×

Surah Al-Muzzammil in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Muzammil

Translation of the Meanings of Surah Muzammil in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Muzammil translated into Chichewa, Surah Al-Muzzammil in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Muzammil in Chichewa - نيانجا, Verses 20 - Surah Number 73 - Page 574.

بسم الله الرحمن الرحيم

يَا أَيُّهَا الْمُزَّمِّلُ (1)
Oh iwe amene wadzikulunga m’chovala
قُمِ اللَّيْلَ إِلَّا قَلِيلًا (2)
Dzuka usiku onse kupatula kwanthawi kochepa
نِّصْفَهُ أَوِ انقُصْ مِنْهُ قَلِيلًا (3)
Theka la usikuwo kapena kanthawi kocheperako
أَوْ زِدْ عَلَيْهِ وَرَتِّلِ الْقُرْآنَ تَرْتِيلًا (4)
Kapena kwa kanthawi kochulukirapo ndipo lakatula Korani modekha ndi modukizadukiza monga mmene umayenera kuchitikira
إِنَّا سَنُلْقِي عَلَيْكَ قَوْلًا ثَقِيلًا (5)
Ndithudi, Ife tidzakutumizira Mawu a mphamvu
إِنَّ نَاشِئَةَ اللَّيْلِ هِيَ أَشَدُّ وَطْئًا وَأَقْوَمُ قِيلًا (6)
Ndithudi kuuka nthawi ya usiku ndi kovuta, ndipo mau amatchulidwa bwino
إِنَّ لَكَ فِي النَّهَارِ سَبْحًا طَوِيلًا (7)
Ndithudi, iwe masana umatangwanika kwambiri
وَاذْكُرِ اسْمَ رَبِّكَ وَتَبَتَّلْ إِلَيْهِ تَبْتِيلًا (8)
Ndipo uzikumbukira dzina la Ambuye wako ndipo udzipereke kwathunthu kwa Iye
رَّبُّ الْمَشْرِقِ وَالْمَغْرِبِ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ فَاتَّخِذْهُ وَكِيلًا (9)
Iye ndiye Ambuye wa kum’mawa ndi wa kumadzulo. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Mulandire Iye kuti akhale Mtetezi wako
وَاصْبِرْ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَاهْجُرْهُمْ هَجْرًا جَمِيلًا (10)
Pirira pa zonse zimene ali kunena ndipo siyana nawo mwaulemu
وَذَرْنِي وَالْمُكَذِّبِينَ أُولِي النَّعْمَةِ وَمَهِّلْهُمْ قَلِيلًا (11)
Undisiyire Ine onse amene amakana choonadi nthawi zonse ndipo pirira ndi iwo pakanthawi kochepa
إِنَّ لَدَيْنَا أَنكَالًا وَجَحِيمًا (12)
Ife, ndithudi, tili ndi unyolo ndipo tawasungira moto wosatha kuuzima
وَطَعَامًا ذَا غُصَّةٍ وَعَذَابًا أَلِيمًا (13)
Ndi chakudya chotsamwitsa ndi chilango chowawa
يَوْمَ تَرْجُفُ الْأَرْضُ وَالْجِبَالُ وَكَانَتِ الْجِبَالُ كَثِيبًا مَّهِيلًا (14)
Patsiku limene dziko ndi mapiri zidzagwedezeka kwambiri ndipo mapiri adzakhala mulu wa mchenga wotaika umene umatuluka kupansi
إِنَّا أَرْسَلْنَا إِلَيْكُمْ رَسُولًا شَاهِدًا عَلَيْكُمْ كَمَا أَرْسَلْنَا إِلَىٰ فِرْعَوْنَ رَسُولًا (15)
Ndithudi Ife tatumiza Mtumwi kukhala umboni wokutsutsani monga momwe tidatumizira Mtumwi kwa Farao
فَعَصَىٰ فِرْعَوْنُ الرَّسُولَ فَأَخَذْنَاهُ أَخْذًا وَبِيلًا (16)
Koma Farao sadamumvere Mtumwi ndipo Ife tidamulanga ndi chilango choopsa
فَكَيْفَ تَتَّقُونَ إِن كَفَرْتُمْ يَوْمًا يَجْعَلُ الْوِلْدَانَ شِيبًا (17)
Kodi ngati inu simukhulupirira, mudzalithawa bwanji tsiku limene lidzachititsa ana anu a ang’ono kukhala ndi imvi
السَّمَاءُ مُنفَطِرٌ بِهِ ۚ كَانَ وَعْدُهُ مَفْعُولًا (18)
Tsiku limene thambo la kumwamba lidzang’ambika pakati. Ndithudi lonjezo la Mulungu lidzakwaniritsidwa
إِنَّ هَٰذِهِ تَذْكِرَةٌ ۖ فَمَن شَاءَ اتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِ سَبِيلًا (19)
Ndithudi ili ndi chenjezo chabe, motero musiyeni aliyense amene afuna kuti atsatire njira yoyenera yonka kwa Ambuye wake kuti aitsatire
۞ إِنَّ رَبَّكَ يَعْلَمُ أَنَّكَ تَقُومُ أَدْنَىٰ مِن ثُلُثَيِ اللَّيْلِ وَنِصْفَهُ وَثُلُثَهُ وَطَائِفَةٌ مِّنَ الَّذِينَ مَعَكَ ۚ وَاللَّهُ يُقَدِّرُ اللَّيْلَ وَالنَّهَارَ ۚ عَلِمَ أَن لَّن تُحْصُوهُ فَتَابَ عَلَيْكُمْ ۖ فَاقْرَءُوا مَا تَيَسَّرَ مِنَ الْقُرْآنِ ۚ عَلِمَ أَن سَيَكُونُ مِنكُم مَّرْضَىٰ ۙ وَآخَرُونَ يَضْرِبُونَ فِي الْأَرْضِ يَبْتَغُونَ مِن فَضْلِ اللَّهِ ۙ وَآخَرُونَ يُقَاتِلُونَ فِي سَبِيلِ اللَّهِ ۖ فَاقْرَءُوا مَا تَيَسَّرَ مِنْهُ ۚ وَأَقِيمُوا الصَّلَاةَ وَآتُوا الزَّكَاةَ وَأَقْرِضُوا اللَّهَ قَرْضًا حَسَنًا ۚ وَمَا تُقَدِّمُوا لِأَنفُسِكُم مِّنْ خَيْرٍ تَجِدُوهُ عِندَ اللَّهِ هُوَ خَيْرًا وَأَعْظَمَ أَجْرًا ۚ وَاسْتَغْفِرُوا اللَّهَ ۖ إِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (20)
NdithudiAmbuye wako amadziwa kuti nthawi zina iwe umakhala tcheru mphindi ziwiri pakati pa mphindi zitatu za usiku, mwina theka la usiku ndipo nthawi zina mphindi imodzi pakati pa mphindi zitatu za usiku, monga momwe gulu lina la anthu amene ali nawe. Ndipo Mulungu ndiye amene amasiyanitsa usiku ndi usana. Iye amadziwa kuti siungathe kupemphera mphindi zonse ndipo wakuyang’ana mwachisoni. Kotero lakatula magawo ena a Korani amene angakhale apafupi kwa iwe. Iye amadziwa kuti pakati panu pali anthu odwala ndi ena amene ali kupita uku ndi uku padziko kufunafuna zokoma za Mulungu ndi ena amene ali kumenya nkhondo m’njira ya Mulungu. Motero lakatula, mawu a m’Korani, amene ungathe kulakatula, ndipo pitiriza kupemphera ndipo pereka msonkho wothandiza anthu osauka ndipo kongoza ngongole yabwino kwa Mulungu ndipo chabwino chilichonse chimene muli kutsogoza, mudzachipeza kwa Mulungu, chitasungidwa bwino ndipo mudzalandira mphotho ya mtengo wapatali kuchokera kwa Iye. Ndipo pempha chikhululukiro kwa Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wa chisoni chosatha
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas