حم (1) Ha Mim |
وَالْكِتَابِ الْمُبِينِ (2) Ndilumbira pali Buku limene limanena zoona |
إِنَّا أَنزَلْنَاهُ فِي لَيْلَةٍ مُّبَارَكَةٍ ۚ إِنَّا كُنَّا مُنذِرِينَ (3) Ife tidalivumbulutsa ilo mu usiku wodalitsika. Ndithudi Ife tili kupitirizabe kuchenjeza |
فِيهَا يُفْرَقُ كُلُّ أَمْرٍ حَكِيمٍ (4) Mu umenewu, ntchito iliyonse ili kuonetsedwa poyera |
أَمْرًا مِّنْ عِندِنَا ۚ إِنَّا كُنَّا مُرْسِلِينَ (5) Lamulo lochokera kwa Ife, ndithudi Ife timatumiza |
رَحْمَةً مِّن رَّبِّكَ ۚ إِنَّهُ هُوَ السَّمِيعُ الْعَلِيمُ (6) Chifundo chochokera kwa Ambuye wako, ndithudi Iye ndi wakumva ndi wodziwa |
رَبِّ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَمَا بَيْنَهُمَا ۖ إِن كُنتُم مُّوقِنِينَ (7) Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo, ngati inu nonse mutakhala ndi chikhulupiriro chenicheni |
لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ يُحْيِي وَيُمِيتُ ۖ رَبُّكُمْ وَرَبُّ آبَائِكُمُ الْأَوَّلِينَ (8) Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Ndipo ndiye amene amapereka moyo ndi imfa. Ambuye wako ndi Ambuye wa makolo ako amene adanka kale |
بَلْ هُمْ فِي شَكٍّ يَلْعَبُونَ (9) Iyayi! Iwo amakayika, amasewerera |
فَارْتَقِبْ يَوْمَ تَأْتِي السَّمَاءُ بِدُخَانٍ مُّبِينٍ (10) Motero dikirani tsiku limene kumwamba kudzatsitsa utsi wooneka |
يَغْشَى النَّاسَ ۖ هَٰذَا عَذَابٌ أَلِيمٌ (11) Umene udzazungulira anthu ndipo chimenechi ndi chilango chowawa |
رَّبَّنَا اكْشِفْ عَنَّا الْعَذَابَ إِنَّا مُؤْمِنُونَ (12) Iwo adzati, “Ambuye wathu! Tichotsereni chilango ichi chifukwa tsopano takhulupirira.” |
أَنَّىٰ لَهُمُ الذِّكْرَىٰ وَقَدْ جَاءَهُمْ رَسُولٌ مُّبِينٌ (13) Kodi iwo angachenjezedwe bwanji pamene kunadza kale Mtumwi amene anali kuwauza choonadi |
ثُمَّ تَوَلَّوْا عَنْهُ وَقَالُوا مُعَلَّمٌ مَّجْنُونٌ (14) Iwo adamutembenukira ndi kumati, “Munthu wophunzitsidwa ndi anthu ena, munthu wamisala.” |
إِنَّا كَاشِفُو الْعَذَابِ قَلِيلًا ۚ إِنَّكُمْ عَائِدُونَ (15) Ndithudi Ife tidzachotsa chilango pa kanthawi kochepa koma ndithudi inu mudzabwerera |
يَوْمَ نَبْطِشُ الْبَطْشَةَ الْكُبْرَىٰ إِنَّا مُنتَقِمُونَ (16) Patsiku limene Ife tidzakugwirani mwamphamvu. Ndithudi tidzawabwezera chilango choyenera |
۞ وَلَقَدْ فَتَنَّا قَبْلَهُمْ قَوْمَ فِرْعَوْنَ وَجَاءَهُمْ رَسُولٌ كَرِيمٌ (17) Ndipo, ndithudi, tidawayesa anthu a Farawo, iwo asanabadwe, ndipo kudadza kwa iwo Mtumwi wolemekezeka |
أَنْ أَدُّوا إِلَيَّ عِبَادَ اللَّهِ ۖ إِنِّي لَكُمْ رَسُولٌ أَمِينٌ (18) Naati “Bweretsani kwa ine akapolo a Mulungu.” “Ndithudi ine ndine Mtumwi wokhulupirika kwa inu.” |
وَأَن لَّا تَعْلُوا عَلَى اللَّهِ ۖ إِنِّي آتِيكُم بِسُلْطَانٍ مُّبِينٍ (19) “Ndipo musachitire mwano Mulungu. Ndithudi ine ndadza kwa inu ndi ulamuliro wooneka.” |
وَإِنِّي عُذْتُ بِرَبِّي وَرَبِّكُمْ أَن تَرْجُمُونِ (20) “Ndipo ndithudi ine ndapempha chitetezo cha Ambuye wanga ndi Ambuye wanu kuti musandiononge.” |
وَإِن لَّمْ تُؤْمِنُوا لِي فَاعْتَزِلُونِ (21) “Koma ngati inu simundikhulupirira ine, ndiye mundisiye ndekha.” |
فَدَعَا رَبَّهُ أَنَّ هَٰؤُلَاءِ قَوْمٌ مُّجْرِمُونَ (22) Ndipo iye anati kwa Ambuye wake, “Anthu awa ndi ochimwa.” |
فَأَسْرِ بِعِبَادِي لَيْلًا إِنَّكُم مُّتَّبَعُونَ (23) Choka iwe ndi akapolo anga nthawi yausiku. Ndithudi iwe udzalondoledwa |
وَاتْرُكِ الْبَحْرَ رَهْوًا ۖ إِنَّهُمْ جُندٌ مُّغْرَقُونَ (24) “Ileke nyanja kukhala monga mmene ili. Ndithudi iwo ndi anthu amene adzamizidwa.” |
كَمْ تَرَكُوا مِن جَنَّاتٍ وَعُيُونٍ (25) Kodi ndi minda ingati ndiponso a kasupe angati amene iwo adasiya |
وَزُرُوعٍ وَمَقَامٍ كَرِيمٍ (26) Ndi minda ya chimanga ndi malo olemekezeka |
وَنَعْمَةٍ كَانُوا فِيهَا فَاكِهِينَ (27) Ndi zinthu zabwino zimene amasangalala nazo |
كَذَٰلِكَ ۖ وَأَوْرَثْنَاهَا قَوْمًا آخَرِينَ (28) Kotero zinali choncho. Ndipo Ife tidawasankha anthu ena kuti atenge zinthu zawo |
فَمَا بَكَتْ عَلَيْهِمُ السَّمَاءُ وَالْأَرْضُ وَمَا كَانُوا مُنظَرِينَ (29) Kumwamba kapena dziko lapansi silidakhetse msozi chifukwa cha iwo ndipo iwo sadapatsidwe mpumulo |
وَلَقَدْ نَجَّيْنَا بَنِي إِسْرَائِيلَ مِنَ الْعَذَابِ الْمُهِينِ (30) Ndithudi tidapulumutsa ana a Israyeli ku chilango chochititsa manyazi |
مِن فِرْعَوْنَ ۚ إِنَّهُ كَانَ عَالِيًا مِّنَ الْمُسْرِفِينَ (31) Chimene chidaperekedwa ndi Farawo. Ndithudi iye adali wamwano ndi mmodzi wa anthu oswa malamulo |
وَلَقَدِ اخْتَرْنَاهُمْ عَلَىٰ عِلْمٍ عَلَى الْعَالَمِينَ (32) Ndithudi tidawasankha iwo kuti akhale ndi nzeru kuposa mitundu ina |
وَآتَيْنَاهُم مِّنَ الْآيَاتِ مَا فِيهِ بَلَاءٌ مُّبِينٌ (33) Ndipo tidawapatsa chivumbulutso chimene chidali ndi mayesero ooneka |
إِنَّ هَٰؤُلَاءِ لَيَقُولُونَ (34) Ndithudi iwo akuti |
إِنْ هِيَ إِلَّا مَوْتَتُنَا الْأُولَىٰ وَمَا نَحْنُ بِمُنشَرِينَ (35) “Palibe china chilichonse kupatula imfa yathu yoyamba ndipo ife sitidzaukitsidwa kwa akufa.” |
فَأْتُوا بِآبَائِنَا إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (36) “Kotero bweretsa makolo athu ngati zimene ukunena ndi zoona!” |
أَهُمْ خَيْرٌ أَمْ قَوْمُ تُبَّعٍ وَالَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۚ أَهْلَكْنَاهُمْ ۖ إِنَّهُمْ كَانُوا مُجْرِمِينَ (37) Kodi awa ndi opambana kuposa anthu a Tubba ndi iwo amene adalipo kale? Ife tidawaononga onse ndipo iwo adali olakwa |
وَمَا خَلَقْنَا السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ وَمَا بَيْنَهُمَا لَاعِبِينَ (38) Ndipo ife sitidalenge kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo mwamasewera |
مَا خَلَقْنَاهُمَا إِلَّا بِالْحَقِّ وَلَٰكِنَّ أَكْثَرَهُمْ لَا يَعْلَمُونَ (39) Ife sitidazilenge zonsezi kupatula mwachoonadi ndipo ambiri a iwo sadziwa |
إِنَّ يَوْمَ الْفَصْلِ مِيقَاتُهُمْ أَجْمَعِينَ (40) Ndithudi tsiku lachimaliziro ndi tsiku lomaliza kwa iwo onse |
يَوْمَ لَا يُغْنِي مَوْلًى عَن مَّوْلًى شَيْئًا وَلَا هُمْ يُنصَرُونَ (41) Ndi tsiku limene bwenzi sadzakumbukira bwenzi ake ndipo sadzalandira chithandizo |
إِلَّا مَن رَّحِمَ اللَّهُ ۚ إِنَّهُ هُوَ الْعَزِيزُ الرَّحِيمُ (42) Kupatula yekhawo amene waonetsedwa chisomo cha Mulungu. Ndithudi Iye ndiye Mwini mphamvu ndi Mwini chisoni chosatha |
إِنَّ شَجَرَتَ الزَّقُّومِ (43) Ndithudi mtengo wa Zaqqum |
طَعَامُ الْأَثِيمِ (44) Udzakhala chakudya cha anthu ochimwa |
كَالْمُهْلِ يَغْلِي فِي الْبُطُونِ (45) Monga mafuta owira, chidzabwata m’mimba mwawo |
كَغَلْيِ الْحَمِيمِ (46) Monga ngati madzi ogaduka |
خُذُوهُ فَاعْتِلُوهُ إِلَىٰ سَوَاءِ الْجَحِيمِ (47) “Mugwire iye ndipo mududuzireni m’kati mwa Gahena.” |
ثُمَّ صُبُّوا فَوْقَ رَأْسِهِ مِنْ عَذَابِ الْحَمِيمِ (48) Ndipo thirani pamutu pake chilango cha madzi owira |
ذُقْ إِنَّكَ أَنتَ الْعَزِيزُ الْكَرِيمُ (49) “Lawani ichi! Ndithudi inu munali amphamvu ndi aulemu.” |
إِنَّ هَٰذَا مَا كُنتُم بِهِ تَمْتَرُونَ (50) “Ndithudi! Ichi ndicho chimene munali kukayika.” |
إِنَّ الْمُتَّقِينَ فِي مَقَامٍ أَمِينٍ (51) “Ndithudi! Iwo amene amalewa zoipa adzakhala kumalo otetezedwa.” |
فِي جَنَّاتٍ وَعُيُونٍ (52) Pakati pa minda ndi a kasupe |
يَلْبَسُونَ مِن سُندُسٍ وَإِسْتَبْرَقٍ مُّتَقَابِلِينَ (53) Iwo atavala Silika wokhuthala ndi wokongola, atakhala moyang’anizana |
كَذَٰلِكَ وَزَوَّجْنَاهُم بِحُورٍ عِينٍ (54) Kotero zidzakhala choncho ndipo Ife tidzawakwatitsa kwa akazi a maso aakuluakulu okongola |
يَدْعُونَ فِيهَا بِكُلِّ فَاكِهَةٍ آمِنِينَ (55) Iwo adzaitanitsa chipatso cha mtundu uliwonse mwamtendere ndi mokhazikika |
لَا يَذُوقُونَ فِيهَا الْمَوْتَ إِلَّا الْمَوْتَةَ الْأُولَىٰ ۖ وَوَقَاهُمْ عَذَابَ الْجَحِيمِ (56) Ndipo iwo sadzalawa imfa kupatula imfa yoyamba ndipo Iye adzawapulumutsa ku chilango chowawa cha Gahena |
فَضْلًا مِّن رَّبِّكَ ۚ ذَٰلِكَ هُوَ الْفَوْزُ الْعَظِيمُ (57) Chisomo chochokera kwa Ambuye wako! Chimenechi chidzakhala chinthu chopambana kwambiri |
فَإِنَّمَا يَسَّرْنَاهُ بِلِسَانِكَ لَعَلَّهُمْ يَتَذَكَّرُونَ (58) Ndithudi Ife taipanga Koraniyi kukhala yapafupi m’chiyankhulo chako ndi cholinga chakuti mwina angathe kukumbukira |
فَارْتَقِبْ إِنَّهُم مُّرْتَقِبُونَ (59) Kotero iwe dikira chifukwa nawonso ali kudikira |