وَالذَّارِيَاتِ ذَرْوًا (1) Pali mphepo imene imamwaza fumbi |
فَالْحَامِلَاتِ وِقْرًا (2) Ndi mitambo imene ili yolemedwa ndi madzi |
فَالْجَارِيَاتِ يُسْرًا (3) Ndi zombo zimene zimayenda mosavutika ndi mwabata |
فَالْمُقَسِّمَاتِ أَمْرًا (4) Ndipo pali iwo amene amagawa madalitso ndi chilolezo chathu |
إِنَّمَا تُوعَدُونَ لَصَادِقٌ (5) Ndithudi chimene mwalonjezedwa, ndithudi, ndi choona |
وَإِنَّ الدِّينَ لَوَاقِعٌ (6) Ndithudi chiweruzo chidzakwaniritsidwa |
وَالسَّمَاءِ ذَاتِ الْحُبُكِ (7) Pali kumwamba kumene kuli njira zambiri |
إِنَّكُمْ لَفِي قَوْلٍ مُّخْتَلِفٍ (8) Ndithudi inu muli ndi maganizo osiyana |
يُؤْفَكُ عَنْهُ مَنْ أُفِكَ (9) Amene abwezedwa ku icho ndiye amene wabwezedwa |
قُتِلَ الْخَرَّاصُونَ (10) wotembereredwa akhale amene amanama |
الَّذِينَ هُمْ فِي غَمْرَةٍ سَاهُونَ (11) Amene akutidwa ndi kusamvera |
يَسْأَلُونَ أَيَّانَ يَوْمُ الدِّينِ (12) Iwo amafunsa kuti, “Kodi tsiku lachiweruzo lidzadza liti?” |
يَوْمَ هُمْ عَلَى النَّارِ يُفْتَنُونَ (13) Tsiku limene iwo adzaweruzidwa ndi kuponyedwa ku Zariat 559 moto |
ذُوقُوا فِتْنَتَكُمْ هَٰذَا الَّذِي كُنتُم بِهِ تَسْتَعْجِلُونَ (14) Lawani chilango chanu! Ichi ndicho chimene munali kufuna kuti chidze msanga |
إِنَّ الْمُتَّقِينَ فِي جَنَّاتٍ وَعُيُونٍ (15) Ndithudi iwo amene amalewa machimo adzakhala m’minda imene ili ndi a kasupe |
آخِذِينَ مَا آتَاهُمْ رَبُّهُمْ ۚ إِنَّهُمْ كَانُوا قَبْلَ ذَٰلِكَ مُحْسِنِينَ (16) Kulandira zimene Ambuye wawo awapatsa. Ndithudi kale iwo anali kuchita zinthu zabwino |
كَانُوا قَلِيلًا مِّنَ اللَّيْلِ مَا يَهْجَعُونَ (17) Iwo anali kugona nthawi yochepa usiku |
وَبِالْأَسْحَارِ هُمْ يَسْتَغْفِرُونَ (18) Ndipo m’bandakucha anali kupempha chikhululukiro |
وَفِي أَمْوَالِهِمْ حَقٌّ لِّلسَّائِلِ وَالْمَحْرُومِ (19) Ndipo mu chuma chawo mudali gawo limene linali kuperekedwa kwa anthu opempha ndi osowa |
وَفِي الْأَرْضِ آيَاتٌ لِّلْمُوقِنِينَ (20) Ndipo m’dziko muli zizindikiro kwa iwo okhulupirira |
وَفِي أَنفُسِكُمْ ۚ أَفَلَا تُبْصِرُونَ (21) Ndi mizimu yanu kodi simungaone |
وَفِي السَّمَاءِ رِزْقُكُمْ وَمَا تُوعَدُونَ (22) Ndipo kumwamba ndiko kuli chakudya chanu ndi zimene muli kulonjezedwa |
فَوَرَبِّ السَّمَاءِ وَالْأَرْضِ إِنَّهُ لَحَقٌّ مِّثْلَ مَا أَنَّكُمْ تَنطِقُونَ (23) Ndiye, pali Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chimenechi ndi cholinga ndi choonadi chomwe inu mumayankhula |
هَلْ أَتَاكَ حَدِيثُ ضَيْفِ إِبْرَاهِيمَ الْمُكْرَمِينَ (24) Kodi udamva nkhani ya alendo olemekezeka a Abrahamu |
إِذْ دَخَلُوا عَلَيْهِ فَقَالُوا سَلَامًا ۖ قَالَ سَلَامٌ قَوْمٌ مُّنكَرُونَ (25) Pamene iwo adadza kwa iye, iwo adati, “Mtendere.” Ndipo iye adati, “Mtendere.” Ndipo iye adati, “Inu ndinu alendo kwa ine.” |
فَرَاغَ إِلَىٰ أَهْلِهِ فَجَاءَ بِعِجْلٍ سَمِينٍ (26) Ndipo iye atapita ku banja lake adabweretsa nyama ya ng’ombe yowotcha |
فَقَرَّبَهُ إِلَيْهِمْ قَالَ أَلَا تَأْكُلُونَ (27) Motero iye adadza nayo kwa iwo nati, “Kodi simufuna kudya?” |
فَأَوْجَسَ مِنْهُمْ خِيفَةً ۖ قَالُوا لَا تَخَفْ ۖ وَبَشَّرُوهُ بِغُلَامٍ عَلِيمٍ (28) Motero iye adayamba kuchita mantha mu mtima mwake. Ndipo iwo adati, “Usaope.” Ndipo iwo adamuuza nkhani yabwino yakubadwa kwa mwana wamwamuna yemwe adzakhala wanzeru kwambiri |
فَأَقْبَلَتِ امْرَأَتُهُ فِي صَرَّةٍ فَصَكَّتْ وَجْهَهَا وَقَالَتْ عَجُوزٌ عَقِيمٌ (29) Ndipo mkazi wake adadza modzichepetsa ndipo adamenya pa mphumi pake nati, “Nkhalamba yaikazi yosaberekapo!” |
قَالُوا كَذَٰلِكِ قَالَ رَبُّكِ ۖ إِنَّهُ هُوَ الْحَكِيمُ الْعَلِيمُ (30) Iwo adati, “Ngakhale ndi choncho, Ambuye wako wayankhula. Iye ndi wodzala ndi luntha ndiponso nzeru.” |
۞ قَالَ فَمَا خَطْبُكُمْ أَيُّهَا الْمُرْسَلُونَ (31) Iye adati, “Kodi inu Atumwi uthenga wanu ndi wotani?” |
قَالُوا إِنَّا أُرْسِلْنَا إِلَىٰ قَوْمٍ مُّجْرِمِينَ (32) Iwo adati, “Ife tatumidwa kwa anthu ochimwa.” |
لِنُرْسِلَ عَلَيْهِمْ حِجَارَةً مِّن طِينٍ (33) “Kuti tigwetse pa iwo miyala yamakande.” |
مُّسَوَّمَةً عِندَ رَبِّكَ لِلْمُسْرِفِينَ (34) “Idakonzedwa ndi Ambuye wako kudza kwa anthu oswa malamulo.” |
فَأَخْرَجْنَا مَن كَانَ فِيهَا مِنَ الْمُؤْمِنِينَ (35) Ndipo Ife tidatulutsa anthu okhulupirira amene adali momwemo |
فَمَا وَجَدْنَا فِيهَا غَيْرَ بَيْتٍ مِّنَ الْمُسْلِمِينَ (36) Koma sitidapezemo mabanja a Chisilamu kupatula banja limodzi lokha basi |
وَتَرَكْنَا فِيهَا آيَةً لِّلَّذِينَ يَخَافُونَ الْعَذَابَ الْأَلِيمَ (37) Ndipo Ife tidasiyamo chizindikiro kwa iwo amene amaopa chilango chowawa |
وَفِي مُوسَىٰ إِذْ أَرْسَلْنَاهُ إِلَىٰ فِرْعَوْنَ بِسُلْطَانٍ مُّبِينٍ (38) Ndi mwa Mose. Pamene tidamutumiza kwa Farawo ndi zizindikiro zooneka |
فَتَوَلَّىٰ بِرُكْنِهِ وَقَالَ سَاحِرٌ أَوْ مَجْنُونٌ (39) Koma Farawo adakana pamodzi ndi mafumu ake nati, “Ndiwe munthu wamatsenga kapena munthu wa misala.” |
فَأَخَذْنَاهُ وَجُنُودَهُ فَنَبَذْنَاهُمْ فِي الْيَمِّ وَهُوَ مُلِيمٌ (40) Motero tidamugwira pamodzi ndi gulu la asirikali ake ndi kuwamiza onse m’nyanja pamene iye ndiye adali wolakwa |
وَفِي عَادٍ إِذْ أَرْسَلْنَا عَلَيْهِمُ الرِّيحَ الْعَقِيمَ (41) Ndipo mwa a Aad pamene tidawatumizira mphepo yoononga |
مَا تَذَرُ مِن شَيْءٍ أَتَتْ عَلَيْهِ إِلَّا جَعَلَتْهُ كَالرَّمِيمِ (42) Imene sidasiye chilichonse chimene idalimbana nacho kupatula kuchiononga ndi kuchisandutsa phulusa |
وَفِي ثَمُودَ إِذْ قِيلَ لَهُمْ تَمَتَّعُوا حَتَّىٰ حِينٍ (43) Ndipo mwa anthu a Thamoud. Pamene adauzidwa kuti, “Basangalalani kanthawi kochepa.” |
فَعَتَوْا عَنْ أَمْرِ رَبِّهِمْ فَأَخَذَتْهُمُ الصَّاعِقَةُ وَهُمْ يَنظُرُونَ (44) Koma iwo adaphwanya lamulo la Ambuye wawo mwamwano, kotero mabingu adawaononga iwo ali kuona |
فَمَا اسْتَطَاعُوا مِن قِيَامٍ وَمَا كَانُوا مُنتَصِرِينَ (45) Kotero iwo adalibe mphamvu zodzuka kapena zodzitetezera |
وَقَوْمَ نُوحٍ مِّن قَبْلُ ۖ إِنَّهُمْ كَانُوا قَوْمًا فَاسِقِينَ (46) Ndi anthu a Nowa iwo asanadze. Ndithudi iwo adali anthu oswa malamulo |
وَالسَّمَاءَ بَنَيْنَاهَا بِأَيْدٍ وَإِنَّا لَمُوسِعُونَ (47) Ife tidakonza kumwamba mwamphamvu ndiponso mwaluso. Ndipo, ndithudi, ndife amene timapanga kukula kwa mlengalenga |
وَالْأَرْضَ فَرَشْنَاهَا فَنِعْمَ الْمَاهِدُونَ (48) Ndipo dziko, tidamwaza. Kodi ndife omwaza bwino bwanji |
وَمِن كُلِّ شَيْءٍ خَلَقْنَا زَوْجَيْنِ لَعَلَّكُمْ تَذَكَّرُونَ (49) Ndipo zonse zimene tidalenga tidazilenga ziwiriziwiri kuti mukhoza kukumbukira |
فَفِرُّوا إِلَى اللَّهِ ۖ إِنِّي لَكُم مِّنْهُ نَذِيرٌ مُّبِينٌ (50) Kotero thawirani kwa Mulungu. Ndithudi Ine ndine mchenjezi wooneka kwa inu wochokera kwa Iye |
وَلَا تَجْعَلُوا مَعَ اللَّهِ إِلَٰهًا آخَرَ ۖ إِنِّي لَكُم مِّنْهُ نَذِيرٌ مُّبِينٌ (51) Ndipo musapange fano kukhala lopembedzedwa pamodzi ndi Mulungu. Ndithudi ine ndine mchenjezi wooneka kwa inu wochokera kwa Iye |
كَذَٰلِكَ مَا أَتَى الَّذِينَ مِن قَبْلِهِم مِّن رَّسُولٍ إِلَّا قَالُوا سَاحِرٌ أَوْ مَجْنُونٌ (52) Chimodzimodzi palibe Mtumwi amene adadza kwa anthu amene sadamunenere mawu ofanana monga akuti: “Wamatsenga kapena munthu wopenga!” |
أَتَوَاصَوْا بِهِ ۚ بَلْ هُمْ قَوْمٌ طَاغُونَ (53) Kodi uwu ndi mwambo umene akhala ali kusiyirana wina ndi mnzake? Iyayi, iwo ndi anthu amene ali kuswa malamulo mopyola muyeso |
فَتَوَلَّ عَنْهُمْ فَمَا أَنتَ بِمَلُومٍ (54) Kotero uwaleke chifukwa iwe ulibe mlandu |
وَذَكِّرْ فَإِنَّ الذِّكْرَىٰ تَنفَعُ الْمُؤْمِنِينَ (55) Ndipo kumbutsa chifukwa chikumbutso chimathandiza anthu okhulupirira |
وَمَا خَلَقْتُ الْجِنَّ وَالْإِنسَ إِلَّا لِيَعْبُدُونِ (56) Ndipo Ine ndidalenga majini ndi anthu kuti azindipembedza Ine |
مَا أُرِيدُ مِنْهُم مِّن رِّزْقٍ وَمَا أُرِيدُ أَن يُطْعِمُونِ (57) Ine sindiwapempha chakudya ndipo sindiwafunsa kuti azindidyetsa Ine |
إِنَّ اللَّهَ هُوَ الرَّزَّاقُ ذُو الْقُوَّةِ الْمَتِينُ (58) Ndithudi ndi Mulungu yekha amene amapereka chakudya chonse, Mwini mphamvu zonse ndi wolimba kwambiri |
فَإِنَّ لِلَّذِينَ ظَلَمُوا ذَنُوبًا مِّثْلَ ذَنُوبِ أَصْحَابِهِمْ فَلَا يَسْتَعْجِلُونِ (59) Ndithudi anthu onse olakwa adzalandira gawo longa limene anzawo olakwa akale adalandira, kotero asandifunse Ine kuchita mofulumira |
فَوَيْلٌ لِّلَّذِينَ كَفَرُوا مِن يَوْمِهِمُ الَّذِي يُوعَدُونَ (60) Kotero tsoka kwa onse osakhulupirira kuchokera ku tsiku lomwe iwo alonjezedwa |