلنَّاسِ إِمَامًا ۖ قَالَ وَمِن ذُرِّيَّتِي ۖ قَالَ لَا يَنَالُ عَهْدِي الظَّالِمِينَ (124)
Ndi pamene Abrahamu anayesedwa ndi Ambuye wake kuti atsatire malamulo ena amene iye adakwaniritsa. Iye adati:“Ndithudi Inendidzakupangaiwekukhalamtsogoleri wa mitundu ya anthu onse.” Abrahamu adapempha: “Ndi atsogoleri ochokera mwa ana anga?” Iye adati: “Pangano langa silikhudza anthu ochita zoipa.”
وَإِذْ جَعَلْنَا الْبَيْتَ مَثَابَةً لِّلنَّاسِ وَأَمْنًا وَاتَّخِذُوا مِن مَّقَامِ إِبْرَاهِيمَ مُصَلًّى ۖ وَعَهِدْنَا إِلَىٰ إِبْرَاهِيمَ وَإِسْمَاعِيلَ أَن طَهِّرَا بَيْتِيَ لِلطَّائِفِينَ وَالْعَاكِفِينَ وَالرُّكَّعِ السُّجُودِ (125)
Ndi pamene tidaipanga Nyumba kukhala malo opumuliramo ndi obisalamo anthu: Dzisankhireni malo amene Abrahamu adaimapo, ngati malo opempheramo. Ife tidamulamula Abrahamu ndi Ishimayeli kuti “ayeretse nyumba yanga” kuti anthu amene amayenda moizungulira kapena amaigwiritsa ntchito ngati malo obindikiramo ndi mtima onse kapena malo wolambiramo pamene ali mkati mwa mapemphero
وَإِذْ قَالَ إِبْرَاهِيمُ رَبِّ اجْعَلْ هَٰذَا بَلَدًا آمِنًا وَارْزُقْ أَهْلَهُ مِنَ الثَّمَرَاتِ مَنْ آمَنَ مِنْهُم بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ ۖ قَالَ وَمَن كَفَرَ فَأُمَتِّعُهُ قَلِيلًا ثُمَّ أَضْطَرُّهُ إِلَىٰ عَذَابِ النَّارِ ۖ وَبِئْسَ الْمَصِيرُ (126)
Ndi pamene Abrahamu adati: “Ambuye wanga upangeni Mzinda uno kukhala Mzinda wa mtendere ndipo muwapatse zipatso zambiri anthu ake, iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza.” Iye adati: “Inde koma iye amene akana kukhulupirira, Ine ndidzamusangalatsa mwa kanthawi kochepa koma ndidzamududuluza kupita ku chilango cha ku Gahena, malo oipa zedi kukhalako.”
وَإِذْ يَرْفَعُ إِبْرَاهِيمُ الْقَوَاعِدَ مِنَ الْبَيْتِ وَإِسْمَاعِيلُ رَبَّنَا تَقَبَّلْ مِنَّا ۖ إِنَّكَ أَنتَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ (127)
Ndi pamene Abrahamu ndi Ishimayeli adamanga maziko a Nyumba. Anati: Ambuye wathu; Landirani ichi kuchokera kwa ife. Ndithudi inu mumamva zonse ndipo mumadziwachinthuchinachilichonse.”
رَبَّنَا وَاجْعَلْنَا مُسْلِمَيْنِ لَكَ وَمِن ذُرِّيَّتِنَا أُمَّةً مُّسْلِمَةً لَّكَ وَأَرِنَا مَنَاسِكَنَا وَتُبْ عَلَيْنَا ۖ إِنَّكَ أَنتَ التَّوَّابُ الرَّحِيمُ (128)
“Ambuye wathu! Tipangeni ife kukhala okumverani Inu ndi ana athu kukhala mtundu umene udzakumverani Inu ndipo tiphunzitseni miyambo yathu yopembedzera ndipo mutikhululukire. Ndithudi Inu ndinu okhululukira ndi Wachisoni chosatha.”
رَبَّنَا وَابْعَثْ فِيهِمْ رَسُولًا مِّنْهُمْ يَتْلُو عَلَيْهِمْ آيَاتِكَ وَيُعَلِّمُهُمُ الْكِتَابَ وَالْحِكْمَةَ وَيُزَكِّيهِمْ ۚ إِنَّكَ أَنتَ الْعَزِيزُ الْحَكِيمُ (129)
“Oh Ambuye wathu! Atumizireni Mtumwi kuchokera kumtundu wawo amene adzawawerengera Mawu Anu ndi kuwaphunzitsa Buku ndiponso luntha ndi kuwayeretsa iwo ku machimo awo. Ndithudi Inu ndinu Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse.”
وَمَن يَرْغَبُ عَن مِّلَّةِ إِبْرَاهِيمَ إِلَّا مَن سَفِهَ نَفْسَهُ ۚ وَلَقَدِ اصْطَفَيْنَاهُ فِي الدُّنْيَا ۖ وَإِنَّهُ فِي الْآخِرَةِ لَمِنَ الصَّالِحِينَ (130)
Ndani, kupatula munthu wopusa yekha, amene angaleke kutsatira chikhulupiriro cha Abrahamu? Ndithudi Ife tidamusankha iye m’dziko lino ndipo, ndithudi, m’dziko limene lili nkudza, iye adzakhala pamodzi ndi anthu olungama
إِذْ قَالَ لَهُ رَبُّهُ أَسْلِمْ ۖ قَالَ أَسْلَمْتُ لِرَبِّ الْعَالَمِينَ (131)
Pamene Ambuye wake adati: “Dzipereke,” iye adati: “Ine ndadzipereka kwa Ambuye wa zolengedwa zonse.”
وَوَصَّىٰ بِهَا إِبْرَاهِيمُ بَنِيهِ وَيَعْقُوبُ يَا بَنِيَّ إِنَّ اللَّهَ اصْطَفَىٰ لَكُمُ الدِّينَ فَلَا تَمُوتُنَّ إِلَّا وَأَنتُم مُّسْلِمُونَ (132)
Abrahamu analangiza chikhulupiriro chake pa ana ake ndi Yakobo. “oh ana anga! Ndithudi Mulungu wakusankhirani inu chipembedzo ndipo musamwalire ngati anthu wamba ai koma ngati Asilamu.”
أَمْ كُنتُمْ شُهَدَاءَ إِذْ حَضَرَ يَعْقُوبَ الْمَوْتُ إِذْ قَالَ لِبَنِيهِ مَا تَعْبُدُونَ مِن بَعْدِي قَالُوا نَعْبُدُ إِلَٰهَكَ وَإِلَٰهَ آبَائِكَ إِبْرَاهِيمَ وَإِسْمَاعِيلَ وَإِسْحَاقَ إِلَٰهًا وَاحِدًا وَنَحْنُ لَهُ مُسْلِمُونَ (133)
Kodi kapena inu mudalipo pamene Yakobo imamufikira imfa? Pamene adawauza ana ake kuti: “Kodi inu mudzapembedza ndani pambuyo panga?” Iwo adati: “Ife tidzapembedza Mulungu wanu ndi Mulungu wa makolo anu Abrahamu, Ishimayeli ndi Isake, Mulungu mmodzi yekha. Ndipo kwa Iye, ife tidzadzipereka ngati Asilamu.”
تِلْكَ أُمَّةٌ قَدْ خَلَتْ ۖ لَهَا مَا كَسَبَتْ وَلَكُم مَّا كَسَبْتُمْ ۖ وَلَا تُسْأَلُونَ عَمَّا كَانُوا يَعْمَلُونَ (134)
Umenewu ndi mbadwo umene udafa kale. Iwo adzalandira zimene adachita ndipo inu mudzalandira mphoto ya zimene muchita. Ndipo inu simudzafunsidwa zimene iwo amachita
وَقَالُوا كُونُوا هُودًا أَوْ نَصَارَىٰ تَهْتَدُوا ۗ قُلْ بَلْ مِلَّةَ إِبْرَاهِيمَ حَنِيفًا ۖ وَمَا كَانَ مِنَ الْمُشْرِكِينَ (135)
Iwo adati: “Khalani Ayuda kapena Akhirisitu ndipo mudzatsogozedwa ku choonadi.” Nenani: “Iyayi! Koma Chipembedzo cha Abrahamu wangwiro, ndipo iye sanali kupembedzamafano.”
قُولُوا آمَنَّا بِاللَّهِ وَمَا أُنزِلَ إِلَيْنَا وَمَا أُنزِلَ إِلَىٰ إِبْرَاهِيمَ وَإِسْمَاعِيلَ وَإِسْحَاقَ وَيَعْقُوبَ وَالْأَسْبَاطِ وَمَا أُوتِيَ مُوسَىٰ وَعِيسَىٰ وَمَا أُوتِيَ النَّبِيُّونَ مِن رَّبِّهِمْ لَا نُفَرِّقُ بَيْنَ أَحَدٍ مِّنْهُمْ وَنَحْنُ لَهُ مُسْلِمُونَ (136)
Nenani:“Ifetimakhulupiriramwa Mulungu ndi zimene zavumbulutsidwa kwa ife, ndi zimene zinavumbulutsidwa kwa Abrahamu, Ishimayeli, Isake, Yakobo ndi kwa mitundu ya anthu ndi zimene adapatsidwa Mose ndi Yesu ndi zimene adapatsidwa Atumwi ena kuchokera kwa Ambuye wawo. Ife sitisiyanitsa pakati pa aliyense wa iwo ndipo ndi kwa Iye kumene tadzipereka kwathunthu.”
فَإِنْ آمَنُوا بِمِثْلِ مَا آمَنتُم بِهِ فَقَدِ اهْتَدَوا ۖ وَّإِن تَوَلَّوْا فَإِنَّمَا هُمْ فِي شِقَاقٍ ۖ فَسَيَكْفِيكَهُمُ اللَّهُ ۚ وَهُوَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ (137)
Ndipo ngati iwo akhulupirira monga mmene mwakhulupirira inu ndiye kuti ndi olangizidwa bwino, koma ngati akana, ndithudi iwo ndi otsutsa chabe. Polimbana ndi iwo, Mulungu adzakuteteza. Iye amamva zonse ndipo amadziwa chinthu china chilichonse
صِبْغَةَ اللَّهِ ۖ وَمَنْ أَحْسَنُ مِنَ اللَّهِ صِبْغَةً ۖ وَنَحْنُ لَهُ عَابِدُونَ (138)
Chipembedzo chathu ndi chochokera kwa Mulungu. Kodi chipembedzo chabwino kuposa cha Mulungu ndi chiti? Ndipo ife ndife timamupembedza Iye
قُلْ أَتُحَاجُّونَنَا فِي اللَّهِ وَهُوَ رَبُّنَا وَرَبُّكُمْ وَلَنَا أَعْمَالُنَا وَلَكُمْ أَعْمَالُكُمْ وَنَحْنُ لَهُ مُخْلِصُونَ (139)
Nena: “Kodi mukutsutsana ndi ife pa nkhani zokhudza Mulungu amene ali Ambuye wathu ndi Ambuye wanu? Ife tili ndi udindo pa ntchito zathu, nanu pa ntchito zanu. Ndi kwa Iye yekha kumene ife tadzipereka.”
أَمْ تَقُولُونَ إِنَّ إِبْرَاهِيمَ وَإِسْمَاعِيلَ وَإِسْحَاقَ وَيَعْقُوبَ وَالْأَسْبَاطَ كَانُوا هُودًا أَوْ نَصَارَىٰ ۗ قُلْ أَأَنتُمْ أَعْلَمُ أَمِ اللَّهُ ۗ وَمَنْ أَظْلَمُ مِمَّن كَتَمَ شَهَادَةً عِندَهُ مِنَ اللَّهِ ۗ وَمَا اللَّهُ بِغَافِلٍ عَمَّا تَعْمَلُونَ (140)
Kodi kapena inu mukunena kuti Abrahamu, Ishimayeli, Isake, Yakobo ndi mitundu yake adali Ayuda kapena Akhirisitu? Nena: “Kodi inu mumadziwa kapena Mulungu? Kodi oipa kwambiri ndani kuposa munthu amene amabisa mawu amene walandira kuchokera kwa Mulungu? Koma Mulungu saiwala zimene mukuchita.”
تِلْكَ أُمَّةٌ قَدْ خَلَتْ ۖ لَهَا مَا كَسَبَتْ وَلَكُم مَّا كَسَبْتُمْ ۖ وَلَا تُسْأَلُونَ عَمَّا كَانُوا يَعْمَلُونَ (141)
Umenewo ndi mbadwo umene udafa kale. Iwo adzalandira mphotho ya zimene adachita ndipo inu mudzalandira ya zimene mumachita. Ndipo inu simudzafunsidwa zimene iwo amachita
۞ سَيَقُولُ السُّفَهَاءُ مِنَ النَّاسِ مَا وَلَّاهُمْ عَن قِبْلَتِهِمُ الَّتِي كَانُوا عَلَيْهَا ۚ قُل لِّلَّهِ الْمَشْرِقُ وَالْمَغْرِبُ ۚ يَهْدِي مَن يَشَاءُ إِلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (142)
Anthu opusa adzanena: “Kodi ndi chifukwa chiyani asintha malo oyang’anako akamapemphera?” Nena: “Mwini wake wa ku m’mawa ndi ku madzulo ndi Mulungu. Iye amatsogolera yemwe wamufuna ku njira yoyenera.”
وَكَذَٰلِكَ جَعَلْنَاكُمْ أُمَّةً وَسَطًا لِّتَكُونُوا شُهَدَاءَ عَلَى النَّاسِ وَيَكُونَ الرَّسُولُ عَلَيْكُمْ شَهِيدًا ۗ وَمَا جَعَلْنَا الْقِبْلَةَ الَّتِي كُنتَ عَلَيْهَا إِلَّا لِنَعْلَمَ مَن يَتَّبِعُ الرَّسُولَ مِمَّن يَنقَلِبُ عَلَىٰ عَقِبَيْهِ ۚ وَإِن كَانَتْ لَكَبِيرَةً إِلَّا عَلَى الَّذِينَ هَدَى اللَّهُ ۗ وَمَا كَانَ اللَّهُ لِيُضِيعَ إِيمَانَكُمْ ۚ إِنَّ اللَّهَ بِالنَّاسِ لَرَءُوفٌ رَّحِيمٌ (143)
Motero Ife takupangani inu kukhala mtundu wa anthu angwiro kuti mukhale mboni kwa anthu ndi kuti Mtumwi akhale mboni kwa inu. Ndipo Ife tidakhazikitsa mbali imene unkayang’anako kale ndi cholinga choona anthu amene amatsatira Mtumwi ndi iwo amene amabwerera m’mbuyo. Ndithudi uwu ndi muyeso waukulu kupatula kwa iwo amene adatsogozedwa ndi Mulungu. Ndipo Mulungu sakanapanga chikhulupiriro chanu kuti chikhale chopanda phindu. Ndithudi Mulungu ali ndi chifundo chambiri ndi chisoni kwa anthu
قَدْ نَرَىٰ تَقَلُّبَ وَجْهِكَ فِي السَّمَاءِ ۖ فَلَنُوَلِّيَنَّكَ قِبْلَةً تَرْضَاهَا ۚ فَوَلِّ وَجْهَكَ شَطْرَ الْمَسْجِدِ الْحَرَامِ ۚ وَحَيْثُ مَا كُنتُمْ فَوَلُّوا وُجُوهَكُمْ شَطْرَهُ ۗ وَإِنَّ الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ لَيَعْلَمُونَ أَنَّهُ الْحَقُّ مِن رَّبِّهِمْ ۗ وَمَا اللَّهُ بِغَافِلٍ عَمَّا يَعْمَلُونَ (144)
Ndithudi nthawi zambiri Ife takhala tili kukuona uli kuyang’ana kumwamba. Ndithudi Ife tidzakulamula kuti uziyang’ana ku mbali yimene idzakukondweretsa iwe, motero yang’anitsa nkhope yako kumene kuli Mzikiti woyera ndipo kuli konse kumene muli yang’anani nkhope zanu komweko. Ndithudi iwo amene adapatsidwa Buku kale amadziwa kuti ichi ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wawo. Ndipo Mulungu saiwala zomwe muchita
وَلَئِنْ أَتَيْتَ الَّذِينَ أُوتُوا الْكِتَابَ بِكُلِّ آيَةٍ مَّا تَبِعُوا قِبْلَتَكَ ۚ وَمَا أَنتَ بِتَابِعٍ قِبْلَتَهُمْ ۚ وَمَا بَعْضُهُم بِتَابِعٍ قِبْلَةَ بَعْضٍ ۚ وَلَئِنِ اتَّبَعْتَ أَهْوَاءَهُم مِّن بَعْدِ مَا جَاءَكَ مِنَ الْعِلْمِ ۙ إِنَّكَ إِذًا لَّمِنَ الظَّالِمِينَ (145)
Ngakhale kuti iwe utawapatsa umboni wotsimikiza, iwo amene anapatsidwa Buku, sadzayang’ana kumalo kumene uli kuyang’ana ukamapemphera. Ndipo iwe siudzayang’ana ku mbali kwawo. Ndipo iwo sadzayang’ana ku mbali ya anzawo. Ndipo ngati, pamene nzeru zapatsidwa kwa iwe, uvomeleza zilakolako zawo, ndithudi iwe udzakhala munthu wolakwa kwambiri
الَّذِينَ آتَيْنَاهُمُ الْكِتَابَ يَعْرِفُونَهُ كَمَا يَعْرِفُونَ أَبْنَاءَهُمْ ۖ وَإِنَّ فَرِيقًا مِّنْهُمْ لَيَكْتُمُونَ الْحَقَّ وَهُمْ يَعْلَمُونَ (146)
Iwo amene tidawapatsa Buku, amamuzindikira Mtumwi monga momwe amazindikirira ana awo amuna. Koma, ndithudi, ena mwa iwo amabisa choonadi pamene iwo ali kudziwa
الْحَقُّ مِن رَّبِّكَ ۖ فَلَا تَكُونَنَّ مِنَ الْمُمْتَرِينَ (147)
Ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wako. Motero usachikaikire ayi
وَلِكُلٍّ وِجْهَةٌ هُوَ مُوَلِّيهَا ۖ فَاسْتَبِقُوا الْخَيْرَاتِ ۚ أَيْنَ مَا تَكُونُوا يَأْتِ بِكُمُ اللَّهُ جَمِيعًا ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (148)
Mtundu uli wonse uli ndi mbali imene umayang’ana popemphera. Motero limbikirani pochita zabwino. Kulikonse kumene mudzakhale, Mulungu adzakusonkhanitsani pamodzi. Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse
وَمِنْ حَيْثُ خَرَجْتَ فَوَلِّ وَجْهَكَ شَطْرَ الْمَسْجِدِ الْحَرَامِ ۖ وَإِنَّهُ لَلْحَقُّ مِن رَّبِّكَ ۗ وَمَا اللَّهُ بِغَافِلٍ عَمَّا تَعْمَلُونَ (149)
Ndipo dera lililonse limene uchokera, yang’ana nkhope yako ku Mzikiti woyera popemphera, chifukwa chimenechi ndicho choonadi chochokera kwa Ambuye wako. Ndipo Mulungu saiwala zomwe mumachita
وَمِنْ حَيْثُ خَرَجْتَ فَوَلِّ وَجْهَكَ شَطْرَ الْمَسْجِدِ الْحَرَامِ ۚ وَحَيْثُ مَا كُنتُمْ فَوَلُّوا وُجُوهَكُمْ شَطْرَهُ لِئَلَّا يَكُونَ لِلنَّاسِ عَلَيْكُمْ حُجَّةٌ إِلَّا الَّذِينَ ظَلَمُوا مِنْهُمْ فَلَا تَخْشَوْهُمْ وَاخْشَوْنِي وَلِأُتِمَّ نِعْمَتِي عَلَيْكُمْ وَلَعَلَّكُمْ تَهْتَدُونَ (150)
Ndipo dera lililonse limene uchokera, yang’ana nkhope yako ku Mzikiti Woyera popemphera. Kulikonse kumene mungakhale, yang’anani nkhope zanu komweko kuti anthu asakhale ndi nkhani yokudzudzulani inu kupatula okhawo amene ndi olakwa. Motero musawaope iwo koma opani Ine kuti ndikwaniritse madalitso anga pa inu ndiponso kuti mukhale otsogozedwa
كَمَا أَرْسَلْنَا فِيكُمْ رَسُولًا مِّنكُمْ يَتْلُو عَلَيْكُمْ آيَاتِنَا وَيُزَكِّيكُمْ وَيُعَلِّمُكُمُ الْكِتَابَ وَالْحِكْمَةَ وَيُعَلِّمُكُم مَّا لَمْ تَكُونُوا تَعْلَمُونَ (151)
Monga takutumizirani Mtumwi kuchokera ku mtundu wanu, kuti akuwerengereni chivumbulutso chathu ndi kukuyeretsani machimo ndiponso kukuphunzitsani inu za Buku ndi nzeru zakuya ndiponso akuphunzitseni zinthu zimene simudali kuzidziwa
فَاذْكُرُونِي أَذْكُرْكُمْ وَاشْكُرُوا لِي وَلَا تَكْفُرُونِ (152)
Motero ndikumbukireni Ine. Ndipo Ine ndidzakukumbukirani inu ndipo ndiyamikeni Ine ndipo musakhale wosathokoza
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا اسْتَعِينُوا بِالصَّبْرِ وَالصَّلَاةِ ۚ إِنَّ اللَّهَ مَعَ الصَّابِرِينَ (153)
Oh Inu anthu okhulupirira! Funani chithandizo popirira ndi popemphera. Ndithudi! Mulungu ali pamodzi ndi anthu opirira
وَلَا تَقُولُوا لِمَن يُقْتَلُ فِي سَبِيلِ اللَّهِ أَمْوَاتٌ ۚ بَلْ أَحْيَاءٌ وَلَٰكِن لَّا تَشْعُرُونَ (154)
Ndipo musanene za iwo amene aphedwa mu njira ya Mulungu kuti ndi akufa ayi, chifukwa iwo ali ndi moyo koma inu simudziwa
وَلَنَبْلُوَنَّكُم بِشَيْءٍ مِّنَ الْخَوْفِ وَالْجُوعِ وَنَقْصٍ مِّنَ الْأَمْوَالِ وَالْأَنفُسِ وَالثَّمَرَاتِ ۗ وَبَشِّرِ الصَّابِرِينَ (155)
Ndipo, ndithudi, Ife tidzakuyesani ndi mantha ndi njala ndi kuchepetsa chuma chanu, moyo wanu ndi zipatso, koma auzeni nkhani yabwino iwo amene amapirira kwambiri
الَّذِينَ إِذَا أَصَابَتْهُم مُّصِيبَةٌ قَالُوا إِنَّا لِلَّهِ وَإِنَّا إِلَيْهِ رَاجِعُونَ (156)
Amene amati akapeza mavuto, amanena kuti: “Ndithudi! Ambuye wathu ndi Mulungu ndipo ndi kwa Iye kumene tidzabwerera.”
أُولَٰئِكَ عَلَيْهِمْ صَلَوَاتٌ مِّن رَّبِّهِمْ وَرَحْمَةٌ ۖ وَأُولَٰئِكَ هُمُ الْمُهْتَدُونَ (157)
Iwo ndiwo adzalandira madalitso ndi chisoni chochokera kwa Ambuye wawo, ndipo ndiwo amene ali otsogozedwa kwenikweni
۞ إِنَّ الصَّفَا وَالْمَرْوَةَ مِن شَعَائِرِ اللَّهِ ۖ فَمَنْ حَجَّ الْبَيْتَ أَوِ اعْتَمَرَ فَلَا جُنَاحَ عَلَيْهِ أَن يَطَّوَّفَ بِهِمَا ۚ وَمَن تَطَوَّعَ خَيْرًا فَإِنَّ اللَّهَ شَاكِرٌ عَلِيمٌ (158)
Ndithudi! Swafa ndi Marwa ndi zizindikiro za Mulungu kwa amene amabwera kudzachita mapemphero ku Nyumba ya Mulungu. Palibe cholakwa kwa amene achita Hajji kapena Umra ngati azungulira pa malo awiriwa. Ndipo kwa amene achita chabwino mosakakamizidwa, ndithudi, Mulungu ndi wosangalala ndipo ndi wozindikira
إِنَّ الَّذِينَ يَكْتُمُونَ مَا أَنزَلْنَا مِنَ الْبَيِّنَاتِ وَالْهُدَىٰ مِن بَعْدِ مَا بَيَّنَّاهُ لِلنَّاسِ فِي الْكِتَابِ ۙ أُولَٰئِكَ يَلْعَنُهُمُ اللَّهُ وَيَلْعَنُهُمُ اللَّاعِنُونَ (159)
Ndithudi iwo amene amabisa umboni wooneka ndi ulangiziumenetidatumiza Ifetitaululakwaanthuam’Buku, iwo ndiwo otembereredwa ndi Mulungu ndi iwo omwe ali ndi mphamvu yotemberera
إِلَّا الَّذِينَ تَابُوا وَأَصْلَحُوا وَبَيَّنُوا فَأُولَٰئِكَ أَتُوبُ عَلَيْهِمْ ۚ وَأَنَا التَّوَّابُ الرَّحِيمُ (160)
Kupatula okhawo, amene alapa machimo awo ndi kumachita ntchito zabwino ndipo aulula poyera. Awa ndiwo amene ndidzawakhululukira. Ndipo Ine ndine wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
إِنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا وَمَاتُوا وَهُمْ كُفَّارٌ أُولَٰئِكَ عَلَيْهِمْ لَعْنَةُ اللَّهِ وَالْمَلَائِكَةِ وَالنَّاسِ أَجْمَعِينَ (161)
Ndithudi iwo amene sakhulupirira ndipo afa ali osakhulupirira, ndi pa iwo pamene pali temberero la Mulungu, temberero la angelo ndiponso la anthu onse
خَالِدِينَ فِيهَا ۖ لَا يُخَفَّفُ عَنْهُمُ الْعَذَابُ وَلَا هُمْ يُنظَرُونَ (162)
Iwo adzakhalamo mpaka kalekale, ndipo chilango chawo sichidzachepetsedwa ayi ndiponso sadzapatsidwa nthawi yopuma
وَإِلَٰهُكُمْ إِلَٰهٌ وَاحِدٌ ۖ لَّا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ الرَّحْمَٰنُ الرَّحِيمُ (163)
Mulungu wanu ndi Mulungu m’modzi yekha. Kulibenso wina wopembedzedwa muchoonadi koma Iye yekha. Iye ndi Mwini chifundo ndi chisoni chosatha
إِنَّ فِي خَلْقِ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَاخْتِلَافِ اللَّيْلِ وَالنَّهَارِ وَالْفُلْكِ الَّتِي تَجْرِي فِي الْبَحْرِ بِمَا يَنفَعُ النَّاسَ وَمَا أَنزَلَ اللَّهُ مِنَ السَّمَاءِ مِن مَّاءٍ فَأَحْيَا بِهِ الْأَرْضَ بَعْدَ مَوْتِهَا وَبَثَّ فِيهَا مِن كُلِّ دَابَّةٍ وَتَصْرِيفِ الرِّيَاحِ وَالسَّحَابِ الْمُسَخَّرِ بَيْنَ السَّمَاءِ وَالْأَرْضِ لَآيَاتٍ لِّقَوْمٍ يَعْقِلُونَ (164)
Ndithudi! Muchilengedwe chakumwamba ndi dziko lapansi ndiponso mukasinthidwe ka usiku ndi usana, ndi m’zombo zimene zimayenda pa nyanja zitanyamula katundu wothandiza anthu, ndi mvula imene Mulungu amagwetsa kuchokera ku mitambo ndipo imaukitsa nthaka imene idali yakufa, ndi mayendedwe a nyama zosiyanasiyana zimene Iye amazimwanza pa dziko lapansi; ndiponso mphepo ndi mitambo imene imakhala pakati pa kumwamba ndi dziko lapansi, ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro kwa anthu anzeru
وَمِنَ النَّاسِ مَن يَتَّخِذُ مِن دُونِ اللَّهِ أَندَادًا يُحِبُّونَهُمْ كَحُبِّ اللَّهِ ۖ وَالَّذِينَ آمَنُوا أَشَدُّ حُبًّا لِّلَّهِ ۗ وَلَوْ يَرَى الَّذِينَ ظَلَمُوا إِذْ يَرَوْنَ الْعَذَابَ أَنَّ الْقُوَّةَ لِلَّهِ جَمِيعًا وَأَنَّ اللَّهَ شَدِيدُ الْعَذَابِ (165)
Ndipo pakati pawo pali anthu amene amapembedza milungu ina m’malo mwa Mulungu weniweni. Iwo amaikonda iyo monga momwe amkondera Mulungu. Koma iwo amene ali okhulupirira amakhala ndi chikondi chosefukira pa Mulungu. Ngati anthu osakhulupirira akadaona, pamene iwo adzaona chilango chawo akadadziwa kuti Mulungu ndiye mwini mphamvu ndi kuti Mulungu amapereka chilango chowawa
إِذْ تَبَرَّأَ الَّذِينَ اتُّبِعُوا مِنَ الَّذِينَ اتَّبَعُوا وَرَأَوُا الْعَذَابَ وَتَقَطَّعَتْ بِهِمُ الْأَسْبَابُ (166)
Pamene iwo amene anali kutsatiridwa adzawakana iwo amene adali kuwatsatira, ndi kuona chilango, ubale wonse umene unali pakati pawo udzatha
وَقَالَ الَّذِينَ اتَّبَعُوا لَوْ أَنَّ لَنَا كَرَّةً فَنَتَبَرَّأَ مِنْهُمْ كَمَا تَبَرَّءُوا مِنَّا ۗ كَذَٰلِكَ يُرِيهِمُ اللَّهُ أَعْمَالَهُمْ حَسَرَاتٍ عَلَيْهِمْ ۖ وَمَا هُم بِخَارِجِينَ مِنَ النَّارِ (167)
Ndipo iwo amene adali kuwatsatira adzati: “Kukanakhala kuti tikadatha kubwereranso, Ife tikadawakana monga momwe atikanira ife tsopano.” Motero Mulungu adzawaonetsa ntchito zawo kukhala zinthu zopanda pake. Ndipo sipadzakhala njira yothawira ku moto
يَا أَيُّهَا النَّاسُ كُلُوا مِمَّا فِي الْأَرْضِ حَلَالًا طَيِّبًا وَلَا تَتَّبِعُوا خُطُوَاتِ الشَّيْطَانِ ۚ إِنَّهُ لَكُمْ عَدُوٌّ مُّبِينٌ (168)
Oh Inu anthu! Idyani zinthu zabwino zimene mwaloledwa kudya pa dziko lapansi ndipo musatsatire mapazi a Satana chifukwa iye ndi mdani wanu weniweni
إِنَّمَا يَأْمُرُكُم بِالسُّوءِ وَالْفَحْشَاءِ وَأَن تَقُولُوا عَلَى اللَّهِ مَا لَا تَعْلَمُونَ (169)
Iye amakulamulirani kuti muzichita zoipa ndi zonyansa ndi kuti muzinena zokhudza Mulungu zimene inu simuzidziwa
وَإِذَا قِيلَ لَهُمُ اتَّبِعُوا مَا أَنزَلَ اللَّهُ قَالُوا بَلْ نَتَّبِعُ مَا أَلْفَيْنَا عَلَيْهِ آبَاءَنَا ۗ أَوَلَوْ كَانَ آبَاؤُهُمْ لَا يَعْقِلُونَ شَيْئًا وَلَا يَهْتَدُونَ (170)
Ndipo pamene zimanenedwa kwa iwo kuti: Tsatirani zimene Mulungu wavumbulutsa, iwo amayankha: “Iyayi, ife tidzatsatira zimene tidapeza makolo athu ali kuchita.” Ngakhale kuti makolo awo adali osadziwa kapena osowa chilangizo
وَمَثَلُ الَّذِينَ كَفَرُوا كَمَثَلِ الَّذِي يَنْعِقُ بِمَا لَا يَسْمَعُ إِلَّا دُعَاءً وَنِدَاءً ۚ صُمٌّ بُكْمٌ عُمْيٌ فَهُمْ لَا يَعْقِلُونَ (171)
Ndipo fanizo la anthu osakhulupirira lili ngati la iye amene aitana zinthu zimene sizizindikira china chilichonse koma kuitanidwa ndi kulira. Osamva, osalankhula ndi akhungu, iwo sazindikira china chilichonse
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا كُلُوا مِن طَيِّبَاتِ مَا رَزَقْنَاكُمْ وَاشْكُرُوا لِلَّهِ إِن كُنتُمْ إِيَّاهُ تَعْبُدُونَ (172)
Oh inu anthu okhulupirira! Idyani zinthu zabwino zimene takupatsani inu ndipo thokozani Mulungu ngati Iye ndiye amene inu mumampembedza
إِنَّمَا حَرَّمَ عَلَيْكُمُ الْمَيْتَةَ وَالدَّمَ وَلَحْمَ الْخِنزِيرِ وَمَا أُهِلَّ بِهِ لِغَيْرِ اللَّهِ ۖ فَمَنِ اضْطُرَّ غَيْرَ بَاغٍ وَلَا عَادٍ فَلَا إِثْمَ عَلَيْهِ ۚ إِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (173)
Iye wakuletsani kudya nyama yofa yokha, liwende ndi nyama ya nkhumba, ndiponso nyama ina iliyonse imene yaphedwa ngati nsembe m’dzina lina lililonse kupatula dzina la Mulungu. Koma aliyense amene wapanikizidwa kudya zina za izi, osati ndi cholinga choipa kapena kuswa malamulo, iye sali olakwa ayi. Mulungu ndi wokhululukira ndiponso ndi wachisoni
إِنَّ الَّذِينَ يَكْتُمُونَ مَا أَنزَلَ اللَّهُ مِنَ الْكِتَابِ وَيَشْتَرُونَ بِهِ ثَمَنًا قَلِيلًا ۙ أُولَٰئِكَ مَا يَأْكُلُونَ فِي بُطُونِهِمْ إِلَّا النَّارَ وَلَا يُكَلِّمُهُمُ اللَّهُ يَوْمَ الْقِيَامَةِ وَلَا يُزَكِّيهِمْ وَلَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (174)
Ndithudi iwo amene amabisa chivumbulutso cha Mulungu chimene chili m’Buku ndipo amagula phindu lochepa ndi icho, sameza m’mimba mwawo china chilichonse koma moto. Mulungu sadzalankhula nawo pa tsiku louka kwa akufa kapena kuwayeretsa. Chawo chidzakhala chilango chowawa
أُولَٰئِكَ الَّذِينَ اشْتَرَوُا الضَّلَالَةَ بِالْهُدَىٰ وَالْعَذَابَ بِالْمَغْفِرَةِ ۚ فَمَا أَصْبَرَهُمْ عَلَى النَّارِ (175)
Amenewa ndiwo amene agula chinthu choipa pa mtengo wa chilangizo chabwino ndi chilango pa mtengo wa chikhululukiriro. Iwo ndi wodzipereka ku moto
ذَٰلِكَ بِأَنَّ اللَّهَ نَزَّلَ الْكِتَابَ بِالْحَقِّ ۗ وَإِنَّ الَّذِينَ اخْتَلَفُوا فِي الْكِتَابِ لَفِي شِقَاقٍ بَعِيدٍ (176)
Ichi ndi chifukwa chakuti Mulungu adatumiza Buku mwa choonadi. Ndithudi iwo amene amatsutsa zimene zili m’Buku ali kutali ndi chilungamo
۞ لَّيْسَ الْبِرَّ أَن تُوَلُّوا وُجُوهَكُمْ قِبَلَ الْمَشْرِقِ وَالْمَغْرِبِ وَلَٰكِنَّ الْبِرَّ مَنْ آمَنَ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ وَالْمَلَائِكَةِ وَالْكِتَابِ وَالنَّبِيِّينَ وَآتَى الْمَالَ عَلَىٰ حُبِّهِ ذَوِي الْقُرْبَىٰ وَالْيَتَامَىٰ وَالْمَسَاكِينَ وَابْنَ السَّبِيلِ وَالسَّائِلِينَ وَفِي الرِّقَابِ وَأَقَامَ الصَّلَاةَ وَآتَى الزَّكَاةَ وَالْمُوفُونَ بِعَهْدِهِمْ إِذَا عَاهَدُوا ۖ وَالصَّابِرِينَ فِي الْبَأْسَاءِ وَالضَّرَّاءِ وَحِينَ الْبَأْسِ ۗ أُولَٰئِكَ الَّذِينَ صَدَقُوا ۖ وَأُولَٰئِكَ هُمُ الْمُتَّقُونَ (177)
Chilungamo sichili m’machitidwe oti muziyang’ana ku m’mawa kapena ku madzulo, koma chilungamo ndi kukhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza, mwa angelo ndi Buku la Mulungu, mwa Atumwi ndiponso kupereka chuma chimene amachikonda kwa abale ake, kwa a masiye, kwa anthu osauka, kwa a paulendo, kwa anthu opempha ndi kuombola a kapolo. Ndipo onse amene amasamala mapemphero ndipo amapereka msonkho wothandiza anthu osauka ndi amene amakwaniritsa lonjezo lawo akalonjeza ndipo amakhala opirira pa mayesero ndi m’mavuto ndiponso m’nthawi za nkhondo, amenewa ndiwo okhulupirira enieni ndiponso amenewa ndiwo amene amaopa Mulungu
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا كُتِبَ عَلَيْكُمُ الْقِصَاصُ فِي الْقَتْلَى ۖ الْحُرُّ بِالْحُرِّ وَالْعَبْدُ بِالْعَبْدِ وَالْأُنثَىٰ بِالْأُنثَىٰ ۚ فَمَنْ عُفِيَ لَهُ مِنْ أَخِيهِ شَيْءٌ فَاتِّبَاعٌ بِالْمَعْرُوفِ وَأَدَاءٌ إِلَيْهِ بِإِحْسَانٍ ۗ ذَٰلِكَ تَخْفِيفٌ مِّن رَّبِّكُمْ وَرَحْمَةٌ ۗ فَمَنِ اعْتَدَىٰ بَعْدَ ذَٰلِكَ فَلَهُ عَذَابٌ أَلِيمٌ (178)
Oh inu anthu okhulupirira! Kubwezera ndi kololedwa kwa inu pa nkhani zokhudza kukhetsa mwazi. Mfulu kwa mfulu, kapolo kwa kapolo, mkazi kwa mkazi. Aliyense amene akhululukidwa ndi m’bale wa ophedwa chiweruzo chake chikhale choyenera polipira ndipo alipire kwa iwo wofedwa mwaubwino. Umenewu ndi mwambo wachifundo wochokerakwaAmbuyewanu.Aliyenseameneadzalumpha malire pambuyo pake, adzakhala ndi chilango chowawa
وَلَكُمْ فِي الْقِصَاصِ حَيَاةٌ يَا أُولِي الْأَلْبَابِ لَعَلَّكُمْ تَتَّقُونَ (179)
Muli moyo mu kubwezera, Oh inu anthu ozindikira
كُتِبَ عَلَيْكُمْ إِذَا حَضَرَ أَحَدَكُمُ الْمَوْتُ إِن تَرَكَ خَيْرًا الْوَصِيَّةُ لِلْوَالِدَيْنِ وَالْأَقْرَبِينَ بِالْمَعْرُوفِ ۖ حَقًّا عَلَى الْمُتَّقِينَ (180)
Mwalamulidwa kuti ngati imfa idza kwa mmodzi wa inu, ngati iye asiya chuma chake, kuti asiye mawu ofotokoza kagawidwe ka chuma chake mwachilungamo kwa makolo ndi achibale ake. Uwu ndi udindo wokhazikitsidwa kwa anthu olungama
فَمَن بَدَّلَهُ بَعْدَمَا سَمِعَهُ فَإِنَّمَا إِثْمُهُ عَلَى الَّذِينَ يُبَدِّلُونَهُ ۚ إِنَّ اللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (181)
Ndipo yense amene adzasintha mawu osiyidwa ndi munthu wakufa, uchimo udzakhala pa munthu osinthayo. Ndithudi Mulungu ndi Wakumva ndi Wozindikira
فَمَنْ خَافَ مِن مُّوصٍ جَنَفًا أَوْ إِثْمًا فَأَصْلَحَ بَيْنَهُمْ فَلَا إِثْمَ عَلَيْهِ ۚ إِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (182)
Koma iye amene aopa kuti munthu wochitira umboni akhoza kukondera kapena kulakwa ndipo abweretsa chiweruzo chabwino pakati pa anthu otsutsana, iye sali wolakwa pa china chilichonse. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا كُتِبَ عَلَيْكُمُ الصِّيَامُ كَمَا كُتِبَ عَلَى الَّذِينَ مِن قَبْلِكُمْ لَعَلَّكُمْ تَتَّقُونَ (183)
oh inu anthu okhulupirira! Kusala kudalamulidwa kwa inu monga momwe kudalamulidwa kwa iwo amene adalipo kalero inu musanadze kuti inu mukhale woyera
أَيَّامًا مَّعْدُودَاتٍ ۚ فَمَن كَانَ مِنكُم مَّرِيضًا أَوْ عَلَىٰ سَفَرٍ فَعِدَّةٌ مِّنْ أَيَّامٍ أُخَرَ ۚ وَعَلَى الَّذِينَ يُطِيقُونَهُ فِدْيَةٌ طَعَامُ مِسْكِينٍ ۖ فَمَن تَطَوَّعَ خَيْرًا فَهُوَ خَيْرٌ لَّهُ ۚ وَأَن تَصُومُوا خَيْرٌ لَّكُمْ ۖ إِن كُنتُمْ تَعْلَمُونَ (184)
M’masiku owerengeka, koma ngati wina wa inu ndi wodwala kapena ali pa ulendo, awerengere kuti adzasale masiku ena olingana ndi amene sadasale. Ndipo iwo amene sangathe, apereke nsembe yodyetsa munthu wosauka. Koma wina aliyense amene amachita chabwino mwayekha adzalipidwa ndi manja awiri. Koma ngati inu musala chimenecho ndicho chinthu chabwino kwa inu ngati inu mukadadziwa
شَهْرُ رَمَضَانَ الَّذِي أُنزِلَ فِيهِ الْقُرْآنُ هُدًى لِّلنَّاسِ وَبَيِّنَاتٍ مِّنَ الْهُدَىٰ وَالْفُرْقَانِ ۚ فَمَن شَهِدَ مِنكُمُ الشَّهْرَ فَلْيَصُمْهُ ۖ وَمَن كَانَ مَرِيضًا أَوْ عَلَىٰ سَفَرٍ فَعِدَّةٌ مِّنْ أَيَّامٍ أُخَرَ ۗ يُرِيدُ اللَّهُ بِكُمُ الْيُسْرَ وَلَا يُرِيدُ بِكُمُ الْعُسْرَ وَلِتُكْمِلُوا الْعِدَّةَ وَلِتُكَبِّرُوا اللَّهَ عَلَىٰ مَا هَدَاكُمْ وَلَعَلَّكُمْ تَشْكُرُونَ (185)
M’mwezi wa Ramazani ndi mmene Korani idavumbulutsidwa. Iyo ndi ulangizi kwa anthu ndi umboni wooneka wolangiza ndi kusiyanitsa. Motero aliyense wa inu amene wauona mwezi umenewu, ayenera kusala. Koma yense amene ali kudwala kapena ali paulendo, adzasale masiku ofanana ndi amene sadasale. Mulungu akufuna kukupeputsirani zinthu osati kuonjeza masautso ayi. (Iye) afuna kuti mukwaniritse kusala masiku onse olamulidwa ndiponso muyenera kumalemekeza Mulungu chifukwa chokutsogolerani kuti mukhale othokoza
وَإِذَا سَأَلَكَ عِبَادِي عَنِّي فَإِنِّي قَرِيبٌ ۖ أُجِيبُ دَعْوَةَ الدَّاعِ إِذَا دَعَانِ ۖ فَلْيَسْتَجِيبُوا لِي وَلْيُؤْمِنُوا بِي لَعَلَّهُمْ يَرْشُدُونَ (186)
Ndipo pamene akapolo anga akufunsa za Ine, auze kuti: “Ndithudi Ine ndili pafupi ndipo ndimayankha pempho la aliyense akandipempha. Motero andimvere Ine ndi kukhulupirira kuti akhoza kuyenda m’njira yoyenera
أُحِلَّ لَكُمْ لَيْلَةَ الصِّيَامِ الرَّفَثُ إِلَىٰ نِسَائِكُمْ ۚ هُنَّ لِبَاسٌ لَّكُمْ وَأَنتُمْ لِبَاسٌ لَّهُنَّ ۗ عَلِمَ اللَّهُ أَنَّكُمْ كُنتُمْ تَخْتَانُونَ أَنفُسَكُمْ فَتَابَ عَلَيْكُمْ وَعَفَا عَنكُمْ ۖ فَالْآنَ بَاشِرُوهُنَّ وَابْتَغُوا مَا كَتَبَ اللَّهُ لَكُمْ ۚ وَكُلُوا وَاشْرَبُوا حَتَّىٰ يَتَبَيَّنَ لَكُمُ الْخَيْطُ الْأَبْيَضُ مِنَ الْخَيْطِ الْأَسْوَدِ مِنَ الْفَجْرِ ۖ ثُمَّ أَتِمُّوا الصِّيَامَ إِلَى اللَّيْلِ ۚ وَلَا تُبَاشِرُوهُنَّ وَأَنتُمْ عَاكِفُونَ فِي الْمَسَاجِدِ ۗ تِلْكَ حُدُودُ اللَّهِ فَلَا تَقْرَبُوهَا ۗ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ اللَّهُ آيَاتِهِ لِلنَّاسِ لَعَلَّهُمْ يَتَّقُونَ (187)
Ndikololedwa kwa inu kugona ndi akazi anu mu usiku wa kusala. Iwo ndi chofunda chanu pamene nanu ndi chofunda chawo. Mulungu amadziwa kuti munali kudzinyenga nokha pogona nawo opanda chilolezo. Iye adavomera kulapa kwanu ndipo adakukhululukirani. Tsopano mukhoza kugona nawo ndipo funani zimene Mulungu wakulamulirani inu. Idyani ndi kumwa mpaka pamene mukhoza kusiyanitsa pakati pa ulusi woyera ndi wakuda pamene kuli nkucha. Ndipo pitirizani kusala mpaka pamene dzuwa lilowa ndipo musawakhudze akazi anu pamene muli kubindikira m’mapemphero. Amenewa ndi malire a Mulungu ndipo musawayandikire ayi. Motero Mulungu amafotokoza chivumbulutso chake kwa anthu kuti akhale omuopa Iye
وَلَا تَأْكُلُوا أَمْوَالَكُم بَيْنَكُم بِالْبَاطِلِ وَتُدْلُوا بِهَا إِلَى الْحُكَّامِ لِتَأْكُلُوا فَرِيقًا مِّنْ أَمْوَالِ النَّاسِ بِالْإِثْمِ وَأَنتُمْ تَعْلَمُونَ (188)
Musadyerane chuma chanu pakati panu mu njira yosalungama kapena kupereka chiphuphu kwa anthu oweruza ndi cholinga chakuti mudye chuma cha anthu ena mosalungama pamene inu muli nkudziwa
۞ يَسْأَلُونَكَ عَنِ الْأَهِلَّةِ ۖ قُلْ هِيَ مَوَاقِيتُ لِلنَّاسِ وَالْحَجِّ ۗ وَلَيْسَ الْبِرُّ بِأَن تَأْتُوا الْبُيُوتَ مِن ظُهُورِهَا وَلَٰكِنَّ الْبِرَّ مَنِ اتَّقَىٰ ۗ وَأْتُوا الْبُيُوتَ مِنْ أَبْوَابِهَا ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ لَعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ (189)
Iwo akukufunsani za miyezi yatsopano. Nena: “Zimenezi ndi zizindikiro za nyengo kwa anthu ndi nthawi ya Hajji. Ndipo sichilungamo kulowa m’nyumba podzera ku khomo la kumbuyo. Koma chilungamo ndi kuopa Mulungu. Motero lowani m’nyumba zanu kudzera m’makomo oyenera, ndipo opani Mulungu kuti mukhale opambana.”
وَقَاتِلُوا فِي سَبِيلِ اللَّهِ الَّذِينَ يُقَاتِلُونَكُمْ وَلَا تَعْتَدُوا ۚ إِنَّ اللَّهَ لَا يُحِبُّ الْمُعْتَدِينَ (190)
Menyanani nawo mu njira ya Mulungu, iwo amene amenyana nanu koma musapyole malire. Ndithudi Mulungu sakonda anthu oswa malamulo
وَاقْتُلُوهُمْ حَيْثُ ثَقِفْتُمُوهُمْ وَأَخْرِجُوهُم مِّنْ حَيْثُ أَخْرَجُوكُمْ ۚ وَالْفِتْنَةُ أَشَدُّ مِنَ الْقَتْلِ ۚ وَلَا تُقَاتِلُوهُمْ عِندَ الْمَسْجِدِ الْحَرَامِ حَتَّىٰ يُقَاتِلُوكُمْ فِيهِ ۖ فَإِن قَاتَلُوكُمْ فَاقْتُلُوهُمْ ۗ كَذَٰلِكَ جَزَاءُ الْكَافِرِينَ (191)
Ndipo muwaphe paliponse pamene muwapeza, ndipo achotseni m’malo monse m’mene adakuchotsani inu. Kusakhulupilira ndi kupembedza mafano ndi koipa kuposa kupha. Koma musamenyane nawo pa Mzikiti Woyera pokhapokha atakuputani. Koma ngati iwo akuputani, muwaphe. Imeneyo ndiyo mphotho ya anthu amene amakana choonadi
فَإِنِ انتَهَوْا فَإِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (192)
Koma ngati iwo asiya, ndithudi Mulungu ndi okhululuka ndi wachisoni chosatha
وَقَاتِلُوهُمْ حَتَّىٰ لَا تَكُونَ فِتْنَةٌ وَيَكُونَ الدِّينُ لِلَّهِ ۖ فَإِنِ انتَهَوْا فَلَا عُدْوَانَ إِلَّا عَلَى الظَّالِمِينَ (193)
Menyanani nawo mpaka pamene kusakhulupilira ndi kupembedza mafano kutha ndiponso chipembedzo chikhala cha Mulungu yekha. Koma ngati iwo asiya, pasakhale chidani kupatula ndi anthu ochita zoipa
الشَّهْرُ الْحَرَامُ بِالشَّهْرِ الْحَرَامِ وَالْحُرُمَاتُ قِصَاصٌ ۚ فَمَنِ اعْتَدَىٰ عَلَيْكُمْ فَاعْتَدُوا عَلَيْهِ بِمِثْلِ مَا اعْتَدَىٰ عَلَيْكُمْ ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ وَاعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ مَعَ الْمُتَّقِينَ (194)
Mwezi Woyera ndi Mwezi Woyera ndipo zinthu zosaloledwa nazonso zimabwezeredwa. Ndipo aliyense amene akuputani mubwezereni molingana ndi mmene wachitira iye. Ndipo muopeni Mulungu ndipo dziwani kuti Mulungu ali pamodzi ndi iwo amene amalewa zoipa
وَأَنفِقُوا فِي سَبِيلِ اللَّهِ وَلَا تُلْقُوا بِأَيْدِيكُمْ إِلَى التَّهْلُكَةِ ۛ وَأَحْسِنُوا ۛ إِنَّ اللَّهَ يُحِبُّ الْمُحْسِنِينَ (195)
Ndipoperekanim’njiraya Mulungundipomusadziponye nokha kuchionongeko. Chitani zabwino. Ndithudi Mulungu amakonda anthu ochita zabwino
وَأَتِمُّوا الْحَجَّ وَالْعُمْرَةَ لِلَّهِ ۚ فَإِنْ أُحْصِرْتُمْ فَمَا اسْتَيْسَرَ مِنَ الْهَدْيِ ۖ وَلَا تَحْلِقُوا رُءُوسَكُمْ حَتَّىٰ يَبْلُغَ الْهَدْيُ مَحِلَّهُ ۚ فَمَن كَانَ مِنكُم مَّرِيضًا أَوْ بِهِ أَذًى مِّن رَّأْسِهِ فَفِدْيَةٌ مِّن صِيَامٍ أَوْ صَدَقَةٍ أَوْ نُسُكٍ ۚ فَإِذَا أَمِنتُمْ فَمَن تَمَتَّعَ بِالْعُمْرَةِ إِلَى الْحَجِّ فَمَا اسْتَيْسَرَ مِنَ الْهَدْيِ ۚ فَمَن لَّمْ يَجِدْ فَصِيَامُ ثَلَاثَةِ أَيَّامٍ فِي الْحَجِّ وَسَبْعَةٍ إِذَا رَجَعْتُمْ ۗ تِلْكَ عَشَرَةٌ كَامِلَةٌ ۗ ذَٰلِكَ لِمَن لَّمْ يَكُنْ أَهْلُهُ حَاضِرِي الْمَسْجِدِ الْحَرَامِ ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ وَاعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ شَدِيدُ الْعِقَابِ (196)
Kwaniritsani miyambo ya Hajji ndi Umra chifukwa cha Mulungu. Ndipo ngati mwatsekerezedwa, iphani, ngati nsembe, nyama zimene sizili zovuta kuzipeza ndipo musamete mitu yanu mpaka nyama zitafika pa malo ake ophera. Koma aliyense wa inu amene ndi wodwala kapena ali ndi vuto m’mutu mwake ayenera kudziombola posala kapena kupereka nsembe kapena kupha nyama. Ngati muli pa mtendere ndiponso wina wa inu aphatikiza Umra ndi Hajji, ayenera kupha nyama imene angaipeze mosavutikira kwambiri. Koma ngati sangathe kuipeza ayenera kusala masiku atatu pa nthawi ya Hajji ndi masiku asanu ndi awiri akabwerera kwawo; amenewo ndi masiku khumi okwana. Zimenezi ndi za iye amene banja lake silili pafupi ndi Mzikiti Woyera. Muopeni Mulungu. Ndipo dziwani kuti Mulungu amakhwimitsa chilango
الْحَجُّ أَشْهُرٌ مَّعْلُومَاتٌ ۚ فَمَن فَرَضَ فِيهِنَّ الْحَجَّ فَلَا رَفَثَ وَلَا فُسُوقَ وَلَا جِدَالَ فِي الْحَجِّ ۗ وَمَا تَفْعَلُوا مِنْ خَيْرٍ يَعْلَمْهُ اللَّهُ ۗ وَتَزَوَّدُوا فَإِنَّ خَيْرَ الزَّادِ التَّقْوَىٰ ۚ وَاتَّقُونِ يَا أُولِي الْأَلْبَابِ (197)
Nthawi ya Hajji ili ndi miyezi yake yodziwika. Aliyense amene afuna kupanga Hajji m’menemu sayenera kugona ndi mkazi wake kapena kuchitazoipakapenakukanganandianzakenthawiya Hajji. Ndipo chabwino chilichonse chimene muchita, Mulungu amachidziwa. Mutenge kamba wa paulendo, koma kamba wabwino ndi kuopa Mulungu. Motero ndiopeni Ine, inu anthu ozindikira
لَيْسَ عَلَيْكُمْ جُنَاحٌ أَن تَبْتَغُوا فَضْلًا مِّن رَّبِّكُمْ ۚ فَإِذَا أَفَضْتُم مِّنْ عَرَفَاتٍ فَاذْكُرُوا اللَّهَ عِندَ الْمَشْعَرِ الْحَرَامِ ۖ وَاذْكُرُوهُ كَمَا هَدَاكُمْ وَإِن كُنتُم مِّن قَبْلِهِ لَمِنَ الضَّالِّينَ (198)
Palibe mlandu kwa inu ngati inu mufuna zabwino kuchokera kwa Ambuye wanu. Motero pamene muchoka ku Arafat, kumbukirani Mulungu pafupi ndi chizindikiro choyera. Ndipo mukumbukeni Iye chifukwa Iye wakutsogolerani, popeza kale ndithudi inu mudali wa iwo amene adasokera
ثُمَّ أَفِيضُوا مِنْ حَيْثُ أَفَاضَ النَّاسُ وَاسْتَغْفِرُوا اللَّهَ ۚ إِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (199)
Ndipo pitani kumalo kumene anthu onse amapitako ndipo pemphani chikhululukiro cha Mulungu. Ndithudi Iye ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha
فَإِذَا قَضَيْتُم مَّنَاسِكَكُمْ فَاذْكُرُوا اللَّهَ كَذِكْرِكُمْ آبَاءَكُمْ أَوْ أَشَدَّ ذِكْرًا ۗ فَمِنَ النَّاسِ مَن يَقُولُ رَبَّنَا آتِنَا فِي الدُّنْيَا وَمَا لَهُ فِي الْآخِرَةِ مِنْ خَلَاقٍ (200)
Ndipo pamene inu mukwaniritsa mapemphero anu a Hajji, kumbukirani Mulungu monga momwe mumakumbukira makolo anu kapena kuposa pamenepo. Ndipo pakati pawo pali iye amene amanena kuti: “Ambuye wathu! Tipatseni zabwino m’dziko lapansi!” Ndipo munthu wotere sadzakhala ndi gawo m’moyo umene uli nkudza
وَمِنْهُم مَّن يَقُولُ رَبَّنَا آتِنَا فِي الدُّنْيَا حَسَنَةً وَفِي الْآخِرَةِ حَسَنَةً وَقِنَا عَذَابَ النَّارِ (201)
Ndipo pakati pawo alipo wina wa iwo amene amati: “Ambuye wathu! Tipatseni zabwino m’dziko lino ndiponso zabwino m’dziko limene lili nkudza ndipo titetezeni ku chilango cha moto.”
أُولَٰئِكَ لَهُمْ نَصِيبٌ مِّمَّا كَسَبُوا ۚ وَاللَّهُ سَرِيعُ الْحِسَابِ (202)
Iwo adzakhala ndi gawo chifukwa cha ntchito zomwe amachita. Mulungu ndi wachangu powerengera
۞ وَاذْكُرُوا اللَّهَ فِي أَيَّامٍ مَّعْدُودَاتٍ ۚ فَمَن تَعَجَّلَ فِي يَوْمَيْنِ فَلَا إِثْمَ عَلَيْهِ وَمَن تَأَخَّرَ فَلَا إِثْمَ عَلَيْهِ ۚ لِمَنِ اتَّقَىٰ ۗ وَاتَّقُوا اللَّهَ وَاعْلَمُوا أَنَّكُمْ إِلَيْهِ تُحْشَرُونَ (203)
Ndipo kumbukira Mulungu m’masiku owerengeka. Koma iye amene afulumira kuchoka pa masiku awiri salakwa ayi ndiponso naye amene amachedwerapo salakwa ayi ngati cholinga chake ndi kuchita zabwino ndi kumvera Mulungu. Ndipo dziwani kuti nonse, ndithudi, mudzasonkhanitsidwa kunka kwa Iye
وَمِنَ النَّاسِ مَن يُعْجِبُكَ قَوْلُهُ فِي الْحَيَاةِ الدُّنْيَا وَيُشْهِدُ اللَّهَ عَلَىٰ مَا فِي قَلْبِهِ وَهُوَ أَلَدُّ الْخِصَامِ (204)
Pakati pa anthu pali wina amene zolankhula zake zokhudza moyo uno zimakukondweretsa ndipo iye amaitana Mulungu kuti achitire umboni pa zimene zili mumtima mwake pamene iye ndiye wolongolola pa gulu la adani onse
وَإِذَا تَوَلَّىٰ سَعَىٰ فِي الْأَرْضِ لِيُفْسِدَ فِيهَا وَيُهْلِكَ الْحَرْثَ وَالنَّسْلَ ۗ وَاللَّهُ لَا يُحِبُّ الْفَسَادَ (205)
Ndipo pamene iye achoka, amapita uku ndi uku kuyambitsa chisokonezo m’dziko ndi kuononga mbeu ndi ng’ombe ndipo Mulungu sakonda chisokonezo
وَإِذَا قِيلَ لَهُ اتَّقِ اللَّهَ أَخَذَتْهُ الْعِزَّةُ بِالْإِثْمِ ۚ فَحَسْبُهُ جَهَنَّمُ ۚ وَلَبِئْسَ الْمِهَادُ (206)
Ndipo zikanenedwa kwa iye kuti: “Opa Mulungu,” kudzitukumula kwake kumamupangitsa kuchita zoipa. Motero Gahena ndi yomuyenera. Ndipo ndi malo oipa kupumirako
وَمِنَ النَّاسِ مَن يَشْرِي نَفْسَهُ ابْتِغَاءَ مَرْضَاتِ اللَّهِ ۗ وَاللَّهُ رَءُوفٌ بِالْعِبَادِ (207)
Ndipo pakati pawo pali munthu amene amadzipereka ndi cholinga chofuna chisangalalo cha Mulungu. Ndipo Mulungu ndi odzadza ndi chifundo kwa akapolo ake
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا ادْخُلُوا فِي السِّلْمِ كَافَّةً وَلَا تَتَّبِعُوا خُطُوَاتِ الشَّيْطَانِ ۚ إِنَّهُ لَكُمْ عَدُوٌّ مُّبِينٌ (208)
oh Inu anthu okhulupirira! Lowani Chisilamu ndi mtima wanu wonse ndipo musayende m’mapazi a Satana. Ndithudi iye ndiye mdani wanu weniweni
فَإِن زَلَلْتُم مِّن بَعْدِ مَا جَاءَتْكُمُ الْبَيِّنَاتُ فَاعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ عَزِيزٌ حَكِيمٌ (209)
Ndipo ngati inu muterera ndi kubwerera m’mbuyo pamene zizindikiro zadza kwa inu, dziwani kuti Mulungu ndi wa Mphamvu ndi Wanzeru
هَلْ يَنظُرُونَ إِلَّا أَن يَأْتِيَهُمُ اللَّهُ فِي ظُلَلٍ مِّنَ الْغَمَامِ وَالْمَلَائِكَةُ وَقُضِيَ الْأَمْرُ ۚ وَإِلَى اللَّهِ تُرْجَعُ الْأُمُورُ (210)
Kodi iwo ali kudikira china chake kupatula kuti Mulungu awabwerere mu mthunzi wa mitambo pamodzi ndi angelo pa zomwe zatsimikizidwa ndipo zonse zimabwezedwa kwa Mulungu
سَلْ بَنِي إِسْرَائِيلَ كَمْ آتَيْنَاهُم مِّنْ آيَةٍ بَيِّنَةٍ ۗ وَمَن يُبَدِّلْ نِعْمَةَ اللَّهِ مِن بَعْدِ مَا جَاءَتْهُ فَإِنَّ اللَّهَ شَدِيدُ الْعِقَابِ (211)
Afunse ana a Israeli kuti kodi ndi zizindikiro zingati zooneka zimene tidawapatsa? Ndipo aliyense amene asintha madalitso a Mulungu atawalandira, ndithudi, Mulungu ndi wokhwimitsa chilango
زُيِّنَ لِلَّذِينَ كَفَرُوا الْحَيَاةُ الدُّنْيَا وَيَسْخَرُونَ مِنَ الَّذِينَ آمَنُوا ۘ وَالَّذِينَ اتَّقَوْا فَوْقَهُمْ يَوْمَ الْقِيَامَةِ ۗ وَاللَّهُ يَرْزُقُ مَن يَشَاءُ بِغَيْرِ حِسَابٍ (212)
Moyo wa pa dziko lino lapansi ndi wosangalatsa kwa anthu osakhulupirira ndipo iwo amanyogodola anthu okhulupirira. Koma iwo amene amamvera malamulo a Mulungu ndipo amalewa zoipa adzakhala wopambana pa tsiku la kuuka kwa akufa. Mulungu amapereka mopanda muyeso kwa aliyense amene Iye wamufuna
كَانَ النَّاسُ أُمَّةً وَاحِدَةً فَبَعَثَ اللَّهُ النَّبِيِّينَ مُبَشِّرِينَ وَمُنذِرِينَ وَأَنزَلَ مَعَهُمُ الْكِتَابَ بِالْحَقِّ لِيَحْكُمَ بَيْنَ النَّاسِ فِيمَا اخْتَلَفُوا فِيهِ ۚ وَمَا اخْتَلَفَ فِيهِ إِلَّا الَّذِينَ أُوتُوهُ مِن بَعْدِ مَا جَاءَتْهُمُ الْبَيِّنَاتُ بَغْيًا بَيْنَهُمْ ۖ فَهَدَى اللَّهُ الَّذِينَ آمَنُوا لِمَا اخْتَلَفُوا فِيهِ مِنَ الْحَقِّ بِإِذْنِهِ ۗ وَاللَّهُ يَهْدِي مَن يَشَاءُ إِلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (213)
Anthu onse anali mtundu umodzi ndipo Mulungu adatumiza Atumwi kudzawauza nkhani yabwino ndi kuwachenjeza ndipo ndi iwo adatumiza mau ake mwa choonadi kuti aweruze pa mikangano imene ili pakati pawo. Ndipo okhawo amene adaperekedwa amatsutsa za ilo iwo atalandira zizindikiro zooneka chifukwa cha udani wa wina ndi mzake. Ndipo Mulungu analangiza mwa chifuniro chake iwo amene amakhulupirira m’choonadi chimene chinali kutsutsidwa. Ndipo Mulungu amatsogolera wina aliyense amene wamufuna ku njira yoyenera
أَمْ حَسِبْتُمْ أَن تَدْخُلُوا الْجَنَّةَ وَلَمَّا يَأْتِكُم مَّثَلُ الَّذِينَ خَلَوْا مِن قَبْلِكُم ۖ مَّسَّتْهُمُ الْبَأْسَاءُ وَالضَّرَّاءُ وَزُلْزِلُوا حَتَّىٰ يَقُولَ الرَّسُولُ وَالَّذِينَ آمَنُوا مَعَهُ مَتَىٰ نَصْرُ اللَّهِ ۗ أَلَا إِنَّ نَصْرَ اللَّهِ قَرِيبٌ (214)
Kapena inu mumaganiza kuti mukalowa ku Paradiso popanda kuyesedwa monga momwe anthu amene analipo kale anaona? Iwo anapeza mavuto ndi masautso ochuluka ndipo anada nkhawa moti Mtumwi pamodzi ndi iwo amene adakhulupirira ndi iye adati: “Kodi chithandizo cha Mulungu chidzadza liti? Inde! Ndithudi, chithandizo cha Mulungu tsopano chili pafupi.”
يَسْأَلُونَكَ مَاذَا يُنفِقُونَ ۖ قُلْ مَا أَنفَقْتُم مِّنْ خَيْرٍ فَلِلْوَالِدَيْنِ وَالْأَقْرَبِينَ وَالْيَتَامَىٰ وَالْمَسَاكِينِ وَابْنِ السَّبِيلِ ۗ وَمَا تَفْعَلُوا مِنْ خَيْرٍ فَإِنَّ اللَّهَ بِهِ عَلِيمٌ (215)
Iwo akukufunsa iwe kuti apeleke chiani. Nena: “Chilichonse chabwino chimene mupeleka chiyenera kuperekedwa kwa makolo anu ndi kwa abale anu, kwa ana a masiye, ndi kwa anthu osauka ndi alendo. Ndipo zabwino zilizonse zimene muchita, ndithudi Mulungu amazidziwa.”
كُتِبَ عَلَيْكُمُ الْقِتَالُ وَهُوَ كُرْهٌ لَّكُمْ ۖ وَعَسَىٰ أَن تَكْرَهُوا شَيْئًا وَهُوَ خَيْرٌ لَّكُمْ ۖ وَعَسَىٰ أَن تُحِبُّوا شَيْئًا وَهُوَ شَرٌّ لَّكُمْ ۗ وَاللَّهُ يَعْلَمُ وَأَنتُمْ لَا تَعْلَمُونَ (216)
Nkhondo yalamulidwa kwa inu ngakhale inu simuikonda ndipo mwina inu mukhoza kudana ndi chinthu chimene chili chabwino kwa inu ndipo kuti inu mumakonda chinthu chimene chili choipa kwa inu. Mulungu amadziwa koma inu simudziwa
يَسْأَلُونَكَ عَنِ الشَّهْرِ الْحَرَامِ قِتَالٍ فِيهِ ۖ قُلْ قِتَالٌ فِيهِ كَبِيرٌ ۖ وَصَدٌّ عَن سَبِيلِ اللَّهِ وَكُفْرٌ بِهِ وَالْمَسْجِدِ الْحَرَامِ وَإِخْرَاجُ أَهْلِهِ مِنْهُ أَكْبَرُ عِندَ اللَّهِ ۚ وَالْفِتْنَةُ أَكْبَرُ مِنَ الْقَتْلِ ۗ وَلَا يَزَالُونَ يُقَاتِلُونَكُمْ حَتَّىٰ يَرُدُّوكُمْ عَن دِينِكُمْ إِنِ اسْتَطَاعُوا ۚ وَمَن يَرْتَدِدْ مِنكُمْ عَن دِينِهِ فَيَمُتْ وَهُوَ كَافِرٌ فَأُولَٰئِكَ حَبِطَتْ أَعْمَالُهُمْ فِي الدُّنْيَا وَالْآخِرَةِ ۖ وَأُولَٰئِكَ أَصْحَابُ النَّارِ ۖ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (217)
Iwo akukufunsa zomenya nkhondo M’mwezi Woyera. Nena: “Kumenya nkhondo m’mwezi uwu ndi kulakwa kwakukulu koma kulakwa kwakukulu zedi pamaso pa Mulungu ndi kutsekereza anthu kuti atsatire njira ya Mulungu, kumukana Iye ndi kuletsa anthu kulowa mu Mzikiti Woyera ndi kupirikitsa anthu ake opembedza m’menemo. Ndipo kuchita zinthu zosokoneza chipembedzo ndi koipa kwambiri kuposa kupha munthu.” Ndipo iwo sadzasiya kumenyana nanu mpaka atakuchotsani mchipembedzo chanu ngati angathe kutero. Ndipo aliyense wa inu amene adzasiye chipembedzo chake chenicheni ndipo afa ali osakhulupirira, ntchito zake zonse zidzakhala zopanda pake m’dziko lino ndiponso m’dziko limene lili nkudza. Anthu otere adzakhala eni ake a ku Gahena ndipo kumeneko adzakhalako mpaka kalekale
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَالَّذِينَ هَاجَرُوا وَجَاهَدُوا فِي سَبِيلِ اللَّهِ أُولَٰئِكَ يَرْجُونَ رَحْمَتَ اللَّهِ ۚ وَاللَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (218)
Ndithudi iwo amene akhulupirira ndi iwo amene adasamuka ndi kumenya nkhondo mnjira ya Mulungu, onsewa ali ndi chiyembekezo chachifundo cha Mulungu. Ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
۞ يَسْأَلُونَكَ عَنِ الْخَمْرِ وَالْمَيْسِرِ ۖ قُلْ فِيهِمَا إِثْمٌ كَبِيرٌ وَمَنَافِعُ لِلنَّاسِ وَإِثْمُهُمَا أَكْبَرُ مِن نَّفْعِهِمَا ۗ وَيَسْأَلُونَكَ مَاذَا يُنفِقُونَ قُلِ الْعَفْوَ ۗ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ اللَّهُ لَكُمُ الْآيَاتِ لَعَلَّكُمْ تَتَفَكَّرُونَ (219)
Iwoakukufunsazamowandimaseweraamwayi. Nena: “Mu zonsezi muli zoipa zambiri ndi zabwino kwa anthu ena. Koma zoipa zake ndi zambiri kuposa zabwino.” Ndipo akukufunsa chimene angapereke. Nena: “Chilichonse chimene ndi chapadera. Mmenemo Mulungu akulangizira poyera chivumbulutso chake kuti inu mukhoza kuganizira bwino.”
