يَا أَيُّهَا الْمُزَّمِّلُ (1) Oh iwe amene wadzikulunga m’chovala |
قُمِ اللَّيْلَ إِلَّا قَلِيلًا (2) Dzuka usiku onse kupatula kwanthawi kochepa |
نِّصْفَهُ أَوِ انقُصْ مِنْهُ قَلِيلًا (3) Theka la usikuwo kapena kanthawi kocheperako |
أَوْ زِدْ عَلَيْهِ وَرَتِّلِ الْقُرْآنَ تَرْتِيلًا (4) Kapena kwa kanthawi kochulukirapo ndipo lakatula Korani modekha ndi modukizadukiza monga mmene umayenera kuchitikira |
إِنَّا سَنُلْقِي عَلَيْكَ قَوْلًا ثَقِيلًا (5) Ndithudi, Ife tidzakutumizira Mawu a mphamvu |
إِنَّ نَاشِئَةَ اللَّيْلِ هِيَ أَشَدُّ وَطْئًا وَأَقْوَمُ قِيلًا (6) Ndithudi kuuka nthawi ya usiku ndi kovuta, ndipo mau amatchulidwa bwino |
إِنَّ لَكَ فِي النَّهَارِ سَبْحًا طَوِيلًا (7) Ndithudi, iwe masana umatangwanika kwambiri |
وَاذْكُرِ اسْمَ رَبِّكَ وَتَبَتَّلْ إِلَيْهِ تَبْتِيلًا (8) Ndipo uzikumbukira dzina la Ambuye wako ndipo udzipereke kwathunthu kwa Iye |
رَّبُّ الْمَشْرِقِ وَالْمَغْرِبِ لَا إِلَٰهَ إِلَّا هُوَ فَاتَّخِذْهُ وَكِيلًا (9) Iye ndiye Ambuye wa kum’mawa ndi wa kumadzulo. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Mulandire Iye kuti akhale Mtetezi wako |
وَاصْبِرْ عَلَىٰ مَا يَقُولُونَ وَاهْجُرْهُمْ هَجْرًا جَمِيلًا (10) Pirira pa zonse zimene ali kunena ndipo siyana nawo mwaulemu |
وَذَرْنِي وَالْمُكَذِّبِينَ أُولِي النَّعْمَةِ وَمَهِّلْهُمْ قَلِيلًا (11) Undisiyire Ine onse amene amakana choonadi nthawi zonse ndipo pirira ndi iwo pakanthawi kochepa |
إِنَّ لَدَيْنَا أَنكَالًا وَجَحِيمًا (12) Ife, ndithudi, tili ndi unyolo ndipo tawasungira moto wosatha kuuzima |
وَطَعَامًا ذَا غُصَّةٍ وَعَذَابًا أَلِيمًا (13) Ndi chakudya chotsamwitsa ndi chilango chowawa |
يَوْمَ تَرْجُفُ الْأَرْضُ وَالْجِبَالُ وَكَانَتِ الْجِبَالُ كَثِيبًا مَّهِيلًا (14) Patsiku limene dziko ndi mapiri zidzagwedezeka kwambiri ndipo mapiri adzakhala mulu wa mchenga wotaika umene umatuluka kupansi |
إِنَّا أَرْسَلْنَا إِلَيْكُمْ رَسُولًا شَاهِدًا عَلَيْكُمْ كَمَا أَرْسَلْنَا إِلَىٰ فِرْعَوْنَ رَسُولًا (15) Ndithudi Ife tatumiza Mtumwi kukhala umboni wokutsutsani monga momwe tidatumizira Mtumwi kwa Farao |
فَعَصَىٰ فِرْعَوْنُ الرَّسُولَ فَأَخَذْنَاهُ أَخْذًا وَبِيلًا (16) Koma Farao sadamumvere Mtumwi ndipo Ife tidamulanga ndi chilango choopsa |
فَكَيْفَ تَتَّقُونَ إِن كَفَرْتُمْ يَوْمًا يَجْعَلُ الْوِلْدَانَ شِيبًا (17) Kodi ngati inu simukhulupirira, mudzalithawa bwanji tsiku limene lidzachititsa ana anu a ang’ono kukhala ndi imvi |
