×

Surah Al-Mulk in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Mulk

Translation of the Meanings of Surah Mulk in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Mulk translated into Chichewa, Surah Al-Mulk in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Mulk in Chichewa - نيانجا, Verses 30 - Surah Number 67 - Page 562.

بسم الله الرحمن الرحيم

تَبَارَكَ الَّذِي بِيَدِهِ الْمُلْكُ وَهُوَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (1)
wodalitsika ndiye amene mmanja mwake muli Ufumu ndipo ali ndi mphamvu pa zinthu zonse
الَّذِي خَلَقَ الْمَوْتَ وَالْحَيَاةَ لِيَبْلُوَكُمْ أَيُّكُمْ أَحْسَنُ عَمَلًا ۚ وَهُوَ الْعَزِيزُ الْغَفُورُ (2)
Iye amene adalenga imfa ndi moyo kuti akhoza kukuyesani inu kuti ndani wa inu amene wasunga malamulo onse mwaubwino. Ndipo Iye ndi Wamphamvu ndi Wokhululukira
الَّذِي خَلَقَ سَبْعَ سَمَاوَاتٍ طِبَاقًا ۖ مَّا تَرَىٰ فِي خَلْقِ الرَّحْمَٰنِ مِن تَفَاوُتٍ ۖ فَارْجِعِ الْبَصَرَ هَلْ تَرَىٰ مِن فُطُورٍ (3)
Iye ndi amene adalenga miyamba isanu ndi iwiri, wina pamwamba pa unzake. Inu simungaone cholakwa china chilichonse mu chilengedwe cha Mwini chisoni chosatha. Tapenyetsetsani! Kodi inu mungaone cholakwika china chilichonse
ثُمَّ ارْجِعِ الْبَصَرَ كَرَّتَيْنِ يَنقَلِبْ إِلَيْكَ الْبَصَرُ خَاسِئًا وَهُوَ حَسِيرٌ (4)
Tapenyetsetsaninso! Ndipo mawonekedwe anu adzakubwererani pamene ali osokonezeka ndi otopa
وَلَقَدْ زَيَّنَّا السَّمَاءَ الدُّنْيَا بِمَصَابِيحَ وَجَعَلْنَاهَا رُجُومًا لِّلشَّيَاطِينِ ۖ وَأَعْتَدْنَا لَهُمْ عَذَابَ السَّعِيرِ (5)
Ndithudi Ife takongoletsa thambo loyamba ndi nyali ndipo tazipanga nyalizo ngati mipaliro yothamangitsira Satana ndipo tawakonzera iwo chilango chamoto woyaka
وَلِلَّذِينَ كَفَرُوا بِرَبِّهِمْ عَذَابُ جَهَنَّمَ ۖ وَبِئْسَ الْمَصِيرُ (6)
Ndipo iwo amene sakhulupirira mwa Ambuye wawo, kuli chilango cha kumoto ndipo chimaliziro chawo chidzakhala choipa
إِذَا أُلْقُوا فِيهَا سَمِعُوا لَهَا شَهِيقًا وَهِيَ تَفُورُ (7)
Ndipo pamene iwo adzaponyedwa m’moto, iwo adzaumva uli kuyaka ndi kubwata
تَكَادُ تَمَيَّزُ مِنَ الْغَيْظِ ۖ كُلَّمَا أُلْقِيَ فِيهَا فَوْجٌ سَأَلَهُمْ خَزَنَتُهَا أَلَمْ يَأْتِكُمْ نَذِيرٌ (8)
Pafupifupi kuphulika chifukwa cha kukwiya. Ndipo nthawi zonse pamene gulu liponyedwamo, amene amayang’anira moto adzafunsa kuti: “Kodi panalibe wina aliyense amene adadza kwa inu kudzakuchenjezani?”
قَالُوا بَلَىٰ قَدْ جَاءَنَا نَذِيرٌ فَكَذَّبْنَا وَقُلْنَا مَا نَزَّلَ اللَّهُ مِن شَيْءٍ إِنْ أَنتُمْ إِلَّا فِي ضَلَالٍ كَبِيرٍ (9)
Ndipo iwo adzati: “Inde. Ndithudi Mchenjezi adadza kwa ife koma tidamukana ndipo tinkati: Mulungu sadavumbulutse china chilichonse ndipo iwe ndiwe wosokoneza kwambiri.”
وَقَالُوا لَوْ كُنَّا نَسْمَعُ أَوْ نَعْقِلُ مَا كُنَّا فِي أَصْحَابِ السَّعِيرِ (10)
Ndipo iwo adzati: “Tikadakhala kuti tidamvera kapena kuganiza bwino, ife sitikadakhala m’gulu la anthu opita ku moto.”
فَاعْتَرَفُوا بِذَنبِهِمْ فَسُحْقًا لِّأَصْحَابِ السَّعِيرِ (11)
Motero iwo adzabvomera machimo awo. Motero apite kutali anthu a ku moto
إِنَّ الَّذِينَ يَخْشَوْنَ رَبَّهُم بِالْغَيْبِ لَهُم مَّغْفِرَةٌ وَأَجْرٌ كَبِيرٌ (12)
Ndithudi! Iwo amene amaopa Ambuye wawo ngakhale samuona, ndithudi, iwo adzawakhululukira machimo awo ndipo adzalandira mphotho ya mtengo wapatali
وَأَسِرُّوا قَوْلَكُمْ أَوِ اجْهَرُوا بِهِ ۖ إِنَّهُ عَلِيمٌ بِذَاتِ الصُّدُورِ (13)
Ndipo kaya mubisa mawu anu kapena muulula, Iye amadziwa zonse zimene zili m’mitima mwanu
أَلَا يَعْلَمُ مَنْ خَلَقَ وَهُوَ اللَّطِيفُ الْخَبِيرُ (14)
Kodi Iye amene adalenga zinthu zonse asadziwe? Ndithudi Iye ndi wa Chisoni chosatha ndi Mwini kudziwa chili chonse
هُوَ الَّذِي جَعَلَ لَكُمُ الْأَرْضَ ذَلُولًا فَامْشُوا فِي مَنَاكِبِهَا وَكُلُوا مِن رِّزْقِهِ ۖ وَإِلَيْهِ النُّشُورُ (15)
Iye ndiye amene anakukonzerani dziko, motero pitani paliponse mu ilo, ndipo idyani zokoma zake zimene wakupatsanindipondikwaIyekumenezonsezidzabwerera
أَأَمِنتُم مَّن فِي السَّمَاءِ أَن يَخْسِفَ بِكُمُ الْأَرْضَ فَإِذَا هِيَ تَمُورُ (16)
Kodi inu mumaganiza kuti ndinu wokhazikika moti Iye amene ali pamwamba pa kumwamba sangathe kung’amba nthaka imene ili pansi panu kuti ikumezeni? Taonani! Ili kugwedezeka
أَمْ أَمِنتُم مَّن فِي السَّمَاءِ أَن يُرْسِلَ عَلَيْكُمْ حَاصِبًا ۖ فَسَتَعْلَمُونَ كَيْفَ نَذِيرِ (17)
Kapena mumaganiza kuti inu ndinu okhazikika kuposa zimene zili kumwamba kuti Iye sangathe kukutumizirani mphepo ya mkuntho? Kotero inu mudzadziwa kuopsa kwa chenjezo langa
وَلَقَدْ كَذَّبَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ فَكَيْفَ كَانَ نَكِيرِ (18)
Ndithudi iwo amene adalipo kale anakana. Kodi chilango changa chinali bwanji
أَوَلَمْ يَرَوْا إِلَى الطَّيْرِ فَوْقَهُمْ صَافَّاتٍ وَيَقْبِضْنَ ۚ مَا يُمْسِكُهُنَّ إِلَّا الرَّحْمَٰنُ ۚ إِنَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ بَصِيرٌ (19)
Kodiiwosaonambalamezimenezimaulukapamwamba pawo, zikutambasula ndi kutseka mapiko awo? Palibe chimene chimazigwira kupatula Mwini chisoni chosatha. Ndithudi Iye amaona chilichonse
أَمَّنْ هَٰذَا الَّذِي هُوَ جُندٌ لَّكُمْ يَنصُرُكُم مِّن دُونِ الرَّحْمَٰنِ ۚ إِنِ الْكَافِرُونَ إِلَّا فِي غُرُورٍ (20)
Kodi ndani amene angakuthandizeni inu kupatula Mwini chisoni chosatha? Anthu onse osakhulupirira ndi olakwa
أَمَّنْ هَٰذَا الَّذِي يَرْزُقُكُمْ إِنْ أَمْسَكَ رِزْقَهُ ۚ بَل لَّجُّوا فِي عُتُوٍّ وَنُفُورٍ (21)
Kodi ndani amene angakupatseni chisamaliro ngati Iye atakaniza chisamaliro chake? Koma iwo amapitiriza kuchita mtudzu ndi kugalukira
أَفَمَن يَمْشِي مُكِبًّا عَلَىٰ وَجْهِهِ أَهْدَىٰ أَمَّن يَمْشِي سَوِيًّا عَلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (22)
Kodi iye amene amayenda osaona ndi ofanana ndi amene walangizidwa kapena amene amayenda mu njira yoyenera
قُلْ هُوَ الَّذِي أَنشَأَكُمْ وَجَعَلَ لَكُمُ السَّمْعَ وَالْأَبْصَارَ وَالْأَفْئِدَةَ ۖ قَلِيلًا مَّا تَشْكُرُونَ (23)
Nena: “Ndiye amene adakulengani inu ndipo adakupatsani makutu, maso ndi mitima. Inu simuthokoza kawirikawiri.”
قُلْ هُوَ الَّذِي ذَرَأَكُمْ فِي الْأَرْضِ وَإِلَيْهِ تُحْشَرُونَ (24)
Nena: “Ndiye amene anakulengani inu kuchokera ku doti ndipo kwa Iye nonse mudzasonkhanitsidwa.”
وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هَٰذَا الْوَعْدُ إِن كُنتُمْ صَادِقِينَ (25)
Iwo amati: “Kodi lonjezo limeneli lidzakwaniritsidwa liti ngati zimene ulikunena ndi zoona?”
قُلْ إِنَّمَا الْعِلْمُ عِندَ اللَّهِ وَإِنَّمَا أَنَا نَذِيرٌ مُّبِينٌ (26)
Nena: “Mulungu yekha ndiye amene adziwa nthawi yake. Ntchito yanga ndikungokuchenjezani basi.”
فَلَمَّا رَأَوْهُ زُلْفَةً سِيئَتْ وُجُوهُ الَّذِينَ كَفَرُوا وَقِيلَ هَٰذَا الَّذِي كُنتُم بِهِ تَدَّعُونَ (27)
Koma pamene iwo adzachiona chili nkudza pafupi, nkhope za anthu osakhulupirira zidzakhala za chisoni ndipo kudzanenedwa kuti: “Ichi ndi chimaliziro chimene munkafunsa kuti chidzafika liti?”
قُلْ أَرَأَيْتُمْ إِنْ أَهْلَكَنِيَ اللَّهُ وَمَن مَّعِيَ أَوْ رَحِمَنَا فَمَن يُجِيرُ الْكَافِرِينَ مِنْ عَذَابٍ أَلِيمٍ (28)
Nena: “Ndiuzeni! Kodi ngati Mulungu atandiononga ine pamodzi ndi iwo amene ali nane, ngakhale kuti Iye adzaonetsa chifundo pa ife, ndani amene angateteze anthu osakhulupirira ku chilango chowawa?”
قُلْ هُوَ الرَّحْمَٰنُ آمَنَّا بِهِ وَعَلَيْهِ تَوَكَّلْنَا ۖ فَسَتَعْلَمُونَ مَنْ هُوَ فِي ضَلَالٍ مُّبِينٍ (29)
Nena: “Iye ndi Mwini chifundo chosatha, mwa Iye ife timakhulupirira ndipo mwa Iye ife timaika chikhulupiriro chathu. Kotero inu mudzadziwa posachedwapa kuti ndani amene ali wochimwa.”
قُلْ أَرَأَيْتُمْ إِنْ أَصْبَحَ مَاؤُكُمْ غَوْرًا فَمَن يَأْتِيكُم بِمَاءٍ مَّعِينٍ (30)
Nena: “Ndiuzeni! Kodi ngati madzi anu ataphwa, ndani amene angakupatseni inu madzi oyenda?”
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas