×

Surah Qaf in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Qaf

Translation of the Meanings of Surah Qaf in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Qaf translated into Chichewa, Surah Qaf in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Qaf in Chichewa - نيانجا, Verses 45 - Surah Number 50 - Page 518.

بسم الله الرحمن الرحيم

ق ۚ وَالْقُرْآنِ الْمَجِيدِ (1)
Qaf. Pali Buku lolemekezeka la Korani
بَلْ عَجِبُوا أَن جَاءَهُم مُّنذِرٌ مِّنْهُمْ فَقَالَ الْكَافِرُونَ هَٰذَا شَيْءٌ عَجِيبٌ (2)
Koma iwo alikudabwa kuti kwa iwo kwadza mchenjezi wochokera pakati pawo. Motero anthu osakhulupirira amati, “chimenechi ndi chinthu chachilendo!”
أَإِذَا مِتْنَا وَكُنَّا تُرَابًا ۖ ذَٰلِكَ رَجْعٌ بَعِيدٌ (3)
“Pamene ife tafa ndi kusanduka dothi, kubwerera kotero ndi kosatheka.”
قَدْ عَلِمْنَا مَا تَنقُصُ الْأَرْضُ مِنْهُمْ ۖ وَعِندَنَا كِتَابٌ حَفِيظٌ (4)
Ife timadziwa onse amene adamezedwa ndi nthaka ndipo Ife tili ndi Buku la mbiri yawo
بَلْ كَذَّبُوا بِالْحَقِّ لَمَّا جَاءَهُمْ فَهُمْ فِي أَمْرٍ مَّرِيجٍ (5)
Iyayi, koma iwo adakana choonadi pamene chidadza kwa iwo. Kotero iwo, tsopano, asokonezeka
أَفَلَمْ يَنظُرُوا إِلَى السَّمَاءِ فَوْقَهُمْ كَيْفَ بَنَيْنَاهَا وَزَيَّنَّاهَا وَمَا لَهَا مِن فُرُوجٍ (6)
Kodi iwo sayang’ana kumwamba ndi kuona mmene tidakukonzera ndi kukukongoletsera ndi kuona kuti kulibe mipata
وَالْأَرْضَ مَدَدْنَاهَا وَأَلْقَيْنَا فِيهَا رَوَاسِيَ وَأَنبَتْنَا فِيهَا مِن كُلِّ زَوْجٍ بَهِيجٍ (7)
Ndipo dziko lapansi Ife talipanga kukhala losalala ndi kuikamo mapiri ndipo tidameretsa mu dzikolo mbewu zokongola zosiyanasiyana
تَبْصِرَةً وَذِكْرَىٰ لِكُلِّ عَبْدٍ مُّنِيبٍ (8)
Choonetsa ndi chikumbutso kwa kapolo aliyense amene amatembenukira nthawi zonse kwa Mulungu
وَنَزَّلْنَا مِنَ السَّمَاءِ مَاءً مُّبَارَكًا فَأَنبَتْنَا بِهِ جَنَّاتٍ وَحَبَّ الْحَصِيدِ (9)
Ndipo timatumiza kuchokera ku mitambo mvula yodalitsika ndipo timameretsa m’minda mbewu zimene zimakololedwa
وَالنَّخْلَ بَاسِقَاتٍ لَّهَا طَلْعٌ نَّضِيدٌ (10)
Ndi mitengo italiitali ya tende yolemedwa ndi zipatso
رِّزْقًا لِّلْعِبَادِ ۖ وَأَحْيَيْنَا بِهِ بَلْدَةً مَّيْتًا ۚ كَذَٰلِكَ الْخُرُوجُ (11)
Chakudya cha akapolo. Ndipo Ife timapereka moyo kunthaka imene idali yakufa. Kumeneko ndiko kuuka kwa akufa
كَذَّبَتْ قَبْلَهُمْ قَوْمُ نُوحٍ وَأَصْحَابُ الرَّسِّ وَثَمُودُ (12)
Adakana iwo asanadze, anthu a Nowa ndi iwo amene anali kukhala ku Ar-rass ndi Thamoud
وَعَادٌ وَفِرْعَوْنُ وَإِخْوَانُ لُوطٍ (13)
Anthu a mtundu wa Aad ndi Farawo ndi abale ake a Loti
وَأَصْحَابُ الْأَيْكَةِ وَقَوْمُ تُبَّعٍ ۚ كُلٌّ كَذَّبَ الرُّسُلَ فَحَقَّ وَعِيدِ (14)
Ndi iwo amene anali kukhala m’nkhalango ndi anthu a ku Tuba, aliyense wa iwo adakana Atumwi ndipo chenjezo langa lidakwaniritsidwa
أَفَعَيِينَا بِالْخَلْقِ الْأَوَّلِ ۚ بَلْ هُمْ فِي لَبْسٍ مِّنْ خَلْقٍ جَدِيدٍ (15)
Kodi Ife tidatopa ndi chilengedwe choyamba? Iyayi. Iwo asokonezeka ndi nkhani zokhudza chilengedwe chatsopano
وَلَقَدْ خَلَقْنَا الْإِنسَانَ وَنَعْلَمُ مَا تُوَسْوِسُ بِهِ نَفْسُهُ ۖ وَنَحْنُ أَقْرَبُ إِلَيْهِ مِنْ حَبْلِ الْوَرِيدِ (16)
Ndithudi Ife tidamulenga munthu ndipo timadziwa zimene mtima wake umamuuza. Ndipo Ife tili pafupi ndi iye kuposa mtsempha wa moyo wake
إِذْ يَتَلَقَّى الْمُتَلَقِّيَانِ عَنِ الْيَمِينِ وَعَنِ الشِّمَالِ قَعِيدٌ (17)
Pamene asungi awiri amulandira, wina atakhala kudzanja lamanja ndi wina ku dzanja lamanzere
مَّا يَلْفِظُ مِن قَوْلٍ إِلَّا لَدَيْهِ رَقِيبٌ عَتِيدٌ (18)
Palibe mawu amene amayankhula amene samveka kwa Msungi wa tcheru
وَجَاءَتْ سَكْرَةُ الْمَوْتِ بِالْحَقِّ ۖ ذَٰلِكَ مَا كُنتَ مِنْهُ تَحِيدُ (19)
Ndipo ululu wa imfa udzadza pa iye mwachoonadi. Ichi ndicho chimene iwe unali kuyesetsa kuchithawa
وَنُفِخَ فِي الصُّورِ ۚ ذَٰلِكَ يَوْمُ الْوَعِيدِ (20)
Ndipo lipenga lidzaombedwa ndipo limeneli lidzakhala tsiku loopseza
وَجَاءَتْ كُلُّ نَفْسٍ مَّعَهَا سَائِقٌ وَشَهِيدٌ (21)
Ndipo mzimu uliwonse udzadza pamodzi ndi mngelo wouyendetsa ndi mngelo wochitira umboni
لَّقَدْ كُنتَ فِي غَفْلَةٍ مِّنْ هَٰذَا فَكَشَفْنَا عَنكَ غِطَاءَكَ فَبَصَرُكَ الْيَوْمَ حَدِيدٌ (22)
(Ndipo kudzanenedwa kwa anthu ochimwa) kuti, “Ndithudi inu simudafune kuchenjezedwa za chimenechi ndipotsopano Ifetavundukulachimenechimakuphimbani. Ndipo lero maso anu ali kuona zenizeni.”
وَقَالَ قَرِينُهُ هَٰذَا مَا لَدَيَّ عَتِيدٌ (23)
Ndipo mnzake adzati, “Uwu ndi umboni umene ndili nawo.”
أَلْقِيَا فِي جَهَنَّمَ كُلَّ كَفَّارٍ عَنِيدٍ (24)
“Ponyani ku Gahena aliyense wosathokoza ndiponso wosamvera.”
مَّنَّاعٍ لِّلْخَيْرِ مُعْتَدٍ مُّرِيبٍ (25)
“Woletsa kuchita ntchito zabwino, woswa malamulo ndiponso wokayika.”
الَّذِي جَعَلَ مَعَ اللَّهِ إِلَٰهًا آخَرَ فَأَلْقِيَاهُ فِي الْعَذَابِ الشَّدِيدِ (26)
“Iye amene anali kukhazikitsa milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni, motero mponyeni ku chilango chowawa.”
۞ قَالَ قَرِينُهُ رَبَّنَا مَا أَطْغَيْتُهُ وَلَٰكِن كَانَ فِي ضَلَالٍ بَعِيدٍ (27)
Mnzake adzanena kuti, “Ambuye wathu! Ine sindidamuuze kuti aziswa malamulo ayi koma iye adadzisocheretsa yekha.”
قَالَ لَا تَخْتَصِمُوا لَدَيَّ وَقَدْ قَدَّمْتُ إِلَيْكُم بِالْوَعِيدِ (28)
Mulungu adzati, “Musakangane pamaso panga. Ine ndidakutumizirani chenjezo lokwanira.”
مَا يُبَدَّلُ الْقَوْلُ لَدَيَّ وَمَا أَنَا بِظَلَّامٍ لِّلْعَبِيدِ (29)
Chilango sichisintha ayi ndipo Ine sindionetsa chinyengo kwa akapolo anga
يَوْمَ نَقُولُ لِجَهَنَّمَ هَلِ امْتَلَأْتِ وَتَقُولُ هَلْ مِن مَّزِيدٍ (30)
Patsiku limene Ife tidzaifunsa Gahena kuti, “Kodi mwadzadza?” Ndipo iyo idzati, “Kodi akanalipobe ena?”
وَأُزْلِفَتِ الْجَنَّةُ لِلْمُتَّقِينَ غَيْرَ بَعِيدٍ (31)
Ndipo Paradiso idzabweretsedwa kufupi kwa anthu olungama
هَٰذَا مَا تُوعَدُونَ لِكُلِّ أَوَّابٍ حَفِيظٍ (32)
Ichi ndicho chimene mudalonjezedwa ndipo ndi mphotho kwa iye amene amadzipereka kwa Mulungu nthawi zonse nasunga malamulo ake
مَّنْ خَشِيَ الرَّحْمَٰنَ بِالْغَيْبِ وَجَاءَ بِقَلْبٍ مُّنِيبٍ (33)
Ndiponso kwa iye amene amaopa Mwini chisoni chosatha wosaoneka ndipo amadza kwa Iye ndi mtima wodzichepetsa
ادْخُلُوهَا بِسَلَامٍ ۖ ذَٰلِكَ يَوْمُ الْخُلُودِ (34)
Lowani m’menemo mwamtendere ndi mosaopa ayi. Ili ndi tsiku la moyo wosatha
لَهُم مَّا يَشَاءُونَ فِيهَا وَلَدَيْنَا مَزِيدٌ (35)
M’menemo mudzakhala chilichonse chimene iwo adzafuna ndipo Ife tili ndi zinthu zambiri
وَكَمْ أَهْلَكْنَا قَبْلَهُم مِّن قَرْنٍ هُمْ أَشَدُّ مِنْهُم بَطْشًا فَنَقَّبُوا فِي الْبِلَادِ هَلْ مِن مَّحِيصٍ (36)
Kodi ndi mibadwo ingati imene Ife tidaiononga iwo asanabadwe amene adali ndi mphamvu zoposa iwo ndipo iwo adafuna chitetezo padziko? Kodi iwo anali ndi kwina kothawira
إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَذِكْرَىٰ لِمَن كَانَ لَهُ قَلْبٌ أَوْ أَلْقَى السَّمْعَ وَهُوَ شَهِيدٌ (37)
Ndithudi muli chikumbutso mu zimenezi kwa iye amene ali ndi mtima kapena amatchera khutu pamene achenjezedwa
وَلَقَدْ خَلَقْنَا السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضَ وَمَا بَيْنَهُمَا فِي سِتَّةِ أَيَّامٍ وَمَا مَسَّنَا مِن لُّغُوبٍ (38)
Ndithudi Ife tidalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo m’masiku asanu ndi limodzi ndipo sitidatope ayi
فَاصْبِرْ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَسَبِّحْ بِحَمْدِ رَبِّكَ قَبْلَ طُلُوعِ الشَّمْسِ وَقَبْلَ الْغُرُوبِ (39)
Kotero pirira pa zonse zimene amanena ndipo lemekeza Ambuye wako dzuwa lisanatuluke ndiponso lisanalowe
وَمِنَ اللَّيْلِ فَسَبِّحْهُ وَأَدْبَارَ السُّجُودِ (40)
Ndipo mulemekeze Iye usiku ndipo utatha kupemphera
وَاسْتَمِعْ يَوْمَ يُنَادِ الْمُنَادِ مِن مَّكَانٍ قَرِيبٍ (41)
Ndipo udzamve patsiku limene woitana adzaitana kuchokera pafupi
يَوْمَ يَسْمَعُونَ الصَّيْحَةَ بِالْحَقِّ ۚ ذَٰلِكَ يَوْمُ الْخُرُوجِ (42)
Tsiku limene iwo adzamva kulira kwa mfuwu woona. Limeneli lidzakhala tsiku louka kwa akufa
إِنَّا نَحْنُ نُحْيِي وَنُمِيتُ وَإِلَيْنَا الْمَصِيرُ (43)
Ndithudi ndife amene timapereka moyo ndi imfa ndipo ndi kwa Ife kumene zonse zidzabwerera
يَوْمَ تَشَقَّقُ الْأَرْضُ عَنْهُمْ سِرَاعًا ۚ ذَٰلِكَ حَشْرٌ عَلَيْنَا يَسِيرٌ (44)
Tsiku limene dziko lidzang’ambika ndipo iwo adzatuluka mofulumira. Kumeneko ndiko kudzakhala kusonkhanitsidwa pamodzi
نَّحْنُ أَعْلَمُ بِمَا يَقُولُونَ ۖ وَمَا أَنتَ عَلَيْهِم بِجَبَّارٍ ۖ فَذَكِّرْ بِالْقُرْآنِ مَن يَخَافُ وَعِيدِ (45)
Ife timadziwa zonse zimene amanena ndipo iwe si ndiwe wankhanza ayi. Koma muchenjeze ndi Korani kwa aliyense amene aopa chilango changa
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas