Quran with Chichewa translation - Surah Al-Baqarah ayat 240 - البَقَرَة - Page - Juz 2
﴿وَٱلَّذِينَ يُتَوَفَّوۡنَ مِنكُمۡ وَيَذَرُونَ أَزۡوَٰجٗا وَصِيَّةٗ لِّأَزۡوَٰجِهِم مَّتَٰعًا إِلَى ٱلۡحَوۡلِ غَيۡرَ إِخۡرَاجٖۚ فَإِنۡ خَرَجۡنَ فَلَا جُنَاحَ عَلَيۡكُمۡ فِي مَا فَعَلۡنَ فِيٓ أَنفُسِهِنَّ مِن مَّعۡرُوفٖۗ وَٱللَّهُ عَزِيزٌ حَكِيمٞ ﴾
[البَقَرَة: 240]
﴿والذين يتوفون منكم ويذرون أزواجا وصية لأزواجهم متاعا إلى الحول غير إخراج﴾ [البَقَرَة: 240]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo mwa inu amene amwalira nasiya akazi awo, alangize (amlowam’malo awo, monga makolo ndi achibale) za akazi awo kuti awapatse zodyera m’nyengo ya chaka chimodzi popanda kutulutsidwa (m’nyumba zomwe ankakhala ndi amuna awo). Koma ngati akaziwo atuluka (okha), palibe kulakwa pa inu pa zimene adzichitira okha zomwe nzogwirizana ndi chilamulo cha Shariya. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya |