Quran with Chichewa translation - Surah Al-Ahzab ayat 37 - الأحزَاب - Page - Juz 22
﴿وَإِذۡ تَقُولُ لِلَّذِيٓ أَنۡعَمَ ٱللَّهُ عَلَيۡهِ وَأَنۡعَمۡتَ عَلَيۡهِ أَمۡسِكۡ عَلَيۡكَ زَوۡجَكَ وَٱتَّقِ ٱللَّهَ وَتُخۡفِي فِي نَفۡسِكَ مَا ٱللَّهُ مُبۡدِيهِ وَتَخۡشَى ٱلنَّاسَ وَٱللَّهُ أَحَقُّ أَن تَخۡشَىٰهُۖ فَلَمَّا قَضَىٰ زَيۡدٞ مِّنۡهَا وَطَرٗا زَوَّجۡنَٰكَهَا لِكَيۡ لَا يَكُونَ عَلَى ٱلۡمُؤۡمِنِينَ حَرَجٞ فِيٓ أَزۡوَٰجِ أَدۡعِيَآئِهِمۡ إِذَا قَضَوۡاْ مِنۡهُنَّ وَطَرٗاۚ وَكَانَ أَمۡرُ ٱللَّهِ مَفۡعُولٗا ﴾
[الأحزَاب: 37]
﴿وإذ تقول للذي أنعم الله عليه وأنعمت عليه أمسك عليك زوجك واتق﴾ [الأحزَاب: 37]
Khaled Ibrahim Betala “Ndipo (kumbuka) pamene udamuuza yemwe Allah adampatsa mtendere (pomuongolera ku Chisilamu, ndipo) iwenso udampatsa mtendere (pomulera ndi kumpatsa ufulu, yemwe ndi Zaid Bun Haritha, udati kwa iye): “Gwirizana ndi mkazi wako, ndipo wopa Allah.” Ukubisa mu mtima mwako chimene Allah afuna kuchisonyeza poyera (chomwe ndi kuti Allah akulamula kumkwatira mkazi ameneyo akamuleka Zaid Bun Haritha kuti chichoke chizolowezi choti mwana wongomulera chabe nkumuyesa mwana wako weniweni). Ndipo ukuopa anthu (kuti akudzudzula pa zimenezo), pomwe woyenera kumuopa ndi Allah. Choncho pamene Zaid adamaliza chilakolako chake pa mkazi ameneyo, tidakukwatitsa iwe kuti pasakhale masautso pa okhulupirira pokwatira akazi a ana awo akungowalera chabe ngati (anawo) atamaliza zilakolako zawo pa akaziwo, ndipo lamulo la Allah ndilochitika, (palibe chingalepheretse kuti lisachitike) |