Quran with Chichewa translation - Surah An-Nur ayat 58 - النور - Page - Juz 18
﴿يَٰٓأَيُّهَا ٱلَّذِينَ ءَامَنُواْ لِيَسۡتَـٔۡذِنكُمُ ٱلَّذِينَ مَلَكَتۡ أَيۡمَٰنُكُمۡ وَٱلَّذِينَ لَمۡ يَبۡلُغُواْ ٱلۡحُلُمَ مِنكُمۡ ثَلَٰثَ مَرَّٰتٖۚ مِّن قَبۡلِ صَلَوٰةِ ٱلۡفَجۡرِ وَحِينَ تَضَعُونَ ثِيَابَكُم مِّنَ ٱلظَّهِيرَةِ وَمِنۢ بَعۡدِ صَلَوٰةِ ٱلۡعِشَآءِۚ ثَلَٰثُ عَوۡرَٰتٖ لَّكُمۡۚ لَيۡسَ عَلَيۡكُمۡ وَلَا عَلَيۡهِمۡ جُنَاحُۢ بَعۡدَهُنَّۚ طَوَّٰفُونَ عَلَيۡكُم بَعۡضُكُمۡ عَلَىٰ بَعۡضٖۚ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ ٱللَّهُ لَكُمُ ٱلۡأٓيَٰتِۗ وَٱللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٞ ﴾
[النور: 58]
﴿ياأيها الذين آمنوا ليستأذنكم الذين ملكت أيمانكم والذين لم يبلغوا الحلم منكم﴾ [النور: 58]
Khaled Ibrahim Betala “E inu amene mwakhulupirira! Akuodireni amene manja anu akumanja apeza ndi amene mwa inu sanathe nsinkhu, awodire nthawi zitatu: Isanapempheredwe Swala ya m’mawa, ndi pamene mukuvula nsalu zanu nthawi yamasana (kuti mupumule), ndi pambuyo pa Swala ya Isha (usiku). Izi ndi nthawi zitatu zomwe inu mumakhala wamba. Palibe uchimo pa inu ngakhale pa iwo pambuyo pa nthawi zimenezo (kulowa popanda kuodira); mumazungulirana pakati panu, umo ndi momwe akukufotokozerani Allah Ayah (ndime) Zake. Ndipo Allah Ngodziwa; Ngwanzeru zakuya |