السَّمَاءُ مُنفَطِرٌ بِهِ ۚ كَانَ وَعْدُهُ مَفْعُولًا (18) Tsiku limene thambo la kumwamba lidzang’ambika pakati. Ndithudi lonjezo la Mulungu lidzakwaniritsidwa |
إِنَّ هَٰذِهِ تَذْكِرَةٌ ۖ فَمَن شَاءَ اتَّخَذَ إِلَىٰ رَبِّهِ سَبِيلًا (19) Ndithudi ili ndi chenjezo chabe, motero musiyeni aliyense amene afuna kuti atsatire njira yoyenera yonka kwa Ambuye wake kuti aitsatire |
۞ إِنَّ رَبَّكَ يَعْلَمُ أَنَّكَ تَقُومُ أَدْنَىٰ مِن ثُلُثَيِ اللَّيْلِ وَنِصْفَهُ وَثُلُثَهُ وَطَائِفَةٌ مِّنَ الَّذِينَ مَعَكَ ۚ وَاللَّهُ يُقَدِّرُ اللَّيْلَ وَالنَّهَارَ ۚ عَلِمَ أَن لَّن تُحْصُوهُ فَتَابَ عَلَيْكُمْ ۖ فَاقْرَءُوا مَا تَيَسَّرَ مِنَ الْقُرْآنِ ۚ عَلِمَ أَن سَيَكُونُ مِنكُم مَّرْضَىٰ ۙ وَآخَرُونَ يَضْرِبُونَ فِي الْأَرْضِ يَبْتَغُونَ مِن فَضْلِ اللَّهِ ۙ وَآخَرُونَ يُقَاتِلُونَ فِي سَبِيلِ اللَّهِ ۖ فَاقْرَءُوا مَا تَيَسَّرَ مِنْهُ ۚ وَأَقِيمُوا الصَّلَاةَ وَآتُوا الزَّكَاةَ وَأَقْرِضُوا اللَّهَ قَرْضًا حَسَنًا ۚ وَمَا تُقَدِّمُوا لِأَنفُسِكُم مِّنْ خَيْرٍ تَجِدُوهُ عِندَ اللَّهِ هُوَ خَيْرًا وَأَعْظَمَ أَجْرًا ۚ وَاسْتَغْفِرُوا اللَّهَ ۖ إِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (20) NdithudiAmbuye wako amadziwa kuti nthawi zina iwe umakhala tcheru mphindi ziwiri pakati pa mphindi zitatu za usiku, mwina theka la usiku ndipo nthawi zina mphindi imodzi pakati pa mphindi zitatu za usiku, monga momwe gulu lina la anthu amene ali nawe. Ndipo Mulungu ndiye amene amasiyanitsa usiku ndi usana. Iye amadziwa kuti siungathe kupemphera mphindi zonse ndipo wakuyang’ana mwachisoni. Kotero lakatula magawo ena a Korani amene angakhale apafupi kwa iwe. Iye amadziwa kuti pakati panu pali anthu odwala ndi ena amene ali kupita uku ndi uku padziko kufunafuna zokoma za Mulungu ndi ena amene ali kumenya nkhondo m’njira ya Mulungu. Motero lakatula, mawu a m’Korani, amene ungathe kulakatula, ndipo pitiriza kupemphera ndipo pereka msonkho wothandiza anthu osauka ndipo kongoza ngongole yabwino kwa Mulungu ndipo chabwino chilichonse chimene muli kutsogoza, mudzachipeza kwa Mulungu, chitasungidwa bwino ndipo mudzalandira mphotho ya mtengo wapatali kuchokera kwa Iye. Ndipo pempha chikhululukiro kwa Mulungu. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wa chisoni chosatha |