Quran with Chichewa translation - Surah Al-Muzzammil ayat 20 - المُزمل - Page - Juz 29
﴿۞ إِنَّ رَبَّكَ يَعۡلَمُ أَنَّكَ تَقُومُ أَدۡنَىٰ مِن ثُلُثَيِ ٱلَّيۡلِ وَنِصۡفَهُۥ وَثُلُثَهُۥ وَطَآئِفَةٞ مِّنَ ٱلَّذِينَ مَعَكَۚ وَٱللَّهُ يُقَدِّرُ ٱلَّيۡلَ وَٱلنَّهَارَۚ عَلِمَ أَن لَّن تُحۡصُوهُ فَتَابَ عَلَيۡكُمۡۖ فَٱقۡرَءُواْ مَا تَيَسَّرَ مِنَ ٱلۡقُرۡءَانِۚ عَلِمَ أَن سَيَكُونُ مِنكُم مَّرۡضَىٰ وَءَاخَرُونَ يَضۡرِبُونَ فِي ٱلۡأَرۡضِ يَبۡتَغُونَ مِن فَضۡلِ ٱللَّهِ وَءَاخَرُونَ يُقَٰتِلُونَ فِي سَبِيلِ ٱللَّهِۖ فَٱقۡرَءُواْ مَا تَيَسَّرَ مِنۡهُۚ وَأَقِيمُواْ ٱلصَّلَوٰةَ وَءَاتُواْ ٱلزَّكَوٰةَ وَأَقۡرِضُواْ ٱللَّهَ قَرۡضًا حَسَنٗاۚ وَمَا تُقَدِّمُواْ لِأَنفُسِكُم مِّنۡ خَيۡرٖ تَجِدُوهُ عِندَ ٱللَّهِ هُوَ خَيۡرٗا وَأَعۡظَمَ أَجۡرٗاۚ وَٱسۡتَغۡفِرُواْ ٱللَّهَۖ إِنَّ ٱللَّهَ غَفُورٞ رَّحِيمُۢ ﴾
[المُزمل: 20]
﴿إن ربك يعلم أنك تقوم أدنى من ثلثي الليل ونصفه وثلثه وطائفة﴾ [المُزمل: 20]
Khaled Ibrahim Betala “Ndithu Mbuye wako akudziwa kuti iwe ukuima (kupemphera) pafupifupi magawo awiri mwa magawo atatu a usiku kapena theka lake, kape’nanso gawo limodzi mwa magawo atatu a usiku, pamodzi ndi gulu la omwe uli nawo. Ndipo Allah ndi Amene amadziwa bwino muyeso wa (nthawi za) usiku ndi usana, wadziwa kuti simungathe kuwerengera zimenezo, choncho wakukhululukirani. Werengani ndime imene yapepuka yochokera m’Qur’an. Wadziwa kuti ena mwa inu adzakhala odwala; (kudzawavuta kuimilira ndi kuchezera usiku), ndipo ena adzakhala akuyendayenda pa dziko (ndi cholinga cha malonda ndi ntchito) kunka nafunafuna ubwino wa Allah. Ndipo ena adzakhala akumenya nkhondo pa njira ya Allah (ncholinga chotukula mawu Ake), werengani chimene chapepuka chochokera mmenemo (m’Qur’an). Ndipo pitirizani kupemphera Swala, perekani chopereka (chimene chakakamizidwa kwa inu). Ndipo mkongozeni Allah ngongole yabwino. Ndipo chilichonse chabwino chimene mwadzitsogozera mudzachipeza kwa Allah chili chabwino (kuposa zomwe mudazisiya m’mbuyo) ndi malipiro akulu zedi ndipo mpempheni Allah chikhululuko (pa uchimo wanu ndi chikhululuko pakunyozera kwanu kuchita zabwino). Ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha |