Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 178 - البَقَرَة - Page - Juz 2
﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ كُتِبَ عَلَيۡكُمُ ٱلۡقِصَاصُ فِي ٱلۡقَتۡلَىۖ ٱلۡحُرُّ بِٱلۡحُرِّ وَٱلۡعَبۡدُ بِٱلۡعَبۡدِ وَٱلۡأُنثَىٰ بِٱلۡأُنثَىٰۚ فَمَنۡ عُفِيَ لَهُۥ مِنۡ أَخِيهِ شَيۡءٞ فَٱتِّبَاعُۢ بِٱلۡمَعۡرُوفِ وَأَدَآءٌ إِلَيۡهِ بِإِحۡسَٰنٖۗ ذَٰلِكَ تَخۡفِيفٞ مِّن رَّبِّكُمۡ وَرَحۡمَةٞۗ فَمَنِ ٱعۡتَدَىٰ بَعۡدَ ذَٰلِكَ فَلَهُۥ عَذَابٌ أَلِيمٞ ﴾
[البَقَرَة: 178]
﴿ياأيها الذين آمنوا كتب عليكم القصاص في القتلى الحر بالحر والعبد بالعبد﴾ [البَقَرَة: 178]
Khaled Ibrahim Betala “E inu amene mwakhulupirira! Kwalamulidwa kwa inu Qiswas (kubwezerana) molingana kwa ophedwa; mfulu kwa mfulu, kapolo kwa kapolo, mkazi kwa mkazi. Koma amene wakhululukidwa ndi m’bale wakeyo pa chinthu Chilichonse, atsatire ndi kulonjelera dipolo mwaubwino. (Nayenso wolipa) apereke kwa iye mwa ubwino. Kumeneko ndikufewetsa kumene kwachokera kwa Mbuye wanu, ndiponso chifundo. Ndipo amene alumphe malire pambuyo pa izi, iye adzapeza chilango chopweteka |