×

سورة النور باللغة نيانجا

ترجمات القرآنباللغة نيانجا ⬅ سورة النور

ترجمة معاني سورة النور باللغة نيانجا - Chichewa

القرآن باللغة نيانجا - سورة النور مترجمة إلى اللغة نيانجا، Surah An Nur in Chichewa. نوفر ترجمة دقيقة سورة النور باللغة نيانجا - Chichewa, الآيات 64 - رقم السورة 24 - الصفحة 350.

بسم الله الرحمن الرحيم

سُورَةٌ أَنزَلْنَاهَا وَفَرَضْنَاهَا وَأَنزَلْنَا فِيهَا آيَاتٍ بَيِّنَاتٍ لَّعَلَّكُمْ تَذَكَّرُونَ (1)
Ife tavumbulutsa mutu uwu ndipo taupanga kukhala wokakamiza ndipo ndi mwa iwo mmene tavumbulutsa chivumbulutsochoonekakutiinumukhozakuchenjezedwa
الزَّانِيَةُ وَالزَّانِي فَاجْلِدُوا كُلَّ وَاحِدٍ مِّنْهُمَا مِائَةَ جَلْدَةٍ ۖ وَلَا تَأْخُذْكُم بِهِمَا رَأْفَةٌ فِي دِينِ اللَّهِ إِن كُنتُمْ تُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ وَالْيَوْمِ الْآخِرِ ۖ وَلْيَشْهَدْ عَذَابَهُمَا طَائِفَةٌ مِّنَ الْمُؤْمِنِينَ (2)
Munthu wamkazi wosakwatiwa akachita chigololo ndi munthu wamwamuna wosakwatira, mukwapule aliyense wa iwo zikoti zana limodzi ndipo musalole kuti chifundo chikulepheretseni kumvera lamulo la Mulungu ngati inu mumakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza. Ndipo onetsetsani kuti chilango chawo chachitidwa umboni ndi anthu ambiri okhulupirira
الزَّانِي لَا يَنكِحُ إِلَّا زَانِيَةً أَوْ مُشْرِكَةً وَالزَّانِيَةُ لَا يَنكِحُهَا إِلَّا زَانٍ أَوْ مُشْرِكٌ ۚ وَحُرِّمَ ذَٰلِكَ عَلَى الْمُؤْمِنِينَ (3)
Mwamuna wachigololo asakwatire wina koma mkazi wachigololo kapena mkazi wopembedza mafano. Mkazi wachigololo asakwatiwe ndi wina koma mwamuna wachigololo kapena wopembedza mafano. Anthu okhulupirira moona saloledwa maukwati otere
وَالَّذِينَ يَرْمُونَ الْمُحْصَنَاتِ ثُمَّ لَمْ يَأْتُوا بِأَرْبَعَةِ شُهَدَاءَ فَاجْلِدُوهُمْ ثَمَانِينَ جَلْدَةً وَلَا تَقْبَلُوا لَهُمْ شَهَادَةً أَبَدًا ۚ وَأُولَٰئِكَ هُمُ الْفَاسِقُونَ (4)
Iwo amene amanamizira akazi odzisunga kuti achita chigololo ndipo sangathe kutulutsa mboni zinayi, akwapulidwe zikoti makumi asanu ndi atatu. Mukane umboni wawo mpaka kalekale. Anthu otere ndi oononga
إِلَّا الَّذِينَ تَابُوا مِن بَعْدِ ذَٰلِكَ وَأَصْلَحُوا فَإِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (5)
Kupatulaokhawoamene, patapitanthawi, alapandikusiya makhalidwe awo onyansa. Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha
وَالَّذِينَ يَرْمُونَ أَزْوَاجَهُمْ وَلَمْ يَكُن لَّهُمْ شُهَدَاءُ إِلَّا أَنفُسُهُمْ فَشَهَادَةُ أَحَدِهِمْ أَرْبَعُ شَهَادَاتٍ بِاللَّهِ ۙ إِنَّهُ لَمِنَ الصَّادِقِينَ (6)
Ndipo ngati mwamuna akuti mkazi wake wachita chigololo koma alibe mboni kupatula iye mwini, iye alumbire kanayi dzina la Mulungu kuti zimene ali kunena ndi zoona
وَالْخَامِسَةُ أَنَّ لَعْنَتَ اللَّهِ عَلَيْهِ إِن كَانَ مِنَ الْكَاذِبِينَ (7)
Ndipo kachisanu anene kuti matemberero a Mulungu akhale pa iye mwamunayo ngati ali kunama
وَيَدْرَأُ عَنْهَا الْعَذَابَ أَن تَشْهَدَ أَرْبَعَ شَهَادَاتٍ بِاللَّهِ ۙ إِنَّهُ لَمِنَ الْكَاذِبِينَ (8)
Koma ngati mkazi wake alumbira kanayi, potchula dzina la Mulungu, kutsutsa kuti zimene ali kunena mwamuna wake ndi zabodza, sadzalandira chilango
وَالْخَامِسَةَ أَنَّ غَضَبَ اللَّهِ عَلَيْهَا إِن كَانَ مِنَ الصَّادِقِينَ (9)
Ndipo kachisanu ayenera kunena kuti mkwiyo wa Mulungu ukhale pa iye mkaziyo ngati ali kunama
وَلَوْلَا فَضْلُ اللَّهِ عَلَيْكُمْ وَرَحْمَتُهُ وَأَنَّ اللَّهَ تَوَّابٌ حَكِيمٌ (10)
Pakadapanda chisoni ndi chisomo cha Mulungu mukadaonongeka. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi waluntha
إِنَّ الَّذِينَ جَاءُوا بِالْإِفْكِ عُصْبَةٌ مِّنكُمْ ۚ لَا تَحْسَبُوهُ شَرًّا لَّكُم ۖ بَلْ هُوَ خَيْرٌ لَّكُمْ ۚ لِكُلِّ امْرِئٍ مِّنْهُم مَّا اكْتَسَبَ مِنَ الْإِثْمِ ۚ وَالَّذِي تَوَلَّىٰ كِبْرَهُ مِنْهُمْ لَهُ عَذَابٌ عَظِيمٌ (11)
Iwo amene adapeka nkhani yabodzayi, adali gulu la anthu anu omwe. Usaganize kuti ndi masoka koma ndi zabwino kwa inu. Aliyense adzalangidwa molingana ndi tchimo lake. Akakhala iye amene amaikulitsa nkhaniyi, chilango chake chidzakhala chowawa kwambiri
لَّوْلَا إِذْ سَمِعْتُمُوهُ ظَنَّ الْمُؤْمِنُونَ وَالْمُؤْمِنَاتُ بِأَنفُسِهِمْ خَيْرًا وَقَالُوا هَٰذَا إِفْكٌ مُّبِينٌ (12)
Pamenemudamvankhaniyi, bwanjianthuokhulupirira, amuna ndi akazi, sadafune kuganizira zabwino za anthu awo ndi kunena kuti, “Ili ndi bodza loonekera poyera?”
لَّوْلَا جَاءُوا عَلَيْهِ بِأَرْبَعَةِ شُهَدَاءَ ۚ فَإِذْ لَمْ يَأْتُوا بِالشُّهَدَاءِ فَأُولَٰئِكَ عِندَ اللَّهِ هُمُ الْكَاذِبُونَ (13)
Kodi ndi chifukwa chiyani iwo sadabweretse mboni zinayi? Ngati iwo adalephera kutulutsa mboni ndiye kuti iwo anali kunama pamaso pa Mulungu
وَلَوْلَا فَضْلُ اللَّهِ عَلَيْكُمْ وَرَحْمَتُهُ فِي الدُّنْيَا وَالْآخِرَةِ لَمَسَّكُمْ فِي مَا أَفَضْتُمْ فِيهِ عَذَابٌ عَظِيمٌ (14)
Kukadakhala kuti Mulungu sadaonetse chisomo ndi chifundo chake pa inu, m’moyo uno ndiponso m’moyo umene uli nkudza, mukadalangidwa kwambiri chifukwa cha zimene mwakhala mukuchita
إِذْ تَلَقَّوْنَهُ بِأَلْسِنَتِكُمْ وَتَقُولُونَ بِأَفْوَاهِكُم مَّا لَيْسَ لَكُم بِهِ عِلْمٌ وَتَحْسَبُونَهُ هَيِّنًا وَهُوَ عِندَ اللَّهِ عَظِيمٌ (15)
Pamene inu munali kunena ndi malirime anu ndiponso kuyankhula ndi pakamwa panu zinthu zimene simunali kuzidziwa, inu munali kuganiza kuti izi zidali zopepuka koma pamaso pa Mulungu zinali zazikulu
وَلَوْلَا إِذْ سَمِعْتُمُوهُ قُلْتُم مَّا يَكُونُ لَنَا أَن نَّتَكَلَّمَ بِهَٰذَا سُبْحَانَكَ هَٰذَا بُهْتَانٌ عَظِيمٌ (16)
Pamene mudazimva, bwanji inu simudanene kuti, “Si koyenera kuti ife tikambe izi ayi. Mulungu ayeretsedwe! Kumeneku ndiko kunama kwenikweni.”
يَعِظُكُمُ اللَّهُ أَن تَعُودُوا لِمِثْلِهِ أَبَدًا إِن كُنتُم مُّؤْمِنِينَ (17)
Mulungu ali kukuchenjezani kuti musadzachitenso izi ngati inu ndinu anthu okhulupirira m’choonadi
وَيُبَيِّنُ اللَّهُ لَكُمُ الْآيَاتِ ۚ وَاللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ (18)
Mulungu ali kukufotokozerani momveka chivumbulutso chake. Iye ndi wanzeru ndipo amadziwa zonse
إِنَّ الَّذِينَ يُحِبُّونَ أَن تَشِيعَ الْفَاحِشَةُ فِي الَّذِينَ آمَنُوا لَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ فِي الدُّنْيَا وَالْآخِرَةِ ۚ وَاللَّهُ يَعْلَمُ وَأَنتُمْ لَا تَعْلَمُونَ (19)
Iwo amene amasangalala kuti nkhani zoipa zokhudza anthu okhulupirira zifalikire, adzalangidwa kwambiri m’moyo umene uli nkudza. Mulungu ali kudziwa zonse pamene inu simudziwa
وَلَوْلَا فَضْلُ اللَّهِ عَلَيْكُمْ وَرَحْمَتُهُ وَأَنَّ اللَّهَ رَءُوفٌ رَّحِيمٌ (20)
Pakadakhala popanda chisomo cha Mulungu kwa inu, nonse mukanaonongedwa. Ndithudi Mulungu ndi wabwino ndiponso wachisoni
۞ يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَتَّبِعُوا خُطُوَاتِ الشَّيْطَانِ ۚ وَمَن يَتَّبِعْ خُطُوَاتِ الشَّيْطَانِ فَإِنَّهُ يَأْمُرُ بِالْفَحْشَاءِ وَالْمُنكَرِ ۚ وَلَوْلَا فَضْلُ اللَّهِ عَلَيْكُمْ وَرَحْمَتُهُ مَا زَكَىٰ مِنكُم مِّنْ أَحَدٍ أَبَدًا وَلَٰكِنَّ اللَّهَ يُزَكِّي مَن يَشَاءُ ۗ وَاللَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (21)
oh inu anthu okhulupirira m’choonadi! Musatsatire mapazi a Satana. Aliyense amene atsatira mapazi a Satana, ndithudi, iye amalamulira zinthu zochititsa manyazi ndi zoipa. Koma pakadapanda chisomo cha Mulungu, panalibe wina wa inu amene akadayeretsedwa zoipa zake. Koma Mulungu amayeretsa aliyense amene Iye wamufuna. Mulungu amamva zonse ndiponso amadziwa chinthu china chilichonse
وَلَا يَأْتَلِ أُولُو الْفَضْلِ مِنكُمْ وَالسَّعَةِ أَن يُؤْتُوا أُولِي الْقُرْبَىٰ وَالْمَسَاكِينَ وَالْمُهَاجِرِينَ فِي سَبِيلِ اللَّهِ ۖ وَلْيَعْفُوا وَلْيَصْفَحُوا ۗ أَلَا تُحِبُّونَ أَن يَغْفِرَ اللَّهُ لَكُمْ ۗ وَاللَّهُ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (22)
Musalole kuti anthu olemera ndi olemekezeka amene ali pakati panu kuti alumbire kuti sadzapereka chithandizo kwa abale awo, kwa anthu osauka ndiponso kwa iwo amene adathawa ku midzi yawo chifukwa cha nkhani zokhudza Mulungu. Iwo ayenera kuwakhululukira ndi kuwalekerera. Kodi inu simufuna kuti Mulungu akukhululukireni? Mulungu ndi Mwini chikhululukiro ndiponso Mwini chisoni chosatha
إِنَّ الَّذِينَ يَرْمُونَ الْمُحْصَنَاتِ الْغَافِلَاتِ الْمُؤْمِنَاتِ لُعِنُوا فِي الدُّنْيَا وَالْآخِرَةِ وَلَهُمْ عَذَابٌ عَظِيمٌ (23)
Onse amene amaipitsa mbiri ya akazi odzisunga ndiponso okhulupirira amene sachita zoipa, adzakhala otembereredwa m’dziko lino ndiponso mulimene lili nkudza. Chawo chidzakhala chilango choopsa
يَوْمَ تَشْهَدُ عَلَيْهِمْ أَلْسِنَتُهُمْ وَأَيْدِيهِمْ وَأَرْجُلُهُم بِمَا كَانُوا يَعْمَلُونَ (24)
Patsikuli malirime awo, manja awo, ndi miyendo yawo zidzachitira umboni pa zimene iwo anali kuchita
يَوْمَئِذٍ يُوَفِّيهِمُ اللَّهُ دِينَهُمُ الْحَقَّ وَيَعْلَمُونَ أَنَّ اللَّهَ هُوَ الْحَقُّ الْمُبِينُ (25)
Patsiku limeneli Mulungu adzawapatsa dipo lawo loyenera, ndipo iwo adzadziwa kuti Mulungu ndiye choonadi chenicheni
الْخَبِيثَاتُ لِلْخَبِيثِينَ وَالْخَبِيثُونَ لِلْخَبِيثَاتِ ۖ وَالطَّيِّبَاتُ لِلطَّيِّبِينَ وَالطَّيِّبُونَ لِلطَّيِّبَاتِ ۚ أُولَٰئِكَ مُبَرَّءُونَ مِمَّا يَقُولُونَ ۖ لَهُم مَّغْفِرَةٌ وَرِزْقٌ كَرِيمٌ (26)
Zinthu zodetsedwa ndi zoyenera anthu odetsedwa ndipo zinthu zosadetsedwa ndi za anthu osadetsedwa, ndiponso zinthu zabwino ndi zoyenera anthu abwino. Kotero anthu abwino ndi oyenera zinthu zabwino ndipo anthu otere sakhudzidwa ndi zimene akunena; iwowa adzakhululukidwa ndipo adzapatsidwa mphotho yolemekezeka
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لَا تَدْخُلُوا بُيُوتًا غَيْرَ بُيُوتِكُمْ حَتَّىٰ تَسْتَأْنِسُوا وَتُسَلِّمُوا عَلَىٰ أَهْلِهَا ۚ ذَٰلِكُمْ خَيْرٌ لَّكُمْ لَعَلَّكُمْ تَذَكَّرُونَ (27)
Oh inu anthu okhulupirira! Musalowe m’nyumba za anthu ena pokhapokha mutapempha chilolezo cha eni ake ndipo alonjereni powafunira iwo mtendere. Zimenezo ndi zabwino kwa inu kuti muchenjezedwe
فَإِن لَّمْ تَجِدُوا فِيهَا أَحَدًا فَلَا تَدْخُلُوهَا حَتَّىٰ يُؤْذَنَ لَكُمْ ۖ وَإِن قِيلَ لَكُمُ ارْجِعُوا فَارْجِعُوا ۖ هُوَ أَزْكَىٰ لَكُمْ ۚ وَاللَّهُ بِمَا تَعْمَلُونَ عَلِيمٌ (28)
Mukapeza kuti kulibe aliyense, musalowe mpaka pokhapokha mwapatsidwa chilolezo. Ngati akuuzani kuti mubwerere kapena musalowe, ndi chilungamo kuti inu mubwerere kupita komwe mwachokera. Zimenezo ndi zabwino kwa inu. Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita
لَّيْسَ عَلَيْكُمْ جُنَاحٌ أَن تَدْخُلُوا بُيُوتًا غَيْرَ مَسْكُونَةٍ فِيهَا مَتَاعٌ لَّكُمْ ۚ وَاللَّهُ يَعْلَمُ مَا تُبْدُونَ وَمَا تَكْتُمُونَ (29)
Sichidzakhala cholakwa ngati inu mulowa m’nyumba zopanda okhalamo zomwe muli nazo ndi ntchito. Mulungu amadziwa zonse zimene mumaulula ndi zimene mumabista
قُل لِّلْمُؤْمِنِينَ يَغُضُّوا مِنْ أَبْصَارِهِمْ وَيَحْفَظُوا فُرُوجَهُمْ ۚ ذَٰلِكَ أَزْكَىٰ لَهُمْ ۗ إِنَّ اللَّهَ خَبِيرٌ بِمَا يَصْنَعُونَ (30)
Auze amuna okhulupirira kuti azitsitsa maso awo ndi kulewa chigololo. Zimenezi ndizo zimene zidzayeretsa moyo wawo. Mulungu amadziwa zonse zimene mumachita
وَقُل لِّلْمُؤْمِنَاتِ يَغْضُضْنَ مِنْ أَبْصَارِهِنَّ وَيَحْفَظْنَ فُرُوجَهُنَّ وَلَا يُبْدِينَ زِينَتَهُنَّ إِلَّا مَا ظَهَرَ مِنْهَا ۖ وَلْيَضْرِبْنَ بِخُمُرِهِنَّ عَلَىٰ جُيُوبِهِنَّ ۖ وَلَا يُبْدِينَ زِينَتَهُنَّ إِلَّا لِبُعُولَتِهِنَّ أَوْ آبَائِهِنَّ أَوْ آبَاءِ بُعُولَتِهِنَّ أَوْ أَبْنَائِهِنَّ أَوْ أَبْنَاءِ بُعُولَتِهِنَّ أَوْ إِخْوَانِهِنَّ أَوْ بَنِي إِخْوَانِهِنَّ أَوْ بَنِي أَخَوَاتِهِنَّ أَوْ نِسَائِهِنَّ أَوْ مَا مَلَكَتْ أَيْمَانُهُنَّ أَوِ التَّابِعِينَ غَيْرِ أُولِي الْإِرْبَةِ مِنَ الرِّجَالِ أَوِ الطِّفْلِ الَّذِينَ لَمْ يَظْهَرُوا عَلَىٰ عَوْرَاتِ النِّسَاءِ ۖ وَلَا يَضْرِبْنَ بِأَرْجُلِهِنَّ لِيُعْلَمَ مَا يُخْفِينَ مِن زِينَتِهِنَّ ۚ وَتُوبُوا إِلَى اللَّهِ جَمِيعًا أَيُّهَ الْمُؤْمِنُونَ لَعَلَّكُمْ تُفْلِحُونَ (31)
Auze akazi okhulupirira kuti azitsitsa maso awo ndipo asachite chiwerewere ndiponso azibisa zinthu zimene zimawakongoletsa kupatula zokhazo zimene sizingabisike. Ndipo azifunda nsalu kumutu ndi pa chifuwa chawo ndiponso asaonetse kukongola kwawo kupatula kwa amuna awo, abambo awo, abambo a amuna awo, ana awo aamuna, ana a amuna awo, ana a chemwali awo kapena ana a achimwene awo kapena ana a alongo awo kapena akazi anzawo owakhulupirira; ndiponso antchito awo aakazi, a ntchito awo a amuna ndi ana amene alibe chilakolako cha akazi. Ndipo iwo asamamenyetse mapazi awo pansi akamayenda ndi cholinga choonetsa zina zokongola zawo zobisika. Oh inu okhulupirira! Lapani kwa Mulungu mogonja kuti mupambane
وَأَنكِحُوا الْأَيَامَىٰ مِنكُمْ وَالصَّالِحِينَ مِنْ عِبَادِكُمْ وَإِمَائِكُمْ ۚ إِن يَكُونُوا فُقَرَاءَ يُغْنِهِمُ اللَّهُ مِن فَضْلِهِ ۗ وَاللَّهُ وَاسِعٌ عَلِيمٌ (32)
Kwatiranani ndi iwo a pakati panu amene ndi osakwatiwa ndiponso akapolo anu aamuna kapena aakazi amene ali olungama. Ngati iwo ndi osauka, Mulungu adzawalemeretsa iwo kuchokera ku zabwino zake. Mulungu ndiye wopatsa ndi wodziwa
وَلْيَسْتَعْفِفِ الَّذِينَ لَا يَجِدُونَ نِكَاحًا حَتَّىٰ يُغْنِيَهُمُ اللَّهُ مِن فَضْلِهِ ۗ وَالَّذِينَ يَبْتَغُونَ الْكِتَابَ مِمَّا مَلَكَتْ أَيْمَانُكُمْ فَكَاتِبُوهُمْ إِنْ عَلِمْتُمْ فِيهِمْ خَيْرًا ۖ وَآتُوهُم مِّن مَّالِ اللَّهِ الَّذِي آتَاكُمْ ۚ وَلَا تُكْرِهُوا فَتَيَاتِكُمْ عَلَى الْبِغَاءِ إِنْ أَرَدْنَ تَحَصُّنًا لِّتَبْتَغُوا عَرَضَ الْحَيَاةِ الدُّنْيَا ۚ وَمَن يُكْرِههُّنَّ فَإِنَّ اللَّهَ مِن بَعْدِ إِكْرَاهِهِنَّ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (33)
onse amene sangathe kukwatira adzisunge mpaka pamene Mulungu awapatsa iwo zabwino zake. Akakhala a kapolo anu amene afuna kugula ufulu wawo, amasuleni ngati inu muona kuti iwo ndi abwino ndipo muwapatseko gawo la chuma chimene Mulungu wakupatsani inu. Inu musadzakakamize akapolo anu aakazi kuti azichita chiwerewere ngati iwo afuna kudzisunga ndi cholinga chofuna kupeza zinthu zabwino za padziko lapansi. Ngati wina aliyense awakakamiza iwo, Mulungu adzawakhululukira ndi kuonetsa chisoni chake pa iwo
وَلَقَدْ أَنزَلْنَا إِلَيْكُمْ آيَاتٍ مُّبَيِّنَاتٍ وَمَثَلًا مِّنَ الَّذِينَ خَلَوْا مِن قَبْلِكُمْ وَمَوْعِظَةً لِّلْمُتَّقِينَ (34)
Ife takutumizirani inu chivumbulutso chooneka bwino ndipo takupatsani chitsanzo cha anthu amene adalipo kale ndi chilangizo kwa anthu angwiro
۞ اللَّهُ نُورُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۚ مَثَلُ نُورِهِ كَمِشْكَاةٍ فِيهَا مِصْبَاحٌ ۖ الْمِصْبَاحُ فِي زُجَاجَةٍ ۖ الزُّجَاجَةُ كَأَنَّهَا كَوْكَبٌ دُرِّيٌّ يُوقَدُ مِن شَجَرَةٍ مُّبَارَكَةٍ زَيْتُونَةٍ لَّا شَرْقِيَّةٍ وَلَا غَرْبِيَّةٍ يَكَادُ زَيْتُهَا يُضِيءُ وَلَوْ لَمْ تَمْسَسْهُ نَارٌ ۚ نُّورٌ عَلَىٰ نُورٍ ۗ يَهْدِي اللَّهُ لِنُورِهِ مَن يَشَاءُ ۚ وَيَضْرِبُ اللَّهُ الْأَمْثَالَ لِلنَّاسِ ۗ وَاللَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (35)
Mulungu ndi Muuni wa kumwamba ndi dziko lapansi. Kuunika kwake kukhoza kufaniziridwa ndi malo olowa m’chipupa amene m’kati mwake muli nyali imene ili m’galasi looneka ngati nyenyezi yowala. Iyo imayatsidwa kuchokera ku mtengo wodalitsika wa Azitona umene siuli kum’mawa kapena kumadzulo. Mafuta ake amatha kuwala ngakhale kuti palibe moto owayakitsa mafutawo. Muuni pa Muuni unzake ndipo Mulungu amatsogolera, ndi kuwala kwake, aliyense amene Iye wamufuna. Mulungu amapereka zitsanzo kwa anthu. Ndipo Mulungu amadziwa chilichonse
فِي بُيُوتٍ أَذِنَ اللَّهُ أَن تُرْفَعَ وَيُذْكَرَ فِيهَا اسْمُهُ يُسَبِّحُ لَهُ فِيهَا بِالْغُدُوِّ وَالْآصَالِ (36)
M’nyumba zimene Mulungu adalamula kuti zimangidwe ndipo m’menemo dzina lake limakumbukirika, Mulungu amalemekezeka m’menemo m’mawa ndi madzulo
رِجَالٌ لَّا تُلْهِيهِمْ تِجَارَةٌ وَلَا بَيْعٌ عَن ذِكْرِ اللَّهِ وَإِقَامِ الصَّلَاةِ وَإِيتَاءِ الزَّكَاةِ ۙ يَخَافُونَ يَوْمًا تَتَقَلَّبُ فِيهِ الْقُلُوبُ وَالْأَبْصَارُ (37)
Pali anthu amene malonda kapena zogulitsa sizingathe kuwaiwalitsa kukumbukira Mulungu kapena kupemphera kapena kupereka msonkho wothandiza anthu osauka. Iwo amene amaopa tsiku limene mitima ndi maso adzatembenuka
لِيَجْزِيَهُمُ اللَّهُ أَحْسَنَ مَا عَمِلُوا وَيَزِيدَهُم مِّن فَضْلِهِ ۗ وَاللَّهُ يَرْزُقُ مَن يَشَاءُ بِغَيْرِ حِسَابٍ (38)
Kotero Mulungu adzawalipira chifukwa cha ntchito zawo zabwino ndiponso adzawapatsa zabwino zochokera m’chisomo chake. Mulungu amapereka mopanda muyeso kwa aliyense amene Iye wamufuna
وَالَّذِينَ كَفَرُوا أَعْمَالُهُمْ كَسَرَابٍ بِقِيعَةٍ يَحْسَبُهُ الظَّمْآنُ مَاءً حَتَّىٰ إِذَا جَاءَهُ لَمْ يَجِدْهُ شَيْئًا وَوَجَدَ اللَّهَ عِندَهُ فَوَفَّاهُ حِسَابَهُ ۗ وَاللَّهُ سَرِيعُ الْحِسَابِ (39)
Akakhala anthu osakhulupirira, ntchito zawo zili ngati chizirezire cha m’chipululu. Wapaulendo amene ali ndi ludzu amaganiza kuti ndi madzi koma akachiyandikira amaona kuti palibe chilichonse. Iye amamupeza Mulungu pomwepo amene amamupatsa molingana ndi ntchito zake. Mulungu amachita chiwerengero cha zinthu mofulumira
أَوْ كَظُلُمَاتٍ فِي بَحْرٍ لُّجِّيٍّ يَغْشَاهُ مَوْجٌ مِّن فَوْقِهِ مَوْجٌ مِّن فَوْقِهِ سَحَابٌ ۚ ظُلُمَاتٌ بَعْضُهَا فَوْقَ بَعْضٍ إِذَا أَخْرَجَ يَدَهُ لَمْ يَكَدْ يَرَاهَا ۗ وَمَن لَّمْ يَجْعَلِ اللَّهُ لَهُ نُورًا فَمَا لَهُ مِن نُّورٍ (40)
Kapena monga mdima wa m’nyanja yozama kwambiri yokutidwa ndi mafunde aakulu oyenda pamwamba pa mafunde anzake ndi mitambo pamwamba pake ndiponso mdima wosanjana ndi mdima unzake. Ndipo ngati iye atambasula dzanja lake sangathe kuliona. Ndithudi munthu amene saunikidwa ndi Mulungu sangathe kuona kuwala kwa mtundu wina uliwonse
أَلَمْ تَرَ أَنَّ اللَّهَ يُسَبِّحُ لَهُ مَن فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ وَالطَّيْرُ صَافَّاتٍ ۖ كُلٌّ قَدْ عَلِمَ صَلَاتَهُ وَتَسْبِيحَهُ ۗ وَاللَّهُ عَلِيمٌ بِمَا يَفْعَلُونَ (41)
Kodi iwe siunaone kuti zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko la pansi zimalemekeza Mulungu ndiponso pamene mbalame zikutambasula mapiko ake? Chilichonse chimadziwa mapemphero ndi mayamiko omupatsa Iye ndipo Mulungu amadziwa ntchito zawo zonse
وَلِلَّهِ مُلْكُ السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ وَإِلَى اللَّهِ الْمَصِيرُ (42)
Ndipo Mulungu ndiye mwini ufumu wa kumwamba ndi wa padziko lapansi. Ndi kwa Mulungu kumene zinthu zonse zidzabwerera
أَلَمْ تَرَ أَنَّ اللَّهَ يُزْجِي سَحَابًا ثُمَّ يُؤَلِّفُ بَيْنَهُ ثُمَّ يَجْعَلُهُ رُكَامًا فَتَرَى الْوَدْقَ يَخْرُجُ مِنْ خِلَالِهِ وَيُنَزِّلُ مِنَ السَّمَاءِ مِن جِبَالٍ فِيهَا مِن بَرَدٍ فَيُصِيبُ بِهِ مَن يَشَاءُ وَيَصْرِفُهُ عَن مَّن يَشَاءُ ۖ يَكَادُ سَنَا بَرْقِهِ يَذْهَبُ بِالْأَبْصَارِ (43)
Kodi inu simuona mmene Mulungu amayendetsera mitambo? Ndipo amaisonkhanitsira ndi kuiika m’gulu limodzi ndipo inu mumaona mvula ili kuchokera mu mitamboyo. Kuchokera ku mapiri a kumwamba, Iye amatumiza mphepo kuti ipeze kumupeza wina aliyense amene wamufuna ndi kusiya aliyense amene wamufuna. Chilangali cha mphenzi zake chimakhala pang’ono kuti chilande maso a anthu
يُقَلِّبُ اللَّهُ اللَّيْلَ وَالنَّهَارَ ۚ إِنَّ فِي ذَٰلِكَ لَعِبْرَةً لِّأُولِي الْأَبْصَارِ (44)
Mulungu amasanduliza usiku ndi usana. Ndithudi mu izi muli chizindikiro kwa anthu ozindikira
وَاللَّهُ خَلَقَ كُلَّ دَابَّةٍ مِّن مَّاءٍ ۖ فَمِنْهُم مَّن يَمْشِي عَلَىٰ بَطْنِهِ وَمِنْهُم مَّن يَمْشِي عَلَىٰ رِجْلَيْنِ وَمِنْهُم مَّن يَمْشِي عَلَىٰ أَرْبَعٍ ۚ يَخْلُقُ اللَّهُ مَا يَشَاءُ ۚ إِنَّ اللَّهَ عَلَىٰ كُلِّ شَيْءٍ قَدِيرٌ (45)
Mulungu adalenga cholengedwa chilichonse kuchokera ku madzi ndipo zina zimayenda chafufumimba, zina zimayenda ndi miyendo iwiri ndi zina zimayenda ndi miyendo inayi. Mulungu amalenga chilichonse chimene wafuna. Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse
لَّقَدْ أَنزَلْنَا آيَاتٍ مُّبَيِّنَاتٍ ۚ وَاللَّهُ يَهْدِي مَن يَشَاءُ إِلَىٰ صِرَاطٍ مُّسْتَقِيمٍ (46)
Ndithudi Ife tatumiza chivumbulutso choonetsa choonadi. Ndipo Mulungu amalangiza aliyense amene Iye wamufuna ku njira yoyenera
وَيَقُولُونَ آمَنَّا بِاللَّهِ وَبِالرَّسُولِ وَأَطَعْنَا ثُمَّ يَتَوَلَّىٰ فَرِيقٌ مِّنْهُم مِّن بَعْدِ ذَٰلِكَ ۚ وَمَا أُولَٰئِكَ بِالْمُؤْمِنِينَ (47)
Iwo amanena monenetsa kuti, “Ife timakhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo timawamvera onsewa.” Koma pambuyo pake ena a iwo amabwerera m’mbuyo. Ndithudi awa si okhulupirira ayi
وَإِذَا دُعُوا إِلَى اللَّهِ وَرَسُولِهِ لِيَحْكُمَ بَيْنَهُمْ إِذَا فَرِيقٌ مِّنْهُم مُّعْرِضُونَ (48)
Ndipo pamene iwo amaitanidwa kuti adze kwa Mulungu ndi Mtumwi wake, kuti akhoza kuwaweruza, ena amakana
وَإِن يَكُن لَّهُمُ الْحَقُّ يَأْتُوا إِلَيْهِ مُذْعِنِينَ (49)
Chikadakhala kuti choonadi chili mwa iwo, iwo akadadza kwa iye modzipereka
أَفِي قُلُوبِهِم مَّرَضٌ أَمِ ارْتَابُوا أَمْ يَخَافُونَ أَن يَحِيفَ اللَّهُ عَلَيْهِمْ وَرَسُولُهُ ۚ بَلْ أُولَٰئِكَ هُمُ الظَّالِمُونَ (50)
Kodi m’mitima mwawo muli matenda kapena ali ndi chikayiko? Kapena iwo amaopa kuti Mulungu ndi Mtumwi wake akhoza kuwakaniza chiweruzo cholungama? Koma oterewa ndi ochita zoipa
إِنَّمَا كَانَ قَوْلَ الْمُؤْمِنِينَ إِذَا دُعُوا إِلَى اللَّهِ وَرَسُولِهِ لِيَحْكُمَ بَيْنَهُمْ أَن يَقُولُوا سَمِعْنَا وَأَطَعْنَا ۚ وَأُولَٰئِكَ هُمُ الْمُفْلِحُونَ (51)
Koma pamene anthu okhulupirira enieni amaitanidwa kwa Mulungu ndi Mtumwi wake kuti akhoza kuwaweruza, yankho lawo limangokhala lakuti, “Tamva ndipo titsatira.” Anthu otere ndiwo opambana
وَمَن يُطِعِ اللَّهَ وَرَسُولَهُ وَيَخْشَ اللَّهَ وَيَتَّقْهِ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْفَائِزُونَ (52)
Ndipo iye amene amvera Mulungu ndi Mtumwi wake ndi kuopa Mulungu ndipo amadzichepetsa kwa Iye, oterewa ndi opambana
۞ وَأَقْسَمُوا بِاللَّهِ جَهْدَ أَيْمَانِهِمْ لَئِنْ أَمَرْتَهُمْ لَيَخْرُجُنَّ ۖ قُل لَّا تُقْسِمُوا ۖ طَاعَةٌ مَّعْرُوفَةٌ ۚ إِنَّ اللَّهَ خَبِيرٌ بِمَا تَعْمَلُونَ (53)
Iwo amalumbira pali Mulungu molimba kuti ngati iwe uwalamulira kumenya nkhondo, adzakumvera iwe. Nena “Musalumbire ayi! Chofunika ndi kumvera basi. Ndithudi Mulungu amadziwa chilichonse chimene mumachita.”
قُلْ أَطِيعُوا اللَّهَ وَأَطِيعُوا الرَّسُولَ ۖ فَإِن تَوَلَّوْا فَإِنَّمَا عَلَيْهِ مَا حُمِّلَ وَعَلَيْكُم مَّا حُمِّلْتُمْ ۖ وَإِن تُطِيعُوهُ تَهْتَدُوا ۚ وَمَا عَلَى الرَّسُولِ إِلَّا الْبَلَاغُ الْمُبِينُ (54)
Nena “Mverani Mulungu ndipo mverani Mtumwi wake. Ngati simungamvere, iye ali ndi udindo wake monga momwe inu muli ndi udindo wanu. Ngati inu mumumvera, inu mudzatsogozedwa ndipo udindo wa Mtumwi ndi kungopereka uthenga womveka.”
وَعَدَ اللَّهُ الَّذِينَ آمَنُوا مِنكُمْ وَعَمِلُوا الصَّالِحَاتِ لَيَسْتَخْلِفَنَّهُمْ فِي الْأَرْضِ كَمَا اسْتَخْلَفَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ وَلَيُمَكِّنَنَّ لَهُمْ دِينَهُمُ الَّذِي ارْتَضَىٰ لَهُمْ وَلَيُبَدِّلَنَّهُم مِّن بَعْدِ خَوْفِهِمْ أَمْنًا ۚ يَعْبُدُونَنِي لَا يُشْرِكُونَ بِي شَيْئًا ۚ وَمَن كَفَرَ بَعْدَ ذَٰلِكَ فَأُولَٰئِكَ هُمُ الْفَاسِقُونَ (55)
Mulungu walonjeza ena a inu amene akhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino kuti adzawasandutsa kukhala olowa m’malo padziko monga momwe adasandutsira anthu amene adalipo kale iwo asanadze. Ndipo Iye adzawapatsa mphamvu yoyendetsa chipembedzo chawo chimene adawasankhira. Ndithudi Iye adzawapatsa m’malo mwake chitetezo chokwana atawachokera mantha ngati iwo andipembedza Ine ndipo sandiphatikiza ndi china chilichonse. Ndipo onse amene sakhulupirira atamva izi ndi ochimwa
وَأَقِيمُوا الصَّلَاةَ وَآتُوا الزَّكَاةَ وَأَطِيعُوا الرَّسُولَ لَعَلَّكُمْ تُرْحَمُونَ (56)
Kwaniritsani mapemphero anu, perekani msonkho wothandiza osauka, ndipo muzimvera Mtumwi kuti mupeze chisomo cha Mulungu
لَا تَحْسَبَنَّ الَّذِينَ كَفَرُوا مُعْجِزِينَ فِي الْأَرْضِ ۚ وَمَأْوَاهُمُ النَّارُ ۖ وَلَبِئْسَ الْمَصِيرُ (57)
Musaganize kuti anthu osakhulupirira adzathawa mdziko lino. Moto ndi imene idzakhala mudzi wawo. Ndipo kutsiliza koipa
يَا أَيُّهَا الَّذِينَ آمَنُوا لِيَسْتَأْذِنكُمُ الَّذِينَ مَلَكَتْ أَيْمَانُكُمْ وَالَّذِينَ لَمْ يَبْلُغُوا الْحُلُمَ مِنكُمْ ثَلَاثَ مَرَّاتٍ ۚ مِّن قَبْلِ صَلَاةِ الْفَجْرِ وَحِينَ تَضَعُونَ ثِيَابَكُم مِّنَ الظَّهِيرَةِ وَمِن بَعْدِ صَلَاةِ الْعِشَاءِ ۚ ثَلَاثُ عَوْرَاتٍ لَّكُمْ ۚ لَيْسَ عَلَيْكُمْ وَلَا عَلَيْهِمْ جُنَاحٌ بَعْدَهُنَّ ۚ طَوَّافُونَ عَلَيْكُم بَعْضُكُمْ عَلَىٰ بَعْضٍ ۚ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ اللَّهُ لَكُمُ الْآيَاتِ ۗ وَاللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ (58)
oh inu anthu okhulupirira! Lolani akapolo anu aamuna ndi aakazi ndi ana amene sanathe msinkhu kuti apemphe poyamba pa nthawi zitatu, musadapemphere pemphero la m’mawa kapena pamene mwavula zovala zanu masana chifukwa cha kutentha kapena mutatha kupemphera mapemphero a usiku. Izi ndi nthawi zitatu zokhala panokha. Palibe chifukwa kwa inu kapena kwa iwo kuchezerana, wina ndi mnzake mu nthawi zina kupatula nthawi zimene zatchulidwazi. Kotero Mulungu amaulula poyera chivumbulutso chake kwa inu. Ndipo Mulungu ndi Wodziwa ndi Waluntha
وَإِذَا بَلَغَ الْأَطْفَالُ مِنكُمُ الْحُلُمَ فَلْيَسْتَأْذِنُوا كَمَا اسْتَأْذَنَ الَّذِينَ مِن قَبْلِهِمْ ۚ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ اللَّهُ لَكُمْ آيَاتِهِ ۗ وَاللَّهُ عَلِيمٌ حَكِيمٌ (59)
Ndipo pamene ana akula msinkhu, alekeni kuti apemphe chilolezo chanu monga akuluakulu awo amachitira. Kotero ndi mmene Mulungu amaululira chivumbulutso chake kwa inu. Ndipo Mulungu ndi wodziwa ndi waluntha
وَالْقَوَاعِدُ مِنَ النِّسَاءِ اللَّاتِي لَا يَرْجُونَ نِكَاحًا فَلَيْسَ عَلَيْهِنَّ جُنَاحٌ أَن يَضَعْنَ ثِيَابَهُنَّ غَيْرَ مُتَبَرِّجَاتٍ بِزِينَةٍ ۖ وَأَن يَسْتَعْفِفْنَ خَيْرٌ لَّهُنَّ ۗ وَاللَّهُ سَمِيعٌ عَلِيمٌ (60)
Sichidzakhala cholakwa kwa amayi okalamba amene alibe maganizo a ukwati ngati angasiye zovala zawo zakunja popanda kuonetsa kukongola kwawo. Kungakhale bwino ngati iwo angavale modzilemekeza. Ndipo Mulungu ndi wakumva ndi wodziwa
لَّيْسَ عَلَى الْأَعْمَىٰ حَرَجٌ وَلَا عَلَى الْأَعْرَجِ حَرَجٌ وَلَا عَلَى الْمَرِيضِ حَرَجٌ وَلَا عَلَىٰ أَنفُسِكُمْ أَن تَأْكُلُوا مِن بُيُوتِكُمْ أَوْ بُيُوتِ آبَائِكُمْ أَوْ بُيُوتِ أُمَّهَاتِكُمْ أَوْ بُيُوتِ إِخْوَانِكُمْ أَوْ بُيُوتِ أَخَوَاتِكُمْ أَوْ بُيُوتِ أَعْمَامِكُمْ أَوْ بُيُوتِ عَمَّاتِكُمْ أَوْ بُيُوتِ أَخْوَالِكُمْ أَوْ بُيُوتِ خَالَاتِكُمْ أَوْ مَا مَلَكْتُم مَّفَاتِحَهُ أَوْ صَدِيقِكُمْ ۚ لَيْسَ عَلَيْكُمْ جُنَاحٌ أَن تَأْكُلُوا جَمِيعًا أَوْ أَشْتَاتًا ۚ فَإِذَا دَخَلْتُم بُيُوتًا فَسَلِّمُوا عَلَىٰ أَنفُسِكُمْ تَحِيَّةً مِّنْ عِندِ اللَّهِ مُبَارَكَةً طَيِّبَةً ۚ كَذَٰلِكَ يُبَيِّنُ اللَّهُ لَكُمُ الْآيَاتِ لَعَلَّكُمْ تَعْقِلُونَ (61)
Si cholakwa ngati munthu wakhungu kapena wolumala kapena wodwala kapena inu eni ake mudya m’nyumba zanu kapena m’nyumba za atate anu kapena m’nyumba za amayi anu kapena m’nyumba za achimwene anu kapena m’nyumba za alongo anu kapena m’nyumba za achimwene a atate anu kapena alongo awo atate anu kapena m’nyumba za amalume anu kapena m’nyumba za achemwali a amayi anu kapena m’nyumba zimene makiyi ake mwasunga kapena aliyense m’nyumba za abwenzi anu. Palibe cholakwa kwa inu ngati mudya pamodzi kapena payekha payekha. Pamene mulowa m’nyumba, lonjeranani wina ndi mnzake malonje odalitsika ochokera kwa Mulungu. Kotero Mulungu ali kukufotokozerani zizindikiro kuti mukhoza kukhala ozindikira
إِنَّمَا الْمُؤْمِنُونَ الَّذِينَ آمَنُوا بِاللَّهِ وَرَسُولِهِ وَإِذَا كَانُوا مَعَهُ عَلَىٰ أَمْرٍ جَامِعٍ لَّمْ يَذْهَبُوا حَتَّىٰ يَسْتَأْذِنُوهُ ۚ إِنَّ الَّذِينَ يَسْتَأْذِنُونَكَ أُولَٰئِكَ الَّذِينَ يُؤْمِنُونَ بِاللَّهِ وَرَسُولِهِ ۚ فَإِذَا اسْتَأْذَنُوكَ لِبَعْضِ شَأْنِهِمْ فَأْذَن لِّمَن شِئْتَ مِنْهُمْ وَاسْتَغْفِرْ لَهُمُ اللَّهَ ۚ إِنَّ اللَّهَ غَفُورٌ رَّحِيمٌ (62)
Ndi okhawo amene ali ndi chikhulupiriro, amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo amati akasonkhana pamodzi ndi iye pa zinthu zofunika sachoka mpaka pamene apempha chilolezo chake. Ndithudi anthu amene amakupempha chilolezo ndiwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi Mtumwi wake. Pamene akupempha iwe chilolezo choti achoke ndi cholinga chokagwira ntchito zawo, pereka chilolezo kwa aliyense amene iwe wamufuna ndipo mumupemphe Mulungu kuti awakhululukire machimo awo. Mulungu amakhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha
لَّا تَجْعَلُوا دُعَاءَ الرَّسُولِ بَيْنَكُمْ كَدُعَاءِ بَعْضِكُم بَعْضًا ۚ قَدْ يَعْلَمُ اللَّهُ الَّذِينَ يَتَسَلَّلُونَ مِنكُمْ لِوَاذًا ۚ فَلْيَحْذَرِ الَّذِينَ يُخَالِفُونَ عَنْ أَمْرِهِ أَن تُصِيبَهُمْ فِتْنَةٌ أَوْ يُصِيبَهُمْ عَذَابٌ أَلِيمٌ (63)
Musamuitane Mtumwi pomutchula dzina monga momwe mumaitanirana wina ndi mnzake. Mulungu amadziwa ena a inu amene amazemba ndi kuchoka pakati panu. Aleke onse amene samvera Mtumwi kuti achenjere mwina mayesero kapena chilango chowawa chikhoza kugwa pa iwo
أَلَا إِنَّ لِلَّهِ مَا فِي السَّمَاوَاتِ وَالْأَرْضِ ۖ قَدْ يَعْلَمُ مَا أَنتُمْ عَلَيْهِ وَيَوْمَ يُرْجَعُونَ إِلَيْهِ فَيُنَبِّئُهُم بِمَا عَمِلُوا ۗ وَاللَّهُ بِكُلِّ شَيْءٍ عَلِيمٌ (64)
Ndithudi mwini wake wa chilichonse chimene chili kumwamba ndi dziko lapansi ndi Mulungu. Ndithudi Iye amadziwa zonse zimene zili m’mitima mwanu. Ndipo patsiku limene iwo adzabwerera kwa Iye, Iye adzawauza zonse zimene amachita. Ndipo Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse
❮ السورة السابقة السورة التـالية ❯

قراءة المزيد من سور القرآن الكريم :

1- الفاتحة2- البقرة3- آل عمران
4- النساء5- المائدة6- الأنعام
7- الأعراف8- الأنفال9- التوبة
10- يونس11- هود12- يوسف
13- الرعد14- إبراهيم15- الحجر
16- النحل17- الإسراء18- الكهف
19- مريم20- طه21- الأنبياء
22- الحج23- المؤمنون24- النور
25- الفرقان26- الشعراء27- النمل
28- القصص29- العنكبوت30- الروم
31- لقمان32- السجدة33- الأحزاب
34- سبأ35- فاطر36- يس
37- الصافات38- ص39- الزمر
40- غافر41- فصلت42- الشورى
43- الزخرف44- الدخان45- الجاثية
46- الأحقاف47- محمد48- الفتح
49- الحجرات50- ق51- الذاريات
52- الطور53- النجم54- القمر
55- الرحمن56- الواقعة57- الحديد
58- المجادلة59- الحشر60- الممتحنة
61- الصف62- الجمعة63- المنافقون
64- التغابن65- الطلاق66- التحريم
67- الملك68- القلم69- الحاقة
70- المعارج71- نوح72- الجن
73- المزمل74- المدثر75- القيامة
76- الإنسان77- المرسلات78- النبأ
79- النازعات80- عبس81- التكوير
82- الإنفطار83- المطففين84- الانشقاق
85- البروج86- الطارق87- الأعلى
88- الغاشية89- الفجر90- البلد
91- الشمس92- الليل93- الضحى
94- الشرح95- التين96- العلق
97- القدر98- البينة99- الزلزلة
100- العاديات101- القارعة102- التكاثر
103- العصر104- الهمزة105- الفيل
106- قريش107- الماعون108- الكوثر
109- الكافرون110- النصر111- المسد
112- الإخلاص113- الفلق114- الناس