فِي الدُّنْيَا وَالْآخِرَةِ ۗ وَيَسْأَلُونَكَ عَنِ الْيَتَامَىٰ ۖ قُلْ إِصْلَاحٌ لَّهُمْ خَيْرٌ ۖ وَإِن تُخَالِطُوهُمْ فَإِخْوَانُكُمْ ۚ وَاللَّهُ يَعْلَمُ الْمُفْسِدَ مِنَ الْمُصْلِحِ ۚ وَلَوْ شَاءَ اللَّهُ لَأَعْنَتَكُمْ ۚ إِنَّ اللَّهَ عَزِيزٌ حَكِيمٌ (220)
Mu za m’moyo wa m’dziko lino ndi m’moyo umene uli nkudza. Ndipo iwo akukufunsa za ana amasiye. Nena: Kuchita chilungamo kwa iwo ndi kwabwino ndipo ngati inu mukhalira pamodzi ndiye kuti, iwo ndi abale anu. Ndipo Mulungu amadziwa amene amachita zoipa ndi amene amachita zabwino, ndipo ngati Mulungu akadafuna akadakupatsani mavuto; Ndithudi Mulungu ndi wamphamvu ndi Wanzeru
وَلَا تَنكِحُوا الْمُشْرِكَاتِ حَتَّىٰ يُؤْمِنَّ ۚ وَلَأَمَةٌ مُّؤْمِنَةٌ خَيْرٌ مِّن مُّشْرِكَةٍ وَلَوْ أَعْجَبَتْكُمْ ۗ وَلَا تُنكِحُوا الْمُشْرِكِينَ حَتَّىٰ يُؤْمِنُوا ۚ وَلَعَبْدٌ مُّؤْمِنٌ خَيْرٌ مِّن مُّشْرِكٍ وَلَوْ أَعْجَبَكُمْ ۗ أُولَٰئِكَ يَدْعُونَ إِلَى النَّارِ ۖ وَاللَّهُ يَدْعُو إِلَى الْجَنَّةِ وَالْمَغْفِرَةِ بِإِذْنِهِ ۖ وَيُبَيِّنُ آيَاتِهِ لِلنَّاسِ لَعَلَّهُمْ يَتَذَكَّرُونَ (221)
Musakwatire akazi opembedza mafano mpaka atakhulupirira. Ndipo, ndithudi, kapolo wachikazi wokhulupirira ali bwino kuposa mfulu yaikazi yopembedza mafano ngakhale atakukondweretsani. Ndiponso musadzakwatitse aliyense wopembedza mafano mpaka atakhulupirira. Ndithudi kapolo wokhulupirira ali bwino kuposa mfulu yopembedza mafano ngakhale kuti iye wakusangalatsani. Iwo amakuitanirani ku moto pamene Mulungu amakuitanirani ku Paradiso ndi ku chikhululukiro mwachifuniro chake, ndipo Iye amafotokoza bwino bwino chivumbulutso chake kwa anthu kuti mwina akhoza kukumbukira
وَيَسْأَلُونَكَ عَنِ الْمَحِيضِ ۖ قُلْ هُوَ أَذًى فَاعْتَزِلُوا النِّسَاءَ فِي الْمَحِيضِ ۖ وَلَا تَقْرَبُوهُنَّ حَتَّىٰ يَطْهُرْنَ ۖ فَإِذَا تَطَهَّرْنَ فَأْتُوهُنَّ مِنْ حَيْثُ أَمَرَكُمُ اللَّهُ ۚ إِنَّ اللَّهَ يُحِبُّ التَّوَّابِينَ وَيُحِبُّ الْمُتَطَهِّرِينَ (222)
Ndipo iwo akukufunsa za msambo. Nena: “Uwu ndi umve. Motero aleweni akazi panthawi ya msambo ndipo musawakhudze mpaka atayeretsedwa. Ndipo akayeretsedwa, mukhoza kukhala nawo malo amodzi monga momwe Mulungu adakulamulirani. Ndithudi Mulungu amakonda iwo amene amadza ndi kulapa kwa Iye. Ndipo Iye amakonda iwo wodziyeretsa.”
نِسَاؤُكُمْ حَرْثٌ لَّكُمْ فَأْتُوا حَرْثَكُمْ أَنَّىٰ شِئْتُمْ ۖ وَقَدِّمُوا لِأَنفُسِكُمْ ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ وَاعْلَمُوا أَنَّكُم مُّلَاقُوهُ ۗ وَبَشِّرِ الْمُؤْمِنِينَ (223)
Akazi anu ndi minda yanu kotero lowani m’minda yanu monga momwe mufunira, dzitsogozereni nokha ntchito zabwino. Ndipo muopeni Mulungu, ndipo dziwani kuti mudzakumana naye. Ndipo pelekani nkhani yabwino kwa anthu okhulupirira
وَلَا تَجْعَلُوا اللَّهَ عُرْضَةً لِّأَيْمَانِكُمْ أَن تَبَرُّوا وَتَتَّقُوا وَتُصْلِحُوا بَيْنَ النَّاسِ ۗ وَاللَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (224)
Musalipange dzina la Mulungu kukhala chida chonamizira wina ndi mzake pa malonjezo anu polumbira ndi kusiya kuchita zabwino ndi kuopa kukhazikitsa mtendere pakati pa anthu. Mulungu amamva ndipo amadziwa
لَّا يُؤَاخِذُكُمُ اللَّهُ بِاللَّغْوِ فِي أَيْمَانِكُمْ وَلَٰكِن يُؤَاخِذُكُم بِمَا كَسَبَتْ قُلُوبُكُمْ ۗ وَاللَّهُ غَفُورٌ حَلِيمٌ (225)
Mulungu sadzakulangani chifukwa cha kuphwanya mwangozi malonjezo anu amene mudachita. Koma adzakulangani pa zinthu zimene mitima yanu yachita ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi wopirira kwambiri
لِّلَّذِينَ يُؤْلُونَ مِن نِّسَائِهِمْ تَرَبُّصُ أَرْبَعَةِ أَشْهُرٍ ۖ فَإِن فَاءُوا فَإِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (226)
Iwo amene amalumbira kuti sadzakhala malo amodzi ndi akazi awo adikire miyezi inayi, ndipo ngati iwo abwererana, ndithudi, Mulungu ndi wokhululukira ndi wachifundo chosatha
وَإِنْ عَزَمُوا الطَّلَاقَ فَإِنَّ اللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (227)
Ndipo ngati atsimikiza zowasudzula, pamenepo Mulungu amamva ndipo amadziwa zonse
وَالْمُطَلَّقَاتُ يَتَرَبَّصْنَ بِأَنفُسِهِنَّ ثَلَاثَةَ قُرُوءٍ ۚ وَلَا يَحِلُّ لَهُنَّ أَن يَكْتُمْنَ مَا خَلَقَ اللَّهُ فِي أَرْحَامِهِنَّ إِن كُنَّ يُؤْمِنَّ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ ۚ وَبُعُولَتُهُنَّ أَحَقُّ بِرَدِّهِنَّ فِي ذَٰلِكَ إِنْ أَرَادُوا إِصْلَاحًا ۚ وَلَهُنَّ مِثْلُ الَّذِي عَلَيْهِنَّ بِالْمَعْرُوفِ ۚ وَلِلرِّجَالِ عَلَيْهِنَّ دَرَجَةٌ ۗ وَاللَّهُ عَزِيزٌ حَكِيمٌ (228)
Ndipo akazi osudzulidwa asakwatiwe mpaka atasamba miyezi itatu. Ndipo ndikosaloledwa kwa iwo, kubisa zimene Mulungu walenga m’mimba mwawo ngati iwo amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza. Ndipo amuna awo akhoza kuwatenganso ngati iwo atafuna kuyanjana: Ndipo akazi adzakhala ndi mwayi wolingana ndi umene uli ndi amuna koma amuna ndi a udindo kuposa akazi. Mulungu ndi Wamphamvu ndi Wanzeru
الطَّلَاقُ مَرَّتَانِ ۖ فَإِمْسَاكٌ بِمَعْرُوفٍ أَوْ تَسْرِيحٌ بِإِحْسَانٍ ۗ وَلَا يَحِلُّ لَكُمْ أَن تَأْخُذُوا مِمَّا آتَيْتُمُوهُنَّ شَيْئًا إِلَّا أَن يَخَافَا أَلَّا يُقِيمَا حُدُودَ اللَّهِ ۖ فَإِنْ خِفْتُمْ أَلَّا يُقِيمَا حُدُودَ اللَّهِ فَلَا جُنَاحَ عَلَيْهِمَا فِيمَا افْتَدَتْ بِهِ ۗ تِلْكَ حُدُودُ اللَّهِ فَلَا تَعْتَدُوهَا ۚ وَمَن يَتَعَدَّ حُدُودَ اللَّهِ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الظَّالِمُونَ (229)
Chisudzulo ndi chololedwa kawiri kokha ndipo pambuyopake,mukhozakukhalanayelimodzimogwirizana kapena kusiyana mwaulemu. Ndi choletsedwa kwa inu amuna kutenga katundu wina aliyense amene mudawapatsa akazi anu pokhapokha ngati onse awiri aopa kuti sadzatha kukwaniritsa malamulo a Mulungu. Ndipo ngati inu muopa kuti iwo sadzakwaniritsa malamulo a Mulungu, palibe mlandu kwa iwo ngati mkazi apereka mphatso kapena gawo lake ngati chodziombolera. Awa ndi malamulo a Mulungu ndipo musawaswe. Ndipo aliyense amene aswa malamulo amene anakhazikitsa Mulungu, wotere ndiwo olakwa
فَإِن طَلَّقَهَا فَلَا تَحِلُّ لَهُ مِن بَعْدُ حَتَّىٰ تَنكِحَ زَوْجًا غَيْرَهُ ۗ فَإِن طَلَّقَهَا فَلَا جُنَاحَ عَلَيْهِمَا أَن يَتَرَاجَعَا إِن ظَنَّا أَن يُقِيمَا حُدُودَ اللَّهِ ۗ وَتِلْكَ حُدُودُ اللَّهِ يُبَيِّنُهَا لِقَوْمٍ يَعْلَمُونَ (230)
Ngati munthu asudzula mkazi wake kachitatu, iye saloledwa kumukwatiranso pokhapokha ngati atakwatiwa ndi mwamuna wina ndipo mwamunayo amusudzulanso. Sicholakwa kwa iwo kubwererana, ngati iwo atsimikiza kuti adzasunga malamulo a Mulungu. Amenewa ndi malamulo a Mulungu amene akuwaonetsa poyera kwa anthu ozindikira
وَإِذَا طَلَّقْتُمُ النِّسَاءَ فَبَلَغْنَ أَجَلَهُنَّ فَأَمْسِكُوهُنَّ بِمَعْرُوفٍ أَوْ سَرِّحُوهُنَّ بِمَعْرُوفٍ ۚ وَلَا تُمْسِكُوهُنَّ ضِرَارًا لِّتَعْتَدُوا ۚ وَمَن يَفْعَلْ ذَٰلِكَ فَقَدْ ظَلَمَ نَفْسَهُ ۚ وَلَا تَتَّخِذُوا آيَاتِ اللَّهِ هُزُوًا ۚ وَاذْكُرُوا نِعْمَتَ اللَّهِ عَلَيْكُمْ وَمَا أَنزَلَ عَلَيْكُم مِّنَ الْكِتَابِ وَالْحِكْمَةِ يَعِظُكُم بِهِ ۚ وَاتَّقُوا اللَّهَ وَاعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (231)
Ndipo pamene musudzula akazi ndipo iwo akwanitsa nthawi yawo yodikira, asungeni mwaubwino kapena alekeni mwa mtendere. Koma musawasunge ndi cholinga chowazunza. Ndipo aliyense amene achita ichi, ndithudi adzilakwira yekha. Ndipo musachite chipongwe Mau a Mulungu koma kumbukirani madalitso a Mulungu kwa inu ndi zimene Iye watumiza m’Buku ndi luntha limene Iye akulangizani inu. Muopeni Mulungu ndipo dziwani kuti Mulungu amadziwa chilichonse
وَإِذَا طَلَّقْتُمُ النِّسَاءَ فَبَلَغْنَ أَجَلَهُنَّ فَلَا تَعْضُلُوهُنَّ أَن يَنكِحْنَ أَزْوَاجَهُنَّ إِذَا تَرَاضَوْا بَيْنَهُم بِالْمَعْرُوفِ ۗ ذَٰلِكَ يُوعَظُ بِهِ مَن كَانَ مِنكُمْ يُؤْمِنُ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ ۗ ذَٰلِكُمْ أَزْكَىٰ لَكُمْ وَأَطْهَرُ ۗ وَاللَّهُ يَعْلَمُ وَأَنتُمْ لَا تَعْلَمُونَ (232)
Ndipo ngati inu musudzula akazi ndipo iwo akwanitsa nthawi yawo yodikira, musawaletse kukwatiwa ndi amuna awo akale ngati agwirizana pakati pawo mwaubwino. Ili ndi lonjezo kwa aliyense amene ali pakati panu amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza. Zimenezo ndi zabwino ndi zoyenera kwa inu. Mulungu ndiye amene amadziwa zonse koma inu simudziwa
۞ وَالْوَالِدَاتُ يُرْضِعْنَ أَوْلَادَهُنَّ حَوْلَيْنِ كَامِلَيْنِ ۖ لِمَنْ أَرَادَ أَن يُتِمَّ الرَّضَاعَةَ ۚ وَعَلَى الْمَوْلُودِ لَهُ رِزْقُهُنَّ وَكِسْوَتُهُنَّ بِالْمَعْرُوفِ ۚ لَا تُكَلَّفُ نَفْسٌ إِلَّا وُسْعَهَا ۚ لَا تُضَارَّ وَالِدَةٌ بِوَلَدِهَا وَلَا مَوْلُودٌ لَّهُ بِوَلَدِهِ ۚ وَعَلَى الْوَارِثِ مِثْلُ ذَٰلِكَ ۗ فَإِنْ أَرَادَا فِصَالًا عَن تَرَاضٍ مِّنْهُمَا وَتَشَاوُرٍ فَلَا جُنَاحَ عَلَيْهِمَا ۗ وَإِنْ أَرَدتُّمْ أَن تَسْتَرْضِعُوا أَوْلَادَكُمْ فَلَا جُنَاحَ عَلَيْكُمْ إِذَا سَلَّمْتُم مَّا آتَيْتُم بِالْمَعْرُوفِ ۗ وَاتَّقُوا اللَّهَ وَاعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (233)
Amayi adzayamwitsa ana awo zaka ziwiri zathunthu, izi ndi za makolo amene afuna kukwaniritsa kuyamwitsa. Koma ndi udindo wa atate kupereka chakudya ndi zovala za amai potsatira malamulo. Munthu sadzanyamula chinthu chimene sangathe kuchichita. Mayi asazunzidwe chifukwa cha mwana wake kapena bambo asavutitsidwe chifukwa cha mwana wake. Udindo umenewu umagweranso aliyense amene alowa chokolo. Koma ngati onse agwirizana kuti amuletse kuyamwa mwana, iwo sadzakhala ndi mlandu. Ngati inu muganiza kuti wina akuyamwitsireni mwana wanu, sikulakwa ngati inu mumulipira mtengo umene mwagwirizana. Ndipo opani Mulungu, ndipo dziwani kuti Mulungu amaona zimene muchita
وَالَّذِينَ يُتَوَفَّوْنَ مِنكُمْ وَيَذَرُونَ أَزْوَاجًا يَتَرَبَّصْنَ بِأَنفُسِهِنَّ أَرْبَعَةَ أَشْهُرٍ وَعَشْرًا ۖ فَإِذَا بَلَغْنَ أَجَلَهُنَّ فَلَا جُنَاحَ عَلَيْكُمْ فِيمَا فَعَلْنَ فِي أَنفُسِهِنَّ بِالْمَعْرُوفِ ۗ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرٌ (234)
Ndipo iwo amene akufa ndi kusiya akazi, akaziwo ayenera kudikira, osakwatiwa miyezi inayi ndi masiku khumi, ndipo iwo akakwaniritsa nthawi iyi, inu simudzakhala ndi mlandu pa zimene iwo achita molingana ndi malamulo. Ndipo Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita
وَلَا جُنَاحَ عَلَيْكُمْ فِيمَا عَرَّضْتُم بِهِ مِنْ خِطْبَةِ النِّسَاءِ أَوْ أَكْنَنتُمْ فِي أَنفُسِكُمْ ۚ عَلِمَ اللَّهُ أَنَّكُمْ سَتَذْكُرُونَهُنَّ وَلَٰكِن لَّا تُوَاعِدُوهُنَّ سِرًّا إِلَّا أَن تَقُولُوا قَوْلًا مَّعْرُوفًا ۚ وَلَا تَعْزِمُوا عُقْدَةَ النِّكَاحِ حَتَّىٰ يَبْلُغَ الْكِتَابُ أَجَلَهُ ۚ وَاعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ يَعْلَمُ مَا فِي أَنفُسِكُمْ فَاحْذَرُوهُ ۚ وَاعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ غَفُورٌ حَلِيمٌ (235)
Siudzakhala mlandu kwa inu ngati muonetsa chidwi choti mudzawafunsira chikwati amayi ofedwa kapena kuwaganizira m’mitima mwanu. Mulungu amadziwa kuti inu mudzawakumbukira iwo. Koma inu musapereke lonjezo la ukwati mwa mseri, koma lankhulani nawo mwaulemu. Ndipo inu musawakwatire nthawi yawo yodikira isanathe. Ndipo dziwani kuti Mulungu amadziwa zimene zili m’mitima mwanu, kotero muopeni Iye ndipo dziwani kuti Mulungu ndi wokhululukira ndi wopilira
لَّا جُنَاحَ عَلَيْكُمْ إِن طَلَّقْتُمُ النِّسَاءَ مَا لَمْ تَمَسُّوهُنَّ أَوْ تَفْرِضُوا لَهُنَّ فَرِيضَةً ۚ وَمَتِّعُوهُنَّ عَلَى الْمُوسِعِ قَدَرُهُ وَعَلَى الْمُقْتِرِ قَدَرُهُ مَتَاعًا بِالْمَعْرُوفِ ۖ حَقًّا عَلَى الْمُحْسِنِينَ (236)
Simlandu kwa inu ngati musudzula akazi musanalowane nawo kapena musanapereke mphotho ya ukwati. Koma apatseni moyenera, ndipo munthu wolemera apereke molingana ndi chuma chake ndi osauka molingana ndi zimene ali nazo. Mphatso yoyenera ndi udindo kwa ochita zabwino
وَإِن طَلَّقْتُمُوهُنَّ مِن قَبْلِ أَن تَمَسُّوهُنَّ وَقَدْ فَرَضْتُمْ لَهُنَّ فَرِيضَةً فَنِصْفُ مَا فَرَضْتُمْ إِلَّا أَن يَعْفُونَ أَوْ يَعْفُوَ الَّذِي بِيَدِهِ عُقْدَةُ النِّكَاحِ ۚ وَأَن تَعْفُوا أَقْرَبُ لِلتَّقْوَىٰ ۚ وَلَا تَنسَوُا الْفَضْلَ بَيْنَكُمْ ۚ إِنَّ اللَّهَ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (237)
Ndipo ngati inu muwasudzula musanalowane nawo kupatula pamene mupereka mphatso ya ukwati, agawireni theka la mphatso ya ukwati kupatula ngati iwo akana kulandira kapena mwamuna avomeleza kuti akhoza kumusiyira theka la mphatsoyo. Ndipo ngati mwamuna asiya mphatsoyo ndiye kuti iye waonetsa chilungamo. Ndipo musaiwale kuonetsana chifundo pakati panu. Ndithudi Mulungu amaona zochita zanu
حَافِظُوا عَلَى الصَّلَوَاتِ وَالصَّلَاةِ الْوُسْطَىٰ وَقُومُوا لِلَّهِ قَانِتِينَ (238)
Pemphera mapemphero onse panthawi yake makamakapempherolapakati. Ndipoimanimodzichipetsa pamaso pa Mulungu
فَإِنْ خِفْتُمْ فَرِجَالًا أَوْ رُكْبَانًا ۖ فَإِذَا أَمِنتُمْ فَاذْكُرُوا اللَّهَ كَمَا عَلَّمَكُم مَّا لَمْ تَكُونُوا تَعْلَمُونَ (239)
Ndipo ngati inu muchita mantha, pempherani chiimirire kapena mutakwera. Ndipo mukakhala pa mtendere, kumbukirani Mulungu monga momwe adakuphunzitsirani zimene simudali kuzidziwa kale
وَالَّذِينَ يُتَوَفَّوْنَ مِنكُمْ وَيَذَرُونَ أَزْوَاجًا وَصِيَّةً لِّأَزْوَاجِهِم مَّتَاعًا إِلَى الْحَوْلِ غَيْرَ إِخْرَاجٍ ۚ فَإِنْ خَرَجْنَ فَلَا جُنَاحَ عَلَيْكُمْ فِي مَا فَعَلْنَ فِي أَنفُسِهِنَّ مِن مَّعْرُوفٍ ۗ وَاللَّهُ عَزِيزٌ حَكِيمٌ (240)
Ndipo iwo amene amwalira ndi kusiya akazi awo, ayenera kusiya malangizo kuti akazi awo ayang’aniridwe chaka chathunthu ndipo kuti asachotsedwe m’nyumba. Koma ngati achoka mwa chifuniro chawo palibe mlandu kwa inu pa zimene iwo angachite ngati ndi zinthu zabwino. Mulungu ndi wa Mphamvu ndiponso Wanzeru
وَلِلْمُطَلَّقَاتِ مَتَاعٌ بِالْمَعْرُوفِ ۖ حَقًّا عَلَى الْمُتَّقِينَ (241)
Amayi osudzulidwa nawonso ayenera kupatsidwa gawo loyenera. Uwu ndi udindo wa anthu onse olungama
كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ اللَّهُ لَكُمْ آيَاتِهِ لَعَلَّكُمْ تَعْقِلُونَ (242)
Motero Mulungu akukufotokozerani zizindikiro zake kwa inu kuti mukhale wozindikira
۞ أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِينَ خَرَجُوا مِن دِيَارِهِمْ وَهُمْ أُلُوفٌ حَذَرَ الْمَوْتِ فَقَالَ لَهُمُ اللَّهُ مُوتُوا ثُمَّ أَحْيَاهُمْ ۚ إِنَّ اللَّهَ لَذُو فَضْلٍ عَلَى النَّاسِ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَ النَّاسِ لَا يَشْكُرُونَ (243)
Kodi siudawaone iwo amene adachoka zikwi zikwi m’nyumba zawo chifukwa choopa imfa? Ndipo Mulungu adati kwa iwo: “Ifani.” Ndipo atatero Iye adawaukitsanso kwa akufa. Ndithudi Mulungu ndi wabwino kwa anthu koma ambiri sayamika
وَقَاتِلُوا فِي سَبِيلِ اللَّهِ وَاعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (244)
Ndipo menyani nkhondo mu njira ya Mulungu ndipo dziwani kuti Mulungu ndiwakumva ndi wodziwa
مَّن ذَا الَّذِي يُقْرِضُ اللَّهَ قَرْضًا حَسَنًا فَيُضَاعِفَهُ لَهُ أَضْعَافًا كَثِيرَةً ۚ وَاللَّهُ يَقْبِضُ وَيَبْسُطُ وَإِلَيْهِ تُرْجَعُونَ (245)
Kodi ndani amene angakongoze Mulungu ngongole yabwino kuti Iye adzamuonjezere zambirimbiri? Ndi Mulungu amene amachepetsa ndiponso amachulukitsa ndipo kwa Iye nonsenu mudzabwerera
أَلَمْ تَرَ إِلَى الْمَلَإِ مِن بَنِي إِسْرَائِيلَ مِن بَعْدِ مُوسَىٰ إِذْ قَالُوا لِنَبِيٍّ لَّهُمُ ابْعَثْ لَنَا مَلِكًا نُّقَاتِلْ فِي سَبِيلِ اللَّهِ ۖ قَالَ هَلْ عَسَيْتُمْ إِن كُتِبَ عَلَيْكُمُ الْقِتَالُ أَلَّا تُقَاتِلُوا ۖ قَالُوا وَمَا لَنَا أَلَّا نُقَاتِلَ فِي سَبِيلِ اللَّهِ وَقَدْ أُخْرِجْنَا مِن دِيَارِنَا وَأَبْنَائِنَا ۖ فَلَمَّا كُتِبَ عَلَيْهِمُ الْقِتَالُ تَوَلَّوْا إِلَّا قَلِيلًا مِّنْهُمْ ۗ وَاللَّهُ عَلِيمٌ بِالظَّالِمِينَ (246)
Kodi iwe siudawone zimene gulu la ana a Israyeli adachita Mose atafa? Pamene iwo adati kwa Mtumwi wawo: “Tisankhire Mfumu,” ndipo ife tidzamenya nkhondo m’njira ya Mulungu. Iye adati: “Kodi inu simungamenye nkhondo ngati mutalamulidwa kutero?” Iwo adati: “Kodi ife tingakane bwanji kumenya nkhondo mmene afunira Mulungu pamene ife tidaumilizidwa kuchoka m’nyumba mwathu ndi kusiya ana athu?” Koma pamene adalamulidwa kuti amenye nkhondo, onse adathawa kupatula anthu owerengeka okha. Ndipo Mulungu amadziwa anthu osalungama
وَقَالَ لَهُمْ نَبِيُّهُمْ إِنَّ اللَّهَ قَدْ بَعَثَ لَكُمْ طَالُوتَ مَلِكًا ۚ قَالُوا أَنَّىٰ يَكُونُ لَهُ الْمُلْكُ عَلَيْنَا وَنَحْنُ أَحَقُّ بِالْمُلْكِ مِنْهُ وَلَمْ يُؤْتَ سَعَةً مِّنَ الْمَالِ ۚ قَالَ إِنَّ اللَّهَ اصْطَفَاهُ عَلَيْكُمْ وَزَادَهُ بَسْطَةً فِي الْعِلْمِ وَالْجِسْمِ ۖ وَاللَّهُ يُؤْتِي مُلْكَهُ مَن يَشَاءُ ۚ وَاللَّهُ وَاسِعٌ عَلِيمٌ (247)
Ndipo Mtumwi wawo adati kwa iwo: Ndithudi Mulungu wasankha Saulo kuti akhale Mfumu yanu. Iwo adati: “Iye angapatsidwe bwanji Ufumu pamene ife ndife oyenera kukhala Mfumu m’malo mwa iye ndipo iye alibe chuma chambiri?” Iye adati: “Ndithudi Mulungu wamusankha iye m’malo mwa inuyo ndipo Mulungu wamuonjezera nzeru zambiri ndiponso mphamvu. Ndipo Mulungu amapereka Ufumu kwa aliyense amene Iye wamufuna. Ndipo Mulungu sasowa chilichonse ndiponso amadziwa chinthu china chilichonse.”
وَقَالَ لَهُمْ نَبِيُّهُمْ إِنَّ آيَةَ مُلْكِهِ أَن يَأْتِيَكُمُ التَّابُوتُ فِيهِ سَكِينَةٌ مِّن رَّبِّكُمْ وَبَقِيَّةٌ مِّمَّا تَرَكَ آلُ مُوسَىٰ وَآلُ هَارُونَ تَحْمِلُهُ الْمَلَائِكَةُ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَآيَةً لَّكُمْ إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (248)
Ndipo Mtumwi wawo adati kwa iwo: Ndithudi! Chizindikiro cha ufumu wake ndi chakuti kudzadza kwa inu Likasa la malamulo limene lidzakhala ndi mtendere wochokera kwa Ambuye wanu ndi nyenyeswa zimene adasiya anthu a banja la Mose ndi a banja la Aroni litanyamulidwa ndi angelo. Ndithudi mu ichi muli chizindikiro kwa inu muli okhulupirira.”
فَلَمَّا فَصَلَ طَالُوتُ بِالْجُنُودِ قَالَ إِنَّ اللَّهَ مُبْتَلِيكُم بِنَهَرٍ فَمَن شَرِبَ مِنْهُ فَلَيْسَ مِنِّي وَمَن لَّمْ يَطْعَمْهُ فَإِنَّهُ مِنِّي إِلَّا مَنِ اغْتَرَفَ غُرْفَةً بِيَدِهِ ۚ فَشَرِبُوا مِنْهُ إِلَّا قَلِيلًا مِّنْهُمْ ۚ فَلَمَّا جَاوَزَهُ هُوَ وَالَّذِينَ آمَنُوا مَعَهُ قَالُوا لَا طَاقَةَ لَنَا الْيَوْمَ بِجَالُوتَ وَجُنُودِهِ ۚ قَالَ الَّذِينَ يَظُنُّونَ أَنَّهُم مُّلَاقُو اللَّهِ كَم مِّن فِئَةٍ قَلِيلَةٍ غَلَبَتْ فِئَةً كَثِيرَةً بِإِذْنِ اللَّهِ ۗ وَاللَّهُ مَعَ الصَّابِرِينَ (249)
Ndipo pamene Saulo ananyamuka ndi gulu lake la nkhondo, iye adati: “Ndithudi! Mulungu adzakuyesani pa mtsinje. Motero aliyense amene adzamwa madzi pamenepo sadzakhala wa gulu langa, ndipo yense amene sadzamwa adzakhala wa gulu langa, kupatula yekhayo amene adzatunge muyeso wa pa chikhato pake.” Koma padali kagulu kochepa kamene kadamwa motero. Motero iye atawoloka mtsinjewo, iye ndi iwo amene adakukhulupirira mwa iye, adati: “Ife lero tilibe mphamvu zogonjetsera Goliati ndi Asirikali ake.” Koma iwo amene adali ndi chikukhulupiriro choti adzakumana ndi Ambuye wawo adati: “Kodi ndi kangati kagulu kochepa kamagonjetsa chigulu cha nkhondo ndi chilolezo cha Mulungu? Ndipo Mulunguamakhalapamodzindiopirira.”
وَلَمَّا بَرَزُوا لِجَالُوتَ وَجُنُودِهِ قَالُوا رَبَّنَا أَفْرِغْ عَلَيْنَا صَبْرًا وَثَبِّتْ أَقْدَامَنَا وَانصُرْنَا عَلَى الْقَوْمِ الْكَافِرِينَ (250)
Ndipopamene iwo anadza kudzakumana ndi Goliati ndi Asirikali ake, iwo adati: “Ambuye wathu! Dzadzani mitima yathu ndi chipiriro ndipo tithandizeni kugonjetsa anthu osakhulupirira.”
فَهَزَمُوهُم بِإِذْنِ اللَّهِ وَقَتَلَ دَاوُودُ جَالُوتَ وَآتَاهُ اللَّهُ الْمُلْكَ وَالْحِكْمَةَ وَعَلَّمَهُ مِمَّا يَشَاءُ ۗ وَلَوْلَا دَفْعُ اللَّهِ النَّاسَ بَعْضَهُم بِبَعْضٍ لَّفَسَدَتِ الْأَرْضُ وَلَٰكِنَّ اللَّهَ ذُو فَضْلٍ عَلَى الْعَالَمِينَ (251)
Mwa chifuniro cha Mulungu, iwo anamenya nkhondo. Davide anapha Goliati ndipo Mulungu anamupatsa iye ufumu ndi luntha ndipo anamuphunzitsa zimene Mulungu adafuna. Akanakhala kuti Mulungu satchinjiriza anthu ena ndi anzawo, dziko lonse likanaonongeka. Koma Mulungu ndi wopereka moolowa manja kwa zolengedwa zonse
تِلْكَ آيَاتُ اللَّهِ نَتْلُوهَا عَلَيْكَ بِالْحَقِّ ۚ وَإِنَّكَ لَمِنَ الْمُرْسَلِينَ (252)
AmenewandiMauaMulungutilikulakatulakwaiwendi choonadi chonse. Ndithudi iwe ndiwe mmodzi wa Atumwi athu
۞ تِلْكَ الرُّسُلُ فَضَّلْنَا بَعْضَهُمْ عَلَىٰ بَعْضٍ ۘ مِّنْهُم مَّن كَلَّمَ اللَّهُ ۖ وَرَفَعَ بَعْضَهُمْ دَرَجَاتٍ ۚ وَآتَيْنَا عِيسَى ابْنَ مَرْيَمَ الْبَيِّنَاتِ وَأَيَّدْنَاهُ بِرُوحِ الْقُدُسِ ۗ وَلَوْ شَاءَ اللَّهُ مَا اقْتَتَلَ الَّذِينَ مِن بَعْدِهِم مِّن بَعْدِ مَا جَاءَتْهُمُ الْبَيِّنَاتُ وَلَٰكِنِ اخْتَلَفُوا فَمِنْهُم مَّنْ آمَنَ وَمِنْهُم مَّن كَفَرَ ۚ وَلَوْ شَاءَ اللَّهُ مَا اقْتَتَلُوا وَلَٰكِنَّ اللَّهَ يَفْعَلُ مَا يُرِيدُ (253)
Atumwi aja! Ife tidawakweza ena kuposa anzawo. Kwa ena a iwo Mulungu adalankhula nawo mwachindunji, pamene ena adawakweza kukhala a pamwamba ndipo kwa Yesu mwana wa Mwamuna wa Maria, Ife tidampatsa zizindikiro zooneka ndipo tidamulimbikitsa ndi Mzimu Woyera. Mulungu akadafuna, iwo amene adadza pambuyo pawo sakadamenyana wina ndi mnzake pamene zizindikiro zooneka zitadza kwa iwo, koma iwo adakangana. Ena adali ndi chikhulupiriro pamene ena mwa iwo adakana. Koma Mulungu akadafuna, iwo sakadamenyana wina ndi mzake ayi. Mulungu amachita chimene wafuna
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا أَنفِقُوا مِمَّا رَزَقْنَاكُم مِّن قَبْلِ أَن يَأْتِيَ يَوْمٌ لَّا بَيْعٌ فِيهِ وَلَا خُلَّةٌ وَلَا شَفَاعَةٌ ۗ وَالْكَافِرُونَ هُمُ الظَّالِمُونَ (254)
Oh Inu anthu okhulupirira! Perekani gawo la zimene takupatsani lisanafike tsiku limene sikudzakhala malonda, ubwenzi kapena mkhalapakati. Ndithudi ndi anthu osakhulupirira amene ali osalungama
اللَّهُ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ الْحَيُّ الْقَيُّومُ ۚ لَا تَأْخُذُهُ سِنَةٌ وَلَا نَوْمٌ ۚ لَّهُ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۗ مَن ذَا الَّذِي يَشْفَعُ عِندَهُ إِلَّا بِإِذْنِهِ ۚ يَعْلَمُ مَا بَيْنَ أَيْدِيهِمْ وَمَا خَلْفَهُمْ ۖ وَلَا يُحِيطُونَ بِشَيْءٍ مِّنْ عِلْمِهِ إِلَّا بِمَا شَاءَ ۚ وَسِعَ كُرْسِيُّهُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ ۖ وَلَا يَئُودُهُ حِفْظُهُمَا ۚ وَهُوَ الْعَلِيُّ الْعَظِيمُ (255)
Mulungu! Kulibe mulungu wina koma Iye yekha, wamoyo ndi wamuyaya. Iye saodzera kapena kugona. Zake ndi zonse zimene zili kumwamba ndi padziko lapansi. Ndani amene angakhale mkhalapakati pa Iye opanda chilolezo chake? Iye amadziwa zonse zimene zimachitika mdziko lino ndi zimene zidzachitike m’moyo uli nkudza. Ndipo iwo sadzadziwa chilichonse kuchokera ku nzeru zake pokhapokha ngati Iye afuna. Mpando wake umafika kumwamba ndi dziko lapansi. Ndipo chisamaliro chake pazinthu zonse sichimutopetsa ayi. Iye ndi wapamwamba mwamba ndi Wamkulu zedi
لَا إِكْرَاهَ فِي الدِّينِ ۖ قَد تَّبَيَّنَ الرُّشْدُ مِنَ الْغَيِّ ۚ فَمَن يَكْفُرْ بِالطَّاغُوتِ وَيُؤْمِن بِاللَّهِ فَقَدِ اسْتَمْسَكَ بِالْعُرْوَةِ الْوُثْقَىٰ لَا انفِصَامَ لَهَا ۗ وَاللَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (256)
Palibe kukakamizana m’chipembedzo. Ndithudi njira yoyenera yaonekera kusiyana ndi njira yolakwa. Iye amene asiya kupembedza mafano ndipo aika chikhulupiriro chake mwa Mulungu, ndithudi wagwiritsitsa chingwe chimene sichidzaduka. Ndipo Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa
اللَّهُ وَلِيُّ الَّذِينَ آمَنُوا يُخْرِجُهُم مِّنَ الظُّلُمَاتِ إِلَى النُّورِ ۖ وَالَّذِينَ كَفَرُوا أَوْلِيَاؤُهُمُ الطَّاغُوتُ يُخْرِجُونَهُم مِّنَ النُّورِ إِلَى الظُّلُمَاتِ ۗ أُولَٰئِكَ أَصْحَابُ النَّارِ ۖ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (257)
Mulungu ndi Mtetezi wa amene akhulupirira. Iye amawatulutsa kuchokera ku mdima kupita nawo kowala. Koma iwo amene sakhulupirira, owathandiza wawo ndi Satana, amene amatulutsa iwo kuchoka kowala kupita ku mdima. Iwo ndiwo anthu aku moto ndipo adzakhala komweko mpaka kalekale
أَلَمْ تَرَ إِلَى الَّذِي حَاجَّ إِبْرَاهِيمَ فِي رَبِّهِ أَنْ آتَاهُ اللَّهُ الْمُلْكَ إِذْ قَالَ إِبْرَاهِيمُ رَبِّيَ الَّذِي يُحْيِي وَيُمِيتُ قَالَ أَنَا أُحْيِي وَأُمِيتُ ۖ قَالَ إِبْرَاهِيمُ فَإِنَّ اللَّهَ يَأْتِي بِالشَّمْسِ مِنَ الْمَشْرِقِ فَأْتِ بِهَا مِنَ الْمَغْرِبِ فَبُهِتَ الَّذِي كَفَرَ ۗ وَاللَّهُ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الظَّالِمِينَ (258)
Kodi iwe siudamuone iye amene anatsutsana ndi Abrahamu pa nkhani ya Ambuye wake chifukwa cha kuti Mulungu anamupatsa iye ufumu? Pamene Abrahamu adati: “Ambuye wanga ndiye amene amapereka moyo ndi imfa.” Iye adati: “Ine ndimapereka moyo ndi imfa.” Abrahamu adati: “Ndithudi Mulungu amatulutsa dzuwa kuchokera ku m’mawa choncho iwe ulitulutse kuchokera ku madzulo.” Munthu wosakhulupirira uja adathedwa nzeru. Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa
أَوْ كَالَّذِي مَرَّ عَلَىٰ قَرْيَةٍ وَهِيَ خَاوِيَةٌ عَلَىٰ عُرُوشِهَا قَالَ أَنَّىٰ يُحْيِي هَٰذِهِ اللَّهُ بَعْدَ مَوْتِهَا ۖ فَأَمَاتَهُ اللَّهُ مِائَةَ عَامٍ ثُمَّ بَعَثَهُ ۖ قَالَ كَمْ لَبِثْتَ ۖ قَالَ لَبِثْتُ يَوْمًا أَوْ بَعْضَ يَوْمٍ ۖ قَالَ بَل لَّبِثْتَ مِائَةَ عَامٍ فَانظُرْ إِلَىٰ طَعَامِكَ وَشَرَابِكَ لَمْ يَتَسَنَّهْ ۖ وَانظُرْ إِلَىٰ حِمَارِكَ وَلِنَجْعَلَكَ آيَةً لِّلنَّاسِ ۖ وَانظُرْ إِلَى الْعِظَامِ كَيْفَ نُنشِزُهَا ثُمَّ نَكْسُوهَا لَحْمًا ۚ فَلَمَّا تَبَيَّنَ لَهُ قَالَ أَعْلَمُ أَنَّ اللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (259)
Kapena iye amene adadutsa Mumzinda umene udaonongeka ndi kusanduka bwinja ndipo adanena kuti: “Kodi Mulungu angapereke moyo bwanji ku Mzinda pamene utafa?” Motero Mulungu adamupha iye ndipo patatha zaka zana limodzi Iye adamuukitsa kwa akufa. Mulungu adati: “Kodi iwe wakhala chifere nthawi yotani?” Iye adati: “Mwina tsiku limodzi kapena maola owerengeka basi.” Mulungu adati: “Iyayi, iwe wakhala zaka zana limodzi. Taona chakudya chako ndi chakumwa chako, sizinasinthe ayi ndipo taona bulu wako! Ife tikusandutsa kuti ukhale chizindikiro kwa anthu. Ndipo taona mafupa m’mene timawaikira pamodzi ndi kuwakuta ndi mnofu.” Ndipo pamene zonse zinaonetsedwa kwa iye, iye adati: “Ndadziwa tsopano kuti Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse.”
وَإِذْ قَالَ إِبْرَاهِيمُ رَبِّ أَرِنِي كَيْفَ تُحْيِي الْمَوْتَىٰ ۖ قَالَ أَوَلَمْ تُؤْمِن ۖ قَالَ بَلَىٰ وَلَٰكِن لِّيَطْمَئِنَّ قَلْبِي ۖ قَالَ فَخُذْ أَرْبَعَةً مِّنَ الطَّيْرِ فَصُرْهُنَّ إِلَيْكَ ثُمَّ اجْعَلْ عَلَىٰ كُلِّ جَبَلٍ مِّنْهُنَّ جُزْءًا ثُمَّ ادْعُهُنَّ يَأْتِينَكَ سَعْيًا ۚ وَاعْلَمْ أَنَّ اللَّهَ عَزِيزٌ حَكِيمٌ (260)
Ndipo pamene Abrahamu adati: “Ambuye wanga! Ndionetseni mmene Inu mumaukitsira zinthu zakufa.” Mulungu adati: “Kodi iwe siukhulupirira?” Abrahamu adati: “Ndimakhulupirira, koma ndifuna kuti ndikhutitsidwe mumtima mwanga.” Mulungu adati: “Tenga mbalame zinayi ndipo uziwete kenaka uziphe ndi kuika pa phiri lililonse zigawozigawo za mbalame ndipo uziitane. Ndipo izo zibwera kwa iwe mwaliwiro. Ndipo dziwa kuti Mulungu ndi Wamphamvu ndi Wanzeru.”
مَّثَلُ الَّذِينَ يُنفِقُونَ أَمْوَالَهُمْ فِي سَبِيلِ اللَّهِ كَمَثَلِ حَبَّةٍ أَنبَتَتْ سَبْعَ سَنَابِلَ فِي كُلِّ سُنبُلَةٍ مِّائَةُ حَبَّةٍ ۗ وَاللَّهُ يُضَاعِفُ لِمَن يَشَاءُ ۗ وَاللَّهُ وَاسِعٌ عَلِيمٌ (261)
Kufanana kwa amene amapereka chuma chawo m’njira ya Mulungu kuli ngati njere ya tirigu imene imabereka njere zina zisanu ndi ziwiri ndipo ililonse imabereka njere zana limodzi. Mulungu amapereka moolowa manja kwa amene wamufuna. Ndipo Mulungu ali ndi zonse zimene zolengedwa zake zimafuna. Iye amadziwa chinthu china chilichonse
الَّذِينَ يُنفِقُونَ أَمْوَالَهُمْ فِي سَبِيلِ اللَّهِ ثُمَّ لَا يُتْبِعُونَ مَا أَنفَقُوا مَنًّا وَلَا أَذًى ۙ لَّهُمْ أَجْرُهُمْ عِندَ رَبِّهِمْ وَلَا خَوْفٌ عَلَيْهِمْ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ (262)
Iwo amene amapereka chuma chawo m’njira ya Mulungu ndipo sakumba wina aliyense chifukwa cha choperekacho kapena mtozo, mphotho yawo ili ndi Ambuye wawo. Iwo sadzaopa kapena kudandaula
۞ قَوْلٌ مَّعْرُوفٌ وَمَغْفِرَةٌ خَيْرٌ مِّن صَدَقَةٍ يَتْبَعُهَا أَذًى ۗ وَاللَّهُ غَنِيٌّ حَلِيمٌ (263)
Mawu abwino ndi chikhululukiro ndi zinthu zabwino kuposa chopereka chaulere chimene chimatsatiridwa ndi kutafula. Mulungu ndi wolemera ndipo ndi wopirira kwambiri
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تُبْطِلُوا صَدَقَاتِكُم بِالْمَنِّ وَالْأَذَىٰ كَالَّذِي يُنفِقُ مَالَهُ رِئَاءَ النَّاسِ وَلَا يُؤْمِنُ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ ۖ فَمَثَلُهُ كَمَثَلِ صَفْوَانٍ عَلَيْهِ تُرَابٌ فَأَصَابَهُ وَابِلٌ فَتَرَكَهُ صَلْدًا ۖ لَّا يَقْدِرُونَ عَلَىٰ شَيْءٍ مِّمَّا كَسَبُوا ۗ وَاللَّهُ لَا يَهْدِي الْقَوْمَ الْكَافِرِينَ (264)
Oh Inu anthu okhulupirira! Musaononge zopereka zanu zaulere pokumbutsa kapena kunyoza. Monga amene amapereka chuma chake ndi cholinga chodzionetsera kwa anthu ndipo sakhulupirira mwa Mulungu kapena mwa tsiku la chimaliziro iye ali ngati mwala umene wakutidwa ndi nthaka ndipo pamene mawawa a mvula agwa iwo umaonekera pa mtunda. Iwo sangathe kuchita chilichonse ndi zimene amapeza. Mulungu satsogolera anthu osakhulupirira
وَمَثَلُ الَّذِينَ يُنفِقُونَ أَمْوَالَهُمُ ابْتِغَاءَ مَرْضَاتِ اللَّهِ وَتَثْبِيتًا مِّنْ أَنفُسِهِمْ كَمَثَلِ جَنَّةٍ بِرَبْوَةٍ أَصَابَهَا وَابِلٌ فَآتَتْ أُكُلَهَا ضِعْفَيْنِ فَإِن لَّمْ يُصِبْهَا وَابِلٌ فَطَلٌّ ۗ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ بَصِيرٌ (265)
Ndipo iwo amene amapereka chuma chawo ndi cholinga chokondweretsa Mulungu ndi kulimbikitsa chikhulupiriro m’mitima mwawo, ali ngati munda umene uli pamalo pokwera, ndipo pamene mvula igwa pa iwo, umabereka zakudya mowirikiza. Ndipo ngati mvula siigwa, iwo umathiriridwa ndi mame. Ndipo Mulungu amaona zonse zimene mumachita
أَيَوَدُّ أَحَدُكُمْ أَن تَكُونَ لَهُ جَنَّةٌ مِّن نَّخِيلٍ وَأَعْنَابٍ تَجْرِي مِن تَحْتِهَا الْأَنْهَارُ لَهُ فِيهَا مِن كُلِّ الثَّمَرَاتِ وَأَصَابَهُ الْكِبَرُ وَلَهُ ذُرِّيَّةٌ ضُعَفَاءُ فَأَصَابَهَا إِعْصَارٌ فِيهِ نَارٌ فَاحْتَرَقَتْ ۗ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ اللَّهُ لَكُمُ الْآيَاتِ لَعَلَّكُمْ تَتَفَكَّرُونَ (266)
Kodi wina wa inu angakonde kukhala ndi munda wa tende ndi azitona womwe umathiriridwa ndi mitsinje pansi pake ndipo uli ndi zipatso zosiyanasiyana, pamene ukalamba wampeza, pomwe iye ali ndi ana opanda mphamvu ndipo munda uja uli kukunthidwa ndi mphepo ndipo m’kati mwa mphepoyo muli moto umene utentha mundawo? Kotero Mulungu ali kufotokoza chivumbuluitso chake momveka kwa inu kuti muganize bwino
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا أَنفِقُوا مِن طَيِّبَاتِ مَا كَسَبْتُمْ وَمِمَّا أَخْرَجْنَا لَكُم مِّنَ الْأَرْضِ ۖ وَلَا تَيَمَّمُوا الْخَبِيثَ مِنْهُ تُنفِقُونَ وَلَسْتُم بِآخِذِيهِ إِلَّا أَن تُغْمِضُوا فِيهِ ۚ وَاعْلَمُوا أَنَّ اللَّهَ غَنِيٌّ حَمِيدٌ (267)
oh inu anthu okhulupirira! Perekani chopereka cha ulere kuchokera ku chuma chimene mwachipeza mwa chilungamo ndiponso icho chimene Ife takupatsani kuchokera ku nthaka ndipo musamasankha kupereka chinthu chimene inu simungathe kulandira pokhapokha mutatseka maso anu. Ndipo dziwani kuti Mulungu ndi wolemera ndiponso woyenera kulemekezedwa
الشَّيْطَانُ يَعِدُكُمُ الْفَقْرَ وَيَأْمُرُكُم بِالْفَحْشَاءِ ۖ وَاللَّهُ يَعِدُكُم مَّغْفِرَةً مِّنْهُ وَفَضْلًا ۗ وَاللَّهُ وَاسِعٌ عَلِيمٌ (268)
