Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 164 - البَقَرَة - Page - Juz 2
﴿إِنَّ فِي خَلۡقِ ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِ وَٱخۡتِلَٰفِ ٱلَّيۡلِ وَٱلنَّهَارِ وَٱلۡفُلۡكِ ٱلَّتِي تَجۡرِي فِي ٱلۡبَحۡرِ بِمَا يَنفَعُ ٱلنَّاسَ وَمَآ أَنزَلَ ٱللَّهُ مِنَ ٱلسَّمَآءِ مِن مَّآءٖ فَأَحۡيَا بِهِ ٱلۡأَرۡضَ بَعۡدَ مَوۡتِهَا وَبَثَّ فِيهَا مِن كُلِّ دَآبَّةٖ وَتَصۡرِيفِ ٱلرِّيَٰحِ وَٱلسَّحَابِ ٱلۡمُسَخَّرِ بَيۡنَ ٱلسَّمَآءِ وَٱلۡأَرۡضِ لَأٓيَٰتٖ لِّقَوۡمٖ يَعۡقِلُونَ ﴾
[البَقَرَة: 164]
﴿إن في خلق السموات والأرض واختلاف الليل والنهار والفلك التي تجري في﴾ [البَقَرَة: 164]
Khaled Ibrahim Betala “Ndithudi, m’kulenga kwa thambo ndi nthaka, ndi kusinthana kwa usiku ndi usana, ndi (kuyenda kwa) zombo zikulu-zikulu zomwe zikuyenda pa nyanja (zitasenza zinthu) zothandiza anthu, ndi madzi amene Allah wawatsitsa kuchokera ku mitambo, naukitsira nawo nthaka pambuyo pokhala youma, nawanditsa m’menemo mtundu uliwonse wa nyama (chifukwa cha madziwo), ndi m’kusinthanasinthana kwa mphepo, ndi mitambo yomwe yalamulidwa kuyenda pakati pa thambo ndi nthaka; ndithudi, (m’mzimenezo) muli zisonyezo kwa anthu anzeru, (kuti Allah alipo) |