×

Surah Al-Jinn in Chichewa

Quran Chichewa ⮕ Surah Jinn

Translation of the Meanings of Surah Jinn in Chichewa - نيانجا

The Quran in Chichewa - Surah Jinn translated into Chichewa, Surah Al-Jinn in Chichewa. We provide accurate translation of Surah Jinn in Chichewa - نيانجا, Verses 28 - Surah Number 72 - Page 572.

بسم الله الرحمن الرحيم

قُلْ أُوحِيَ إِلَيَّ أَنَّهُ اسْتَمَعَ نَفَرٌ مِّنَ الْجِنِّ فَقَالُوا إِنَّا سَمِعْنَا قُرْآنًا عَجَبًا (1)
Nena: “Zavumbulutsidwa kwa ine kuti gulu la majini lidamvera chivumbulutso cha Mulungu ndipo lidati: Ndithudi ife tamva mawu odabwitsa.”
يَهْدِي إِلَى الرُّشْدِ فَآمَنَّا بِهِ ۖ وَلَن نُّشْرِكَ بِرَبِّنَا أَحَدًا (2)
“Amene apereka dongosolo la kunjira yoyenera ndipo ife takhulupirira zonse zimene zinali kunenedwa ndipo ife sitidzalambira wina aliyense kupatula Ambuye wathu.”
وَأَنَّهُ تَعَالَىٰ جَدُّ رَبِّنَا مَا اتَّخَذَ صَاحِبَةً وَلَا وَلَدًا (3)
‘Ulemerero ukhale kwa Ambuye wathu. Iye sadakwatire kapena kubereka ana
وَأَنَّهُ كَانَ يَقُولُ سَفِيهُنَا عَلَى اللَّهِ شَطَطًا (4)
‘Ndipo kuti anthu opusa amene ali pakati pathu akhala ali kumanenera Mulungu zinthu zonyasa kwambiri
وَأَنَّا ظَنَنَّا أَن لَّن تَقُولَ الْإِنسُ وَالْجِنُّ عَلَى اللَّهِ كَذِبًا (5)
‘Ndipo, ndithudi, ife timaganiza kuti kulibe munthu kapena majini amene angakanene chinthu chabodza chokhudza Mulungu
وَأَنَّهُ كَانَ رِجَالٌ مِّنَ الْإِنسِ يَعُوذُونَ بِرِجَالٍ مِّنَ الْجِنِّ فَزَادُوهُمْ رَهَقًا (6)
‘Ndipo, ndithudi, padali anthu pakati pa mtundu wa anthu amene amapeza chitetezo kuchokera kwa anthu a mtundu wa majinn. Koma iwo adangoonjezera kuchita zoipa ndi kusakhulupilira
وَأَنَّهُمْ ظَنُّوا كَمَا ظَنَنتُمْ أَن لَّن يَبْعَثَ اللَّهُ أَحَدًا (7)
‘Ndipo iwo adayamba kuganiza monga momwe inu mumaganizira, kuti Mulungu sadzadzutsa wina aliyense
وَأَنَّا لَمَسْنَا السَّمَاءَ فَوَجَدْنَاهَا مُلِئَتْ حَرَسًا شَدِيدًا وَشُهُبًا (8)
‘Ndipo ife tidafuna kupita kuthambo la pamwamba zedi ndipo tidaona kuti linali lodzadzidwa ndi ogwira ntchito a mphamvu ndi nyenyezi za moto
وَأَنَّا كُنَّا نَقْعُدُ مِنْهَا مَقَاعِدَ لِلسَّمْعِ ۖ فَمَن يَسْتَمِعِ الْآنَ يَجِدْ لَهُ شِهَابًا رَّصَدًا (9)
‘Ndithudi ife tinali Al Jinn 623 kukhala m’menemo kumvetsera koma amene azimvetsera tsopano, adzapeza malawi a moto uli kumudikira
وَأَنَّا لَا نَدْرِي أَشَرٌّ أُرِيدَ بِمَن فِي الْأَرْضِ أَمْ أَرَادَ بِهِمْ رَبُّهُمْ رَشَدًا (10)
‘Ife sitidziwa ngati akuwafunira mavuto anthu awo amene ali padziko lapansi kapena kuti Ambuye wawo ali ndi cholinga choti awatsogolere
وَأَنَّا مِنَّا الصَّالِحُونَ وَمِنَّا دُونَ ذَٰلِكَ ۖ كُنَّا طَرَائِقَ قِدَدًا (11)
‘Alipo ena pakati pathu amene ndi angwiro pamene ena ndi ochimwa. Ife ndife magulu otsatira njira zosiyanasiyana
وَأَنَّا ظَنَنَّا أَن لَّن نُّعْجِزَ اللَّهَ فِي الْأَرْضِ وَلَن نُّعْجِزَهُ هَرَبًا (12)
‘Ndipo ife timaganiza kuti sitingathawe Mulungu padziko lapansi ndiponso sitingathawe pothamangitsidwa
وَأَنَّا لَمَّا سَمِعْنَا الْهُدَىٰ آمَنَّا بِهِ ۖ فَمَن يُؤْمِن بِرَبِّهِ فَلَا يَخَافُ بَخْسًا وَلَا رَهَقًا (13)
‘Ndipo, ndithudi, pamene tidamva ulangizi wake, ife tidakhulupirira ndipo aliyense amene amakhulupirira mwa Ambuye wake sakhala ndi mantha otaya zake kapena kuponderezedwa
وَأَنَّا مِنَّا الْمُسْلِمُونَ وَمِنَّا الْقَاسِطُونَ ۖ فَمَنْ أَسْلَمَ فَأُولَٰئِكَ تَحَرَّوْا رَشَدًا (14)
‘Ndipo pakati pathu pali ena amene amadzipereka kwathunthu kwa Mulungu ndi ena amene amachita zoipa. Iwo amene adzipereka kwa Mulungu amatsatira njira yoyenera.”
وَأَمَّا الْقَاسِطُونَ فَكَانُوا لِجَهَنَّمَ حَطَبًا (15)
Ndipo iwo amene amachita zoipa adzakhala nkhuni za ku Gahena
وَأَن لَّوِ اسْتَقَامُوا عَلَى الطَّرِيقَةِ لَأَسْقَيْنَاهُم مَّاءً غَدَقًا (16)
Ngati iwo akanakhulupirira ndi kutsatira njira yoyenera, Ife, ndithudi, tikadawapatsa mvula yambiri
لِّنَفْتِنَهُمْ فِيهِ ۚ وَمَن يُعْرِضْ عَن ذِكْرِ رَبِّهِ يَسْلُكْهُ عَذَابًا صَعَدًا (17)
Kuti tikhoza kuwayesa ndi izo. Ndi aliyense amene samvera chenjezo la Ambuye wake. Iye adzakonza kuti alandire chilango chowawa zedi
وَأَنَّ الْمَسَاجِدَ لِلَّهِ فَلَا تَدْعُوا مَعَ اللَّهِ أَحَدًا (18)
Ndipo Mizikiti ndi ya Mulungu yekha. Motero musapembedze mulungu wina pambali pa Mulungu m’modzi yekha
وَأَنَّهُ لَمَّا قَامَ عَبْدُ اللَّهِ يَدْعُوهُ كَادُوا يَكُونُونَ عَلَيْهِ لِبَدًا (19)
Ndipo pamene kapolo wa Mulungu anaima kupempha kwa Iye, iwo adamuzungulira mu unyinji wawo mopanikizana
قُلْ إِنَّمَا أَدْعُو رَبِّي وَلَا أُشْرِكُ بِهِ أَحَدًا (20)
Nena: “Ine ndimapempha kwa Ambuye wanga ndipo sindimufanizira Iye ndi wina aliyense.”
قُلْ إِنِّي لَا أَمْلِكُ لَكُمْ ضَرًّا وَلَا رَشَدًا (21)
Nena: “Ine ndilibe mphamvu yobweretsa pa inu chinthu choipa kapena kukubweretsani ku njira yoyenera.”
قُلْ إِنِّي لَن يُجِيرَنِي مِنَ اللَّهِ أَحَدٌ وَلَنْ أَجِدَ مِن دُونِهِ مُلْتَحَدًا (22)
Nena: “Palibe wina aliyense amene anganditeteze ine kwa Mulungu ndipo ine sindingapeze kothawira kwina kulikonse kupatula kwa Iye yekha.”
إِلَّا بَلَاغًا مِّنَ اللَّهِ وَرِسَالَاتِهِ ۚ وَمَن يَعْصِ اللَّهَ وَرَسُولَهُ فَإِنَّ لَهُ نَارَ جَهَنَّمَ خَالِدِينَ فِيهَا أَبَدًا (23)
“Udindo wanga ndi kukuuzani choonadi chimene ndalandira kuchokera kwa Mulungu ndi Uthenga wake, ndipo aliyense amene amanyoza Mulungu ndi Mtumwi wake adzakhala ku moto wa ku Gahena nthawi zonse.”
حَتَّىٰ إِذَا رَأَوْا مَا يُوعَدُونَ فَسَيَعْلَمُونَ مَنْ أَضْعَفُ نَاصِرًا وَأَقَلُّ عَدَدًا (24)
Mpaka pamene iwo ataona kuopsa kwa chilango chimene chidalonjezedwa kuti chidzafika pa iwo, pamenepo ndipo pamene adzadziwa mbali imene wopanda mphamvu ali ndipo kuti ndi ayani amene anali wochepa m’chiwerengero
قُلْ إِنْ أَدْرِي أَقَرِيبٌ مَّا تُوعَدُونَ أَمْ يَجْعَلُ لَهُ رَبِّي أَمَدًا (25)
Nena: “Ine sindidziwa ngati chimene mwalonjezedwa chidzafika msanga kapena kuti Ambuye wangaadachiikapatali.”
عَالِمُ الْغَيْبِ فَلَا يُظْهِرُ عَلَىٰ غَيْبِهِ أَحَدًا (26)
Iyeyekhandiyeameneamadziwa zonse zobisika ndipo zinsinsi zake saululira wina aliyense ayi
إِلَّا مَنِ ارْتَضَىٰ مِن رَّسُولٍ فَإِنَّهُ يَسْلُكُ مِن بَيْنِ يَدَيْهِ وَمِنْ خَلْفِهِ رَصَدًا (27)
Kupatula kwa Atumwi ake amene Iye amawasankha yekha. Ndipo Iye amatumiza gulu la Atetezi amene amayenda patsogolo ndi pambuyo pawo
لِّيَعْلَمَ أَن قَدْ أَبْلَغُوا رِسَالَاتِ رَبِّهِمْ وَأَحَاطَ بِمَا لَدَيْهِمْ وَأَحْصَىٰ كُلَّ شَيْءٍ عَدَدًا (28)
Amawateteza mpaka pamene aona kuti iwo apereka uthenga wochokera kwa Ambuye wawo. Ndipo Iye amadziwa chili chonse chimene ali nacho ndipo Iye amasunga chiwerengero cha chinthu chili chonse
❮ Previous Next ❯

Surahs from Quran :

1- Fatiha2- Baqarah
3- Al Imran4- Nisa
5- Maidah6- Anam
7- Araf8- Anfal
9- Tawbah10- Yunus
11- Hud12- Yusuf
13- Raad14- Ibrahim
15- Hijr16- Nahl
17- Al Isra18- Kahf
19- Maryam20- TaHa
21- Anbiya22- Hajj
23- Muminun24- An Nur
25- Furqan26- Shuara
27- Naml28- Qasas
29- Ankabut30- Rum
31- Luqman32- Sajdah
33- Ahzab34- Saba
35- Fatir36- Yasin
37- Assaaffat38- Sad
39- Zumar40- Ghafir
41- Fussilat42- shura
43- Zukhruf44- Ad Dukhaan
45- Jathiyah46- Ahqaf
47- Muhammad48- Al Fath
49- Hujurat50- Qaf
51- zariyat52- Tur
53- Najm54- Al Qamar
55- Rahman56- Waqiah
57- Hadid58- Mujadilah
59- Al Hashr60- Mumtahina
61- Saff62- Jumuah
63- Munafiqun64- Taghabun
65- Talaq66- Tahrim
67- Mulk68- Qalam
69- Al-Haqqah70- Maarij
71- Nuh72- Jinn
73- Muzammil74- Muddathir
75- Qiyamah76- Insan
77- Mursalat78- An Naba
79- Naziat80- Abasa
81- Takwir82- Infitar
83- Mutaffifin84- Inshiqaq
85- Buruj86- Tariq
87- Al Ala88- Ghashiya
89- Fajr90- Al Balad
91- Shams92- Lail
93- Duha94- Sharh
95- Tin96- Al Alaq
97- Qadr98- Bayyinah
99- Zalzalah100- Adiyat
101- Qariah102- Takathur
103- Al Asr104- Humazah
105- Al Fil106- Quraysh
107- Maun108- Kawthar
109- Kafirun110- Nasr
111- Masad112- Ikhlas
113- Falaq114- An Nas