Satana ali kukuopsezani ndi umphawi ndipo ali kukulamulirani kuchita zoipa pamene Mulungu ali kukulonjezani chikhululukiro ndi zabwino. Ndipo Mulungu ali ndi zonse zimene zolengedwa zake zimafuna. Iye amadziwa chinthu china chilichonse
يُؤْتِي الْحِكْمَةَ مَن يَشَاءُ ۚ وَمَن يُؤْتَ الْحِكْمَةَ فَقَدْ أُوتِيَ خَيْرًا كَثِيرًا ۗ وَمَا يَذَّكَّرُ إِلَّا أُولُو الْأَلْبَابِ (269)
Iye amapereka luntha kwa iye amene wamufuna ndipo iye amene wapatsidwa luntha, ndithudi, wapatsidwa chinthu chabwino kwambiri. Koma palibe wina aliyense amene amakumbukira kupatula anthu ozindikira
وَمَا أَنفَقْتُم مِّن نَّفَقَةٍ أَوْ نَذَرْتُم مِّن نَّذْرٍ فَإِنَّ اللَّهَ يَعْلَمُهُ ۗ وَمَا لِلظَّالِمِينَ مِنْ أَنصَارٍ (270)
Chopereka chilichonse chimene mupereka kapena malonjezo ena alionse amene mulonjeza, khulupirirani kuti Mulungu amazidziwa. Ndipo anthu ochita zoipa alibe wina aliyense owathandiza
إِن تُبْدُوا الصَّدَقَاتِ فَنِعِمَّا هِيَ ۖ وَإِن تُخْفُوهَا وَتُؤْتُوهَا الْفُقَرَاءَ فَهُوَ خَيْرٌ لَّكُمْ ۚ وَيُكَفِّرُ عَنكُم مِّن سَيِّئَاتِكُمْ ۗ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ خَبِيرٌ (271)
Kuulula chimene mwapereka ndi bwino koma kupereka mwa mseri kwa anthu osauka ndi kwabwino kwambiri. Mulungu adzakukhululukirani ena mwa machimo anu. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse chimene mumachita
۞ لَّيْسَ عَلَيْكَ هُدَاهُمْ وَلَٰكِنَّ اللَّهَ يَهْدِي مَن يَشَاءُ ۗ وَمَا تُنفِقُوا مِنْ خَيْرٍ فَلِأَنفُسِكُمْ ۚ وَمَا تُنفِقُونَ إِلَّا ابْتِغَاءَ وَجْهِ اللَّهِ ۚ وَمَا تُنفِقُوا مِنْ خَيْرٍ يُوَفَّ إِلَيْكُمْ وَأَنتُمْ لَا تُظْلَمُونَ (272)
Si udindo wako kuwatsogolera iwo koma Mulungu ndiye amene amatsogolera amene Iye wamufuna. Ndipo chopereka chaulere chilichonse chimene mupereka ndi chabwino kwa inu ndipo musapereke pokhapokha ngati mufuna chisangalalo cha Mulungu. Ndipo chopereka chonse chimene mupereka, chidzabwezedwa kwa inu champhumphu ndipo inu simudzaponderezedwa ngakhale ndipang’onopomwe
لِلْفُقَرَاءِ الَّذِينَ أُحْصِرُوا فِي سَبِيلِ اللَّهِ لَا يَسْتَطِيعُونَ ضَرْبًا فِي الْأَرْضِ يَحْسَبُهُمُ الْجَاهِلُ أَغْنِيَاءَ مِنَ التَّعَفُّفِ تَعْرِفُهُم بِسِيمَاهُمْ لَا يَسْأَلُونَ النَّاسَ إِلْحَافًا ۗ وَمَا تُنفِقُوا مِنْ خَيْرٍ فَإِنَّ اللَّهَ بِهِ عَلِيمٌ (273)
Choperekachaulerechiperekedwe kwa osauka amene atangwanika ndi ntchito ya Mulungu ndipo sangathe kuyenda padziko. Munthu amene sawadziwa amaganiza kuti, chifukwa chodzichepetsa kwawo, iwo sasowa chilichonse. Iwe udzawadziwa chifukwa cha maonekedwe awo. Iwo sapempha ayi. Ndipo chilichonse chabwino chimene upereka, ndithudi Mulungu amachidziwa bwino kwambiri
الَّذِينَ يُنفِقُونَ أَمْوَالَهُم بِاللَّيْلِ وَالنَّهَارِ سِرًّا وَعَلَانِيَةً فَلَهُمْ أَجْرُهُمْ عِندَ رَبِّهِمْ وَلَا خَوْفٌ عَلَيْهِمْ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ (274)
onse amene amapereka chaulere masana kapena usiku, mseri ndi moonekera, adzalandira malipiro awo kuchokera kwa Ambuye wawo. Iwo alibe choti aope ndipo sadzakhumudwa
الَّذِينَ يَأْكُلُونَ الرِّبَا لَا يَقُومُونَ إِلَّا كَمَا يَقُومُ الَّذِي يَتَخَبَّطُهُ الشَّيْطَانُ مِنَ الْمَسِّ ۚ ذَٰلِكَ بِأَنَّهُمْ قَالُوا إِنَّمَا الْبَيْعُ مِثْلُ الرِّبَا ۗ وَأَحَلَّ اللَّهُ الْبَيْعَ وَحَرَّمَ الرِّبَا ۚ فَمَن جَاءَهُ مَوْعِظَةٌ مِّن رَّبِّهِ فَانتَهَىٰ فَلَهُ مَا سَلَفَ وَأَمْرُهُ إِلَى اللَّهِ ۖ وَمَنْ عَادَ فَأُولَٰئِكَ أَصْحَابُ النَّارِ ۖ هُمْ فِيهَا خَالِدُونَ (275)
Iwo amene amadya ndalama za katapira, adzaima maimidwe a munthu amene wamenyedwa ndi Satana ndi kumuyambitsa misala. Ichi ndi chifukwa chakuti iwo amanena kuti: “Katapira ali chimodzimodzi ndi kugulitsa malonda.” Pamene Mulungu adaloleza malonda, Iye adakaniza katapira. Ndipo iye amene alandira chidzudzulo kuchokera kwa Ambuye wake, ndipo aleka, adzakhululukidwa zochimwa zake zakale koma nkhani yake ili m’manja mwa Mulungu. Koma iye amene abwerezanso kudya ndalama za katapira iye adzaponyedwa ku moto wa ku Gahena ndipo iwo adzakhala komweko mpaka kalekale
يَمْحَقُ اللَّهُ الرِّبَا وَيُرْبِي الصَّدَقَاتِ ۗ وَاللَّهُ لَا يُحِبُّ كُلَّ كَفَّارٍ أَثِيمٍ (276)
Mulungu sadalitsa ndalama za katapira koma amadalitsa chopereka chaulere. Iye alibe chikondi pa anthu osakhulupirira ndiponso ochimwa
إِنَّ الَّذِينَ آمَنُوا وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ وَأَقَامُوا الصَّلَاةَ وَآتَوُا الزَّكَاةَ لَهُمْ أَجْرُهُمْ عِندَ رَبِّهِمْ وَلَا خَوْفٌ عَلَيْهِمْ وَلَا هُمْ يَحْزَنُونَ (277)
Ndithudi onse amene ali ndi chikhulupiriro ndipo amachita ntchito zabwino, amasamala mapemphero awo ndi kupereka chopereka chothandizira anthu osauka, adzalipidwa ndi Ambuye wawo. Ndipo iwo sadzaopa china chilichonse kapena kudandaula
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا اتَّقُوا اللَّهَ وَذَرُوا مَا بَقِيَ مِنَ الرِّبَا إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (278)
oh inu anthu okhulupirira! Muopeni Mulungu ndipo musalandire gawo lina lililonse loti lidze kwa inu kuchokera ku katapira ngati chikhulupiriro chanu ndi choonadi
فَإِن لَّمْ تَفْعَلُوا فَأْذَنُوا بِحَرْبٍ مِّنَ اللَّهِ وَرَسُولِهِ ۖ وَإِن تُبْتُمْ فَلَكُمْ رُءُوسُ أَمْوَالِكُمْ لَا تَظْلِمُونَ وَلَا تُظْلَمُونَ (279)
Ndipo ngati simusiya izi, yembekezani nkhondo kuchokera kwa Mulungu pamodzi ndi Mtumwi wake. Koma ngati inu mulapa, inu mudzalandira zinthu zanu zoyamba. Musapondereze anzanu ndipo nanunso simudzaponderezedwa ayi
وَإِن كَانَ ذُو عُسْرَةٍ فَنَظِرَةٌ إِلَىٰ مَيْسَرَةٍ ۚ وَأَن تَصَدَّقُوا خَيْرٌ لَّكُمْ ۖ إِن كُنتُمْ تَعْلَمُونَ (280)
Ngati munthu amene ali nanu ndi ngongole ali pa mavuto a chuma, mupatseni nthawi mpaka pamene angakubwezereni koma ngati inu musandutsa ngongoleyi kukhala ngati chopereka chanu chaulere, zotere zidzakhala zabwino kwa inu, ngati mukadadziwa
وَاتَّقُوا يَوْمًا تُرْجَعُونَ فِيهِ إِلَى اللَّهِ ۖ ثُمَّ تُوَفَّىٰ كُلُّ نَفْسٍ مَّا كَسَبَتْ وَهُمْ لَا يُظْلَمُونَ (281)
Ndipo liopeni tsiku limene mudzabwerera kwa Mulungu. Ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa molingana ndi ntchito zake, ndipo palibe amene adzaponderezedwa
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا إِذَا تَدَايَنتُم بِدَيْنٍ إِلَىٰ أَجَلٍ مُّسَمًّى فَاكْتُبُوهُ ۚ وَلْيَكْتُب بَّيْنَكُمْ كَاتِبٌ بِالْعَدْلِ ۚ وَلَا يَأْبَ كَاتِبٌ أَن يَكْتُبَ كَمَا عَلَّمَهُ اللَّهُ ۚ فَلْيَكْتُبْ وَلْيُمْلِلِ الَّذِي عَلَيْهِ الْحَقُّ وَلْيَتَّقِ اللَّهَ رَبَّهُ وَلَا يَبْخَسْ مِنْهُ شَيْئًا ۚ فَإِن كَانَ الَّذِي عَلَيْهِ الْحَقُّ سَفِيهًا أَوْ ضَعِيفًا أَوْ لَا يَسْتَطِيعُ أَن يُمِلَّ هُوَ فَلْيُمْلِلْ وَلِيُّهُ بِالْعَدْلِ ۚ وَاسْتَشْهِدُوا شَهِيدَيْنِ مِن رِّجَالِكُمْ ۖ فَإِن لَّمْ يَكُونَا رَجُلَيْنِ فَرَجُلٌ وَامْرَأَتَانِ مِمَّن تَرْضَوْنَ مِنَ الشُّهَدَاءِ أَن تَضِلَّ إِحْدَاهُمَا فَتُذَكِّرَ إِحْدَاهُمَا الْأُخْرَىٰ ۚ وَلَا يَأْبَ الشُّهَدَاءُ إِذَا مَا دُعُوا ۚ وَلَا تَسْأَمُوا أَن تَكْتُبُوهُ صَغِيرًا أَوْ كَبِيرًا إِلَىٰ أَجَلِهِ ۚ ذَٰلِكُمْ أَقْسَطُ عِندَ اللَّهِ وَأَقْوَمُ لِلشَّهَادَةِ وَأَدْنَىٰ أَلَّا تَرْتَابُوا ۖ إِلَّا أَن تَكُونَ تِجَارَةً حَاضِرَةً تُدِيرُونَهَا بَيْنَكُمْ فَلَيْسَ عَلَيْكُمْ جُنَاحٌ أَلَّا تَكْتُبُوهَا ۗ وَأَشْهِدُوا إِذَا تَبَايَعْتُمْ ۚ وَلَا يُضَارَّ كَاتِبٌ وَلَا شَهِيدٌ ۚ وَإِن تَفْعَلُوا فَإِنَّهُ فُسُوقٌ بِكُمْ ۗ وَاتَّقُوا اللَّهَ ۖ وَيُعَلِّمُكُمُ اللَّهُ ۗ وَاللَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (282)
oh inu anthu okhulupirira! Pamene mukongola ngongole yoperekedwa panthawi yomwe mwagwirizana, lembani pena pake. Mlembi alembe zonse mwachilungamo. Ndipo iye asakane kulemba monga mmene Mulungu wamuphunzitsira, motero alembe. Ndipo mulekeni wokongolakutianenezotizilembedwendipoayenerakuopa Mulungu Ambuye wake ndipo iye asabise mangawa ena aliwonse amene ali nawo. Koma ngati munthu wokongolayo ndi wozerezeka kapena wofoka kapena amene sangathe kuyankhula, muloleni m’bale wake kuti ayankhule m’malo mwa iye komatu mwachilungamo. Ndipo itanani amuna awiri amene ali pakati panu kuti akhale mboni. Ndipo ngati anthu amuna sangathe kupezeka, funani mwamuna mmodzi ndi akazi awiri amene mungavomereze kukhala mboni, kuti achitire umboni; kuti ngati wina wa iwo alakwa, wina adzakumbutse mnzake. Ndipo mboni zisamakane kupereka umboni ngati ziitanidwa kutero. Kotero musatope kulemba ngongole zanu kaya ndi yaing’ono kapena yaikulu, ndipo mulembenso tsiku lodzabwezedwa ngongoleyi. Ichi ndicho chilungamo pamaso pa Mulungu, ndipo zimakhala dongosolo pofuna kutsimikiza ndiponso ndi njira yabwino kuti musakaike kupatula ngati zimene zili kugulitsidwa ndi zinthu zopezeka mwa mwayi ndipo ndi zoti zigulitsidwe msangamsanga, si mlandu ngati inu simulemba. Koma onetsetsani kuti pali mboni pamene muli kugulitsana wina ndi mnzake. Ndipo pasakhale vuto kwa mlembi kapena wochitira umboni koma ngati mutero mudzalakwa. Motero opani Mulungu chifukwa amakuphunzitsani inu. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse
۞ وَإِن كُنتُمْ عَلَىٰ سَفَرٍ وَلَمْ تَجِدُوا كَاتِبًا فَرِهَانٌ مَّقْبُوضَةٌ ۖ فَإِنْ أَمِنَ بَعْضُكُم بَعْضًا فَلْيُؤَدِّ الَّذِي اؤْتُمِنَ أَمَانَتَهُ وَلْيَتَّقِ اللَّهَ رَبَّهُ ۗ وَلَا تَكْتُمُوا الشَّهَادَةَ ۚ وَمَن يَكْتُمْهَا فَإِنَّهُ آثِمٌ قَلْبُهُ ۗ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ عَلِيمٌ (283)
Koma ngati inu muli pa ulendo ndipo simunapeze mlembi, perekani chinthu choti wina agwirizire ngati chikole ndipo ngati wina wa inu asungitsa katundu kwa mnzake, wosunga uja amubwezere mnzakeyo katundu wake ndipo iye aope Mulungu, Ambuye wake. Inu musabise umboni chifukwa aliyense amene abisa umboni ndi ochimwa. Ndipo Mulungu amadziwa zimene mumachita
لِّلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَمَا فِي الْأَرْضِ ۗ وَإِن تُبْدُوا مَا فِي أَنفُسِكُمْ أَوْ تُخْفُوهُ يُحَاسِبْكُم بِهِ اللَّهُ ۖ فَيَغْفِرُ لِمَن يَشَاءُ وَيُعَذِّبُ مَن يَشَاءُ ۗ وَاللَّهُ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (284)
Mwini wa zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi Mulungu. Kaya inu muulula za m’maganizo anu kapena mubisa, Mulungu adzakufunsani za izo. Iye amakhululukira aliyense amene Iye wamufuna ndipo amalanga aliyense amene Iye wamufuna . Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chili chonse
آمَنَ الرَّسُولُ بِمَا أُنزِلَ إِلَيْهِ مِن رَّبِّهِ وَالْمُؤْمِنُونَ ۚ كُلٌّ آمَنَ بِاللَّهِ وَمَلَائِكَتِهِ وَكُتُبِهِ وَرُسُلِهِ لَا نُفَرِّقُ بَيْنَ أَحَدٍ مِّن رُّسُلِهِ ۚ وَقَالُوا سَمِعْنَا وَأَطَعْنَا ۖ غُفْرَانَكَ رَبَّنَا وَإِلَيْكَ الْمَصِيرُ (285)
Mtumwi amakhulupirira mu zimene zavumbulutsidwa kwa iye kuchokera kwa Ambuye wake, ndipo nawonso anthu okhulupirira amatero. Aliyense amakhulupirira mwa Mulungu, Angelo ake, mabuku ake ndi mwa Atumwi ake. Iwo amati “Ife sitisiyanitsa aliyense pakati pa Atumwi ake;” ndipo adati: “Ife tamva ndipo titsatira. Tipempha chikhulukiliro chanu Ambuye chifukwa ndi kwa inu kumene tidzabwerera.”
لَا يُكَلِّفُ اللَّهُ نَفْسًا إِلَّا وُسْعَهَا ۚ لَهَا مَا كَسَبَتْ وَعَلَيْهَا مَا اكْتَسَبَتْ ۗ رَبَّنَا لَا تُؤَاخِذْنَا إِن نَّسِينَا أَوْ أَخْطَأْنَا ۚ رَبَّنَا وَلَا تَحْمِلْ عَلَيْنَا إِصْرًا كَمَا حَمَلْتَهُ عَلَى الَّذِينَ مِن قَبْلِنَا ۚ رَبَّنَا وَلَا تُحَمِّلْنَا مَا لَا طَاقَةَ لَنَا بِهِ ۖ وَاعْفُ عَنَّا وَاغْفِرْ لَنَا وَارْحَمْنَا ۚ أَنتَ مَوْلَانَا فَانصُرْنَا عَلَى الْقَوْمِ الْكَافِرِينَ (286)
Mulungu sapereka katundu wolemera pa mzimu umene siungathe kumunyamula. Mzimuuliwonseumalandirachilichonsechabwinochimene umachita kapena umalangidwa chifukwa cha ntchito zake zoipa zimene umachita. Pemphani kuti: “Ambuye wathu! Musatilange ife ngati tiiwala kapena tilakwa. Ambuye wathu! Musatikundikire ife mavuto monga amene mudakundikira anthu amene adalipo kale. Ambuye wathu! Musatisenzetse zinthu zimene sitingathe kuzinyamula. Tichotsereni machimo, tikhululukireni ndipo tichitireni chifundo ife. Inu nokha ndinu Mtetezi wathu. Tipatseni kupambana pakati pa anthu osakhulupirira.”
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس