| إِذَا الشَّمْسُ كُوِّرَتْ (1) Pamene dzuwa lidzavundikiridwa
 | 
| وَإِذَا النُّجُومُ انكَدَرَتْ (2) Ndi pamene nyenyezi zidzagwa pansi
 | 
| وَإِذَا الْجِبَالُ سُيِّرَتْ (3) Ndi pamene mapiri adzachotsedwa
 | 
| وَإِذَا الْعِشَارُ عُطِّلَتْ (4) Ndi pamene ngamila zabele zizakhala zosasamalidwa
 | 
| وَإِذَا الْوُحُوشُ حُشِرَتْ (5) Ndi nyama za m’tchire zidzasonkhanitsidwa pamodzi
 | 
| وَإِذَا الْبِحَارُ سُجِّرَتْ (6) Ndi pamene nyanja zidzayatsidwa moto kapena zidzasefukira
 | 
| وَإِذَا النُّفُوسُ زُوِّجَتْ (7) Ndi pamene mizimu idzakumanitsidwa ndi matupi awo
 | 
| وَإِذَا الْمَوْءُودَةُ سُئِلَتْ (8) Ndi pamene mwana wa mkazi wa mng’ono, amene adaundilidwa wa moyo adzafunsidwa
 | 
| بِأَيِّ ذَنبٍ قُتِلَتْ (9) Chifukwa chimene anamuphera
 | 
| وَإِذَا الصُّحُفُ نُشِرَتْ (10) Ndi pamene mabuku olembamo ntchito za munthu aliyense adzatulutsidwa
 | 
| وَإِذَا السَّمَاءُ كُشِطَتْ (11) Ndi pamene kumwamba kudzafafanizidwa ndi kuchotsedwa ku malo ake
 | 
| وَإِذَا الْجَحِيمُ سُعِّرَتْ (12) Ndi pamene Gahena idzatenthetsedwa kwambiri
 | 
| وَإِذَا الْجَنَّةُ أُزْلِفَتْ (13) Ndi pamene Paradiso idzafikitsidwa pafupi
 | 
| عَلِمَتْ نَفْسٌ مَّا أَحْضَرَتْ (14) Ndithudi munthu aliyense adzadziwa chimene adachita
 | 
| فَلَا أُقْسِمُ بِالْخُنَّسِ (15) Motero, ndithudi, Ine ndili kulumbira pali nyenyezi zimene zimalowa
 | 
| الْجَوَارِ الْكُنَّسِ (16) Ndi pali maiko zimene zimayenda mofulumira ndi kudzibisa okha
 | 
| وَاللَّيْلِ إِذَا عَسْعَسَ (17) Ndi pali usiku pamene uchoka
 | 
| وَالصُّبْحِ إِذَا تَنَفَّسَ (18) Ndipalim’mawapamenekulikucha
 | 
| إِنَّهُ لَقَوْلُ رَسُولٍ كَرِيمٍ (19) Ndithudi awa ndi Mau a Mtumwi wolemekezeka
 | 
| ذِي قُوَّةٍ عِندَ ذِي الْعَرْشِ مَكِينٍ (20) Mwini mphamvu amene amalemekezedwa ndi Ambuye, Mwini Mpando wa Chifumu
 | 
| مُّطَاعٍ ثَمَّ أَمِينٍ (21) Amamveredwa ndi wokhulupirika
 | 
| وَمَا صَاحِبُكُم بِمَجْنُونٍ (22) Ndipo m’bale wanu uyu si wa misala ayi
 | 
| وَلَقَدْ رَآهُ بِالْأُفُقِ الْمُبِينِ (23) Ndipo, ndithudi, iye adamuona iye mu mlengalenga
 | 
| وَمَا هُوَ عَلَى الْغَيْبِ بِضَنِينٍ (24) Iye sabisa zinthu zosaoneka
 | 
| وَمَا هُوَ بِقَوْلِ شَيْطَانٍ رَّجِيمٍ (25) Ndipo zimene alankhula sizochokera kwa Satana wotembereredwa
 | 
| فَأَيْنَ تَذْهَبُونَ (26) Kodi inu muli kupita kuti
 | 
| إِنْ هُوَ إِلَّا ذِكْرٌ لِّلْعَالَمِينَ (27) Ndithudi ichi si china chilichonse ayi koma chikumbutso kwa anthu a mitundu yonse
 | 
| لِمَن شَاءَ مِنكُمْ أَن يَسْتَقِيمَ (28) Kwa aliyense wa inu amene afuna kuyenda moongoka
 | 
| وَمَا تَشَاءُونَ إِلَّا أَن يَشَاءَ اللَّهُ رَبُّ الْعَالَمِينَ (29) Koma inu simungathe kutero pokhapokha ndi chifuniro cha Mulungu, Ambuye wa zolengedwe zonse
 |