Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 85 - البَقَرَة - Page - Juz 1
﴿ثُمَّ أَنتُمۡ هَٰٓؤُلَآءِ تَقۡتُلُونَ أَنفُسَكُمۡ وَتُخۡرِجُونَ فَرِيقٗا مِّنكُم مِّن دِيَٰرِهِمۡ تَظَٰهَرُونَ عَلَيۡهِم بِٱلۡإِثۡمِ وَٱلۡعُدۡوَٰنِ وَإِن يَأۡتُوكُمۡ أُسَٰرَىٰ تُفَٰدُوهُمۡ وَهُوَ مُحَرَّمٌ عَلَيۡكُمۡ إِخۡرَاجُهُمۡۚ أَفَتُؤۡمِنُونَ بِبَعۡضِ ٱلۡكِتَٰبِ وَتَكۡفُرُونَ بِبَعۡضٖۚ فَمَا جَزَآءُ مَن يَفۡعَلُ ذَٰلِكَ مِنكُمۡ إِلَّا خِزۡيٞ فِي ٱلۡحَيَوٰةِ ٱلدُّنۡيَاۖ وَيَوۡمَ ٱلۡقِيَٰمَةِ يُرَدُّونَ إِلَىٰٓ أَشَدِّ ٱلۡعَذَابِۗ وَمَا ٱللَّهُ بِغَٰفِلٍ عَمَّا تَعۡمَلُونَ ﴾
[البَقَرَة: 85]
﴿ثم أنتم هؤلاء تقتلون أنفسكم وتخرجون فريقا منكم من ديارهم تظاهرون عليهم﴾ [البَقَرَة: 85]
Khaled Ibrahim Betala “Tsono inu nomwe ndi amene mukuphana ndikuwatulutsa ena a inu m’nyumba zawo; mukuthandiza adani anu powachitira (abale anu masautso) mwauchimo ndi molumpha malire. Koma akakudzerani akaidi ogwidwa ku nkhondo, mukuwaombola, pomwe nkoletsedwa kwa inu kuwatulutsa. Kodi mukukhulupirira mbali ina ya buku, mbali ina nkuikana? Choncho palibe mphoto kwa ochita izi mwa inu koma kuyaluka pamoyo wa pa dziko lapansi; ndipo tsiku la chiweruziro adzalowetsedwa ku chilango chokhwima kwambiri. Ndipo Allah sali wonyalanyaza zimene mukuchita |